Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kunama—Kodi Nthaŵi Zina N’kolungama?

Kunama—Kodi Nthaŵi Zina N’kolungama?

Lingaliro la Baibulo

Kunama—Kodi Nthaŵi Zina N’kolungama?

“KUNAMA PANG’ONO NTHAŴI ZINA KUMATHANDIZA KUTI USAVUTIKE KULONGOSOLA ZAMBIRI.”

MAWU ameneŵa akusonyeza mmene anthu ambiri amaganizira pa nkhani ya kunama. Iwo amaganiza kuti kunama si kolakwa ngati sikukuvulaza wina aliyense. Malingaliro otere pa zamaphunziro ali ndi dzina lake, ndipo amatchedwa kuti chiphunzitso cha khalidwe labwino losinthasintha. Chiphunzitsochi chimanena kuti lamulo lokha loyenera kulitsatira n’lomwe amalitcha kuti lamulo lachikondi. Kapena kunena kuti, “ngati ukudzimva kuti zimene ukufuna kulankhula n’zoyenera ndiponso kuti zolinga zake n’zabwino (ndiye kuti) zoti kaya ukunama . . . zilibe ntchito,” anafotokoza motero wolemba mabuku wina dzina lake Diane Komp.

M’dziko lamakonoli, malingaliro otereŵa ali konsekonse. Nkhani zabodza zokambidwa ndi atsogoleri otchuka azandale ndiponso atsogoleri ena a mayiko zakhumudwitsa anthu. Mosonkhezeredwa ndi zimenezi, anthu ambiri akunyalanyaza kuti anatsimikiza mtima kuti adzanena zoona zokhazokha. M’madera ena kunama kwafikira pokhala lamulo la boma. “Ndimalipidwa kuti ndizinama. Ndimapambana mipikisano yazamalonda ndiponso amandiyamikira kwambiri chaka ndi chaka ngati n’tanena bodza. . . . Ameneŵa akuoneka kuti ndiwo maziko amaphunziro azamalonda kulikonse,” anadandaula motero wogulitsa malonda wina. Ambiri amakhulupirira kuti palibe vuto lenileni lokhudza kunama komwe amati n’kosavulaza. Koma kodi zimenezi n’zoona? Kodi pali zochitika zina pamene Akristu angaone kunama kuti n’kolungama?

Muyezo Wapamwamba wa Baibulo

Baibulo limaletsa mwamphamvu kunama kwa mtundu wina uliwonse. Wamasalmo ananena kuti, ‘[Mulungu] adzawononga iwo akunena bodza.’ (Salmo 5:6; onani Chivumbulutso 22:15.) Pa Miyambo 6:16-19, Baibulo limatchula zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene zimanyansa Yehova. “Lilime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza” ndizo zina mwa zinthu zikuluzikulu zotchulidwa pamenepa. Kodi n’chifukwa chiyani? N’chifukwa chakuti Yehova amadana ndi mavuto omwe amachitika chifukwa cha kunama. Chimenechi n’chimodzi mwa zifukwa zomwe Yesu anatchulira Satana kuti ndi wabodza komanso wambanda. Bodza lake linaloŵetsa mtundu wa anthu m’mavuto oopsa ndiponso imfa.—Genesis 3:4, 5; Yohane 8:44; Aroma 5:12.

Umboni wosonyeza mmene Yehova amaonera kuti kunama ndi nkhani yoopsa ukusonyezedwa ndi zimene zinachitikira Hananiya ndi Safira. Aŵiriŵa mwadala ananamiza atumwi poyesa kufuna kuoneka ngati anthu opatsa zedi kusiyana ndi momwe analili. Zimene anachita zinali zadala ndiponso zokonzekeredwa pasadakhale. Chotero mtumwi Petro ananena kuti: “Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.” Chifukwa cha zimenezi, onse aŵiri anafa m’dzanja la Mulungu.—Machitidwe 5:1-10.

Patapita zaka, mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Musamanamizana wina ndi mnzake.” (Akolose 3:9) Malangizo ameneŵa ali ofunika kwambiri makamaka mumpingo wachikristu. Yesu ananena kuti chikondi chalamulo chimenecho ndicho chizindikiro cha atumiki ake oona. (Yohane 13:34, 35) Chikondi chopanda chinyengo choterocho chingakule ndi kufalikira kokha ngati pali kuona mtima ndi kukhulupirika. N’kovuta kukonda munthu winawake ngati sitikutsimikiza kuti munthuyo adzatiuza zoona nthaŵi zonse.

Ngakhale kuti kunama kulikonse n’kosaloleka, kunama kwina n’koopsa moposerapo kwambiri. Mwachitsanzo, munthu wina anganame chifukwa cha mantha. Wina angakhale ndi chizoloŵezi choipa chonena zabodza n’cholinga chofuna kuika ena m’mavuto kapena kuwavulaza. Chifukwa cha mtima wake woyambanitsa anthu, munthu wabodza wotere n’ngoopsa kwambiri ndipo angachotsedwe mumpingo ngati sakulapa. Pokhala kuti si mabodza onse amene amanenedwa n’cholinga cha kufuna kuyambanitsa anthu, tiyenera kusamala kuti tisaweruze mosaganizira koma kuyamba kaye tatsimikiza kuti tikudziŵa bwino mmene nkhani yonse yayendera pamene winawake wanena zabodza. Zolinga zake ndiponso zomwe zam’chititsa kunama ziyenera kulingaliridwa.—Yakobo 2:13.

“Ochenjera Monga Njoka”

N’zoona kuti, kukhala wokhulupirika sikutanthauza kuti tiyenera kuulula nkhani iliyonse kwa aliyense amene watifunsa. Pa Mateyu 7:6 Yesu anachenjeza kuti, “Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti . . . potembenuka zingang’ambe inu.” Mwachitsanzo, anthu a zolinga zoipa angakhale osayenera kuti adziŵe zinthu zina. Akristu akudziŵa kuti akukhala m’dziko laupandu. N’chifukwa chake Yesu analangiza ophunzira ake kuti akhale “ochenjera monga njoka” kwinaku akukhalabe “oona mtima monga nkhunda.”(Mateyu 10:16; Yohane 15:19) Yesu sanaulule nthaŵi zonse choonadi chonse, makamaka pamene kuulula mfundo zimenezo kudakaika iye mwini ndiponso ophunzira ake pa vuto loti akanatha kulipeŵa. Komabe, ngakhale pa nthaŵi ngati zimenezo iye sananene bodza. M’malomwake, anasankha kukhala chete kapena kusinthira zokambiranazo ku nkhani ina.—Mateyu 15:1-6; 21:23-27; Yohane 7:3-10.

Amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo monga Abrahamu, Isake, Rahabi, ndi Davide, nawonso anali ochenjera ndi osamala pamene ankachita zinthu ndi adani. (Genesis 20:11-13; 26:9; Yoswa 2:1-6; 1 Samueli 21:10-14) Baibulo limatchula amuna ndi akazi ameneŵa kukhala alambiri okhulupirika amene miyoyo yawo inadziŵika chifukwa cha kumvera. Zimenezi zimawachititsa kukhala oyeneradi kuwatsanzira.—Aroma 15:4; Ahebri 11:8-10, 20, 31, 32-39.

Mwina nthaŵi zina kunama kungaoneke monga njira yapafupi yothaŵira mavuto. Koma Akristu lerolino amachita bwino kutsanzira njira ya moyo ya Yesu ndiponso chikumbumtima choyera chozikidwa m’Baibulo pamene akumana ndi mikhalidwe yovuta.—Ahebri 5:14.

Baibulo limatilimbikitsa kukhala okhulupirika ndi oona mtima. Kunama n’kulakwa, ndipo tiyenera kutsanzira uphungu wa Baibulo wakuti: “Lankhulani zoona yense ndi mnzake.” (Aefeso 4:25) Mwa kuchita zimenezo, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera, kulimbikitsa mtendere ndiponso chikondi mumpingo, komanso tidzapitiriza kulemekeza “Mulungu wa choonadi.”—Salmo 31:5; Ahebri 13:18.

[Chithunzi patsamba 26]

Hananiya ndi Safira anataya moyo wawo chifukwa cha kunama