Kusiyana Pakati pa Olemera ndi Osauka Kukukula
Kusiyana Pakati pa Olemera ndi Osauka Kukukula
“Ntchito yochepetsa umphaŵi padziko lonse yapita patsogolo kwambiri m’zaka makumi asanu zapitazi kusiyana ndi m’zaka mazana asanu zam’mbuyomo,” inatero Magazini yotchedwa UNDP Today, yofalitsidwa ndi nthambi ya bungwe la United Nations yoyang’anira za chitukuko ya United Nations Development Programme. Mayiko amene akutukuka kumene achepetsa chiŵerengero cha ana akufa ndi theka chiyambire 1960. Ndiponso, achepetsa chiŵerengero cha anthu odwala matenda osoŵa zakudya m’thupi ndi munthu m’modzi mwa anthu atatu alionse, komanso chiŵerengero cha ana opita kusukulu chakwera ndi mwana m’modzi mwa ana asanu alionse.” Komabe, magazini omweŵa akuvomereza kuti ngakhale kuti pali kupita patsogolo kotereku, umphaŵi padziko lapansi “udakali konsekonse.”
Choipa koposa n’chakuti, kusoŵa chilungamo pakati pa anthu kukukula. Catherine Bertini, mkulu wa nthambi ya bungwe la United Nations yoona za chakudya ya World Food Programme ananena kuti, “poyerekeza ndi m’chaka chimodzi chapitacho, anthu ena ambiri padziko lonse akudwala matenda a kusoŵa zakudya m’thupi komanso njala.” Ndiponso, masiku ano anthu ena 840 miliyoni a m’mayiko omwe akutukuka kumene amakhala ndi njala nthaŵi zonse. Anthu enanso oposa biliyoni imodzi alibe madzi abwino akumwa, ndipo enanso pafupifupi biliyoni imodzi ndi theka akukhala ndi moyo pogwiritsa ntchito ndalama zosakwana dola imodzi patsiku. Mary Robinson, mkulu wa nthambi ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe la United Nations High Commission for Human Rights anachenjeza kuti, “tili pangozi yakuti mayiko adzagaŵikana osati kuti ena adzakhala otukuka ndi enawo ongotukuka kumene, koma kuti ena adzakhala otukuka kwambiri ndipo enawo sadzatukuka n’komwe.”
Kodi ndi ndalama zochuluka motani zimene anthu mabiliyoni asanu ndi limodzi a padziko lonse angawononge kuti achepetse kusiyana pakati pa olemera ndi aumphaŵi? N’zochepa zedi kuyerekeza ndi zimene mungaganizire. Bungwe la United Nations linaŵerengera kuti pangafunike ndalama zowonjezera zokwana madola 9 biliyoni (madola 1.50 munthu aliyense) pa chaka kuti anthu padziko lonse akhale aukhondo ndiponso kuti akhale ndi madzi abwino. Padzafunika ndalama zowonjezera zokwana madola 13 biliyoni (pafupifupi madola 2.00 munthu aliyense) pa chaka kuti anthu padziko lonse lapansi akhale athanzi ndiponso kuti apeze chakudya. Ngakhale kuti ndalamazi n’zochulukadi, zikuoneka kuti n’zochepa zedi poyerekeza ndi ndalama zimene dziko limagwiritsa ntchito pa zinthu zina. Mwachitsanzo, m’chaka chimodzi chaposachedwa, dziko linawononga ndalama zokwana madola 435 biliyoni (kuposa madola 70 munthu aliyense) pa ntchito yotsatsa malonda, ndiponso linasakaza ndalama zokwana madola 780 biliyoni (kuposa madola 130 munthu aliyense) pa nkhani za nkhondo. Mwachionekere, vuto la kuchepetsa kusiyana pakati pa osauka ndi olemera si kusoŵa kwa ndalama zokwanira, koma kuti nkhani yagona pa kusankha zinthu zofunika.