Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Vuto la Mabanja Opanda Bambo—Lingathetsedwere

Mmene Vuto la Mabanja Opanda Bambo—Lingathetsedwere

Mmene Vuto la Mabanja Opanda Bambo—Lingathetsedwere

NGATI zinthu zipitirire chonchi, posachedwa mabanja opanda bambo ndiwo akhale chizoloŵezi. Lipoti la Dipatimenti ya Umoyo ndi Kuthandiza Anthu ku United States linati: “Ana oleredwa ndi kholo limodzi nthaŵi zambiri sakhoza m’kalasi, amakhala ndi khalidwe lovuta, ndipo ndiwo amadwala kaŵirikaŵiri matenda aakulu ndi matenda okhudza bongo. . . . Kuleredwa m’banja lokhala ndi mayi okha kumachulukitsa achinyamata obereka ana, osiya sukulu, [ndiponso] omangidwa.”

Choncho, n’zosadabwitsa kuti akatswiri a sayansi ya zakakhalidwe ka anthu, ankhoswe, aphunzitsi, ndipo ngakhale andale akufunitsitsa kupeza njira zothetsera vuto lowonongali. Misonkhano ikuluikulu yakhala ikuchitidwa kaamba ka amuna kuti azinyadira kukhala bambo ndi kuti azichita udindo wawo wam’banja. Mabuku onena za kukhala bambo akugulitsidwa paliponse. Ndiponso anthu ayesa kukakamiza abambo kuti asamalire maudindo awo. Ku United States, abambo olephera kuthandiza ana awo akhala akudzudzulidwa ndi oŵeruza, kunyozedwa pa pulogalamu yofunsa mafunso anthu otchuka pa TV, ndiponso kuchititsidwa manyazi pagulu. Komabe, zimenezi sizinathandize.

Njira Zachidule

Njira yachidule nayo ingakhale ndi zotsatira zokayikitsa. Mwachitsanzo, mayi wosudzulidwa angathe kukwatiwanso mwamsanga, poganiza kuti akatero ana ake akhala ndi bambo watsopano. Komabe ngakhale kuti kukwatiranso kungakhale ndi ubwino wake, pangabuke mavuto. Nthaŵi zina ana safuna kuvomereza munthu wina watsopano kukhala bambo wawo. Nthaŵi zina satero n’komwe. Kafukufuku wina anasonyeza kuti “pafupifupi aŵiri mwa amayi atatu alionse amene anakhalapo ndi bambo wowapeza anachoka kunyumba asanafike zaka 19 . . . , poyerekeza ndi amayi 50 mwa 100 alionse ochokera m’mabanja abwinobwino.” Ngakhale m’mabanja opeza oyenda bwino, nthaŵi zina pamatha zaka zingapo bambo wopeza asanavomerezedwe ndi ana. *

Mofananamo, palibe njira zachidule zothetsera vuto la kutenga mimba kwa atsikana. Mwachitsanzo, kuchotsa mimba, kumaphwanya lamulo la Mulungu ndipo kumachititsa kuti mtsikana akane kusonyeza chikondi chake kwa kakhanda kamoyo kamene kakukula m’mimba mwake. (Eksodo 20:13; 21:22, 23; Salmo 139:14-16; yerekezerani ndi 1 Yohane 3:17.) Kodi nanga zimenezi sizingasiye mabala m’maganizo? Kupereka mwana kwa munthu wina ena amakuona monga njira yachifundo, komabe nayonso ingathe kusiya mabala a m’maganizo; kwa mayiyo ndiponso kwa mwana.

Ayi ndithu, njira zachidule sizingathetse vuto la mabanja opanda bambo. Mavuto amene alipo m’mabanja adzathetsedwa kokha ngati anthu ali ofunitsitsa kusinthadi maganizo awo, kaonedwe kawo ka zinthu, zochita zawo, ndi makhalidwe awo. Kuti anthu asinthe kwambiri motero ayenera kuchita zowonjezereka osati kungolankhula modzitama kapena nzeru zapamwamba. Zinthu “zowonjezereka” zimenezi zimapezeka m’mawu a Mulungu, Baibulo. Pajatu ndi Mulungu amene anakhazikitsa banja. (Aefeso 3:14, 15) Iye amadziŵa bwino kuposa wina aliyense zimene ana amafuna.

Mfundo za Chikhalidwe za M’Baibulo Zimathandiza Mabanja Kupambana

Koma kodi Baibulo lingathedi kuthandiza ana opanda kholo lina? Kodi iwo sanafike poti sangathenso kusintha? Ayi, sanafike potero! Kumayambiriro kwa nkhani ino, talemba mawu a m’lipoti la boma la United States limene likutchula mavuto ambiri amene ana ameneŵa amapeza. Ngakhale kuti ali mawu oopsa, lipotilo likutsiriza ndi kunena kuti: “Kafukufukuyu akusonyezanso kuti ana ambiri m’mabanja a kholo limodzi amakula bwinobwino ngakhale kuti pali umboni wokwanira wakuti nthaŵi zambiri satero.” Inde, mavuto obwera chifukwa chokhala opanda bambo angathe kuthetsedwa kapena kungochepetsedwa chabe. Zimenezi n’zotheka kwenikweni ngati mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zigwiritsidwa ntchito polera ana.

Kuti zimenezi zitheke pamafunika kuti kholo limodzilo ligwire ntchito zolimba, ndipo poyamba zimenezi zingaoneke ngati zovuta. Koma ngati muli mumkhalidwe umenewu, mungaphunzire kudalira Yehova Mulungu ndi mtima wanu wonse. (Miyambo 3:1, 2) Akazi ena achikristu m’nthaŵi za Baibulo anakumana ndi mikhalidwe yovuta kwambiri, monga umasiye. Baibulo limanena za oterewa, kuti: “Iye [“mkazi,” NW] amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m’mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.” (1 Timoteo 5:5) Kumbukirani kuti Yehova amadzitcha kuti ali “Atate wa ana amasiye.” (Salmo 68:5) Mungakhale otsimikiza kuti iye adzachirikiza mayi aliyense woopa Mulungu amene akuyesetsa kulera ana ake.

Kuchita phunziro la Baibulo lapanyumba mokhazikika ndi ana ndi njira yofunika yowathandiza kuti akule n’kudzakhala anthu ochita zinthu molinganizika ndiponso moganiza bwino. (Deuteronomo 6:6-9) Pakati pa Mboni za Yehova makolo ambiri olera ana paokha amagwiritsa ntchito mabuku ozikidwa pa Baibulo amene anapangidwa kaamba ka achinyamata basi, monga buku lakuti Mafunso—Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. * Chidziŵitso chimene chili mmenemo chili ndi miyezo ya chikhalidwe chabwino imene ingathandize achinyamata kupeŵa kuchita zolakwa zimene makolo awo anachita. Pamene ana adziŵa Yehova Mulungu, angayambe kuona kuti ali ndi Tate wawo kumwamba amene amawaganizira kwambiri. (Salmo 27:10) Zimenezi zingawathandize kuti athane ndi malingaliro akuti ndi osiyidwa. Mtsikana wa ku Britain amene banja la makolo ake linatha akukumbukira kuti: “M’nthaŵi yonseyi, mayi anali kundiphunzitsa zolimba kuti kupemphera ndiponso kudalira Yehova ndi mtima wonse n’kofunika. Zimenezi zinatitheketsa kukhala bwinobwino.”

Kukhalabe ndi Mgwirizano Wapakati pa Kholo ndi Mwana

Baibulo limanena momveka bwino kuti mwana ayenera kulemekeza amayi ake ndiponso atate wake. (Eksodo 20:12) Ndipo chisudzulo sichithetsa unansi wapakati pa bambo ndi mwana. Ngakhale kuti mwamuna wakaleyu sangamakhalenso panyumba, ana angapindulebe pokhala ndi mgwirizano wabwino ndi iye. * Vuto n’lakuti mayi angakwiye ndi mwamunayo ndipo angadane ndi zoti nkhani za anawo zizimukhudza. Kodi mayi angathane nawo bwanji malingaliro oterewa?

Baibulo limapereka malangizo abwino pochenjeza kuti: “Muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo . . . Chenjerani, musalunjike kumphulupulu.” (Yobu 36:18-21) N’zoona kuti si kwapafupi kulankhula mokoma mtima posimba za munthu amene watikhumudwitsa kapena kutisiya. Koma dzifunseni kuti: ‘Kodi mtsikana wamng’ono angaphunzire kukhulupirira munthu wamwamuna ngati nthaŵi zonse akuuzidwa kuipa kwa abambo ake? Kodi mnyamata wamng’ono angathe kukula, n’kumadzachita zinthu monga mwamuna ngati polangizidwa amauzidwa kuti, “Unangowatenga ndendende bambo wako”? Kodi ana angaone kuti kumvera n’koyenera ngati akuphunzitsidwa kunyoza bambo wawo kapena ngati akuletsedwa n’kuonana nawo komwe?’ N’zoonekeratu kuti kuletsa unansi wa ana anu ndi abambo wawo n’koipa.

Zingakudabwitseni kudziŵa kuti Baibulo sililetsa kukwiya kolungama. Baibulo limati, “Kwiyani, koma musachimwe.” (Aefeso 4:26) Tchimo si kukwiyako ayi, koma n’kulamulidwa ndi “mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka mkamwa mwanu.” (Akolose 3:8) Choncho pewani kunyoza bambo pamaso pa ana anu. Ngati mukuona kufunika kouza wina zokhumudwitsa zanu, tsatirani malingaliro a Baibulo akuti muuzeko wina “nkhaŵa” zanuzo, koma uzani munthu wina osati ana anu. (Miyambo 12:25) Yesetsani kuona kuti zinthu zili bwino kotero kuti muiŵale zam’mbuyo. (Mlaliki 7:10) Kutero kungakuthandizeni kwambiri kuchepetsa mkwiyo wanu.

Potsirizira, kumbukirani kuti Baibulo limalamula mwana kuti ayenera kulemekeza atate wake, ngakhale kutakhala kuti khalidwe la abambo akewo silopereka chitsanzo chabwino. (Aefeso 6:2, 3) Choncho athandizeni ana anu kuona zolakwitsa za abambo awo mwachikulu. Mtsikana wina amene anakulira m’banja losweka ananena kuti: “Poona bambo wanga mwachikulu, monga munthu wotha kulakwitsa, wopanda ungwiro, ndatha kuwazoloŵera.” Polimbikitsa ana anu kuti azipereka ulemu kwa abambo awo, mumawathandiza kuona moyenerera ulamuliro wanu monga kholo!

N’kofunikanso kuti musabise kusiyana kwa udindo wanu ndi wa ana anu. Iwo adakali pansi pa ‘chilangizo cha amawo.’ (Miyambo 1:8) Anyamata angamve kuti akulemetsedwa ngati akuyembekezedwa kukhala ‘bambo wa m’nyumbayo’. Ana aakazi nawonso zingawakulire ngati akuchititsidwa zinthu monga olimbitsa mtima mayi wawo. Ana amafunika kuwatsimikizira kuti poti kholo ndinu mudzawasamalira, osati kuti iwo adzasamalira inuyo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 12:14.) Chitsimikizo choterechi chingawalimbitse mtima, ngakhale kuti banja lawo silili monga mmene banja liyenera kukhalira.

Abambo Oloŵa M’malo

Kodi nanga n’kutani ngati bambo sali mbali ya banjalo m’pang’ono pomwe? Akatswiri amati ana angathe kupindula pocheza ndi anthu ena aamuna. Ngakhale kuti amalume a mwanayo kapena mnansi wina wachidwi ndi wokoma mtima angathandize, mwanayo angapindule kwambiri popanga maubwenzi oyenera ndi amuna ena mu mpingo wachikristu. Yesu analonjeza kuti mpingo udzakhala ngati banja lochirikiza.—Marko 10:29, 30.

M’nthaŵi za Baibulo Timoteo ali wamng’ono analeredwa mwakuti atakula anakhala munthu wa Mulungu wopatsidwa ulemu, koma mosathandizidwa ndi tate wokhulupirira. Baibulo limanena kuti amene anachita mbali yaikulu ya ntchitoyi ndi amayi ake ndiponso agogo ake. (Machitidwe 16:1; 2 Timoteo 1:1-5) Komabe, iye anapindulanso chifukwa chokhala ndi unansi ndi munthu wina wachikristu—mtumwi Paulo. Paulo anatcha Timoteo “mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye.” (1 Akorinto 4:17) Mofananamo masiku ano, Mboni za Yehova zimalimbikitsidwa kuti zigwiritse ntchito malangizo a Baibulo a “kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye.” (Yakobo 1:27) Amalimbikitsidwa kuti ‘apulumutse ana amasiye’ pokhala ndi chidwi chenicheni ndiponso choyenerera pa anthu otereŵa. (Yobu 29:12) Mayi wachitsikana wotchedwa Annette akukumbukira mmene mkulu wina wachikristu anachitira naye chidwi moyenera pamene anali mwana, ponena kuti: “Iye anali munthu yekhayo amene ndinkamuona monga bambo wanga.”

Kuthetsa Vutoli

Mfundo zachikhalidwe zimenezi zingathandize ana opanda bambo kukhala opambana. Ngakhale kuti paubwana wawo zinthu sizinawayendere bwino, angakule n’kukhala anthu olongosoka, otha kuchita bwino zinthu, ndiponso makolo achikondi, okhulupirika, ndi odzipereka. Ngakhale zinthu zili choncho, kupeŵa n’kwabwino kwambiri kuposa kuchiza kulikonse. Ndipo potsiriza, vuto la mabanja opanda bambo lingathetsedwe pokhapokha ngati amuna ndiponso akazi akufunitsitsa kugwiritsa ntchito Baibulo m’moyo wawo. Mwachitsanzo, angatero, potsatiradi lamulo la Baibulo loletsa kugonana musanakwatirane ndiponso potsata miyezo imene Baibulo limakhazikitsa kaamba ka amuna ndiponso akazi awo.—1 Akorinto 6:9; Aefeso 5:21-33.

Lero ana ambiri ali ndi abambo m’nyumba zawo komabe angatchedwe kuti ali amasiye. Katswiri wina wa nkhani za m’banja anati: “Vuto lalikulu kwambiri limene akupeza. . . ana masiku ano n’lakuti makolo awo samakhala nawo kwa nthaŵi yokwanira ndiponso sachita nawo chidwi.” Mawu a Mulungu amalongosola nkhani imeneyi mosapsatira. Amalamula abambo pa nkhani ya ana awo kuti: “Apatseni malangizo, ndiponso akonzeni, monga mwa maleredwe a Chikristu.” (Aefeso 6:4, New English Bible; Miyambo 24:27) Abambo akamatsatira malangizo a Baibulo, ana sakhala ndi mantha akuti asiyidwa.

Komabe, kodi n’kwanzeru kukhulupirira kuti anthu adzayamba kutsatira Baibulo mwaunyinji? Ayi ndithu. (Mateyu 7:14) Koma Mboni za Yehova zathandiza anthu mamiliyoni kupeza chimwemwe m’banja lawo kudzera m’ntchito ya phunziro la Baibulo lapanyumba. * N’zoonadi, Baibulo limachenjeza kuti okwatira onse “adzakhala nacho chisautso m’thupi” chifukwa cha kupanda ungwiro. (1 Akorinto 7:28) Koma amene amafunadi kulemekeza Mawu a Mulungu amayesetsa kupeza njira yothetsera mavuto awo, osati kusudzulana akangoona chizindikiro choyamba cha mavuto. Inde, pali nthaŵi imene moyenerera Mkristu ayenera kuganiza zopatukana kapena ngakhale kusudzulana. (Mateyu 5:32) Komabe, podziŵa mmene zimenezi zingakhudzire ana ake, Mkristu angafunefune njira zopulumutsira banja lake ngati n’kotheka.

Kutsatira Baibulo si kuti kungapulumutse chabe banja lanu tsopano. Kungatheketse nonse kudzakhala ndi moyo kosatha! Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Kuŵerenga ndiponso kugwiritsa ntchito malangizo amene ali m’Mawu a Mulungu ndi njira yokhayo yabwino kwambiri yotsimikizira kuti banja lanu likhale mpaka kalekale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Chidziŵitso chothandiza makolo opeza chinalembedwa mu Magazini yathu ina yotchedwa Nsanja ya Olonda, ya March 1, 1999.

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 13 Izi sizingagwire ntchito ngati mwana ali pa tsoka lakuzunzidwa kapena kugwiriridwa ndi bamboyo.

^ ndime 24 Buku lotchedwa Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.) lili ndi malangizo ambiri ochokera m’Baibulo amene angathandize mabanja. Mungalipeze popezana ndi a Mboni za Yehova kwanuko.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Potsatira mfundo za chikhalidwe za Baibulo, kholo lingalere ana palokha mopambana

[Chithunzi patsamba 10]

Nthaŵi zambiri Amuna achikristu ‘angapulumutse mwana wamasiye’ pokhala ndi chidwi chenicheni ndiponso choyenera pa iye