Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu a ku Russia Akuyamikira Ufulu wa Kulambira

Anthu a ku Russia Akuyamikira Ufulu wa Kulambira

Anthu a ku Russia Akuyamikira Ufulu wa Kulambira

CHIYAMBIRE PAMENE SOVIET UNION INATHETSEDWA MU 1991, ANTHU OKHALA KUMENEKO AKHALA NDI UFULU WOKULIRAPO WA KULAMBIRA MULUNGU. UFULU UMENEWO WAYAMIKIRIDWANSO NDI OMWE ASAMUKIRA KU MAYIKO ENA.

KWA anthu ambiri amene akukhala m’mayiko omwe kale anali Soviet Union, ufulu wa kusonkhana poyera ndi kulambira Mulungu uli chinthu chamtengo wapatali chimene amanidwa kwa zaka zambiri.

Chitachitika Chisinthiko cha Bolshevik mu 1917, kunakhala koopsa mu Russia kuŵerenga Baibulo, ndipo ndi anthu ochepa kwambiri amene anaika pangozi ufulu wawo mwa kutero. Koma Mboni za Yehova zinali zosiyana. Ndi iko komwe, magazini ya Newsweek ya pa April 16, 1956—pafupifupi zaka 44 zapitazo—inagwira mawu wachinyamata wa ku East Germany akuti: “Palibenso wina amene amaŵerenga Baibulo koma Mboni za Yehova zokha basi.” Komatu, chifukwa chochititsa misonkhano ya phunziro la Baibulo, ndi kulalikira uthenga wa Baibulo, Mboni zinali kuikidwa mu ndende ndi misasa ya chibalo. Kulikonse kumene zimapita, zivute zitani, zimaika maganizo awo onse pa chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo ngati mmene bokosi lotsatira nkhani ino likusonyezera.

Pamene Soviet Union anayamba kupasuka mu 1991, Mboni kumeneko zinapanga misonkhano isanu ndi umodzi yopereka malangizo ochokera m’Baibulo. Onse ofika pamisonkhanoyo anakwana 74,252. Mu 1993, patangopita zaka ziŵiri, okwanira 112,326 anasonkhana pamisonkhano yoteroyo isanu ndi itatu m’mayiko 4 mwa mayiko 15 omwe kale anali mbali za Soviet Union. * Ambiri mwa zikwizikwi zimenezo anathera zaka zambiri mu ndende ndi misasa ya chibalo. Akristu okhulupirika ameneŵa anali osangalala kwambiri popeza ufulu wa kulambira Mulungu popanda choletsa.

Chaka chilichonse chiyambire 1993, anthu a m’mayiko amene kale anali mbali ya Soviet Union ayamikira mwayi wamtengo wapatali wosonkhana mwa ufulu pa misonkhano yachikristu m’dziko lawo. Mwachitsanzo, chaka chatha, Mboni za Yehova zokwana 282,333 pamodzi ndi mabwenzi awo zinali zosangalala kulambira limodzi pa misonkhano ya Chigawo yokwana 80 ya mutu wakuti “Mawu Aulosi a Mulungu” m’mayiko omwe kale anali mbali za Soviet Union. Ndipo onse amene anabatizidwa anapitirira 13,452.

Ngakhale zingaoneke ngati zodabwitsa, chaka chatha kunalinso misonkhano yaikulu ina yachilankhulo cha Chirasha m’mayiko ena. Anthu okwanira 6,336 anafika pamisonkhano imeneyi m’mayiko akunja kwa dziko limene kale linali Soviet Union! Kodi misonkhano imeneyi inachitikira kuti? Ndipo n’chifukwa chiyani anthu olankhula Chirasha ochuluka chotere anali a chidwi ndi Baibulo? Tiyeni poyamba tiyankhe funso loyambiriralo.

Azindikira Chosoŵa Chauzimu

Russia ali ndi mbiri yotchuka yachipembedzo. Matchalitchi ake okongolawo, amene anamangidwa zaka mazana angapo zapitazo, ali pakati pa matchalitchi otchuka kwambiri achikristu. Komatu, Tchalitchi cha Russian Orthodox, mofanana ndi Roma Katolika, chapangitsa anthu kusadziŵa Baibulo.

Buku latsopano lotchedwa The Russian TragedyThe Burden of History, likufotokoza kuti; “Baibulo silinakhale mbali yofunikira kwambiri ya tchalitchi chotchedwa Russian Orthodox.” Zotsatira zake, malinga ndi kunena kwa katswiri wa zachipembedzo wa ku Russia, Sergei Ivanenko, zakhala zakuti “kusalidziŵa bwino Baibulo kwa anthu a matchalitchi a Russian Orthodox kumawapangitsa ambiri a iwo kukhulupirira zamalaulo, ziŵanda, ndi matsenga ngatinso osakhulupirira.”

Wolemba Wachirasha wodziŵika, Tolstoy, anakhala ndi maganizo ofananawo. Analemba kuti: “Ndinakhulupirira kuti chiphunzitso cha tchalitchicho [cha Russian Orthodox] m’mawu chinali chiphunzitso cha chinyengo chowononga, ndipo m’zochitika chinali kutsata zikhulupiriro za mwambo ndi ufiti, zimene zimaphimba tanthauzo lonse la chiphunzitso chachikristu.”

Mkhalidwe umenewu unakhaladi nthaka yachonde yomerapo Komyunizimu ya ku Soviet ndi chiphunzitso chake chosakhulupirira Mulungu chakuti: “Chipembedzo chimapusitsa anthu.” Koma, posapita nthaŵi yaitali Komyunizimu inakhala chipembedzo pachokha, kaŵirikaŵiri chotchedwa Chipembedzo Chofiira. Ndipo, Chipembedzo Chofiiracho sichinapitirire. Pamene Boma la Soviet linagwa mu 1991, miyandamiyanda ya anthu anasokonezeka osadziŵa koloŵera. Koma chifukwa cha chilimbikitso cha Mboni za Yehova, zikwizikwi za Arasha anapeza mayankho mu Baibulo.

Chifukwa cha sukulu zawo zodziŵa kuphunzitsa bwino, Arasha anadziŵika kukhala athu ophunzira kwambiri padziko lonse lapansi. Choncho, Arasha ambiri anakhala osati okonda kuŵerenga Baibulo lokha komanso okonda ziphunzitso zake. Panthaŵi imodzimodziyo, makamaka zaka za ma 1990, mazanamazana a anthu ochokera m’mayiko amene kale anali Soviet Union anasamukira kumayiko ena, ngati Germany, Greece, ndi United States. Kodi panakhala zotsatirapo zotani?

Aufulu Kulambira M’Germany

M’zaka za zana la 18 ndi 19, Ajeremani ambiri anasamukira ku Russia. Wotchuka kwambiri anali Sophie wazaka 15, amene, mu 1762 analoŵa m’malo mwa mwamuna wake paudindo wolamulira Russia. Munthaŵi ya ulamuliro wake wa zaka zambiri, Sophie, amene anadziŵika kuti Catherine Wamkulu, anaitana alimi a ku Germany kukakhala ku Russia. Ndiye pamene Germany anaukira Soviet Union pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anthu a mtundu wachijeremani ambiri anawatumiza ku Siberia ndi ku mayiko ena omwe anali mbali ya Soviet Union monga Kazakhstan, Kyrgyzstan, ndi Uzbekistan. Posachedwapa Ajeremani ambiri olankhula Chirasha, ngakhalenso ena ochokera kumayiko omwe kale anali mu Soviet Union, anasamukira ku Germany kuti akapeze mikhalidwe yabwinoko pazachuma.

Mu December 1992 mpingo woyamba wa Chirasha unakhazikitsidwa ku Germany mu Berlin. Pofika chaka chatha, mipingo 52 ndi magulu 43 ang’onoang’ono anapangidwa m’madera atatu a Chirasha mu Germany. Panali chiŵerengero chapamwamba chokwana 4,920 pa Msonkhano Wachigawo wa Chirasha wa “Mawu Aulosi a Mulungu,” wochitika kuyambira pa July 30 mpaka August 1, kumene anthu okwana 164 anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova. Kumayambiriro, pa April 1, ku mipingo ya Chirasha ya mu Germany, anthu okwana, 6,175, anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu.

Arasha ku United States

United States nayenso walandira anthu olankhula Chirasha ochokera ku mayiko amene kale anali Soviet Union. Nyuzipepala ya New York Times inalengeza kuti: “Pakati pa 1991 ndi 1996, Arasha anali gulu la anthu obwera m’Brooklyn amene chiŵerengero chawo chinali kukwera mofulumira kwambiri. Mu nthaŵi yofananayo, Ofesi yoona za Oloŵa ndi Otuluka m’Dziko ndi Yopereka Unzika inalandira anthu obwera opambana 339,000 mu United States kuchokera kumayiko omwe kale anali Soviet Union.”

Pambuyo pake, nyuzipepala ya Times ya January 1999 inatinso m’zaka makumi angapo zapitazo, Ayuda pafupifupi 400,000 ochokera ku Soviet Union anasamukira ku mzinda wa New York ndi madera ozungulira. Kuwonjezera apo, zikwi zinanso za Arasha akhazikika m’madera osiyanasiyana a United States m’zaka zaposachedwapa. Mwachitsanzo, kumpoto kwa California kunafika Arasha atsopano okwana pafupifupi 35,000, kupangitsa dera limeneli kukhala lachitatu pamadera aakulu kumene kuli anthu ochuluka ochokera kumayiko amene kale anali Soviet Union. Koma ochuluka kwambiri ali ku New York ndi Los Angeles. Anthu olankhula Chirasha ameneŵa alandiranso mwayi wophunzira Baibulo, ndipo mazana a iwo akhala alambiri a Mulungu woona, Yehova.

Pa April 1, 1994, mpingo woyamba wa Mboni za Yehova m’zaka zaposachedwa wa Chirasha ku United States unapangidwa mumzinda wa Brooklyn, ku New York. M’kupita kwa nthaŵi, mipingo ya Chirasha inapangidwanso ku Pennsylvania, California, ndi Washington. Magulu a phunziro anayambidwanso m’mbali zosiyanasiyana za dzikoli.

Woyamba mu United States

Pa August 20 mpaka 22 wapitayu, chiŵerengero chokwera chokwana 670 kuzungulira dziko la United States ndi Canada anasangalala kupezeka pamsonkhano wachigawo woyamba wa Chirasha umene unachitikira mu mzinda wa New York. Nkhani zonse zinakambidwa mu Chirasha, ndipo seŵero la ovala zovala zakale losonyeza Yakobo ndi Esau, linachitidwa ndi Mboni za m’mipingo ya Chirasha ya ku Los Angeles, ndi California. Chinalidi chochitika chapadera cha msonkhanowo.

Mbali ina yosangalatsa pamsonkhano wachigawo umenewu inali kuonera kubatizidwa kwa anthu okwana 14, amene ali pachithunzi chosonyezedwacho. Ambiri anayenda ulendo wa makilomita 4,000 kuchokera ku Portland, Oregon, ndi Los Angeles komanso ku San Francisco, ndi California, kuti akabatizidwe ku msonkhano wachigawo mu mzinda wa New York. Anthu 14 ameneŵa, kale ankakhala kumayiko omwe kale anali mbali ya Soviet Union monga Armenia, Azerbaijan, Belarus, Moldova, Russia, ndi Ukraine. Zokumana nazo zawo zimasonyezadi mmene amayamikirira chidziŵitso cha Mulungu ndi ufulu wa kulambira.

Svetlana (wachitatu kuchokera kumanzere, pamzere wakutsogolo) anakulira ku Moscow. Ali ndi zaka 17 anakwatiwa ndi woimba wotchuka amene anali wamkulu kwambiri kusiyana ndi iye, ndipo mu 1989 anapita ku United States ndi mwana wawo wamwamuna wakhanda. Mwamuna wake anali woyendayenda nthaŵi zambiri, ndipo zaka zisanu pambuyo pake anasudzulana.

Pamene Svetlana anakumana ndi Mboni yogwira nayo ntchito, mabwenzi ake anam’chenjeza kuti asatengeke ndi “kagulu kampatuko kamene kakalamulira moyo wake ndi kumulanda ndalama zake zonse.” Komabe, ankafuna kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa. Pamene anasonyezedwa dzina la Mulungu mu Baibulo, ananena kuti: “Ndinasangalala kudziŵa kuti Mboni zokha ndizo zimadziŵikitsa dzina la Mulungu.”

Ali mnyamata, Andrei (wachitatu kuchokera kumanzere, pamzera wakumbuyo,) anachoka kwawo ku Siberia kukapitiriza maphunziro a maseŵero a zothamangathamanga kumene tsopano ndi St, Petersburg. Posakhalitsa, Soviet Union inatha, ndipo mu 1993, Andrei, ali ndi zaka 22, anasamukira ku United States. Akufotokoza kuti: “Ndinayamba kuganiza za Mulungu ndipo ndinayamba kupita ku tchalitchi cha Russian Orthodox. Tsiku lina, panthaŵi ya chikondwerero cha Isitala ya Chirasha, ndinakhala mu tchalitchi usiku wonse kuyesayesa kuyandikira kwa Mulungu.”

Panthaŵi imeneyi Sventlana anakumana ndi Andrei, ndipo anamuuza zimene anali kuphunzira kuchokera m’phunziro lake la Baibulo. Anavomera kudzatsagana naye kumsonkhano wa Mboni za Yehova, ndipo pambuyo pake anavomera phunziro la Baibulo. Mu January 1999 anakwatirana. Atabatizidwa pamsonkhano wachigawo, anakhala ndi chimwemwe chachikulu kwambiri.

Pavel (pamzera wakumbuyo, wachinayi kuchokera kumanzere) anabadwira pafupi ndi Qaraghandy, ku Kazakhstan, koma pambuyo pake anasamukira ku Nal’chik, ku Russia. Mzinda waukulu umenewu uli pafupi ndi Chechnya ndi Dagestan, dera limene kumenyana kodetsa nkhaŵa kwachitika. Pavel anakumana koyamba ndi Mboni kumeneko mu August 1996, koma anasamukira ku San Francisco mwezi wotsatira. Analoŵerera m’mankhwala osokoneza bongo ndipo anabereka mwana wamkazi, amene anam’siya ku Russia ndi mayi wake.

Mosakhalitsa atangofika ku United States, Pavel anakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anavomera phunziro la Baibulo. Anawongolera moyo wake ndiyeno analembera kalata mayi wa mwana wake uja za chikhulupiro chimene anali atachipeza. Nayenso tsopano akuphunzira limodzi ndi Mboni, ndipo akukonzekera kuti apite ku United States kuti iye ndi Pavel akathe kukwatirana komanso akatumikire Yehova limodzi ndi mwana wawo wamkazi ku California.

George (pamzera wakumbuyo, wachiŵiri kuchokera kumanzere) anabadwira ndi kukulira ku Moscow. Anapita ku United States mu 1996, ndipo chaka chotsatira anakwatira Flora, amene anachokera ku Azerbaijan. George ankapita ku tchalitchi cha Russian Orthodox, koma ataŵerenga magazini ya Nsanja ya Olonda, anakhala ndi mafunso onena za chiphunzitso cha Utatu. Pamene anayankhidwa kalata yake yomwe analembera Watch Tower Society, analandira bulosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? M’chaka cha 1998 iye pamodzi ndi Flora anayamba kuphunzira Baibulo. Tsopano Flora nayenso akukonzekera kubatizidwa.

Chinanso chosangalatsa pamsonkhano wachigawo umenewu chinali kulandira moni wochokera ku Moscow, kumene anthu 15,108 anasonkhana pamsonkhano wa chigawo mapeto a mlungu womwewo. Osonkhana mu mzinda wa New York anasangalala kwambiri kumva chilengezo chakuti anthu 600 anabatizidwa! Ichi chinali chosangalatsadi makamaka poyerekeza ndi nkhani zofooketsa zimene zinafalitsidwa m’nyuzipepala ndi pawailesi yakanema ku United States ndi kumadera ena, kutatsala mlungu umodzi kuti msonkhano wachigawo uyambe.

Zimene Zinali Kuchitika ku Moscow

Pa July 21, 1999, Mboni zinasaina pangano kuti zidzagwiritse ntchito bwalo la maseŵero la Olympic lomwe lili chapakati pa mzinda wa Moscow komanso pafupi kwambiri ndi tchalitchi chachikulu cha Russian Orthodox. Koma kutangotsala mlungu umodzi kuti msonkhano wa chigawo uchitike, zinaonekera kuti padzakhala vuto. Pofika Lachitatu, pa August 18, chilolezo chogwiritsa ntchito bwalo la maseŵero chinali chisanaperekedwe, ngakhale kuti ndalama zinali zitaperekedwa kale. Akuluakulu anali atatsimikiziridwa, monga momwe bokosi la patsamba 28 likusonyezera, kuti Mboni za Yehova zinali chipembedzo chololedwa mwalamulo mu Russia.

Mboni zoimira msonkhanowo zinayamba kuda nkhaŵa chifukwa chakuti nthumwi pafupifupi 15,000 zinali kukonzekera kudzapezeka pamsonkhano umenewu m’maŵa wa Lachisanu. Nthumwi zina zinali kuchokera ku mizinda ndi ma tawuni akutali kwambiri kubwera ku Moscow. Potsirizira pake, atakambirana kwa maola ambiri mpaka pafupifupi 8:00 p.m Lachinayi, August 19, oyang’anira bwalo la maseŵero anasangalala kudziŵitsa Mboni zoimira msonkhano kuti zipitirize kukonzekera. Oyang’anira mzinda anati analibe choletsa china chilichonse pa msonkhano wa chigawo umenewo.

M’maŵa wotsatira zikwizikwi za anthu zinasonkhana kubwalo la maseŵero limeneli. Mboni zodzipereka zinagwira ntchito usiku wonse kuti zikonze malowo. Enanso amene anapezeka tsiku loyamba limeneli anali atolankhani omwe anali atadziŵitsidwa kuti Mboni zinali kukanizidwa kuchitira msonkhano pabwaloli. “Mwagwira ntchito!” Mmodzi wa iwo anakuwa. “Tasangalala kuti msonkhano wanu waloledwa.”

Chitsanzo cha Khalidwe la Bata

Oyang’anira bwalo la maseŵeroli anaganiza kuti kunali kwabwino kukhwimitsa chitetezo. Ndiyetu, asilikali okhala ndi zipangizo zounikira ngati zomwe zimakhala kubwalo la ndege pounika okwera ndi otsika anaikidwa pamalo onse oloŵera. Apolisi anaikidwa mozungulira m’bwalo la maseŵero lonse. Msonkhano unapitirira mwadongosolo ngakhale panali chiopsezo chodetsa nkhawa.

Loŵeruka masana munthu wina anaimba telefoni akunena kuti anthu ena anatchera bomba m’bwalo la maseŵerolo. Chioopsezo chimenechi chinafika kutangotsala pang’ono kumaliza nkhani yotsatizana ndi yomalizira tsikulo. Choncho oyang’anira bwalo anapempha kuti chilengezo chachifupi chiperekedwe kuti anthu atuluke m’bwalomo mofulumira. Pamene aliyense anatuluka mwadongosolo, oyang’anira bwaloli pamodzi ndi apolisi anazizwa. Sanaonepo dongosolo ngati limenelo! Anafunsa ngati zinali zokonzekera.

Bomba silinapezeke, ndipo tsiku lotsatira pulogalamu yamsonkhano inawonjezedwa kuphatikizapo nkhani yomwe siinakambidwe pa tsiku Loŵeruka. Oyang’anira bwalo limeneli anasangalala ndi msonkhano umenewu.

Ku Greece ndi Malo Ena

Mlungu womalizira wa August komanso mlungu woyamba wa September, misonkhano yachigawo ya Chirasha inachitikanso, woyamba mu Greece—ku Athens ndiyeno ku Thessalonica. Okwanira 746 anafikapo, ndipo 34 anabatizidwa. Mu Greece muli mipingo isanu ndi itatu yolankhula Chirasha, ndi magulu ang’onoang’ono 17 opangidwa ndi anthu ochokera mayiko akumwera kwa Soviet Union wakale. Aŵa amachita misonkhano yawo mu Chirasha ndi zilankhulo zina za anthu obwera.

Mmodzi mwa amene anabatizidwa ku Athens anali Victor. Iye sanali kukhulupirira kuti kuli Mulungu, koma mu August 1998 anakamvetsera msonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ku Athens, kumene mkazi wake anabatizidwa. Iye anati anadabwa kwambiri ndi chikondi chimene chimasonyezedwa ndi opezekapo kotero kuti anasonkhezereka kuyamba kuphunzira Baibulo

Mwamuna wina dzina lake Ighor analandira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndipo atatha kuliŵerenga anataya mafano ake. Ndipo anayamba kuuza ena kuti ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Atalembera kalata ku nthambi ya ku Athens ndipo Mboni za Yehova zitam’chezera mu November 1998, nthaŵi yomweyo anapita kwa nthaŵi yoyamba kumsonkhano wampingo ndipo mpaka lero sanaphonye ngakhale umodzi. Tsopano, popeza Ighor anabatizidwa, cholinga chake ndi kukhala mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova.

Anthu ambiri olankhula Chirasha anasamukira ku mayiko ena ambiri omwe sitinatchule. Ambiri a iwo akusangalalanso chifukwa cha ufulu wawo wophunzira Baibulo ndi kusonkhana pamodzi polambira Mulungu. Kwa iwo ndi mwayi wamtengo wapatali ndi wosangalatsa kwambiri!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mayiko 15 otsatiraŵa ndi amene tsopano ali odzilamulira okha: Armenia, Azerbaijan, Belarus, Estonia, Georgia, Kazakhstan, Kyrgyzstan, Latvia, Lithuania, Moldova, Russia, Tajikistan, Turkmenistan, Ukraine, ndi Uzbekistan.

[Bokosi patsamba 22]

Arasha Amene Amakonda Baibulo

Pulofesa Sergei Ivanenko, katswiri wa zipembedzo wolemekezeka wa ku Russia, anafotokoza Mboni za Yehova kukhala athu odzipereka pa kuphunzira Baibulo. M’buku lake laposachedwapa la m’Chirasha lakuti, O lyudyakh, nikogda nye rasstayushchikhsya s bibliey (Anthu Amene Sakhala Opanda ma Baibulo Awo), analemba za mbiri yawo yoyambirira mu Soviet Union kuti: “Ngakhale pamene anawaponya m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Mboni za Yehova nthaŵi zonse zimapeza njira zoŵerengera Baibulo. Popereka chitsanzo cha zimenezi, anasimba chochitika ichi.

“Kunali koletsedwa kuti akaidi akhale ndi Baibulo. Mabaibulo anali kulandidwa pamene kufufuza kumachitika. Mu ndende ina yakumwera, mmodzi wa Mboni za Yehova anali wokonza magetsi ndipo amasunga mabuku a Baibulo m’makina opereka mphamvu yamagetsi, mmene magetsi anali amphamvu kwambiri. Buku lililonse la Baibulo linamangidwa ndi chingwe ku mawaya amagetsi, ndipo ndi iye yekha amene amadziŵa chingwe chimene amayenera kukoka kuti alitulutse—mwachitsanzo, Uthenga wabwino wa Mateyu—koma osagwidwa ndi magetsi. Indetu, ngakhale kuti alonda amafufuza mwakhama chotani, Baibulo lokhali sanathe kulipeza.”

[Bokosi patsamba 28]

Mboni za Yehova Zilembedwanso M’Kaundula ku Russia

Mboni za Yehova zakhala zokangalika kulengeza Ufumu wa Mulungu mu Russia kwa zaka zopitirira zana limodzi tsopano. Komabe, chifukwa cha chiletso cha boma, sizinalembedwe m’kaundula wa boma mpaka pa March 27, 1991. Panthaŵi imeneyo, zinalembedwa m’dzina lakuti Ofesi Yoyang’anira Mipingo ya Mboni za Yehova mu U.S.S.R.

Pa September 26, 1997, lamulo lotchedwa “Ufulu wa Chikumbumtima ndi Chipembedzo” linakhazikitsidwa. Lamulo limeneli linafalitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ambiri anaganiza kuti cholinga cha lamulo limeneli chinali kuletsa zipembedzo zazing’ono mu Russia.

Choncho, ngakhale kuti Mboni za Yehova zinamenya nkhondo kwambiri kuti zilembetsedwe m’kaundula mu 1991, lamulo latsopano la mu Russia la Ufulu wa Chikumbumtima linafuna kuti Mbonizo, kuphatikizapo ngakhale zipembedzo zina zonse, zilembetsenso kachiŵiri. Izi zinadzutsa mafunso ambiri. Kodi izi zinatanthauza kuti akuluakulu a boma a Russia amabwezeretsa lamulo lozunza Mboni za Yehova? Kapena, kodi zinatanthauza kulolera zipembedzo ndi ufulu wakupembedza zolembedwa mu Lamulo la Chitaganya cha Russia?

Pomalizira pake yankho linapezeka. Chisangalalo chinasefukira pakati pa Mboni za Yehova polandira chivomerezo cha kulembedwa m’kaundula kachiŵirinso pamene Unduna Woona za Chilungamo wa Russia unapereka chikalata chovomereza “Ofesi Yoyang’anira Mboni za Yehova mu Russia,” pa April 29, 1999!

[Chithunzi patsamba 23]

Msonkhano wachigawo woyamba wa Chirasha ku United States

[Chithunzi patsamba 24]

Seŵero la Baibulo losonyezedwa ku New York ndi Mpingo wa Chirasha wa ku Los Angeles

[Chithunzi patsamba 25]

Obatizidwa 14 ku New York ochokera ku mayiko asanu ndi limodzi omwe kale anali Soviet Union

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

Oposa 15,000 anasonkhana m’bwalo la maseŵero la Olympic ku Moscow