Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro Choona N’chiyani?

Kodi Chikhulupiriro Choona N’chiyani?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Chikhulupiriro Choona N’chiyani?

“WOPANDA CHIKHULUPIRIRO SIKUTHEKA KUM’KONDWERETSA; PAKUTI IYE WAKUDZA KWA MULUNGU AYENERA KUKHULUPIRIRA KUTI ALIPO, NDI KUTI ALI WOBWEZERA MPHOTHO IWO AKUM’FUNA IYE.”—AHEBRI 11:6.

KODI chikhulupiriro n’chiyani? Ena amati chikhulupiriro ndicho kukhulupirira Mulungu kwachipembedzo popanda umboni weniweni wakuti iye aliko. Mtolankhani wa ku America wotchedwa H. L. Mencken anatanthauzira mawu akuti chikhulupiriro kuti ndiko “kungokhulupirira kuti zinthu zosatheka zingachitike popanda chifukwa chokwanira.” Kodi ichi ndicho chikhulupiriro choona chimene Baibulo limafotokoza? N’kofunika kumvetsa bwino tanthauzo la chikhulupiriro, chifukwa monga mawu ali pamwambawo akunenera ‘wopanda chikhulupiriro sikutheka kumukondweretsa Mulungu.’

Baibulo limati: “Kukhulupirira ndiko kusakayika konse pa zinthu zimene tilikuziyembekeza.” (Ahebri 11:1, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Motero, chikhulupiriro maziko ake ndiwo chidziŵitso cholongosoka, chomwe chili mfundo zimene zimachititsa kusankha molungama. Izi zimafuna osati kukhulupirira kokha komanso kudziŵa chifukwa chake ukukhulupirira.

Mwachitsanzo: Mwina muli ndi mnzanu amene munganene kuti: “Ndimam’khulupirira munthu uja. Ndingathe kum’dalira kuti adzachita zimene wanena. Ndikudziŵa kuti ngati n’takhala ndi vuto adzandithandiza.” Mosalephera munthu amene mwamudziŵa tsiku limodzi kapena aŵiri simungamukhulupirire motere, kodi kapena mungatero? Iye ayenera kukhala munthu amene wasonyeza kudalirika kwakeko mobwerezabwereza. Ndimo mmene chikhulupiriro chachipembedzo chiyenera kukhalira. Chiyenera kupereka chiyembekezo ndiponso chitsimikizo chozikidwa pa umboni wodalirika.

Kodi N’chikhulupiriro Kapena Kutengeka Maganizo?

Zoona n’zakuti kutengeka maganizo ndiko kumene anthu ambiri lerolino amakuona ngati chikhulupiriro. Kutengeka maganizo, ndiko kukhulupirira popanda maziko kapena chifukwa chenicheni. Nthaŵi zambiri kumazikidwa pa maganizo osinthasintha ndiponso miyambo. Chimenechi si chikhulupiriro cholimba chifukwa chakuti chilibe maziko odalirika.

Kutengeka maganizo kungachititse munthu kuchita mosaganizira zinthu zosemphana ndi choonadi cha Baibulo. Moyenerera, Baibulo limachenjeza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; Koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Yesani [“tsimikizirani,” NW] zonse; sungani chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21) Baibulo silikuchirikiza kutengeka maganizo. Ilo limalimbikitsa chikhulupiriro chokhala ndi umboni.

Kutha kusiyanitsa chikhulupiriro choona ndi kutengeka maganizo ndi nkhani yaikulu. Munthu angathe kukhala wopembedza koma alibe chikhulupiriro choona. Paulo anati: “Si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Koma anthu ena ali nacho chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo ndipo chimakhudza miyoyo yawo.

Chikhulupiriro Choona Chimamangirira Anthu kwa Mulungu

Chikhulupiriro chili ngati chingwe chokhala ndi mfundo za chitsimikizo ndi chidaliro chimene chimamangirira munthu kwa Mulungu. Chikhulupiriro choterechi si chobadwa nacho ayi, koma chimachita kupezedwa. Kodi mungapeze bwanji chikhulupiriro choona? Baibulo limafotokoza kuti: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mawu a Kristu.”—Aroma 10:17.

Choncho, kuti mudziŵe Mulungu ndiponso ziphunzitso za Mwana wake Yesu Kristu muyenera kuwonongerapo nthaŵi. Chidziŵitso chimenechi sichipezeka popanda khama. (Miyambo 2:1-9) Muyenera kudzipereka kuti mudziŵe zimene Baibulo limanena kotero kuti mukhutire kuti n’lodalirika.

Komabe, chikhulupiriro choona chimaphatikizapo zambiri koposa kungokhala ndi chidziŵitso kapena kungokhulupirira kuti chinachake n’choona. Chimaphatikizanso mtima umene umachititsa munthu kulingalira zinthu zoti achite. Aroma 10:10 amati: ‘Ndi mtima munthu akhulupira.’ Kodi izi zikutanthauza chiyani? Pamene musinkhasinkha pa zinthu zaumulungu, ndi kukulitsa chiyamikiro pa izo, m’machititsa kuti uthenga wa Baibulo ukhazikike mumtima wanu. Chikhulupiriro chimakula ndiponso kulimba pamene musonkhezeredwa ndi malonjezo a Mulungu komanso pamene muona umboni wa madalitso ake.—2 Atesalonika 1:3.

Kukhala ndi chikhulupiriro choona n’kwamtengo wapatali bwanji! Timapindula mwa kukhala okhoza kukumana ndi mavuto ndi chiyembekezo mwa Mulungu, kudalira mphamvu yake yotitsogolera njira zathu komanso kufunitsitsa kwake kusamalira zosoŵa zathu. Kuwonjezera apo, Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ananenapo za phindu limodzi lokhalitsa lachikhulupiriro kuti: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) N’zoona, moyo wosatha ndi mphatso yabwinodi kwambiri kwa anthu achikhulupiriro!

Kukhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzafupa atumiki ake kumachititsa kuona moyo mosiyana ndi poyamba. Ahebri 11:6 amanena kuti chikhulupiriro choona chimaphatikizapo kukhulupirira kukhoza kwa Mulungu kufupa “mphotho iwo akum’funa Iye.” Choncho, n’zoonekeratu kuti chikhulupiriro choona si kutengeka maganizo ayi, komanso kuti si kungokhulupirira kuti Mulungu aliko kokha ayi. Chikhulupiriro choona chilinso kuvomereza kukhoza kwa Mulungu kupereka mphotho kwa iwo akum’funafuna iye. Kodi mukufunadi ndi mtima wonse kumudziŵa Mulungu? Ngati ndi choncho, pezani chidziŵitso cholongosoka kuchokera m’Mawu ake, Baibulo ndipo chikhulupiriro chanu chidzafupidwa.—Akolose 1:9, 10.

[Mawu a Chithunzi patsamba 20]

Zojambula za Albrecht Dürer/Dover Publications, Inc.