Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndiyenera Kudalira Mulungu”

“Ndiyenera Kudalira Mulungu”

“Ndiyenera Kudalira Mulungu”

Kalata yotsatirayi inapezeka m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya m’dera la Edmonton, m’chigawo cha Alberta, ku Canada.

“Mthenga Wokondedwa:

“Ndalemba kalatayi kuthokoza munthu amene mwina mosadziŵa anachita chozizwitsa m’moyo wanga.

“Milungu ingapo yapitayo, mwamuna wanga ndi ine tinakangana koopsa. Nthaŵiyo ndinali n’tangonena mawu akuti, ‘Izi zokha ndiye zandikulira sindikudziŵa ngati ndingathane nazo.’ Nthaŵi yomweyo belu la pachitseko linalira. Mosayembekezera ndinaona kuti munthuyo anali wa Mboni za Yehova, ndipo sindidakatha kubisala.

“Nditatsegula chitseko, ndinali wosokonezeka maganizo kwambiri kwakuti sindinamve zomwe anali kulankhula. Ndikukumbukirapo mawu akuti ‘ana’ ndiponso ‘banja’. Munthuyo anatulutsa buku lotchedwa Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Nditangoona mutu wa bukulo, ndinayamba kulira ndipo ndinalephera kusiya. Anaŵeramuka, ndipo kenako anapepesa chifukwa chondisokoneza, anandipatsa bukulo, ndipo anachoka.

“Chozizwitsa pamenepa chinali chiyani? Ndicho kundikumbutsa kuti pamene ndathedwa nzeru sindifunika kudera nkhaŵa chifukwa Mulungu amadziŵa. Ndiyenera kudalira Mulungu. Iye amatumiza mthenga. Zikomo kwambiri.”

Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lingapindulitse aliyense m’banja. Ina mwa mitu yake yophunzitsa ndi yakuti, “Tetezani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga,” “Sungani Mtendere m’Banja Mwanu,” ndi “Mukhoza Kulaka Mavuto Owononga Banja.”

Kuti mupeze buku lanu, lembani zofunika pa silipi lotsatirali ndipo tumizani ku adiresi yosonyezedwa pamenepo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa pa tsamba 5 la magazini ano. Mudzalandira malingaliro atsatanetsatane amene angakuthandizeni kuthana ndi mavuto ndi kupangitsa moyo wabanja kukhala wosangalatsa monga mmene Mlengi anafunira.

□ Nditumizireni buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.