Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinapatsidwa Chikhumbo Chokhala ndi Moyo

Tinapatsidwa Chikhumbo Chokhala ndi Moyo

Tinapatsidwa Chikhumbo Chokhala ndi Moyo

MARY anali kudwala matenda a kuvutika maganizo ndiponso matenda ena. Komabe, sanasiye kuganizira za banja lake, ndiponso sanali kumwa moŵa mwauchidakwa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nkhani ya Mary ikuonetseratu kuti si kuti munthu amatsimikiza kufuna kudzipha pokhapokha ngati zifukwa zonse zodziphera zilipo.

Kwakanthaŵi ndithu zinaoneka kuti Mary adzakhala akuŵerengedwa m’gulu la anthu achikulire amene amadzipha motsimikiza. Anali chikomokere kwa masiku angapo, akulephera kuchita chilichonse, ali gone m’chipinda cha odwala matenda akayakaya ku chipatala chakwawo. Sankatha kupuma bwino, thupi lake linazizira, ndipo mtima wake sunkagunda bwino. Mwamuna wake John anali ndi nkhaŵa zedi ndipo nthaŵi yonseyo sanali kutalikira. Madokotala anachenjeza John ndi banjalo kuti mwina Mary sachira ndipo kuti ngakhale atachira n’zotheka kuti ubongo wake udzawonongekeratu.

Mary anali kuzondedwa ndi mnansi wake wina wotchedwa Sally tsiku ndi tsiku, ndipo iyeyu ndi wa Mboni za Yehova. “Ndinali kulimbikitsa banjalo kuti lisataye chiyembekezo,” anatero Sally. “Amayi anga amadwala matenda a shuga ndipo zaka zingapo zapitazi iwo anakhala chikomokere kwa milungu ingapo. Madokotala anauza banja lathu kuti iwo sadzachira, koma anachira. Ndinali kutenga dzanja la Mary ndi kumamulankhulitsa, monga momwe ndinali kuchitira ndi amayi angawo, ndipo ndikatero ndimamva kuti akugwedezeka pang’ono.” Patsiku lachitatu anali kugwedezeka kwambiri ndithu, ndipo zinkaoneka kuti Mary ankatha kuzindikira anthu, ngakhale kuti iye sanali kulankhula.

‘Kodi Ndikanatha Kupeŵa Zimenezi?’

“John anali kudzimva monga wolakwa kwambiri,” anatero Sally. “Iye anali wotsimikiza kuti ndiye analakwa.” Kudzimva m’njira imeneyi n’kofala pamene wokondedwa wadzipha kapena ngati anafuna kudzipha. “Ndinamuuza kuti ayenera kudziŵa kuti Mary anali kulandira chithandizo chamatenda a kuvutika maganizo. Anali kudwala ndipo sakanatha kupeŵa kuvutika maganizo monga mmene John nayenso sangapeŵere kudwala.”

Anthu amene okondedwa awo amadzipha amavutika kwambiri podzifunsa kuti, kodi ndikanachita chiyani kuti ndipeŵe zimenezi? Kukhala tcheru pakakhala zizindikiro zochenjeza ndiponso mikhalidwe yochititsa mchitidwewu kungachititse kuti munthu wofuna kudzipha alephere kutero. Koma ngati mwalephera kutero, muyenera kudziŵa kuti inu si amene mwachititsa kuti munthu adziphe mwadala. (Agalatiya 6:5) Zimenezi n’zofunika kuzikumbukira makamaka pamene mbale wake wina wa munthu wodziphayo wakonza zakuti achititse ena kudzimva monga olakwa. Dr. Hendin, amene mawu ake tawatchula aja, ananena kuti: “Tiyenera kudziŵa kuti kufuna kudzipha nthaŵi zambiri kumachitidwa ndi anthu amene akufuna kukhudza kapena kusintha maganizo a anthu ena ngakhale kuti akadzipha sadzakhalapo kuti adzaone ngati anakwanitsadi zolinga zawo kapena ayi.”

Dr. Hendin anapitiriza kunena kuti: “Anthu achikulire amene amakhala ndi maganizo odzipha, nthaŵi zambiri amafuna kuti ana awo aakulu misinkhu kapena abale awo a bere limodzi kapenanso munthu amene anakwatirana naye amuchititse kapena kumukakamiza kuti aziwateteza kwambiri. Zimene wodwalayo amafuna nthaŵi zambiri zimakhala zovuta kuzichita, ndipo nthaŵi zambiri wodwalayo safuna kugonja, ndipo ngati wayesa kudzipha mongoyerekezera nthaŵi zambiri amadzayesa kudzipha motsimikiza.”

Abale ake omwe amakhala mumkhalidwewu angaone kuti ali pavuto lalikulu kwambiri, loti sangathe kulimbana nawo. Komabe, osaiwala kuti Yehova Mulungu amaukitsa anthu akufa ndipo kuti ena mwa ameneŵa angakhale okondedwa athu amene anadzipha chifukwa cha matenda a kuvutika maganizo, kusokonezeka mutu, kapena kuthedwa nzeru.—Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kudzipha—Kodi Pali Chiukiriro?” mu Galamukani! ya September 8, 1990, masamba 22-3.

Ngakhale kuti kudzipha sikungakhale koyenera, timalimbikitsidwa podziŵa kuti tsogolo la okondedwa athu lili m’manja mwa Mulungu amene amamvetsa kuti kufooka mwakuthupi ndi mwamaganizo kungam’kakamize munthu wothedwa nzeru kuchita zimenezi. Ponenapo za Yehova, Baibulo limati: “Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum’mawa kutanimpha [“kutalikirana,” NW] ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”—Salmo 103:11-14.

Chotsatirapo Chake Chosangalatsa

Kwa masiku aŵiri Mary anali mumkhalidwe wamoyo kapena imfa, komabe iye anapulumuka. Mwapang’onopang’ono maganizo ake anabwereramo, ndipo John amam’tengera kunyumba, apa n’kuti mankhwala onse atawatsekera. Pakali pano antchito yothandiza anthu pa matenda a maganizo amamuyendera Mary ndipo iye akuti sangathe kulongosola kapena kukumbukira chikhumbo choipa chimene chinangotsala pang’ono kumuphetsa.

Pakali pano Sally, amene amakhala moyandikana ndi John ndiponso Mary, amaphunzira nawo Baibulo mlungu uliwonse. Iwo aphunzira kuchokera m’Baibulo kuti ngakhale mavuto amene amaoneka kuti n’ngosatheka kuthetsedwa, makamaka kwa akulu, Mulungu adzawathetsa posachedwapa. “Inde, si kuti palokha phunziro la Baibulo limathetseratu vuto lina lililonse ayi,” anatero Sally. “Uyenera kutsimikizira wekha kuchokera m’Malemba kuti malonjezo ameneŵa ndi enieni, ndiye kenako uyenera kugwiritsa ntchito zimene ukuphunzirazo. Komabe ine ndikuganiza kuti John ndi Mary akupeza chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo.”

Ngati mukuona kuti tsogolo lanu n’lokayikitsa ndipo ngati mungakonde kukhala ndi chiyembekezo chenicheni, bwanji osapezana ndi a Mboni za Yehova? Aloleni kuti akutsimikizireni monga anachitira kwa John ndi Mary, kuti palibe mavuto amene Mulungu sangathe ndiponso sadzatha kuwathetsa m’tsogolo muno posachedwapa. Ngakhale zinthu zitaipa bwanji pakali pano, yankho lilipo. Chonde tiyeni tionere limodzi chiyembekezo chotsimikizika cham’tsogolo chimene chachititsa anthu ambiri kukhalanso ndi chikhumbo chokhala ndi moyo.

[Bokosi patsamba 16]

Zifukwa Ndiponso Zizindikiro za Kufuna Kudzipha

“Zifukwa zimene zingachititse anthu achikulire kudzipha n’zosiyana ndi za achinyamata,” inatero magazini yotchedwa The Journal of the American Medical Association. Zina mwa zifukwa zimenezo ndizo “kufala kwa uchidakwa ndi kuvutika maganizo, kugwiritsa ntchito njira zangozi kwambiri, ndiponso kudzipatula kwa anthu ena. Kuphatikizanso apo, anthu achikulire . . . amakhala ndi zinthu zambiri zowadwalitsa ndiponso mavuto a maganizo.” Buku lotchedwa Suicide, lolembedwa ndi Stephen Flanders, likutchula zifukwa zotsatirazi, zonsezi n’zofunika kuziganizira bwino.

Kuvutika maganizo kwa nthaŵi yaitali:

“Anthu ofufuza anena kuti 50 peresenti kapena kuposerapo ya anthu odzipha amakhala kuti m’mbuyomo anali kuvutika maganizo kwambiri.”

Kupanda chiyembekezo:

Pakufufuza kwina, ngakhale anthu amene sanali kuoneka kuti akuvutika maganizo anali oti angafune kudzipha ngati atapanda chiyembekezo cham’tsogolo.

Uchidakwa ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo:

“Akuti pakati pa 7 ndi 21 peresenti [ya zidakwa] amadzipha, pamene anthu osamwa ndi 1 peresenti yokha.”

Kuchititsidwa ndi achibale:

“Kafukufuku wasonyeza kuti achibale a munthu amene wadzipha ali pangozi yaikulu yakuti nawonso angadziphe.”

Matenda:

“Kwa anthu okalamba kungokhala chabe ndi mantha akuti adzayamba kufooka, ndipo n’kukagonekedwa m’nyumba zosamalira okalamba kungawachititse kufuna kudzipha.”

Zinthu zotaika:

“Chinthu chotaikacho chingakhale chinthu chooneka ndi maso, monga wokwatirana naye kapena mnzanu, ntchito yanu, kapenanso thanzi lanu. Chingakhalenso chinthu chosaoneka ndi maso. Zitsanzo zake zingakhale zinthu monga kudziona monga wofunika, kudzilemekeza, kapena kudzimva monga wotetezeka.”

Kuphatikiza pazifukwa zimenezi, buku la Flander linandandalitsa zizindikiro zochenjeza zotsatirazi zimene siziyenera kunyalanyazidwa.

Mbiri yofuna kudzipha:

“Ichi ndicho chizindikiro chachikulu kwambiri chodziŵira ofuna kudzipha.”

Kulankhula zofuna kudzipha:

“Mawu monga akuti ‘Sadzavutikanso n’kuganiza za ine ayi’ kapena ‘Popanda ine angapume’ ndi zitsanzo za mawu oopseza osonyezeratu kufuna kudzipha.”

Zochita zokonzekera:

“Zinthu zimenezi ndi monga kukonza ndondomeko ya kagaŵidwe ka chuma, kupereka zinthu zimene amazikonda, ndi kupatsa anthu ziŵeto.”

Kusintha umunthu kapena khalidwe:

Pamene munthu wasintha komanso “n’kumalankhula mawu osonyeza kudziona monga wosafunika kapena kusakhala ndi chiyembekezo,” ndiye kuti chingakhale “chizindikiro chokwanira cha kuvutika maganizo kochititsa munthu kudzipha.”

[Chithunzi patsamba 17]

Anthu otsala nthaŵi zambiri amafuna kuthandizidwa kuti apirire imfa ya okwatirana nawo amene adzipha