Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukapolo Wamakono Uli Pafupi Kutha!

Ukapolo Wamakono Uli Pafupi Kutha!

Ukapolo Wamakono Uli Pafupi Kutha!

“Ufulu wamunthu m’modzi uli mbali ya ufulu wa anthu onse. Sizingatheke kuwononga ufulu wa munthu m’modzi popanda kuika ufulu wa anthu onse pangozi.”—Victor Schoelcher, Mtolankhani Ndiponso Wandale Wachifalansa, 1848.

“KODI khalidwe loipa lamunthu limene nthaŵi zonse lakhala likum’chititsa kunyazitsa, kupondereza, ndi kupeputsa anthu anzake n’lotani? Ndipo kodi zatheka bwanji kuti mchitidwe wolakwira anthu ngati umenewu sukulangidwabe ngakhale pamene Ufulu Wachibadwidwe unayamba?” Anafunsa motero akonzi a magazini yotchedwa The UNESCO Courier.

Yankho lake n’lovuta kulimvetsa. Umbombo ndiwo ukusonkhezera mchitidwe wogwiritsa ntchito ana mwankhanza ndi kuwapatsa malipiro ochepa ndiponso mchitidwe wogwira anthu ukapolo chifukwa cha ngongole. Umphaŵi ndiponso kusaphunzira n’zimene akuti zikuchititsa kuti atsikana azigulitsidwa kukachita uhule ndi ukwati waukapolo. Zochita zachipembedzo ndiponso mfundo zamiyambo ndizo zimachititsa ukapolo wamwambo. Komanso chilakolako choipa cha kugonana ndiponso khalidwe loipa n’zimene zimasonkhezera amuna amene amapita ku Bangkok ndi ku Manila kukafuna tiana, tianyamata kapena tiatsikana topanda matenda a AIDS. Malingana ndi zimene ananena mtumwi Paulo, wophunzira chilamulo wa m’zaka za zana loyamba, zonsezi zili mbali ya dziko limene anthu ake ali “odzikonda okha, okonda ndalama, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakhoza kudziletsa, aukali.” (2 Timoteo 3:1-5) Malinga ndi mawu a wolamulira wina wamakedzana wotchedwa Solomo, zimenezi zili mbali ya dziko limene “chokhotakhota sichingawongokenso; ndipo chopereŵera sichingaŵerengedwe.”—Mlaliki 1:15.

Kusintha Malingaliro

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chimene chingachitike kapena chomwe chidzachitika kuti ukapolo, kaya ukhale wamwambo kapena wamakonowu utheretu? Ayi ndithu!

Gulu la bungwe la United Nations loona zaufulu wachibadwidwe lotchedwa Office of the High Commissioner for Human Rights (OHCHR) linanena kuti ukapolo ndi “mkhalidwe wa maganizo.” Linawonjezera kuti: “Ngakhale utathetsedwa, ukapolo umatsalirabe m’maganizo. Uwo umakhalapobe m’maganizo a anthu amene anakhalapo akapolo ndiponso kwa mbadwa zawo, komanso kwa anthu oloŵa m’malo mwa amene ankauchita. Zonsezi zimadzachitika m’tsogolo kwambiri pambuyo pakuti waletsedwa kale mwalamulo.”

Choncho njira imodzi yothetsera ukapolo ndiyo kusintha kaganizidwe ndi mitima ya anthu padziko lonse. Ndipo zimenezi zimaphatikizapo kusintha maphunziro, kuti akhale ophunzitsa anthu kukondana ndi kulemekezana. Izi zikutanthauza kuthandiza anthu kuti achotse umbombo m’mitima yawo ndipo atsatire miyezo yapamwamba yamakhalidwe abwino. Kodi ndani angapereke maphunziro ngati ameneŵa? Gulu la OHCHR linanena kuti “aliyense ayenera kuthandizapo kupanga dongosolo ladziko limene silingalorenso mchitidwe wankhanza wodyerana masuku pamutu.”

Taganizirani za ntchito yophunzitsa imene yakhala ikuchitidwa padziko lonse ndi anthu achikristu a Mboni za Yehova. Ntchitoyi yakwanitsa kuphunzitsa anthu oona mtima kusalola kapena kulekelera mchitidwe wankhanza wodyerana masuku pamutu. Kupyolera m’ntchitoyi, anthu miyandamiyanda m’mayiko oposa 230 aphunzitsidwa kulemekeza anthu anzawo onse. Kodi n’chifukwa chiyani ntchitoyi ikupambana?

N’chifukwa chakuti n’njozikidwa m’Baibulo, buku louziridwa ndi Mlengi wa munthu. Limeneli ndi buku limene limalemekeza anthu. Anthu ophunzitsidwa zochokera m’Baibulo kudzera m’ntchito yophunzitsa ya Mboni za Yehova akudziŵa kuti Mlengi wathu, Yehova, iyemwini ndiye Mulungu waulemu.” (1 Mbiri 16:27) Iye amagaŵira ulemu kwa zolengedwa zake zonse. Izi zikuphatikizapo amuna ndi akazi, ochokera m’mitundu yonse, chikhalidwe chonse, ndiponso amphaŵi kapena olemera.—Onani bokosi lakuti “Ufulu ndi Ulemu wa Anthu—Kodi Zidzachokera Kuti?”

Kulingana Ndiponso Kulemekezana

Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ‘analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.’ (Machitidwe 17:26) Choncho, palibe munthu anganene kuti n’ngwoposa mnzake aliyense kapena kuti ali ndi ufulu wopondereza kapena kudyera ena masuku pamutu. Anthu amene amafuna kuphunzira afika pozindikira mfundo yakuti ‘Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.’ (Machitidwe 10:34, 35) Iwo azindikira kuti chikondi cha Mulungu chilibe malire, popeza kuti anthu onse ali ndi mwayi wokhala pa unansi wolimba ndi iye. Ndiponsotu, ‘Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16.

Maphunziro ozikidwa m’Baibulo ameneŵa amakhudza kwambiri makhalidwe. Amachititsa mitima ndi malingaliro a anthu kuti ‘zikonzeke n’kukhaladi zatsopano.’ (Aefeso 4:22-24 Today’s English Version) Phunziroli limawasonkhezera kulemekeza anthu anzawo. Iwo amakhala otsimikiza ‘kuchitira onse chokoma.’ (Agalatiya 6:10) Palibe munthu angakhale Mkristu woona kwinaku akuchita nawo mchitidwe wankhanza wodyerana masuku pamutu ndiponso kupondereza anthu anzake. Mboni za Yehova zili zokondwa kukhala mtundu wa Akristu ofanana ndi Akristu a mumpingo wa m’zaka za zana loyamba, momwe ‘munalibe Myuda kapena Mhelene, munalibe kapolo kapena mfulu, . . . pakuti onse anali mmodzi mwa Kristu Yesu.’—Agalatiya 3:28.

Kusintha Boma

Komabe, kuti ukapolo wamtundu uliwonse utheretu, anthu afunika kusintha kotheratu. Bungwe lapadziko lonse loona za ntchito, lotchedwa International Labor Organization linanena zoti, kuti tithetse mchitidwe wodyerana masuku pamutu, pafunika “kusintha chikhalidwe chimene chimalola ndiponso kulekelera” mikhalidwe ngati imeneyi. Ntchito zamayiko osiyanasiyana, mgwirizano wamayiko osiyanasiyana, ndiponso kudzipereka kwa anthu padziko lonse ndiwo malingaliro ena othandiza amene bungwelo linapanga.

Ndithudi zimenezi zifunika boma lamphamvu loti likwanitse kulamulira pulaneti lathu lonseli, boma loti likwanitse kuonetsetsa kuti aliyense ali paufulu. Boutros Boutros-Ghali, yemwe kale anali mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, ananena kuti mavuto aakulu amene akuvutitsa dziko lathu lapansili ayenera kuthetsedwa “pamlingo wadziko lonse.” Komabe si aliyense amene ali otsimikiza kuti zimenezi zingadzachitike n’komwe. Zochitika zam’mbuyomu zikusonyeza kuti anthu olamulira ambiri ndi odzikonda zedi ndiponso amangoumilira maganizo awo pazofuna ndiponso zolinga zawo kwakuti sizingatheke kuti agwirizane padziko lonse.

Komabe, Baibulo—buku lomwe laphunzitsa anthu miyandamiyanda kulemekeza anthu anzawo, likusonyeza kuti cholinga cha Mulungu ndicho kukhazikitsa boma loterolo lapadziko lonse. M’Baibulo muli malonjezo ambiri amene mungawapeze onena za dziko latsopano lachilungamo. (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13) Cholinga cha Mulungu n’chakuti achotse padziko lapansi aliyense amene sakonda Mulungu komanso anansi ake. Mulungu wavumbula cholinga chake chokhazikitsira mtundu wa anthu boma lapadziko lonse kuti lilamulire dziko lapansi mwachilungamo. Yesu m’mawu ake odziŵika kuti Pemphero la Ambuye kapena kuti Atate Wathu, anatiuza kupempherera boma limenelo.—Mateyu 6:9, 10.

Mchitidwe wodyerana masuku pamutu ndiponso ukapolo wamtundu wina uliwonse udzachotsedwa muulamuliro wa bomali chifukwa chakuti Kristu Mfumu adzalamulira mwa “chiweruziro ndi chilungamo.” (Yesaya 9:7) Oponderezedwa adzapeza mpumulo muulamuliro wake wachilungamo, pakuti Baibulo limanena kuti: “Adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiŵaŵa.”—Salmo 72:12-14.

Ngati inuyo mukulakalaka kuona mapeto aukapolo, ukapolo wamtundu wina uliwonse, tikukupemphani kuphunzira zowonjezereka ponena za cholinga cha Mulungu chokhazikitsa boma lotero lapadziko lonse limene lidzamasula anthu. Mboni za Yehova zakwanuko zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuchita zimenezi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

UFULU NDI ULEMU WA ANTHU—KODI ZIDZACHOKERA KUTI?

Tonsefe timabadwa ndi khalidwe la kufuna ndiponso kukhumba kupatsidwa ulemu ndi ufulu. Kofi Annan, yemwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, ananena malingaliro amene aliyense ali nawo pamene anafunsa kuti: “Kodi ndani angakane kuti tonsefe timafuna kukhala ndi moyo wopanda mantha, wopanda kuzunzidwa, ndiponso wopanda tsankho? . . . Kodi munamvapo liti kuti munthu waufulu akufuna kuti ufulu uthe? Ndipo kodi n’kuti munamvapo zoti kapolo akulimbikitsa ukapolo?”

Malingaliro otereŵa si achilendo konse. Potsutsa lingaliro lakuti anthu ena amabadwira kudzakhala akapolo, wafilosofi wina wachiroma wa m’zaka za zana loyamba wotchedwa Seneca, analemba m’buku lake lotchedwa Letters to Lucilius kuti: “Chonde zindikira kuti munthu amene ukumutchula kuti kapolo wako, anachokera kumbewu yomwenso unachokerako iwe, nayenso amaona thambo lokongola kumwamba, amapuma monga umachitira iwe, ali ndi moyo monga wako, amafanso monga iwe!”

Mtsogoleri wachisilamu wotchedwa ʽAlī, amene amapatsidwa ulemu monga woloŵa m’malo wachinayi wa Muḥammad, ananena kuti anthu onse “analengedwa molingana.” M’lakatuli wina wa ku Peresiya wa m’zaka zoyambira 1200 wotchedwa Saʽdī anati: “Ana a Adamu ndi a bere limodzi ndiponso m’chilengedwe chawo anachokera ku chinthu chimodzi. Pamene dziko lizunza mwana m’modzi, ana enawo amasoŵa mtendere.”

Nkhani yamakedzana youziridwa ndi Mulungu yopezeka m’Baibulo imagogomeza za kulemekeza anthu onse. Mwachitsanzo, polongosola za chilengedwe cha munthu, Genesis 1:27 amanena kuti: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” Mlengi wathu ndi Mulungu waufulu. Mtumwi Paulo ananena kuti, “pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Polenga munthu m’chifaniziro chake ndiponso m’chikhalidwe chake, Yehova anagaŵira anthu mlingo winawake wa kudzimva kukhala ofunika, kudzilemekeza, ndiponso ulemu. Mwa kumasula zolengedwa zake ku “ukapolo wa chivundi,” iye adzaonetsetsanso kuti anthu adzakhale ndi ufulu ndi ulemu woterewu kwamuyaya.—Aroma 8:21.

[Chithunzi patsamba 9]

Aliyense ayenera kulandira ulemu ndiponso kukhala ndi ufulu

[Zithunzi patsamba 10]

MAPHUNZIRO A BAIBULO AMAGOGOMEZA KULEMEKEZA ANTHU NDIPONSO AMAPEREKA CHIYEMBEKEZO CHAM’TSOGOLO

Phunziro la Baibulo la banja ku Benin

Kukongola kwa mathithi awa a mtsinje wa Blue Nile ku Ethiopia kukupereka chithunzithunzi chabe cha paradaiso wobwezeretsedwayo