Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro Cholimba M’kati mwa Mavuto

Chikhulupiriro Cholimba M’kati mwa Mavuto

Chikhulupiriro Cholimba M’kati mwa Mavuto

PAFUPIFUPI zaka 60 zapitazo, Mina Esch analandira kalata kuchokera kwa mwamuna wake, Peter. Analembamo uthenga wachidule ndiponso wovuta kumvetsa. Komabe, iye ataulandira anasangalala ndiponso mtima wake unakhala pansi. Mwamuna wa Mina anali mkaidi ku msasa wachibalo wotchedwa Buchenwald, kumene anatumizidwa ndi boma la chipani cha Nazi chifukwa chakuti anali wa Mboni za Yehova. Kuseli kwa kalatayo kunali mawu osafunikira akuti: “Mkaidi ameneyu adakachitabe makani kuti adakali Wophunzira Baibulo. [Monga mmene Mboni za Yehova zinkatchulidwira panthaŵiyo] . . . Pachifukwa chokhachi basi, alibe mwaŵi wakuti angalemberane nanu makalata popanda chovuta ngakhale kuti timalola kutero.” Uthenga umenewu unam’dziŵitsa Mina kuti Peter anagwira molimba chikhulupiriro chake.

Kalatayi, tsopano ili yopyapyala kwambiri ndiponso yodetsedwa, ndipo aibwereketsa ku nyumba yosungiramo zinthu zakale zachiyuda yotchedwa Museum of Jewish Heritage—A Living Memorial to the Holocaust, imene ili kudera lotchedwa Battery Park, mu Mzinda wa New York. Pamodzinso ndi chithunzi cha Peter Esch, kalatayo ikuthandiza kulongosola mbali yaing’ono chabe ya tsoka lalikulu limene anthu anaona, la Kupululidwa ndi Chipani cha Nazi, pamene Ayuda okwana 6 miliyoni anafa. Zinthu zofunika kwambiri zimene akuzionetsa m’nyumbayi ndi monga zithunzi zopitirira 2,000 ndiponso zinthu zina zokonzedwa mwaluso zokwanira 800 za mbiri yakale ndiponso zachikhalidwe, zomwe n’zosonyeza zinthu zimene anthu achiyuda akhala akukumana nazo kuyambira cha m’ma 1880 mpaka kufika lero, kuphatikizaponso za Kupululidwa ndi Chipani cha Nazi. Kodi n’chifukwa chiyani nyumba yosungiramo zinthu zakale ya Museum of Jewish Heritage ili yoyenera kusonyezeramo kalata ya Peter Esch?

“Cholinga chachikulu cha nyumbayi n’chofuna kusonyeza mbiri yachiyuda,” analongosola motero katswiri wa mbiri ya zinthu zokhala m’nyumba zakale wotchedwa Dr. Jud Newborn. “Amboni za Yehova anazunzidwa pa chifukwa choti ndi Amboni. Amboni anazunzidwa chifukwa cha zikhulupiriro zawo zachipembedzo basi ndiponso chifukwa chakuti analibe maganizo atsankho, sankalumbira kuti adzachirikiza nawo munthu woipa, amenenso anali wakudziko ndi wankhanza. Ndipo iwo analibe maganizo omumenyera nkhondo. . . . Ayuda anayesetsa kusunga mfundo zawo ndiponso chikhulupiriro chawo uku akutsutsidwa kwadzaoneni. Nyumbayi ikuwaonetsa anthu kulimba kwa uzimu kumeneku. Pachifukwa chimenechi, nyumba ino imayamikira ndiponso imakhumbira chikhulupiriro cha Amboni za Yehova m’nyengo ya chipani cha Nazi.”

Kalata yachiduleyi ikupezeka m’nyumba ya Museum of Jewish Heritage, mmene idzakhalamo kwakanthaŵi chabe ndipo ikusonyeza kulimba kwa munthu mmodzi poyesedwa ngati ali okhulupirika kwa Yehova. Peter Esch anapulumuka m’mavuto amene anali nawo ku msasa wa chipani cha Nazi, ndipo sanataye chikhulupiriro chake.

[Chithunzi patsamba 15]

Nyumba ya Museum of Jewish Heritage, mu mzinda wa New York

[Zithunzi patsamba 15]

Esch, amene ali Wamboni za Yehova, anamangidwa kuchokera m’1938 mpaka 1945 chifukwa chakuti anakana kusiya zimene ankakhulupirira