Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lokoledwa ndi Kusuta

Dziko Lokoledwa ndi Kusuta

Dziko Lokoledwa ndi Kusuta

BILL anali munthu wokoma mtima, munthu wanzeru, munthu wamphamvu. Ankakonda banja lake. Koma, anayamba kusuta fodya akali wamng’ono. Pambuyo pake anayamba kudana ndi chizoloŵezichi. Ngakhale pamene amasuta ndudu, iye ankachenjeza kwambiri ana ake amuna za kusuta, akumafotokoza momwe kusuta kunalili kupusa. Pankakhala nthaŵi zina pamene amapindapinda paketi ya ndudu m’manja ake a mphamvuwo n’kuiponyera kumbali ina ya chipinda, akulumbira kukhala atasuta ndudu yake yomaliza. Komabe, posapita nthaŵi amayambiranso kusuta. Poyamba amasuta mwamtseri, ndipo kenako poyera.

Bill anamwalira ndi matenda a kansa zaka 15 zapitazo, pambuyo pa kuvutika ndi ululu woopsa kwa miyezi yambiri. Akanakhala munthu wosasuta, bwenzi ali moyo lerolino. Mkazi wake akanakhalabe ndi mwamuna; ana ake amuna akanakhalabe ndi atate.

Ngakhale kuti imfa ya Bill inali yomvetsa chisoni kwambiri ku banja lake, si iye yekha amene anafa m’njira imeneyi. Malinga ndi World Health Organization (WHO), matenda oyambika chifukwa cha fodya amapha anthu pafupifupi mamiliyoni anayi chaka chilichonse, kapena kuti munthu mmodzi pa masekondi asanu ndi atatu alionse. Kusuta fodya ndilo gwero lalikulu la matenda padziko lonse lomwe lingapeŵedwe. Ngati mikhalidwe yomwe ilipoyi ipitirizabe, m’zaka 20 zikubwerazi kusuta kudzakhala gwero lalikulu la imfa ndi kulemala, ndi kupha anthu ambiri kuposa chiwonkhetso cha omwalira ndi AIDS, chifuwa cha TB, matenda a amayi apakati, ngozi za galimoto, kudzipha, ndiponso kuphana.

Ndudu zimapha. Koma ngakhale kuti zili choncho anthu osuta fodya ali ponseponse. Padziko lonse lapansi, anthu osachepera 1.1 biliyoni amasuta fodya, inatero WHO. Zimenezo zikutanthauza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa anthu achikulire atatu alionse padziko lonse amasuta.

Ofufuza amanena kuti ngakhale kuti makampani opanga fodya tsopano amapereka madola mamiliyoni mazana ambiri kulipirira milandu yawo ku khothi, ndalama zimenezi n’zochepa kwambiri poziyerekezera ndi phindu ladzaoneni limene amapeza. Mu United States mokha, ndudu pafupifupi 1.5 biliyoni zimapangidwa m’makampani opanga fodya tsiku lililonse. Padziko lonse lapansi, makampani opanga fodya ndiponso maboma amene amapanga okha fodya amagulitsa ndudu zoposa 5,000,000,000,000 chaka chilichonse!

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri chonchi akupitirizabe ndi chizoloŵezi chimene chimaphachi? Ngati inu m’masuta fodya, kodi mungasiye motani? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani zotsatira.