Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kulambira Yesu N’koyenera?

Kodi Kulambira Yesu N’koyenera?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kulambira Yesu N’koyenera?

M’ZAKA mazana ambiri zapitazi, anthu ambiri m’Gawo la Matchalitchi Achikristu alambira Yesu Kristu ngati kuti iye ndiye Mulungu Wamphamvuyonse. Komabe, Yesu mwini, anatsogolera anthu kuganizira ndiponso kulambira Yehova Mulungu yekha. Mwachitsanzo, pamene mdyerekezi anafuna kuti amulambire, Yesu anati: “Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekha yekha udzam’lambira.” (Mateyu 4:10) Nthaŵi ina Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa kumwamba.”—Mateyu 23:9.

Yesu analongosolera mayi wachisamariya mtundu wa kulambira umene anthu ayenera kuchitira Mulungu. Kulambira kwawo kuyenera kukhala kozikidwa mumzimu ndi m’choonadi. N’zoonadi, “Atate afuna otere akhale olambira ake.” (Yohane 4:23, 24) Inde, ndi Mulungu yekha amene ayenera kulambiridwa. Kulambira munthu aliyense kapena chinthu chilichonse ndiko kulambira mafano, ndipo n’koletsedwa m’Malemba Achihebri ndiponso m’Malemba Achigiriki.—Eksodo 20:4, 5; Agalatiya 5:19, 20.

Koma ena anganenepo kuti, ‘komatu, paja Baibulo limanena kuti tiyeneranso kulambira Yesu. Kodi pa Ahebri 1:6 Paulo sananene kuti: “Angelo onse a Mulungu azim’pembedza [Yesu]”?’ (Buku Loyera) Kodi tingalimvetse bwanji lemba limeneli poganiziranso zimene Baibulo limanena zokhudza kulambira mafano?

Zomwe Baibulo Limanena pa za Kulambira

Choyamba, tiyenera kumvetsa zimene Paulo anali kutanthauza pamenepa ponena kuti kulambira. Anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti pro·sky·neʹo. Buku lolongosola mawu a m’Baibulo lotchedwa Unger’s Bible Dictionary limati liwu limeneli tanthauzo lake lachindunji ndilo ‘kumpsompsona dzanja la munthu posonyeza kum’patsa ulemu.’ Buku lothirira ndemanga pa mawu a m’Chipangano Chatsopano lotchedwa An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine, limati liwu limeneli “limatanthauza mchitidwe uliwonse wosonyeza ulemu, kaya womuchitira munthu . . . kapenanso Mulungu.” M’nthaŵi za Baibulo liwu loti pro·sky·neʹo nthaŵi zambiri linali kutanthauzanso kugwada kwenikweni pamaso pamunthu wapamwamba.

Taganizirani za fanizo limene Yesu ananena la kapolo amene analephera kubweza ndalama zochuluka kwa mbuye wake. M’fanizo limeneli muli liwu lina la Chigiriki lochokera ku liwu lomweli, ndipo politembenuza Baibulo la King James Version limati: “Motero kapoloyo anagwada pansi, ndi kulambira [liwu lochokera ku pro·sky·neʹo] [mfumuyo], ndi kunena kuti, Ambuye, mundiyembekeze, ndipo ndidzakulipirani zonse.” (Mateyu 18:26; tapendeketsa mawu ndife.) Kodi munthu ameneyu anali kulambira mafano? Ayi ndithu! Iye anali kungosonyeza chabe thamo ndiponso ulemu woyenera mfumu, amene anali mbuye wake ndiponso wom’posa.

Kugwada, kapena ulemu woterewu, zinali zofala kwambiri m’madera a Kum’mawa m’nthaŵi za Baibulo. Yakobo anaweramira pansi nthaŵi zisanu ndi ziŵiri pamene anakumana ndi mbale wake, Esau. (Genesis 33:3) Abale ake a Yosefe anaweramira pansi, pamaso pake pochitira ulemu udindo wake ku bwalo lamilandu lalikulu la Aigupto. (Genesis 42:6) Podziŵa zimenezi tingathe kumvetsa bwino zimene zinachitika pamene openda nyenyezi aja anapeza Yesu ali khanda, nam’zindikira kuti anali “amene anabadwa Mfumu ya Ayuda.” Monga mmene nkhaniyi inalembedwera m’Baibulo la King James Version, akuti iwo “anagwada pansi, ndi kumulambira [pro·sky·neʹo] iye.”—Mateyu 2:2, 11.

Choncho, n’zachionekere kuti liwu lakuti pro·sky·neʹo, limene mabaibulo ena analitembenuza kuti “kulambira,” silitanthauza kulambira komwe kuli koyenera Yehova Mulungu yekha. Lingathenso kutanthauza ulemu umene ungapatsidwe kwa munthu mnzathu. Poyesa kupewa kusamvetsetsa, mabaibulo ena anatembenuzira liwu lakuti pro·sky·neʹo lomwe lili pa Ahebri 1:6 monga “anakam’chitira ulemu” (New Jerusalem Bible), “kumulemekeza” (The Complete Bible in Modern English), “kuwerama pamaso pake” (Twentieth Century New Testament), kapena “kumugwadira” (New World Translation).

Yesu N’ngwoyenera Kumuchitira Ulemu

Kodi Yesu n’ngwoyenera kumuchitira ulemu woterowo? Inde, ndithu! M’kalata yake yopita kwa Ahebri, mtumwi Paulo analongosola kuti monga “wolowa nyumba wa zonse, . . . ” Yesu ‘wakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m’Mwamba.’ (Ahebri 1:2-4) Motero, “m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afilipi 2:10, 11.

M’njira yosiyana ndi ena, posachedwapa Kristu adzagwiritsa ntchito udindo wake wokwezeka ndiponso mphamvu zake za ulamuliro zochuluka kusandutsa dziko lino kukhala paradaiso. Motsogozedwa ndi Mulungu, ndiponso chifukwa cha nsembe yadipo ya Yesu, iye adzachotsa padziko lapansi zokhumudwitsa zonse, zowawa zonse, ndiponso chisoni kuti anthu ogonjera ku ulamuliro wake wolungama adzakhale bwino. Choncho, kodi iyeyo si oyenera kuti tizimupatsa ulemu ndiponso kumumvera?—Salmo 2:12; Yesaya 9:6; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4.

“Mulungu Wansanje”

Komabe, Baibulo limalongosola momveka bwino, kuti polambira, kutanthauza kulambira kodzipereka mwachipembedzo, tiyenera kulambira Mulungu yekha basi. Mose analongosola kuti iye ndi “Mulungu wansanje.” Ndipo Baibulo limatilimbikitsa kuti “m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.”—Deuteronomo 4:24; Chivumbulutso 14:7.

Mosakayikira Yesu ali ndi mbali yofunika kwambiri pa kulambira koona, imene tiyenera kuilemekeza. (2 Akorinto 1:20, 21; 1 Timoteo 2:5) Iye ndiye njira yokha imene tingathe kudzeramo kuti tifike kwa Yehova Mulungu. (Yohane 14:6) Motero, Akristu oona amachita bwino polambira Yehova Mulungu yekha basi, amene ali Wamphamvuyonse.