Mmene Mungasiyire
Mmene Mungasiyire
MONGA momwe kulili kuphunzira kukwera njinga, nakonso kusiya kusuta fodya, si kaŵirikaŵiri pamene kumatheka pakuyesa koyamba. Choncho ngati mwatsimikizadi kuti musiye, muyenera kukonzekera kuyesayesa mobwerezabwereza kufikira mutasiya. Pamene mwayambiranso kusuta musaone ngati kuti mwalephera. Kulingalireni monga chinthu chopatsa phunziro, monga chopunthwitsa chaching’ono pa ntchito imene ingakhale yopambana kwambiri. Naŵa ena mwa malingaliro amene akhala othandiza kwa anthu ena. Mwina angakuthandizeni kwambiri nanunso.
Konzekeretsani Maganizo Anu Kuti Musiye
■ Choyamba, muyenera kudziŵa kuti kusiya kusuta fodya kumafuna khama. Ndandalikani zifukwa zanu zomwe mukufuna kusiyira, kuphatikizaponso mapindu onse. Mutasiya, kupenda zimenezi kudzalimbitsa chosankha chanu. Chikhumbo cha kusangalatsa Mulungu ndicho chisonkhezero chachikulu chosiyira. Baibulo limanena kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi nzeru zathu zonse, mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse. Zimenezi ndi zinthu zimene sitingathe kuchita ngati ndife oloŵerera m’kusuta fodya.—Marko 12:30.
■ Pendani chizoloŵezi chanu chosuta n’cholinga chakuti mupeze kuti ndi nthaŵi yanji ndipo n’chifukwa chiyani mumasuta. Kulemba pa pepala nthaŵi ndi malo amene mwasuta ndudu iliyonse m’kati mwa tsiku linalake kungakuthandizeni. Zimenezi zidzakuthandizani kuoneratu mikhalidwe imene ingadzakukopeni kuti musute pamene mwasiya.
Sankhani Tsiku Losiyira
■ Sankhani deti losiyira, ndipo lichongeni pa kalendala yanu. N’kwabwino kusankha tsiku limene simudzakhala opsinjika maganizo mosayenerera. Pamene tsikulo lafika, siyani—mwadzidzidzi ndiponso siyiranitu.
■ Deti losiya lisanafike, peŵani kukhala ndi mbale za phulusa, macheso, ndi malaitala. Chapani zovala zanu zonse zomwe zimanunkha fodya.
■ Lembani zilimbikitso za anthu ogwira nawo ntchito, anzanu, ndiponso a pabanja lanu kuti zikulimbikitseni pa zoyesayesa zanu zosiya kusuta. Musachite mantha kupempha ena kuti asamasute panthaŵi imene inu mulipo.
■ Konzani zinthu zoti mudzachite patsiku la kusiya kwanu. Mungakonze zopita kumalo ena omwe kusuta kuli koletsedwa, monga kupita ku malo osungirako zinthu zamakedzana kapena kunyumba ya kanema. Mungachitenso maseŵero olimbitsa thupi, monga kusambira kapena kukwera njinga kapena kuyenda mtunda wautali.
Kulimbana ndi Vuto la Kusiya Kusuta
Ngati ndinu wosuta fodya kwadzaoneni, mosakayikira mudzakumana ndi zizindikiro za kusiya, zimene zidzayamba kuoneka m’maola angapo mutasuta ndudu yanu yomaliza. Zimenezi zingaphatikizepo kupsa mtima msanga, kusaleza mtima, kusagwirizana ndi ena, kuda nkhaŵa, kupsinjika maganizo, kusoŵa tulo, kusakhazikika maganizo, kuwonjezeka kwa mudyo, ndiponso chibaba cha ndudu. Mwinamwake dokotala angakupatseni mankhwala omwe angathandize kuchepetsa zizindikiro zimenezi. Kuwonjezera pamenepo, pali zinthu zimene mungachite kuti zikuthandizeni kupambana pa nkhondo imeneyi.
■ M’kati mwa milungu yoyambirira yovutayo, idyani zakudya zokhala ndi mafuta ochepa, ndipo imwani madzi ambiri. Ena aona kukhala kothandiza kumatafuna ndiwo za masamba zosaphika, komanso makaroti ndi celery. Ngati muchita maseŵero olimbitsa thupi, mudzathandiza kuti muchepetse kunenepa ndi kuthetsa zinjenje.
■ Peŵani malo ndi zochitika komwe mungakopedwe kuti musute.
■ Limbanani ndi malingaliro oipa amene angakukopeni kuti musute. Ena mwa malingaliro oipa amene amafala pamene mukusiya kusuta ndi aŵa: ‘Ndingosutako lero lokha kuti ndithandizike kukhalabe ndi moyo panthaŵi yovutayi.’ ‘Kusuta ndilo tchimo lokhalo limene ndimachita!’ ‘Fodya sangakhale woipa choncho; ena mwa anthu osuta kwadzaoneni amakhala ndi moyo kwa zaka zoposa 90.’ ‘Ndidzafabe ndi chinachake.’ ‘Moyo susangalatsa wopanda fodya.’
■ Ngati mwatsala pang’ono kuti musute, zengerezani. Chibaba cha kanthaŵi kochepacho chingathe mwa kungodikira kwa mphindi khumi zokha. Nthaŵi zina malingaliro a kusadzasutanso fodya angaoneke ngati ochititsa mantha kwambiri. Ngati mukulingalira choncho, yesani kulingalira za kusiya kusuta kwa lero lokha basi.
■ Ngati mukufuna kutumikira Mulungu, pemphererani thandizo. Mlengi wathu wachikondi angapereke ‘thandizo panthaŵi yakusoŵa’ kwa anthu amene akuyesayesa kugwirizanitsa moyo wawo ndi chifuno chake. (Ahebri 4:16) Koma musayembekezere chozizwitsa. Muyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero anu.
Musayambirenso Kusuta Fodya
■ Miyezi itatu yoyambirira ndiyo yovuta kwambiri, komabe ngakhale pambuyo pa miyezi imeneyi muyenera, ngati n’kotheka, kupeŵa anthu amene amasuta ndiponso mikhalidwe imene ingakukopeni kuti musute.
■ Musadzinyenge ndi malingaliro akuti mungakhale wosuta wa apo ndi apo, ngakhale ngati munasiya kusuta kwa chaka chimodzi kapena kuposerapo.
■ Pambanani chiyeso chofuna kungosuta “ndudu imodzi yokha.” Ndudu imodzi yeniyeniyi ingakupangitseni kuti musute zina, ndipo posapita nthaŵi mudzapasula ntchito yonse yovuta yomwe munachita kuti musiye kusuta. Komabe, ngati mwafooka n’kusuta ndudu imodzi, palibe chifukwa choti musutirenso ina. Ngati mwayambiranso kusuta, siyaninso.
Anthu ambiri amene amasuta fodya anasiya mwachipambano. Mwakufunitsitsa ndi kuchita khama, nanunso mungatero!