Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nanga Bwanji za Kuboola Thupi?

Nanga Bwanji za Kuboola Thupi?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Nanga Bwanji za Kuboola Thupi?

‘Nthaŵi yoyamba pamene ndinaona anthu okhala ndi milomo ndi ziwalo zina za matupi awo zili zoboola, ndinaganiza kuti “Basi! Kumeneko ndiye kutsogola.”’—Lisa.

LISA saali yekha. Achinyamata omwe chiŵerengero chawo chikukulirakulira akuvala mphete ndi zipini m’ziŵalo zosiyanasiyana za thupi, ngakhale m’nsidze zawo, palilime, m’milomo, ndi m’michombo. Ndiwo mchitidwe umene umatchedwa kuti kuboola thupi. *

Msungwana wina wa zaka 16 zakubadwa wotchedwa Heather akufunitsitsa kuyamba nawo zimenezi. Akukhulupirira kuti kukhala ndi mphete panchombo pake kudzaoneka kukhala “kwachilendo ndiponso kwapamwamba kwambiri.” Koma, Joe wa zaka 19 anayamba kale kuvala kachipini ka golidi palilime lake modzionetsera ndiponso monyadira. Ndipo mtsikana wina anasankha kuboola m’nsidze chifukwa chakuti amafuna chinachake “chochititsa kaso” chimene “chingadolole anthu.”

Kuvala zodzikometsera sikwachilendo. Kale m’nthaŵi za Baibulo, mkazi woopa Mulungu wotchedwa Rebeka ankavala mphete ya pamphuno. (Genesis 24:22, 47) Pamene amatuluka mu Igupto, Aisrayeli anavala mphete. (Eksodo 32:2) Komabe ngakhale zinali choncho, sizikudziŵika ngati zokometserazo amavala mwa kuboola makutu ndi mphuno. Koma, akapolo okhulupirika ankabooledwa makutu, monga chisonyezero cha kugonjera kwawo kwa mbuye wawo. (Eksodo 21:6) Kuboola matupi kwakhalanso kodziŵika kwambiri m’chikhalidwe china chakale. Aaziteki ndi Amaya ankaboola malilime pazifukwa zauzimu. Kuboola mlomo kukadali kofala kwambiri mu Africa ndiponso pakati pa amwenye okhala ku South America. Kuika zinthu zokometsera mwa kuboola mphuno n’kofala kwambiri pakati pa anthu a ku Melanesia ndiponso nzika za ku India ndi Pakistan.

Mpaka kufikira zaka zingapo zapitazo, ku mayiko a Kumadzulo kuboola thupi kunali kwa makutu a azimayi okha basi. Koma tsopano achinyamata ponse paŵiri achimuna ndi achikazi akuvala zodzikometsera pafupifupi pachiŵalo chilichonse cha thupi pamene chokometseracho chingakhale.

Chifukwa Chimene Amadziboolera

Ambiri amadziboola chifukwa cholingalira kuti kutero ndiko kutsogola—chinthu chotsogola kwambiri. Ena amalingalira kuti kudzakongoletsa kaonekedwe kawo. Ndithudi, chizoloŵezi chimenechi chayambika chifukwa cha anthu opereka zitsanzo otsogola kwambiri, anthu otchuka a zamaseŵera, ndi magulu otchuka a zoyimbayimba amene amagwiritsa ntchito zokongoletsa thupi. Ndipo kwa achinyamata ena, kuboola thupi kumaonekanso ngati chisonyezero cha ufulu, chikhumbo chodziimira paokha, njira yawo yonenera kuti si ofanana ndi munthu wina aliyense. Wolemba nkhani John Leo anati: “Kukuoneka kuti chilakolako chofuna kukwiyitsa makolo ndiponso kuopseza anthu opeza bwino ndizo zisonkhezero zikuluzikulu kwambiri za kuboola matupi mobwerezabwereza.” Kusakhutitsidwa, kusagwirizana, kunyoza, ndiponso kupanduka zikuoneka kuti ndi zimene zikulimbikitsa cholinga chimenechi cha kudzinenera zakukhosi.

Komanso pali ena amene amadziboola n’cholinga chokhutiritsa zosoŵa zawo za m’maganizo. Mwachitsanzo, achinyamata ena amaganiza kuti kuchita zimenezi kudzawonjezera ulemu wawo. Achinyamata ena amene amazunzidwa amaona kuboola thupi monga njira yotetezera matupi awo.

Ngozi za Thanzi

Koma kodi kuboola matupi konse koteroko n’kwabwino? Madokotala ambiri amanena kuti kuboola kwina sikwabwino. Makamaka kudziboola wekha n’koopsa kwambiri. Ndiponso kupita kwa munthu wotchedwa kuti katswiri woboola kungakhalenso ndi ngozi zake. Ambiri amakhala osaphunzitsidwa mokwanira, popeza amaphunzira luso lawolo kuchokera kwa anzawo, m’magazini, ndi m’mavidiyo. Chotsatira chake n’chakuti, mwinamwake sangatsatire njira zaukhondo kapenanso kudziŵa kuopsa koboola matupi. Kuwonjezeranso pamenepo, oboola matupi ambiri sadziŵa bwinobwino momwe thupi linapangidwira. Limeneli ndi vuto lalikulu kwambiri, chifukwa chakuti kuboola malo olakwika kungataitse magazi ochuluka. Kuboola mtsempha kungavulaziretu kosatha.

Vuto lina lalikulu ndi la matenda. Zipangizo zosaŵiritsidwa m’madzi n’cholinga chakupha tizilombo toyambitsa matenda zingafalitse matenda akupha monga nthenda ya kutupa chiŵindi, AIDS, chifuwa cha TB, ndi kafumbata. Ngakhale ngati njira zaukhondo zitatsatidwa, m’pofunikabe kukhala osamala kwambiri pamene mwamaliza kuboolako. Mwachitsanzo, kuboola nchombo kungakhale kopweteka kwambiri chifukwa chakuti chovala chimakhala chikukhudza panchombopo nthaŵi ndi nthaŵi. Choncho pangatenge miyezi isanu ndi inayi kuti papole.

Madokotala amanena kuti kuboola chichereŵechereŵe cha mphuno kapena makutu n’koopsa kwambiri kusiyana ndi kuboola nsonga ya khutu. Kalata yolembedwa ndi American Academy of Facial Plastic and Reconstructive Surgery inati: “Kukhala ndi ziboo zambiri za ndolo kuzungulira m’mwamba mwa khutu n’kodetsa nkhaŵa kwambiri—matenda aakulu angawononge gawo lonse lam’mwamba mwa khutu. Nazonso zipini za pa mphuno n’zoopsa—matenda a malo ameneŵa angakhudze minyewa ya magazi yoyandikana nawo ndiponso matendawo angafalikire ku bongo.” Kalatayo inamaliza ndi kuti: “Choncho, [kuboola thupi] kuyenera kukhala kwa pansonga ya khutu basi.”

Ngozi zina ndizo zipsera zikuluzikulu ndiponso zimene thupi limachita ngati chokometseracho chili chakuti chingaboole thupi. Ngati mphete zomwe zili m’ziŵalo zofeŵa kwambiri, monga pabere, zikodwa kapena kukokedwa ndi chovala, chokometseracho chingathe kung’amba mnofu mosavuta. Khungu lolimba lachipsera m’kati mwa bere la mtsikana lingatseke njira zodutsa mkaka, ndipo ngati salandira thandizo, kungadzakhale kovuta kapena kosatheka kuti iye alere mwana m’tsogolo.

Bungwe la American Dental Association posachedwapa linatcha kuboola mkamwa kukhala upandu waukulu wa thanzi. Zina mwa ngozi za kuboola mkamwa ndizo kutsamwa mutameza mphete, kukhala wosalankhula ndiponso lilime kusatha kumva kukoma kwa chinthu, kutaya magazi kwa nthaŵi yaitali, mano obenthuka kapena owonongeka, kudzala malovu mkamwa, kuchucha malovu, kuwonongeka kwa nkhama, kusalankhula bwino, ndiponso kupuma, kutafuna, ndi kumeza movutikira. Pamene mtsikana wina wotchedwa Kendra anaboola lilime lake, lilimelo “linatupa ngati chibaluni.” Kuipa kwakenso, munthu amene anam’boolayo anagwiritsa ntchito chipini cha pachibwano, ndipo chinaloŵa pa lilime la Kendra n’kung’amba minofu ya m’kati. Iye saatha kulankhula bwinobwino.

Mulungu anaphunzitsa anthu ake, Aisrayeli, kuti azilemekeza matupi awo ndi kupeŵa kudzichekacheka. (Levitiko 19:28; 21:5; Deuteronomo 14:1) Ndipo pamene Akristu lerolino saali pansi pa Chilamulo cha Mose, iwo akulimbikitsidwabe kulemekeza matupi awo. (Aroma 12:1) Tsopano, kodi si kwanzeru kupeŵa ngozi za thanzi zachabechabe? Komanso, kuwonjezera pa za thanzi palinso zinthu zina zomwe muyenera kuzilingalira.

Kodi Zimafalitsa Uthenga Wotani?

Baibulo silipereka lamulo lachindunji lokhudzana ndi kuboola thupi. Koma limatilimbikitsa kudzikometsera “mwaulemu ndi modzichepetsa.” (1 Timoteo 2:9, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Pamene kuli kwakuti chinthu chinachake chingaonedwe kukhala chabwino m’dera lina la dziko lapansi, nkhani ingakhale yakuti kodi chimaonedwa motani kudera limene inu mukukhala. Mwachitsanzo, kumadera ena a dziko lapansi kuboola makutu a akazi kungakhale kovomerezedwa. Koma m’dziko lina kapena m’chikhalidwe china, ena angakhumudwe nazo.

Ngakhale kuti kwakhala kofala kwambiri pakati pa anthu otchuka, kuboola matupi ndi kuvala ndolo kwa amuna n’kosavomerezedwa ndi anthu ambiri a m’mayiko a Kumadzulo. Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti zimenezi kuyambira kale zakhala zizindikiro za akaidi oikidwa m’chipinda chimodzi, anthu oyendera limodzi panjinga zamoto, oyimba nyimbo zoipa, ndi kagulu ka anthu osangalatsidwa ndi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Kwa anthu ambiri, kuboola thupi kumatanthauza kuloŵerera ndi kupanduka. Anthu ambiri amakuona kukhala kochititsa nthumanzi kwambiri, konyansa. Mtsikana wachikristu wotchedwa Ashley anati: “Mnyamata wina m’kalasi mwathu anaboola mphuno. Iye amaganiza kuti ndi zabwino. Koma ine ndimaganiza kuti ndi zonyansa!”

Ndiyeno, m’posadabwitsa kuti sitolo ina yodziŵika bwino kwambiri ku America ili ndi lamulo lakuti anthu ake ogwira ntchito amene amakumana mwachindunji ndi makasitomala amaloledwa kuvala ndolo imodzi pa khutu lililonse ndi kuti kuboola thupi kulikonse kwa pamalo oonekera n’koletsedwa. “Simungadziŵe zimene anthu angaganize,” anatero mlankhuli wa kampaniyo. Nawonso alangizi a zantchito amalangizanso ophunzira achimuna a m’sukulu za maphunziro apamwamba kuti pamene akufunsira ntchito ‘asamavale ndolo kapena zokometsera zoboola thupi; akazi asamavale . . . zipini pamphuno.’

Nawonso achinyamata achikristu ayenera kuonetsetsa kuti akusonyeza makhalidwe abwino kwa anthu ena, kuphatikizanso panthaŵi imene akulalikira. Sakufuna kukhala ‘opatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumiki wawo usanenezedwe.’ (2 Akorinto 6:3, 4) Mulimonse mmene mungaonere nkhani ya kuboola thupi, kaonekedwe kanu mosapeŵeka kamafotokoza za malingaliro ndi khalidwe lanu. Kodi mukufuna kufotokoza za chiyani?

Ndithudi, inu ndiponso makolo anu, muyenera kusankha choti muchite pankhani imeneyi. “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano,” ndiwo uphungu wabwino kwambiri wa Baibulo. (Aroma 12:2) Ndi iko komwe, ndi inuyo amene mudzakumane ndi zotsatira zake.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mwa kutchula zimenezi, sitikunena za kuboola kolongosoka komwe n’kofala ndiponso kovomerezeka pachikhalidwe m’madera ambiri. Koma, tikunena za kuboola matupi konkitsa komwe n’kofala lerolino.—Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1974, masamba 318-19.

[Zithunzi patsamba 21]

Kuboola thupi n’kotchuka kwambiri pakati pa achinyamata