Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthenda Yotchedwa Huntington—Tidziŵe Bwino Tsoka Lachibadwa Limeneli

Nthenda Yotchedwa Huntington—Tidziŵe Bwino Tsoka Lachibadwa Limeneli

Nthenda Yotchedwa Huntington—Tidziŵe Bwino Tsoka Lachibadwa Limeneli

“Pamene Johnny ndi ine tinakwatirana, ndinkaganiza kuti kuchokera nthaŵiyo tidzakhala ndi moyo mosangalala mpaka kalekale. Komabe m’kupita kwanthaŵi, mwamuna wachikondi ndi wosamala ameneyu anasintha khalidwe lake kwambiri. Iye anayamba kufika pomakalipa mwachiwawa, mosaletseka. Patapita nthaŵi, Johnny anaikidwa m’chipatala cha anthu odwala matenda amaganizo, kumene potsirizira pake anamwalirira. Patapita zaka zingapo, tinadziŵa kuti nthenda yosadziŵika imeneyi dzina lake ndi Huntington.”—Janice.

ANTHU zikwizikwi padziko lonse amadwala nthenda imene m’chingelezi amaitcha Huntington (HD), ndipo imagwira majini aubongo ndi a m’fupa la msana. Popeza kuti nthenda ya HD n’njotengera kuchokera kwamakolo, nthaŵi zambiri imagwiranso anthu ena a m’banjalo. “Kuyambira pamene Johnny anamwalira, ana aamuna atatu ndi mtsikana mmodzi anamwalira ndi nthenda yomweyi, ndiponso adzukulu anga atatu ali ndi nthendayi.” Anatero Janice. “Zikuoneka kuti ndakhala ndikulira maliro a anthu a m’banja langa mongotsatizanatsatizana.”

N’chifukwa chake nthenda ya HD yatchulidwa kuti “chinthu choopsa kwambiri,” osati kwa wodwala yekhayo komanso kwa osamalira wodwalayo. * Koma kodi kwenikweni HD ndi nthenda yotani? Kodi amene akudwala nthendayi ndiponso amene akuwasamalira angathandizidwe bwanji?

Zizindikiro Zake

Dzina la nthendayi linatchulidwa potsatira dzina la dokotala amene anayamba kutulukira zizindikiro za nthendayi mu 1872 wotchedwa Dr. George Huntington. Nthenda imeneyi imadziŵika chifukwa cha kusintha kosaonekera kwa umunthu ndiponso kusintha kwa khalidwe zimene zimadzaonekera kwambiri nthendayi ikakula. Izi zimayambira pa kusinthasintha m’khalidwe wamaganizo ndiponso kukwiya kosautsa maganizo komanso kukhala ndi mtima wapachala. Mwinanso thupi la wodwalayo limanjenjemera lokha ndiponso manja ndi mapazi amalobodoka. Wodwalayo amayamba kulephera kuchita zinthu mosajejema ndipo amaphonyetsa zinthu pafupipafupi. Zolankhula zake sizimveka bwino. Amavutika kumeza, ndiponso mphamvu yokumbukira zinthu ndi kulingalira imachepa. Kuphunzira, kukonza zinthu, ndiponso kuthetsa mavuto, zomwe kale ankakwanitsa kuchita, tsopano zimakhala zovuta, mwinanso zosatheka n’komwe. *

Zizindikiro za nthenda ya HD zimapitirizabe ndipo zimawonjezeka kunthaŵi yonse yotsala ya moyo wa wodwalayo. * Mosapeŵeka, wodwalayo adzayenera kusiya ntchito yake ndipo sangathenso kudzisamalira yekha. Nthaŵi zambiri zimenezi ndizo zimapweteka kwambiri munthu wodwala HD. “Kale ndinkamanga nyumba ine, koma tsopano sindichita kalikonse. Ndimakhumudwa kwambiri,” anatero wodwala wina dzina lake Bill.

Ndithudi, zingakhale zopweteka kwambiri kwa munthu wodwala HD kuona thupi lake ndi nzeru zake zikumka zichepa. N’zopwetekanso mtima zedi kwa wokondedwa wake kuona wodwalayo akutsirizika ndi nthenda yakupha imeneyi. Ndiyeno kodi chingachitike n’chiyani kuti tim’thandize munthu wodwala HD?

Kuthandiza Wodwala

Ngakhale kuti nthenda ya HD n’njosachilitsika, chithandizo chokwanira chamankhwala chathandiza anthu ambiri kuthana ndi matenda ena obwera chifukwa cha nthendayi. “Zimenezi siziletsa nthendayi kufooketsa ziwalo zamunthu kwanthaŵi yaitali monga imachitira, komabe zimathandiza kwambiri kuti wodwalayo akhale ndi moyo wabwinopo,” anatero Dr. Kathleen Shannon.

Mwachitsanzo, odwala HD ena athandizidwa ndi mankhwala amene amaletsa kunjenjemera ndiponso kuchepetsa kuvutika maganizo. Katswiri wa zakadyedwe angaperekenso chithandizo chopindulitsa. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa chakuti nthaŵi zambiri odwala HD amaonda, ndipo kaŵirikaŵiri amafunikira zakudya zopatsa thanzi kuti asaonde.

Mwakugwiritsa ntchito luso pang’ono, mabanja ena akwanitsa kuthandiza wodwala kuzoloŵerana ndi zinthu zatsopano zomwe sangathe kuchita. Mwachitsanzo, Monica ananena kuti: “Pamene zolankhula za bambo anga zinafika poti sitinkazimva, tinafunafuna njira yoti tizidziŵira zomwe akufuna kuti tichite.” Monica ndi banja lake anapanga kabuku kamapepala otayanatayana amakatoni, kamene patsamba lililonse panali mawu amodzi kapena chithunzi. “Tinaphatikizapo abambo anga m’ntchitoyi,” anatero Monica. “Iwo anathandiza nawo kusankha zithunzi ndiponso mawu.” Pogwiritsa ntchito chida chatsopanochi, bambo a Monica amatha kulankhula mwa kuloza chithunzi kapena mawu a zinthu zimene ankalephera kutchula.

Ngakhale pamene wodwala wabindikira kunyumba kwake kapena kumalo osungirako anthu ovutika, kulankhulana ndi banja lake ndiponso mabwenzi ake n’kofunika. “Kungakhale kovuta kukacheza ndi wodwala HD amene wapezeka kwambiri,” anavomereza motero Janice, “komabe ana anga ankayamikira kwambiri pamene mabwenzi abwera kudzawalimbikitsa.” N’zachisoni kuti, nthaŵi zina mbali yothandiza imeneyi imanyalanyazidwa. “Nthaŵi zina timakhala osungulumwa,” anatero Beatrice amene mwamuna wake akudwala HD. “Ngati anzathu atangopatuka chabe n’kudzapereka moni yekha kwa mwamuna wanga, iye angaone kuti am’chitira chinthu chachikulu kwabasi!”

Pakuti taona mfundo zonsezi, nanga kodi wodwala HD kwenikweni amafuna chiyani? “Kutimvetsetsa basi,” anayankha motero Bobby, wodwala nthendayi amene ndi wa Mboni za Yehova. Iye anawonjezera kuti, “abale ndi alongo achikristu mumpingo amazindikira kuti zimanditengera nthaŵi kuti ndikonzekere kupereka yankho pamsonkhano, mwina ndimachedwa ndi mphindi imodzi kapena ziŵiri. Ndiponso iwo sakhumudwa ngati nditakalipa, popeza kuti ichi ndi chizindikiro cha nthendayi.”

Kuthandiza Osamala Odwala

N’zoonadi kuti osamala odwala nawonso amafunika kuwathandiza, chifukwa chakuti amakhala ndi nkhaŵa nthaŵi zambiri. “Nthaŵi zonse umadera nkhaŵa za umoyo wa wodwalayo. Matenda akewo akafika poipa, umasoŵa pogwira,” anatero Janice.

Mwachionekere, osamala odwala amafunika kuwalimbikitsa. Beatrice analongosola njira imodzi yochitira zimenezi. “Sindingathe kum’siya yekha mwamuna wanga,” iye anatero “ndipo nthaŵi iliyonse ndikaitanidwa kuphwando, ndimayenera kunena kuti, ‘zikomo kwambiri chifukwa chondiitana, koma sindibwera.’ Zingakhaledi bwino ngati mnzathu wina atanena kuti, ‘Ngati n’kotheka, bwanji mnyamata wanga kapena mwamuna wanga adzadwazikeko amuna anu kwakanthaŵi’!” Ndithudi, osamala odwala amayamikira kuwaganizira mwachifundo kotereku!—1 Petro 3:8.

Pamene nthenda ya HD yafika pachimake, osamala wodwalayo angafunikire kusankha kuchita zimene mwina zingakhale zopweteka mtima kwambiri koposa zonse. “Kunena mawu akuti, ‘sindingapitirizebe kukusamalirani,’ n’kovuta kwambiri,” anatero Janice.

Chinthu chimene Mkristu adzayenera kuchilingalira bwino ndiponso mwapemphero ndicho kukasiya wodwalayo kumalo osungirako anthu ovutika. Baibulo limalamula Akristu ‘kudzisungira mbumba yawo ya iwo okha’ ndipo zimenezi zimaphatikizapo kusamalira makolo athu kapena ana athu odwala. (1 Timoteo 5:8) Munthu aliyense asayese n’komwe kunyalanyaza udindo wa m’Malemba umenewu chifukwa chongofuna kuti apepukidwe. Komabe, mwina pangakhale zifukwa zina, monga ngati kudera nkhaŵa za moyo wa wodwalayo zimene zingachititse chisamaliro cha akatswiri kukhala njira yosonyeza kum’konda ndiponso yothandiza. Banja ndilo lingasankhe chochita pankhaniyi ndipo ena sayenera kuliimba mlandu.—Aroma 14:4.

Chiyembekezo Chodalirika

Baibulo ndilo kwenikweni limatonthoza anthu amene akulimbana ndi nthenda ya HD ndiponso matenda ena osachilitsika. Malemba amapereka chiyembekezo chodalirika cha dziko latsopano lolungama limene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Kuwonjezera apo, Baibulo limalosera kuti “wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 33:24; 35:6.

Bobby, amene mawu ake tawalemba koyambirira kuja, amatonthozedwa ndi chiyembekezo chimenechi. “Ameneŵa ndiwo mankhwala amene ndimawafunafuna,” iye anatero. “Ndilo tsogolo limene lidzapangitsa mavuto onseŵa kukhala zinthu zakale zosakumbukika.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nthenda ya HD imagwira akazi ndi amuna omwe. Komabe, kuti timvetse mosavuta, tidzakamba za nthendayi monga ya amuna.

^ ndime 6 Zizindikiro za nthenda ya HD ndiponso kufulumira kuonekera kwake zingakhale zosiyana kwambiri pakati pa anthu osiyanasiyana. Choncho, zizindikiro zimene talongosola panozi zaperekedwa kuti zikupatseni chithunzithunzi chabe ndipo sikuti zakonzedwa mwatsatanetsatane kotero kuti n’kuzigwiritsira ntchito pofuna kupeza nthendayi ayi.

^ ndime 7 Zaka zimene munthu wodwala HD amayembekezeka kukhalabe ndi moyo ndi pafupifupi 15 mpaka 20 kuchokera pamene zizindikiro za nthendayi zayamba, ngakhale kuti ena amakhala ndi moyo kwakanthaŵi ndithu. Nthaŵi zambiri wodwalayo amafa chifukwa cha chibayo popeza kuti satsokomola mokwanira kuti achotse makhololo amatenda m’chifuwa.

[Bokosi patsamba 13]

Tsoka Lotengera Nthenda ya HD Kwamakolo N’lalikulu

Tsoka ndiponso mwayi wakuti mwana aliyense amene makolo ake ali ndi nthenda ya HD atengera kapena satengera nthendayi n’zofanana. Kodi n’chifukwa chiyani zili motere?

Inuyo muli ndi tinthu tokwana magulu 23 totchedwa chromosomes. Timakhala tiŵiritiŵiri pagulu lililonse ndipo n’tolongedzedwa m’selo iliyonse ya thupi lanu. Kanthu kamodzi pagulu lililonse kanachokera kwa bambo anu; ndipo kanzakeko kanachokera kwa mayi anu. Ndiyeno, tangoyerekezani kuti bambo anu ali ndi HD. Popeza kuti bambowo adzapereka kamodzi mwa tinthu tawo tiŵiri tija ndipo kuti n’kamodzi kokha kamene kali kowonongeka, tsoka lakuti mungatengere nthenda ya HD kwamakolo n’lalikulu.

Popeza kuti zizindikiro za HD nthaŵi zambiri sizimaonekera msanga mpaka munthu atafika zaka zapakati pa 30 ndi 50, nthaŵi zina wodwalayo amapezedwa ndi nthendayi atabereka kale ana.

[Bokosi patsamba 14]

Kumuuza Kapena Kusamuuza

Pamene wodwala amupima kuti aone ngati ali ndi HD, kodi ayenera kuuzidwa zambiri motani? Mabanja ena amaopa kuti wodwalayo sadzamva bwino ngati atadziŵa kuti ali ndi nthenda yosachiritsika, ndiponso yoondetsa. Komabe, sikwanzeru kungolingalira chabe kuti iye safunika kudziŵitsidwa. “Mantha ndi chisoni chathu zingachititse kuti tizimuteteza momkitsa,” kanachenjeza motero kabuku kena kofotokoza za HD, ndipo kanawonjezera kuti: “[Wodwalayo mwina] angadzimve kukhala womasuka ngati atadziŵa chimene chikuchititsa matenda osautsa amene akudwala.” Komanso, popeza kuti nthendayi n’njopatsirana mwachibadwa, n’kofunika kuti amene ali ndi nthendayi adziŵe za kuopsa kopatsira mwana aliyense amene angadzakhale naye m’tsogolo.

[Chithunzi patsamba 13]

Janice, amene ana ake anayi anamwalira ndi nthenda yotchedwa Huntington