Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Loyenera Kulikumbukira

Tsiku Loyenera Kulikumbukira

April 19, 2000

Tsiku Loyenera Kulikumbukira

MADZULO a pambuyo pa tsiku limene anafa, Yesu anakhazikitsa chikumbutso cha imfa yake. Linali phwando laling’ono. Phwandolo lili m’kati iye anauza ophunzira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.

Chaka chino tsiku la chikumbutso chapachaka cha chochitika chimenechi ndilo Lachitatu, April 19, dzuŵa litangolowa.

Motero, Mboni za Yehova kuzungulira padziko lonse zidzasonkhana pausiku wapadera umenewu kuti zichite chikumbutsochi m’njira imene Yesu ananena. Mukuitanidwa mwachisangalalo kuti mudzakhale nazo limodzi. Lankhulani ndi a Mboni za Yehova kwanuko kuti akuuzeni nthaŵi ndiponso malo enieni a msonkhanowu.