Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lopanda Mabomba Okwirira

Dziko Lopanda Mabomba Okwirira

Dziko Lopanda Mabomba Okwirira

NDANI angathetse vuto la mabomba okwirira? Monga taonera, zoyesa za anthu sizingathetseretu chidani, makani, ndiponso umbombo. Komabe, ophunzira Baibulo amazindikira kuti Mlengi angathe kubweretsa njira yokhalitsa yothetsera vutoli. Koma kodi adzachita bwanji zimenezi?

Kukhazikitsa Dziko Lamtendere

Amamenya nkhondo ndi anthu, osati zida. Choncho ngati tikufuna mtendere, chidani chimene chimagawa anthu m’mafuko, m’mitundu, ndiponso m’zigawo chiyenera kuthetsedwa. Mulungu akulonjeza kuti adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake, umene anthu ambiri padziko lapansi akhala akuphunzitsidwa kuupempherera.—Mateyu 6:9, 10.

Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Aroma 15:33, Buku Loyera) Mtendere umene Mulungu amapereka si wozikidwa pa mfundo zoletsa kapena mapangano, ndiponso si wozikidwa pa kuopa dziko la adani lokhala ndi zida zamphamvu. Mosiyana ndi zimenezi, mtendere wopatsidwa ndi Mulungu umasintha maganizo a anthu ndi mmene amaonera anthu anzawo.

Yehova Mulungu adzaphunzitsa ofatsa njira zake za mtendere. (Salmo 25:9) Mawu ake Baibulo amalonjeza kuti kukubwera nthaŵi imene onse okhala ndi moyo “adzaphunzitsidwa ndi Yehova ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Zimenezi zayamba kale kuchitika kumlingo winawake. Padziko lonse, Mboni za Yehova n’zodziŵika kuti zimalimbikitsa mtendere ngakhale pakati pa anthu amene ali osiyana kwambiri. Anthu amene amaphunzitsidwa mfundo zapamwamba za m’Baibulo amayesetsa kukhala mogwirizana ngakhale patakhala nkhani zimene zingawagawanitse. Kuphunzira Baibulo kumasinthiratu maganizo awo kuchoka pa chidani kufika pa chikondi.—Yohane 13:34, 35; 1 Akorinto 13:4-8.

Kuphatikiza pa kuphunzira, njira inanso imene kwa nthaŵi yaitali yaoneka monga yofunika kwambiri pothetsa zida ndiyo kugwirizana kwa padziko lonse. Mwachitsanzo, bungwe lotchedwa International Committee of the Red Cross limati mayiko onse agwirizane polimbikitsa mfundo zopeŵera ndiponso zothetsera vuto la mabomba okwirira.

Yehova akulonjeza kuti adzabweretsa zinthu zoposa pamenepa. Mneneri Danieli analosera kuti: “Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [alipowa], nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zimene munthu sangathe. Mwachitsanzo Salmo 46:9 amanena mwaulosi kuti: “[Yehova] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.” Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mikhalidwe yotheketsa munthu kudzakhaladi mumtendere ndi Mlengi wake komanso ndi munthu mnzake.—Yesaya 2:4; Zefaniya 3:9; Chivumbulutso 21:3, 4; 22:2.

Augusto, amene tamutchula m’nkhani ya m’mbuyo ija, amatonthozedwa ndi uthenga wa m’Baibulo umenewu. Makolo ake, amene ali a Mboni za Yehova, akumuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro m’malonjezo osangalatsa a Baibulo. (Marko 3:1-5) N’zoona kuti pakali pano ayenera kupirirabe zoŵaŵa zobwera chifukwa cha bomba limene linamupundula. Komabe, Augusto akuyembekezera nthaŵi imene lonjezo la Mulungu la paradaiso lidzakwaniritsidwe. Mneneri Yesaya anati: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa . . . wopunduka adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:5, 6.

M’paradaiso amene akubwerayu, mabomba okwirira sadzakhalanso chinthu choopsa pa moyo kapena ziwalo za munthu. M’malo mwake anthu kulikonse padziko lapansi adzakhala mopanda mantha. Mneneri Mika analongosola zimenezi motere: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Mika 4:4.

Kodi mukufuna kupitiriza kuphunzira zinthu zina zokhudza malonjezo a Mulungu monga analembedwera m’Mawu ake, Baibulo? Pezani a Mboni za Yehova a kwanuko, kapena lemberani kalata ku adiresi yoyenera pa maadiresi olembedwa patsamba 5 la magazini ino.

[Chithunzi patsamba 8, 9]

Mu Ufumu wa Mulungu, mabomba okwirira sadzaopsanso anthu