Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dziko Lidzagwirizana?

Kodi Dziko Lidzagwirizana?

Kodi Dziko Lidzagwirizana?

M’ZAKA zaposachedwapa anthu miyandamiyanda a ku Eastern Europe ndiponso madera ena akumana ndi mavuto ochititsidwa ndi nkhondo zogaŵanitsa. Komabe, ngakhale kuti mikangano yoopsa ngati imeneyi inkachitika, anthu ena zikwizikwi m’mayiko a nkhondo ameneŵa ankatha kukulitsa ndiponso kukhalabe ndi mgwirizano weniweni pakati pawo. Taonani zitsanzo zochepazi.

Mu 1991 chinamtindi cha anthu pafupifupi 15,000 ochokera m’mayiko osiyanasiyana, anasonkhana mu mzinda wa Zagreb, ku Croatia. Wapolisi amene anali nawo kumeneko anachita chidwi kwambiri mpaka ananena kuti: “Zingakhale bwino kusonyeza m’zofalitsira nkhani zimene zikuchitika m’sitediyamu ino, momwe muno, muli anthu a ku Serbia, Croatia, Slovenia, Montenegro, ndi a mayiko ena ndipo akhala mogundizana mumtendere.” Kodi chimachititsa mgwirizano wosoŵa umenewu n’chiyani?

Mu 1993 msonkhano wa mayiko waukulu kuposa uwu, umene unali ndi mutu wakuti “Kuphunzitsa Kwaumulungu,” unachitika mumzinda wa Kiev, womwe ndi likulu la dziko la Ukraine. Chiŵerengero chachikulu kwambiri cha opezeka pamsonkhanowo chinali pafupifupi 65,000. Nyuzipepala yotchedwa Evening Kiev, patsamba lake loyamba inalemba kuti: “Mboni za Yehova . . . zili zogwirizana osati kokha chifukwa cha mabaji abluu olembedwa kuti ‘Kuphunzitsa Kwaumulungu’ komanso chifukwa cha chikhulupiriro choona.”

Chiphunzitso Chaumulungu Chili Mphamvu Yogwirizanitsa

Kodi m’madabwa kuti n’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakhala zogwirizana pamene kusagwirizana kuli kofala kwambiri? Pulofesa wina wa ku Poland dzina lake Wojciech Modzelewski akupeza chifukwa chake ponena motere zimene anaona zokhudza Mboni: “Chinsinsi chachikulu chamtendere wawo ndicho cholinga chawo chofuna kuti m’nthawi ino atsatire mfundo zachikhalidwe, zovumbulidwa m’Baibulo.” N’zoonadi, Mboni n’zogwirizana padziko lonse chifukwa cha chiphunzitso chaumulungu cha Mlengi, Yehova Mulungu. Kodi chiphunzitso chimenechi n’chiyani?

Yesu Kristu anatchula mfundo yofunika yogwirizanitsa anthu pamene ananena za ophunzira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” Inde, kwina kulikonse Mboni za Yehova siziloŵerera mbali iliyonse ndipo zimenezi zimawayanjanitsa. Zimenezi n’zogwirizana ndi mawu a Yesu pamene anapemphera kuti: “Ndipempherera . . . kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife.”—Yohane 17:16-21.

Kusachirikiza mbali iliyonse kumeneku ndiko kukuchititsa mgwirizanowu chifukwa chakuti kumasonkhezera Mboni m’madera onse adziko lapansi kukhala mogwirizana ndi mawu a mneneri Yesaya onena za anthu onse amene Mulungu ‘adzawaphunzitsa za njira zake.’ Yesaya ananena kuti anthu otereŵa “adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape.” Mneneriyo anapitiriza kuti: “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:2-4.

Mgwirizano ndi mtendere zimene zinali pamisonkhano ya Mboni za Yehova ku Eastern Europe m’zaka khumi zapitazi zikusonyeza kuti ulosi wa Yesaya wayamba kale kukwaniritsidwa pamlingo wochepa. Ku Ulaya ndiponso kwina konse, Mboni mophiphiritsira zasula malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape. Zotsatira zake n’zakuti, izo zimakhala mwamtendere ndi mogwirizana m’dziko losagwirizanali. N’zosadabwitsa kuti nkhani yamkonzi wa nyuzipepala ina inati: “Ngati dziko lonse litatsatira chiphunzitso cha [Baibulo] cha Mboni za [Yehova] kukhetsa mwazi ndi udani zingathe, ndipo chikondi chingalamulire monga mfumu”! Kodi umu ndimo zinthu zidzachitikire?

Mmene Mgwirizano Wapadziko Lonse Udzabwerere

Kuti pakhale mgwirizano padziko lonse lapansi, pafunika zambiri koposa kungokhala chabe ndi kagulu kochepa ka anthu amakhalidwe abwino. Pafunikanso boma limene lili ndi mphamvu zoletsa chisonkhezero cha odana ndi mgwirizano ndi mtendere. Ndiponsotu Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera boma limeneli kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Inde, Yesu anasonyeza kuti boma la Mulungu lokha, “Ufumu Wakumwamba,” ndilo lingathetse mavuto a dziko lapansi, kuphatikizapo vuto la kusagwirizana.—Mateyu 4:17.

Yesu Kristu ndiye Mfumu ya Ufumu wakumwamba umenewu. Muulamuliro wake anthu padziko lapansi adzakhala paufulu ndi mtendere womwe sunachitikepo. Mgwirizano umenewu sudzabwera chifukwa cha kukonzanso chuma kwa anthu ayi. Boma lapadziko lonse lokha lolamulidwa ndi “Kalonga Wamtendere” ndilo lingachite zimenezi.—Yesaya 9:6, 7.

Kalonga Wamtendere sadzalekerera kusoŵa chilungamo kwamasiku ano, kumene nthaŵi zambiri kumachitika chifukwa cha umphaŵi ndiponso kugwiritsa ntchito molakwa ulamuliro. Baibulo limalonjeza kuti: “Mafumu onse adzam’gwadira iye: Amitundu onse adzam’tumikira. Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; Ndi wozunzika amene alibe m’thandizi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa . . . M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri; Zipatso zake zidzati waa.”—Salmo 72:11, 12, 14, 16.

Ulova nawonso udzakhala chinthu chakale muulamuliro wa Kristu. Mneneri Yesaya ananena kuti: “Sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.” (Yesaya 65:22) Taganizani, aliyense padziko lapansi adzagwira ntchito yopindulitsa, ndiponso yokhutiritsa!

Mgwirizano Weniweni Udzabwera Liti?

Koma kodi ulamuliro wa Kristu padziko lapansi udzayamba liti? Poyankha funso limeneli Yesu Kristu anatchula za nthaŵi yodziŵika ndi nkhondo, mbiri zankhondo, matenda, zivomezi, ndi zochitika zina. Komabe, anatchulanso chinthu china chosangalatsa ichi, kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:11) Yesu anati, chimake cha zochitika zimenezi chidzakhala ‘chisautso chachikulu’ chomwe mapeto ake adzakhala kusintha kotheratu kwa ulamuliro wadziko lapansi. (Mateyu 24:21) Ŵerengani zimene iye analankhula pa Mateyu mutu 24 ndiponso pa Luka mutu 21. Yerekezani mikhalidwe imene iye ananeneratu ndi zomwe mukuona padziko lapansi. Mungaone bwino lomwe kuti tikukhala m’nthaŵi yongotsatizana ndi nthaŵi imene Mulungu adzasokoneze ulamuliro woikidwa ndi anthu. Ufumu wake, pamodzi ndi Yesu Kristu monga Mfumu ndiwo udzalande ulamuliro. Dziko logwirizana liri kutsogolo!

Funso n’lakuti, Kodi tiyenera kuchitanji kuti tione lonjezo limeneli likukwaniritsidwa? Popeza kuti Baibulo ndilo limafotokoza zambiri ponena za chiyembekezo cham’tsogolo cha mtundu wa anthu, n’kwanzeru kuchita khama kuti tilidziŵe bwino Baibulo. Choncho, Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kufika panyumba panu kudzachita nanu phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. * Ngati mutavomereza zimenezi, posakhalitsa mudzaona nokha kuti mgwirizano wa padziko lonse uli pafupi kwambiri ndipo kuti inunso mungadzakhalemo!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Ngati mukufuna kudziŵa zambiri zokhudza ndondomeko ya phunziro la Baibulo limeneli, lemberani kwa ofalitsa magazini ino kapena pezani Mboni za Yehova zakwanuko.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Kuzungulira padziko lonse, Mboni za Yehova zimakhala zogwirizana modabwitsa

Kiev, Ukraine

Zagreb, Croatia

[Chithunzi patsamba 18]

Chifuno cha Mulungu n’chakuti anthu akhale banja limodzi logwirizana lapadziko lonse