Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mbalame Ingam’phunzitsenji Mkaidi?

Kodi Mbalame Ingam’phunzitsenji Mkaidi?

Kodi Mbalame Ingam’phunzitsenji Mkaidi?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

MALINGA ndi nyuzipepala ya Sunday Tribune ya ku Durban, m’dziko la South Africa, mbalame zikuchita nawo ntchito yofeŵetsa mitima ya akaidi a ku Ndende ya Pollsmoor. Pakali pano akaidi okwanira 14 akugwira nawo ntchito yosamalira mbalame za m’gulu la zinkhwe m’zipinda zawo za ku ndende.

Kodi ntchito imeneyi imagwiridwa motani? M’chipinda cha mkaidi aliyense amene akuchita nawo ntchitoyi muli kanyumba kongogwirizira kosungiramo anapiye. Kamwanapiye kamasamalidwa ndi mkaidiyo, amene amadyetsa kacholengedwa kakang’ono kofuna chithandizoko pambuyo pa ola lililonse kapena maola aŵiri, masana ndi usiku womwe, kwa masabata pafupifupi asanu. Kenako mbalameyo imaikidwa m’chikwere, chimene chimasungidwanso m’chipinda momwemo. Mbalameyo ikakula amaigulitsa. Akaidi ena amakhala paubwenzi waukulu kwambiri ndi mbalame zawo kwakuti amalira panthaŵi imene kusiyana kosaletsekako kukuchitika.

Ngakhale opanduka ena omwe anali ouma mtima kwambiri asintha n’kukhala okoma mtima ndiponso ofatsa pambuyo poyankhula kwa mbalamezo komanso kuzisamalira tsiku lililonse. Mkaidi wina anati: “Ndimaŵeta mbalame, koma nazonso zandilera.” Wina ananena kuti mbalamezo zam’phunzitsa kuleza mtima ndiponso kudziletsa. Wakuba wina amene anamangidwa ananena kuti kusamalira mbalame kwam’zindikiritsa kuti kukhala kholo “ndi udindo waukulu”—ntchito imene ankainyalanyaza kwa ana ake panthaŵi imene anali asanamangidwe.

Kusamalira mbalame zimenezi kuli ndi phindu linanso kwa akaidiwo. “Pogwiritsa ntchito maluso amene akuphunzira kuno,” anatero Wikus Gresse, amene anayambitsa ntchito imeneyi, “iwo angadzapeze ntchito kunja m’makampani oŵeta mbalame kapena kwa madokotala azinyama.”