Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungasangalalire ndi Moyo wa Banja

Mmene Mungasangalalire ndi Moyo wa Banja

Mmene Mungasangalalire ndi Moyo wa Banja

“NDAKHALA ndikuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa zaka zokwanira 40,” analemba motero Graciela wa ku Argentina ku South America. “Lerolino, pambuyo pa zaka zambiri, ndinganene mochokera pansi pa mtima kuti magazini ameneŵa akwaniritsa zosoŵa zanga. Anandithandiza paubwana, m’zaka zanga zaunyamata, kuchita chitomero ndi ukwati, ndiponso kulera ana anga asanu ndi mmodzi.

“Magaziniŵa akutithandiza ineyo ndi mwamuna wanga kulera ana athu anayi amene akukhalabe panyumba pathu. Ndimagwiritsa ntchito bwino kwambiri magaziniŵa pamene ndikuyankhula ndi ana anga ndiponso aphunzitsi awo ku sukulu. Ndinaŵerengapo mwachindunji kuchokera mu Galamukani! pamene ndimayankhula ndi madokotala nkhani za matenda. Ndi chithandizo cha nkhani za “Kusakhoza Kuphunzira” (March 8, 1997), tinazindikira kuti mmodzi wa ana athu akazi anali ndi vuto la kuphunzira.”

Zofalitsa za Watch Tower Society zingathandize mabanja kupirira mavuto amene amakumana nawo ndi kukhalira pamodzi ndi moyo wachimwemwe. Mwachitsanzo, buku la masamba 192 la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lingapindulitse amuna, akazi, makolo, ana, agogo—munthu aliyense m’banja. Ena mwa machaputala amene ndi opindulitsa kwambiri ndi aŵa: “Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake,” “Thandizani Wachinyamata Wanu Kukula Bwino,” “Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga,” ndi “Mukhoza Kulaka Mavuto Owononga Banja.”

Kuti mupeze buku lanulanu, chonde lembani m’kabokosi kotsatiraka, ndi kutumiza ku adiresi imene yasonyezedwapo kapena ku adiresi yoyenerera imene yasonyezedwa patsamba 5 la magazini ano. Mudzalandira mfundo zoyenerera zimene zingakuthandizeni kuthetsa mavuto a m’banja komanso amene angapangitse moyo wa banja kukhala wosangalatsa monga momwe Mlengi anafunira.

□ Nditumizireni buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Chithunzi patsamba 32]

Graciela ndi banja lake