Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzitetezeni Nokha Ndiponso Okondedwa Anu

Dzitetezeni Nokha Ndiponso Okondedwa Anu

Dzitetezeni Nokha Ndiponso Okondedwa Anu

INTANETI ingakhale chida chothandiza. Komabe, monga zida zambiri, ingagwiritsidwe ntchito molakwa. Ndipo zithunzi zamaliseche zimene zimapezekapo ndizo chitsanzo cha kuigwiritsa ntchito molakwa.

Podziŵa kuti zithunzithunzi zimakopa zedi, makolo ayenera kuyesetsa kuchita zimene angathe kuti ana asamathe kutsegula malo okayikitsa pa intaneti. Buku lotchedwa Teen Safety on the Information Highway limapereka chidziŵitso chothandiza pankhaniyi. Ilo limati: “Tsopano pali mabungwe amene amadziŵitsa anthu za ubwino kapena kuipa kwa Malo a Chidziŵitso osiyanasiyana malingana ndi mapulogalamu amene amasonyezapo, ndiponso pali mapulogalamu oyendetsera kompyuta amene amatheketsa munthu kufufuza malo osiyanasiyana ndipo makolo angawagwiritse ntchito kuti atseke malo amene akuona kuti n’ngwoipa. Mapulogalamu ameneŵa amagwira ntchito m’njira zosiyanasiyana. Ena amatseka malo odziŵika kuti amakhala ndi zinthu zokayikitsa. Ena amaletsa anthu amene akuwagwiritsira ntchito kulemba zinthu zina zofunika kudziŵa monga dzina ndi adiresi yawo. Mapulogalamu ena salola ana anu kuloŵa m’zipinda zochezera za pa intaneti kapena salola wamba kuti atumize kapena kuŵerenga makalata pa intaneti. Nthaŵi zambiri makolo angatchere mapulogalamu ameneŵa kuti azingotseka malo okha amene iwo akuona kuti n’ngwokayikitsa.”—Onaninso kabokosi kakuti “Kuteteza Ana Kuti Asaone Zamaliseche.”

Komabe, tiyenera kudziŵa kuti makolo sangatchinge njira iliyonse imene ana awo angaonere malo osayenera. Sangalonde ana awo nthaŵi iliyonse. Ndipo mwana kapena wachinyamata amene sangaone zamaliseche kunyumba kwawo angakazipeze zili mbwee pakompyuta ya kusukulu kapena ya kunyumba ya mnzake wakusukulu. Choncho, kuwonjezera pa zimene angachite polepheretsa ana awo kuona zamaliseche, makolo ayenera kuthandiza anawo kukhala ndi chikumbumtima champhamvu chimene chingawaletse kuyang’ana zamaliseche ngakhale asanauzidwe.

N’kulakwitsa kunena kuti achikulire ndiwo angaone zamaliseche pakuti n’ngokhwima maganizo koposa ana. Monga taonera m’nkhani yapita, kuona zamaliseche sikwabwino kwa munthu aliyense!

Komabe, tiyeni tiyerekeze kuti mwakhala mukuona zamaliseche kwanthaŵi ndithu. Mwazindikira kuti zimene mukuchita sizisangalatsa Mulungu, ndipo mukufuna kusiya chizoloŵezi chimenechi. Kodi n’zotheka? Inde n’zotheka. Anthu amasiya zizoloŵezi zoipa tsiku lililonse. Ngati mukufunadi kusiya kuona zamaliseche mungatero.

Ngati Mukufuna Kusiya

Njira yoyamba ndiyo kusiya kuyang’ana pa zithunzi zamaliseche, nthaŵi yomwe ino! Mukadikira mudzavutika kwambiri kuti musiye. Komabe, n’kosavuta kungonena kuti ndisiya koma kusiyadi n’kovuta. Baibulo limanena moonadi kuti tchimo lingakhale lokondweretsa kwakanthaŵi. (Ahebri 11:25) Koma uchimo ungathenso kuphula imfa. (Aroma 6:23) Poyamba, mungaone kuti mukungopeza tizifukwa tosiyanasiyana takuti muone zamaliseche komaliza. Osadzimvera! Ndipo musagonjere kuchiyesocho n’kumayang’anabe!

Monga tinanenera poyamba m’nkhani zino, kuyang’ana zamaliseche kungavulaze moyo wanu moipa zedi. Onani moona mtima mmene chizoloŵezicho chikukhudzira ubwenzi wapakati pa banja lanu ndi anzanu. Kodi ndinu wokwatira ndipo muli ndi ana? N’zotheka kuti mkazi ndi ana anu aona kuti khalidwe lanu likusintha. Kuyambira pamene munayamba kuona zamaliseche, mwina munayamba kukhala amtima wapachala, andwii, ochita zinthu mwachinsinsi, kapena odzipatula, mwina m’matero musakudziŵa n’komwe. Nthaŵi zina mungakalipire anthu a m’banja mwanu popanda chifukwa. Ngati mumaona zithunzi zamaliseche, khalidwe lanu likukuululani. Anzanu ndiponso a m’banja lanu aona kuti chinachake sichili bwino. Kungoti pakali pano sanadziŵe kuti n’chiyani makamaka.

Ngati mukuona kuti muli ndi vuto lokonda kuona zamaliseche, musayese kulimbana nalo panokha. Pezani chithandizo. Pezani mnzanu amene wakumana ndi zinthu zambiri m’moyo ndipo muuzeni zakukhosi. N’zoona kuti mufunika kulimba mtima kuti muvomereze kuti muli ndi vuto loona zamaliseche, koma mnzanu wokhwima maganizo angakutayireni kamtengo chifukwa chochita zotheka kuti mulithetse.

Ndithudi, chifukwa chachikulu kwambiri cholimbanira ndi vuto la kuona zamaliseche ndicho kufunitsitsa zedi kusangalatsa Mulungu. Tikamalimbikira kuyenda m’njira yabwino timasangalatsa mtima wa Mulungu. (Miyambo 27:11) Tikamayenda m’njira ya zoipa, timam’chititsa Mulungu kuti ‘avutike m’mtima mwake.’ (Genesis 6:6) Ngati muli Mkristu, mosakayikira mumakhala ndi nkhaŵa yakuti musakhumudwitse Mulungu. Muyeneranso kukhala ndi nkhaŵa ya mmene mumagwiritsira ntchito maganizo ndi mtima wanu, zimene zili zopatulidwira kwa Mulungu ndipo ziyenera kukhala zoyera kuti zim’tumikire. (Ezekieli 44:23) Baibulo limalimbikitsa Akristu “kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Inde, mantha oyenera a kuopa kukhumudwitsa Mulungu, amene amaona zinthu zonse, angathe kukupatsani mphamvu zakuti musiye kuona zamaliseche.

Komabe, tayerekezerani, kuti muli m’kati molimbana ndi vutoli, mwangozindikira kuti mwatsoka mwatsegula Malo Achidziŵitso amene amaonetsapo zamaliseche. Tsekani malowo nthaŵi yomweyo! Ngati kuli kofunika tsekani intaneti! Ngati mutaona kuti mtima wanu uli dyokodyoko kufuna kubwereranso, fikani kwa Mulungu popemphera moona mtima ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kulimbana ndi chiyesocho. Baibulo limati “m’zonse . . . zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Ngati mukuona kuti mukuvutitsidwa ndi maganizo osayenera, pempherani mpaka mutapeza mpumulo. Mukatero ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mtima wanu ndi maganizo anu.’ (Afilipi 4:6, 7) N’zoona kuti m’malo mwa maganizo osayenera muyenera kuloŵetsamo maganizo ‘oona, olemekezeka, olungama, oyera, okongola, omveka okoma.’—Afilipi 4:8.

Mungaone kuti n’kothandiza kuloŵeza ndi kusinkhasinkha pa malemba a m’Baibulo monga otsatiraŵa.

“Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.”—Salmo 97:10.

“Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:27.

“Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi.”—Akolose 3:5.

“Yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa.”—1 Atesalonika 4:4, 5.

“Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”—Mateyu 5:28.

“Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha.”—Aefeso 5:28.

Pali zifukwa zambiri zopeŵera kuona zamaliseche. Zingawononge moyo wanu moipa zedi, kukhotetsa malingaliro anu, kuwononga maubwenzi anu ndi anthu ena ndipo, koposa zonse, kuwononga ubwenzi wanu ndi Mulungu. Ngati mulibe chizoloŵezi choyang’ana zamaliseche, musayambe. Ngati muli nacho, siyani nthaŵi yomwe ino! Kaya n’zosonyezedwa m’buku kaya m’magazini kapena pa intaneti, zamaliseche sizoyenera Akristu. Yesetsani kuzipeŵa ngakhale kutavuta maka!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Kuteteza Ana Kuti Asaone Zithunzi Zamaliseche

Malingaliro otsatiraŵa angakuthandizeni kuteteza ana anu kuti asawonongeke chifukwa choona zamaliseche pa intaneti.

● Musalole kuti mwana wanu azitsegula intaneti ali kuchipinda chake chogona. Ikani makompyuta onse olumikizidwa ku intaneti m’chipinda chimene aliyense wa m’banjamo amaloŵamo mosavuta.

● Dziŵani mapulogalamu a kompyuta amene mwana wanu amagwiritsa ntchito.

● Onani ngati mwana wanu wapanga Malo akeake Achidziŵitso inu musakudziŵa. Kuti mutero, yesani kufunafuna dzina lake pogwiritsa ntchito mapulogalamu ofunira zinthu pa intaneti amene amafufuza intaneti yonse. Kuti musatsegule malo olakwa lembani dzina lake lonse ndi kulitseka ndi zizindikiro zosonyeza mawu ogwidwa.

● Musalole kuti mwana wanu akonze zodzaonana pamaso m’pamaso ndi munthu wina wom’dziŵira pa kompyuta amene inuyo simukum’dziŵa.​​—⁠Onani bokosi lakuti “Si Kucheza Chabe.”

● Osanenapo kanthu pa mauthenga kapena macheza a nkhani zokayikitsa, zolaula, zotukwanizana, kapena zoopseza.

● Chenjezani ana anu kuti asamatsegule zinthu zosayenera za pa Intaneti. Aphunzitseni kudziletsa okha ngati inuyo palibe. Musaiŵale kuti makompyuta a kusukulu kapena kunyumba kwa mnzawo sangakhale otetezedwa mwakuti ana angaonepo zamaliseche pa Intaneti.

[Mawu a Chithunzi]

Ena mwa malingaliroŵa atengedwa m’bulosha yotchedwa Child Safety on the Information Highway ndiponso m’nkhani ya pa July 5, 1999 ya m’nyuzipepala ya Los Angeles Times.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

Sikucheza Chabe

Muyenera kusamala kwambiri mukamagwiritsa ntchito chipinda chochezera chapakompyuta. Chipinda chochezera ndiyo njira imene imatheketsa ogwiritsa ntchito intaneti kuyankhulitsana. N’zoona kuti anthu ambiri amayankhulitsana ndi anzawo apamtima pogwiritsa ntchito njira yotumizira makalata pakompyuta yotchedwa E-mail. Anthu ena okhala kutali ndi achibale awo amatha kuyankhulitsana nawo kaŵirikaŵiri m’njira imeneyi. Koma kutumiza kalata pakompyuta yopita kwa munthu womudziŵa n’kosiyana ndi kucheza ndi munthu wosam’dziŵa. Kodi mungafune kuimba telefoni mwachisawawa ndipo kenako n’kupalana ubwenzi ndi munthu aliyense amene angaiyankhe? N’zachidziŵikire kuti simungatero! Nanga mungapalane bwanji ubwenzi pakompyuta ndi munthu amene simukum’dziŵa ngakhale pang’ono?

Vuto lina loyankhulana ndi munthu wosam’dziŵa n’lakuti simungadziŵe khalidwe lake lenileni. Mwachitsanzo angakhale munthu wogona ana amene akufuna kupeza mwana kapena wachinyamata wongokhulupirira zililonse.

Parry Aftab, amene ndi loya wa milandu yokhudza intaneti, analongosola mmene zimenezi zingachitikire mosavuta. Iye anati: “Ana amaloŵa m’zipinda zochezera zapaintaneti monga mwa nthaŵi zonse. Anthu ogona ana amaona zimenezi, n’kumaŵerenga nkhani zimene anawo akutumizirana ndipo amaona ana amene ali osungulumwa. Mwana wina angatumize uthenga monga wakuti ‘Makolo anga akusudzulana . . . Ndimadana nawo amayi anga, sandigulira maseŵera apakompyuta amene ndimafuna.’ . . . Wogona ana uja amaloŵererapo n’kuyankha kuti ‘Makolo anga akusudzulana . . . Ndimadana nawo amayi anga . . . ndakhala ndikulephera kupeza maseŵera apakompyuta amene ndikufuna, mpaka pamene a Timmy anandigulira. . . . Ungopita kum’sika basi n’kukakumana ndi a Timmy.’” “A Timmy” akunenawo kwenikweni ndi munthu wogona ana uja amene ali pakalikiliki wofuna mwana woti amugone.

Motero, makolo ayenera kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndi ana awo. Aloleni anawo kuti azicheza nanu mosavuta kuopa kuti angayambe kudalira anthu olakwika akathedwa nzeru.

Achikulire amene ali osungulumwa kapena amene mabanja awo sakuyenda bwino sayenera kutsegula zipinda zochezera zapakompyuta akathedwa nzeru. Kudalira anthu osawadziŵa n’koopsa. Anthu ena achikulire asiya akazi kapena amuna awo n’kukakwatirana ndi munthu amene “anakumana” naye pa intaneti. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 38 Kuti mumve zambiri pankhani ya zipinda zochezera zapakompyuta, onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndingapeŵe Bwanji Zoopsa pa Intaneti?” m’magazini ya Galamukani! ya pa February 8, 2000.

[Chithunzi patsamba 8]

Pemphero lingathandize munthu kukaniza chiyeso