Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amasandulika?

Kodi Mulungu Amasandulika?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amasandulika?

KATSWIRI wasayansi yamoyo wamunthu wotchedwa George Dorsey anafotokoza kuti Mulungu wa “m’Chipangano Chakale” anali “Mulungu wankhanza.” Iye anawonjezera kuti: “Yahweh ndi . . . woipa zedi. Iye ndi Mulungu wa anthu achifwamba, anthu ozunza, anthu ankhondo, ndipo n’ngwolanda.” Pali anthu ena amenenso amamuganizira choncho Mulungu wa “m’Chipangano Chakale” Yahweh kapena kuti Yehova. Motero, anthu ena lero amadzifunsa ngati Yehova analidi Mulungu wankhanza amene m’kupita kwanthaŵi anasandulika n’kukhala Mulungu wachikondi ndi wachifundo wa “m’Chipangano Chatsopano.”

Kuganizira Mulungu wa m’Baibulo motero si kwachilendo ayi. Anakuyambitsa ndi Marcion, amene ankakhulupirira zinthu zina za m’chiphunzitso cha m’zaka za zana lachiŵiri C.E. chotchedwa nositisizimu chimene chinkalola zoipa zonse. Marcion anakana Mulungu wa “m’Chipangano Chakale.” Iye anaona kuti Mulungu ameneyo n’ngwachiŵaŵa, ndiponso n’ngwosunga mangawa, ndiponso wopondereza amene amapereka malipiro kwa anthu amene amamulambira. Mosiyana ndi zimenezi, Marcion anafotokoza kuti Mulungu wa “m’Chipangano Chatsopano” amene mikhalidwe yake inavumbulidwa kudzera mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu wangwiro, Mulungu wachikondi ndi chifundo chenicheni, wachisomo ndiponso wokhululukira.

Yehova Amachita Zinthu Malingana ndi Kusintha kwa Mikhalidwe

Dzina la Mulungu lenilenilo lakuti, Yehova, limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadzichititsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo ake onse. Mose atam’funsa Mulungu dzina lake, Yehova analongosola tanthauzo la dzinalo motere: “Ndidzakhala chimene ndidzakhala.” (Eksodo 3:14, NW) Baibulo la Rotherham limanena motere: “Ndidzakhala chilichonse chimene ndifuna.”

Choncho, Yehova amasankha kukhala kapena kutsimikiza kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse zolinga ndi malonjezo ake olungama. Umboni wa zimenezi ndi mayina aulemu ndiponso om’fotokoza ambirimbiri amene ali nawo monga: Yehova wamakamu, Woweruza, Mfumu, Wansanje, Ambuye Mfumu, Mlengi, Atate, Mlangizi Wamkulu, Mbusa, Wakumva pemphero, Mombolo, Mulungu wachimwemwe, ndi mayina ena ambiri. Iye wasankha kukhala zinthu zonsezi, ndiponso pali zina zambiri, kuti akwaniritse zolinga zake zachikondi.—Eksodo 34:14; Oweruza 11:27; Salmo 23:1; 65:2; 73:28; 89:26; Yesaya 8:13; 30:20; 40:28; 41:14; 1 Timoteo 1:11.

Ndiyeno kodi zimenezi zikutanthauza kuti umunthu kapena miyezo ya Mulungu zimasintha? Ayi ndithu. Ponena za Mulungu, Yakobo 1:7 amati: ‘Iye alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” Kodi Mulungu angachite bwanji zinthu malingana ndi kusintha kwa mikhalidwe yosiyanasiyana pamene iyeyo ali wosasandulika?

Chitsanzo cha makolo osamala amene amagwira ntchito zosiyanasiyana chifukwa cha ana awo chikusonyeza mmene zimenezi zilili zotheka. Patsiku limodzi, kholo lingakhale wophika, wosamala panyumba, wokonza zipangizo zamagetsi, namwino, phungu, mphunzitsi, mlangizi, ndi zinthu zina zambiri. Kholo silisandulika pochita ntchito zimenezi; ilo limangochita zinthu malinga ndi zimene zikufunika panthaŵiyo. Ndi mmenenso zilili ndi Yehova, komatu pamlingo waukulu koposa. Palibe malire a zimene angafune kukhala kuti akwaniritse zolinga zake kuti zolengedwa zake zipindule.—Aroma 11:33.

Mwachitsanzo, Yehova amadziŵika monga Mulungu wachikondi ndi wachifundo m’Malemba Achihebri ndi m’Malemba Achigiriki Achikristu. Mneneri Mika wa m’zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E. anafunsa za Yehova kuti: “Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a choloŵa chake? Sasunga mkwiyo wake ku nthaŵi yonse popeza akondwera nacho chifundo.” (Mika 7:18) Mofananamo, mtumwi Yohane analemba mawu otchuka aŵa: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.

Komanso, m’mbali zonse za Baibulo, Yehova watchulidwa kukhala Woweruza wachilungamo wa anthu amene amaphwanya malamulo ake mosalapa, ndiponso kuvulaza anthu ena. Wamasalmo ananena kuti, “oipa onse [Yehova] adzawawononga.” (Salmo 145:20) Mofananamo, Yohane 3:36 amanena kuti: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”

Mikhalidwe Yosasinthika

Umunthu wa Yehova komanso mikhalidwe yake yaikulu monga chikondi, nzeru, chilungamo, ndi mphamvu sizinasinthe. Iye anauza anthu a ku Israyeli kuti: ‘Ine ndine Yehova sindisinthika.’ (Malaki 3:6) Panthaŵiyi n’kuti patapita zaka 3,500 Mulungu atalenga kale anthu. Mogwirizana ndi mawu a Mulungu ameneŵo, kufufuza mozama Baibulo lonse kumavumbula kuti Mulungu samasintha miyezo yake ndiponso mikhalidwe yake. Umunthu wa Yehova Mulungu sunasinthepo m’zaka zonsezi, popeza kuti kusintha koteroko sikunali kofunika.

Kumamatira pachilungamo kwa Mulungu, monga kwadziŵikira m’Baibulo lonse, sikocheperapo ayi, ndiponso chikondi chake sichokulirapo kuposa mmene chinalili pachiyambi cha zochita zake ndi anthu mu Edene. Kumene kumaoneka ngati n’kusiyanasiyana kwa umunthu wake m’mbali zosiyanasiyana za Baibulo kwenikweni kuli mbali ya umunthu wosasintha womwewo. Zimenezi zimachitika chifukwa cha zochitika zosiyanasiyana ndiponso anthu osiyanasiyana amene anafunikira kaonedwe kosiyana ka zinthu kapenanso maunansi osiyana.

Choncho, Malemba amasonyeza momveka bwino kuti umunthu wa Mulungu sunasinthe kwazaka mazana onseŵa ndiponso sudzasintha m’tsogolo. Yehova ali wamkulu koposa zonse pa kusaleka ndi kusasinthika. Nthaŵi zonse iye n’ngwodalirika ndi wokhulupirika. Tingam’dalire nthaŵi zonse.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Mulungu yemweyo amene anawononga Sodomu ndi Gomora . . .

. . . adzabweretsa dziko latsopano lolungama