Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zovulazadi?

Kodi N’zovulazadi?

Kodi N’zovulazadi?

MONGA taonera, Intaneti yachititsa kuti achikulire ndi ana omwe aziona zithunzi zamaliseche mosavuta. Kodi muyenera kukhudzidwa ndi nkhaniyi? Kodi zithunzi zamaliseche n’zovulazadi?

Anthu ambiri amaganiza kuti kuona zamaliseche pang’ono chabe n’kosavulaza. Komabe, zochitika zikutsutsana ndi maganizoŵa. Taganizirani za nkhani ya mkazi ndi mwamuna wina amene ukwati wawo unkaoneka kuti uli bwino. Anali ndi ndalama zokwanira, ndipo ankakonda kuyendayenda. Anzawo ankawaona monga anthu ogwirizana kwambiri, okondana, ndiponso okhulupirirana, ndipo analidi choncho m’njira zambiri.

Komabe mavuto anadza pamene mwamunayo anayamba kuona zithunzi zamaliseche. Mkazi wake pothedwa nzeru analemba kalata kwa munthu wotchuka wopereka malangizo m’nyuzipepala, n’kulongosola nkhaŵa yake motere: “Pamene [mwamuna wanga] anayamba kugwiritsa ntchito kompyuta kwa nthaŵi yaitali pakati pa usiku ndi m’matanda kucha, anandiuza kuti anali kuchita ‘kafukufuku.’ Tsiku lina m’maŵa ndinamuzembera ndipo ndinamupezerera akuona [zamaliseche] . . . Anandiuza kuti anangochita chidwi basi. Nditayang’anitsitsa zimene anali kuonazo, zinandinyansa kwambiri. Anachita manyazi ndipo analonjeza kuti asiya, ndipo ine ndinakhulupirira kuti akunenetsadi. M’mbuyo monsemu anali munthu wolemekezeka, wosaphwanya malonjezo ake.”

Monga mwamunayu, anthu ambiri amayamba kuona zamaliseche pochita chidwi basi. Poopa kuti ena angawapezerere, amatsegula intaneti pakati pa usiku kapena m’matanda kucha. Ngati wina atawapezerera, nthaŵi zambiri amafuna kubisa zimene anali kuchita ponena bodza, monga anachitira mwamunayu. Kodi ndani anganene momveka bwino kuti “chosangalatsa” chimene chimachititsa “munthu wosaphwanya malonjezo ake” kuzemba pakati pa usiku ndiponso kunamiza anthu amene amawakonda n’chosavulaza?

Mchitidwewu ungadzetse mavuto aakulu aumwini ndiponso a banja. Ena avomereza kuti kuona zamaliseche kwawalepheretsa kukhala ndi maubwenzi enieni ndi anzawo. Akamakhutiritsa chikhumbo chawo cha kuona zamaliseche safuna kuti pakhale anthu ena. Anthu akamaona zamaliseche amaganizira zinthu zoti sizichitika m’moyo weniweni, ndipo kuganizira zinthu zoterezi sikupangitsa munthu kukhala ndi maubwenzi olimba kapena kuthana ndi mavuto enieni m’moyo. Kodi chinthu chongosangalatsa chabe chimene chimalekanitsa anthu kwa anzawo amene amawakonda kwambiri chingakhale chosavulazadi?

Nthaŵi zina anthu amene amaona kapena kuŵerenga nkhani zamaliseche zimawavuta kuti akhale malo amodzi mosangalala ndi amene anakwatirana naye. Kuti timvetse chifukwa chake, tiyeni tione cholinga choyambirira cha Mulungu kwa anthu okwatirana. Iye mwachikondi anapatsa amuna ndi akazi awo mphamvu zotha kusonyezana chikondi pokhala malo amodzi m’njira yolemekezeka. Miyambo 5:18, 19 amaonetsa kuti kusonyezana chikondi m’njira imeneyi kunapangidwa kukhala kosangalatsa ponena kuti: ‘Ukondwere ndi mkazi wokula nayo . . . Mawere ake akukwanire nthaŵi zonse. Ukondwe ndi chikondi chake mosaleka.’

Onani kuti chikondi ndicho chinali maziko a kukhalira malo amodzi. Kodi munthu amene amaona zamaliseche amakhala akukulitsa ubwenzi wachikondi chenicheni? Ayi, iye akungokhutiritsa zilakolako zake za kugonana ndipo nthaŵi zambiri amatero ali payekha. Munthu wokwatira amene amaona zamaliseche angayambe kuona mkazi wake monga pothetsera zilakolako zake basi. Zimenezi n’zotalikirana kwambiri ndi ulemu umene Mlengi anafuna kuti amuna azipatsa akazi. (1 Petro 3:7) Kodi khalidwe limene limasokoneza mbali zosonyezana chikondi chapansi pa mtima muukwati lingaonedwe monga losangalatsa?

Ndiponsotu, pofuna kungosangalatsa maso chabe mapeto ake angakhale chizoloŵezi chovuta kusiya. Wolemba wina anati pankhaniyi: “Monga mmene anthu ozoloŵera kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amafunira mankhwala amphamvu zowonjezereka kuti ‘afikepo,’ anthu oona zamaliseche nawo amafunikira kuona zinthu zolaula mowonjezereka kuti ziwafike pamtima monga poyamba.”

Mwachionekere zimenezo n’zimene zinachitikira mwamuna amene tam’tchula poyamba paja m’nkhani ino. Madzulo ena patatha miyezi ingapo atalonjeza kuti sadzaonanso zamaliseche, mkazi wake anabwerera kunyumba n’kumupeza akugwiritsa ntchito kompyuta. Atangoona nkhope yake anadziŵa kuti chinachake sichili bwino. Mkaziyo analemba kuti “Anali kuoneka ngati womangika kwambiri ndiponso wosokonezeka maganizo. Nditayang’ana pakompyuta, ndinatsimikizadi kuti anali kuona zinthu zonyansa kwambiri. Anandiuza kuti ankanena moona mtima polonjeza kuti adzasiya, koma akulephera kusiya.”

Popeza kuti zamaliseche zingathe kuvulaza ndiponso pakuti n’zopezeka ponseponse, mpake kuti nkhaniyi ikukhudzeni. Kodi inuyo pamodzi ndi ana anu mungadziteteze bwanji? M’gawo lotsiriza la nkhani zino tidzaona mayankho afunso limeneli.

[Chithunzi patsamba 6]

Kuona zamaliseche kumawononga khalidwe