Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Banja Lathu Linagwirizanirananso

Mmene Banja Lathu Linagwirizanirananso

Mmene Banja Lathu Linagwirizanirananso

Yosimbidwa ndi Lars ndi Judith Westergaard

YUMBA yawo imaoneka kukhala malo oyenera kukhalamo banja lililonse lachimwemwe ku Denmark. Nyumbayo ili m’mudzi wabata ndipo n’njaikulu bwino komanso kunja kwake kuli munda wa maluŵa okongola. M’kati mwakemo, muli chithunzi chachikulu pakhoma. Pachithunzipo, pali ana athanzi a m’banjalo akumwetulira.

Bambo wa m’nyumbamo, Lars, ndi mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova. Mkazi wake, Judith, ndi mpainiya (mlaliki wanthaŵi zonse). Ngakhale kuti banjali n’lachimwemwe, sikuti zinthu zakhala zili choncho nthaŵi zonse. Lars ndi Judith anaona mavuto komanso anadanapo koopsa kufikira mpaka posudzulana ndi kugaŵa banja lawo. Koma panopo, banjalo linagwirizananso. Chinachititsa n’chiyani? Eni akewo akusimba zimene zinachitika.

Lars ndi Judith sakuda nkhaŵa kusimba zimene zinasokoneza ukwati wawo ndi mmene zinakhalira kuti abwereranenso. Akukhulupirira kuti zimene zinawachitikirazo zingathandizenso ena.

Poyamba Zonse Zinali Bwino

Lars: Pamene tinakwatirana mu April 1973, banja lathu linali lachimwemwe chokhachokha. Kwa ifeyo, zinthu zonse zimaoneka ngati zidzatiyendera bwino. Baibulo sitinkalidziŵa, ndipo ngakhale Mboni za Yehova sitinkazidziŵanso. Koma tinkakhulupirira kuti tingathe kusintha dziko kukhala malo abwino okhalamo malinga ngati anthu onse angayesetse kutero. Choncho tinaloŵa m’zochitika zambiri zandale. Chimwemwe chathu chinakula pamene banja lathu linawonjezeka ndi ana aamuna atatu komanso athanzi ndi ojijirika—Martin, Thomas, ndi Jonas.

Judith: Ndinali ndi malo apamwamba m’nthambi ina ya antchito zaboma. Komanso, ndinali m’ndale ndiponso m’bungwe la antchito. Pang’ono ndi pang’ono, anandipatsa malo autsogoleri.

Lars: Ine ndinkagwira ntchito m’bungwe lina lalikulu la antchito, ndipo ndinafika pa kukhala ndi malo antchito apamwamba. Ntchito zathu zinkapita patsogolo kwambiri, popanda chilichonse choopseza moyo wathu wachimwemwe.

Kulekana

Lars: Ngakhale kuti zinthu zinali choncho, tinali otanganidwa kwambiri ndi ntchito za payekhapayekha kotero kuti tinkakhala ndi nthaŵi yochepa kwambiri yocheza. Tinkatumikira chipani cha ndale chimodzi koma ntchito zosiyana. Ana athu aamuna atatuwo ankaleredwa ndi anthu ena, ndi wantchito kapena m’malo olererako ana nthaŵi yamasana. Popeza kuti tonse aŵirife maganizo athu anali pazinthu zaumwini, moyo wathu wam’banja unasokonezeka. Nthaŵi zambiri tonse aŵirife tikakhala panyumba, tinkakangana kwabasi. Ndiyeno ndinayamba kumwa moŵa monga mankhwala oziziritsira mtima.

Judith: Tinkakondana ndithu komanso ana athu tinkawakonda. Koma chikondi chathu sitinachikulitse kufikira momwe chinayenera kukhalira; chimaoneka kuti chikuzilara. Banja lathu linasokonekera kwambiri, ndipo ana anazunzika chifukwa cha zimenezi.

Lars: Pofuna kubwezeretsa mtendere wa banja lathu n’tathedwa nzeru, ndinaganiza zosiya ntchito. Mu 1985 tinasamuka mu mzindawo kupita ku mudzi umene tikukhala panopa. Zinthu zinayenda bwino kwanthaŵi yochepa chabe, komabe ine ndi mkazi wanga tinapitirizabe kukhazika maganizo pa zinthu zaumwini aliyense payekha. Pomaliza pake, mu February 1989, ukwati wathu wa zaka 16 unatha ndi chisudzulo. Banja lathu linapasuka.

Judith: Zinali zomvetsa chisoni kwambiri kuona banja lathu likugaŵikana ndi kuona mmene ana anazunzikira. Tinali aukali kwambiri moti sitinagwirizane zoti tizithandizana kusamalira anawo, choncho ndinatenga ana onsewo kuti ndiziwasamalira.

Lars: Ineyo ndi Judith tinayesetsa kugwirizanitsa banja lathu pomwe limapasuka, koma zinali zosaphula kanthu. Tinkapempheranso kwa Mulungu kaamba ka thandizo. Koma tinkadziŵa zochepa kwambiri ponena za Mulungu.

Judith: Mapemphero athu anatipatsa malingaliro akuti Mulungu sankamvetsera. Timayamikira kwambiri chifukwa chakuti kuchokera pamenepo taona kuti Mulungu amamvetsera mapemphero.

Lars: Sitinkadziŵa kuti timafunikira kusintha ife eni komanso kuchita khama. Choncho chisudzulo chomvetsa chisoni chinachitika.

Lars Aona Zomwe Sanayembekeze

Lars: Panthaŵi yomwe ndinkakhala ndekha, zinthu zinandisinthira kwambiri. Tsiku lina ndinalandira magazini aŵiri kuchokera kwa Mboni za Yehova. Koma nthaŵiyo isanafike ndinkangoti ndikaona a Mboni basi n’kuwabweza. Koma pamene ndimaŵerenga magaziniwo, ndinaona kuti Mboni zimakhulupiriradi Mulungu ndi Yesu Kristu. Zinali zodabwitsa kwambiri. Sindinkalingalira kuti iwo anali Akristu.

Pafupifupi nthaŵi yofananayo, ndinayamba kukhala ndi mkazi wina yemwe ndinadziŵana naye. Ndinadzazindikira kuti iye anakhalapo wa Mboni za Yehova. Nditayamba kumam’funsa mafunso osiyanasiyana, iye anandisonyeza m’Baibulo kuti Yehova ndi dzina la Mulungu. Choncho dzina lakuti “Mboni za Yehova” limatanthauza “Mboni za Mulungu”!

Mkaziyo anakonza kuti ndikamvere nawo nkhani yapoyera pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova. Zimene ndinakaona kumeneko zinalimbikitsa kwambiri chidwi changa. Ndinakafika pa Nyumba ya Ufumu ya kwathu kuti ndikaphunzire zambiri, ndipo phunziro la Baibulo linakhazikitsidwa. Sizinanditengere nthaŵi yaitali kuzindikira kuti makhalidwe anga anali olakwika, choncho ndinasiyana ndi chibwenzi changa chija ndi kukakhala kwandekha m’tauni ya kumudzi kwathu. Nditazengereza kwa kanthaŵi kochepa chabe, ndinakaonana ndi Mboni za Yehova komweko ndipo ndinapitiriza kuphunzira Baibulo.

Komabe, panali zinthu zina zimene ndinkakayikira. Kodi Mboni za Yehova zinalidi anthu a Mulungu? Nanga bwanji ponena za zinthu zonse zimene ndinaphunzira pamene ndinali mwana? Ndiyeno ndinakaonana ndi mbusa wa Adventist chifukwa chakuti ndinaleredwa monga wa Seventh Day Adventist. Iye anavomera kuti aziphunzira nane Lachitatu lililonse, pamene Mboni za Yehova zinkaphunzira nane Lolemba lililonse. Ndinkafuna mayankho omveka bwino kuchokera ku magulu onse aŵiri pankhani zinayi: kubweranso kwa Kristu, chiukiriro, chiphunzitso cha Utatu, ndi mmene mpingo uyenera kuyendetsedwera. Zinanditengera miyezi yoŵerengeka chabe kuthetsa kukayikira konseko. Zikhulupiriro za Mboni za Yehova ndizo zokha zinali zozikidwadi m’Baibulo pankhani iliyonse mwa nkhani zinayizi, ndiponso pankhani ina iliyonse. Chifukwa cha zimenezo, ndinayamba kuchita nawo mosangalala ntchito zonse za mpingo ndipo mwamsanga ndinadzipatulira kwa Yehova. Mu May 1990, ndinabatizidwa.

Bwanji Ponena za Judith?

Judith: Pamene ukwati wathu umatha, n’kuti nditayambiranso kupita ku tchalitchi. Ndinaipidwa kwambiri pamene ndinamva kuti Lars akufuna kukhala wa Mboni za Yehova. Jonas, mwana wathu wamng’ono yemwe anali ndi zaka khumi zakubadwa, nthaŵi zina ankapita kukachezera atate wake, koma ndinaletsa Lars kupita ndi Jonas ku msonkhano uliwonse wa Mboni. Lars anakadandaula kuboma, koma iwo anagwirizana ndi malingaliro anga.

Ndinali pachibwenzi ndi mwamuna wina. Kuwonjezera pamenepo, ndinali wokangalika kwambiri m’nkhani zandale ndiponso pantchito zonse za m’mudzi. Choncho panthaŵi imeneyo zikanaoneka kukhala zosatheka ngati wina akananenapo za kubwererananso kwathu.

Pofunafuna njira yolimbanirana ndi Mboni za Yehova, ndinapita kwa mbusa wa parishi ya kwathu komweko. Iye anandiuza mwachindunji kuti sakudziŵa kalikonse ponena za Mboni za Yehova ndiponso kuti analibe buku lililonse lokhudzana ndi iwo. Anangonena kuti ndingachite bwino ngati nditawapeŵa. Kunena zoona, zimenezi sizinasinthe malingaliro anga oipidwa ndi Mboni za Yehova. Komabe ndinakakamizika kukumana nazo mwanjira yomwe sindinayembekezere n’komwe.

Mchimwene wanga amene akukhala ku Sweden anakhala wa Mboni za Yehova, ndipo ndinaitanidwa ku ukwati wake umene unachitikira m’Nyumba ya Ufumu! Zimenezo zinandisinthitsa kwambiri malingaliro anga okhudza Mboni. Ndinadabwa kuti, iwo sanali anthu osasangalatsa monga momwe ndinkawalingalirira nthaŵi zonse. Anali anthu okoma mtima, osangalala, ndiponso anthabwala.

Panthaŵi imeneyi, mwamuna wanga wakale, Lars, anali atasinthiratu. Anali wosamalira zinthu kwambiri, ankacheza ndi ana ake, anali wokoma mtima komanso wodekha m’kayankhulidwe, ndiponso sankamwa moŵa mwauchidakwa monga momwe ankachitira kale. Umunthu wake unali wosiririka kwambiri! Tsopano anali munthu wa makhalidwe ofanana ndendende ndi mmene ndinkafunira kuti azikhalira. Zinali kundipweteka mtima kwambiri n’kaganizira kuti sindinalinso mkazi wake ndiponso kuti mwinamwake nthaŵi ina yake adzakwatira mkazi wina!

Kenako ndinakonza “zokamunyengerera” mochenjera. Nthaŵi ina yake Jonas akukhala ndi atate wake, ndinakonza ulendo pamodzi ndi achemwali anga aŵiri wokaona Jonas ndi Lars. Ndinanamizira kuti amayi aang’ono a Jonas aŵiriwo ayenera kukhala ndi mwayi woona mwana wawo. Tinakakumana m’paki. Pamene achemwali anga ankacheza ndi mwanayo, ine ndi Lars tinakhala pabenchi.

Ndinadabwa kuti, nditangoyambitsa nkhani yokhudza za tsogolo lathu, Lars anatulutsa buku m’thumba mwake. Linali lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. * Anandipatsa bukulo ndi kundiuza kuti ndikaŵerenge mitu yonena za udindo wa mwamuna ndiponso udindo wa mkazi m’banja. Anandilimbikitsa kuti ndikaŵerenge malemba.

Kenako, ine ndi Lars titaimirira kuchoka pabenchipo, ndinafuna kuti tigwirane manja, koma mokoma mtima iye anakana kuchita zimenezo. Lars sanafune kugwirizananso ndi ine popanda kudziŵa malingaliro anga pa chipembedzo chake chatsopano. Zimenezo zinandikhumudwitsa ndithu, komano ndinazindikira kuti maganizo akewo anali abwino kwambiri ndiponso angadzapindulitse ine ndemwe ngati atadzakhalanso mwamuna wanga.

Zonsezi zinandipatsa chidwi kwambiri ponena za Mboni za Yehova kusiyana ndi kale lonse. Tsiku lotsatira ndinaonana ndi mkazi wina yemwe ndinkadziŵa kuti anali Mboni, ndipo tinagwirizana kuti iye ndi mwamuna wake adzandidziŵitse zinthu zimene ndinkafuna ponena za chipembedzo chawo. Anali ndi mayankho a m’Baibulo pa mafunso anga onse ambirimbiriwo. Ndinaona kuti zinthu zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa ndi zozikidwa m’Baibulo. Pa mfundo iliyonse yomwe tinakambirana, sindinachitire mwina koma kuvomereza kuti inali yoona.

Nthaŵi imeneyo ndinasiya Tchalitchi cha Evangelical Lutheran ndiponso ndinasiya ntchito zanga zandale. Ndinasiyanso kusuta. Imeneyo ndiyo inali ntchito yovuta kwambiri pa zonse. Ndinayamba kuphunzira Baibulo mu August 1990, ndipo mu April 1991, ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.

Ukwati Wawo Wachiŵiri

Judith: Tsopano tonsefe tinali Mboni zobatizidwa. Ngakhale kuti tinali titalekana, tonsefe tinali titaphunzira Baibulo. Ndi ziphunzitso zake zabwino, tinathandizidwa kusintha kusiyana ndi mmene tinalili poyamba. Tinkakondanabe, mwinanso kwambiri kusiyana ndi kale. Tsopano tinali ndi ufulu wokwatirananso—ndipo ndi zomwedi tinachita. Tinalumbirirana kachiŵiri, komano nthaŵi ino munali m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

Lars: Chinthu chodabwitsa kwambiri chinali chitachitika—banja lathu linagwirizananso! Panthaŵiyi, tinali osangalala ndi achimwemwe!

Judith: Paukwatiwo panafika ana athu, achibale ambiri, komanso mabwenzi athu ambiri atsopano ndi akale omwe. Unali wosangalatsa kwambiri. Mwa alendo omwe anafikapo panali anthu amene anatidziŵa m’kati mwa ukwati wathu woyamba. Iwo anasangalala kwambiri kutiona tili pamodzinso ndipo anadabwa kuona chimwemwe chenicheni chimene Mboni za Yehova zili nacho.

Ana

Lars: Kuchokera pamene tinabatizidwa takhala ndi chimwemwe kuona ana athu aŵiri akusankha kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova.

Judith: Jonas anazindikira choonadi cha Baibulo kuchokera pamene anachiphunzira akadali mwana pamene amapita kukaona atate wake. Anali ndi zaka khumi zokha pamene anandiuza kuti akufuna kukakhala ndi atate wake chifukwa chakuti, monga momwe iye anafotokozerera, “Atate amatsatira Baibulo.” Jonas anabatizidwa ali ndi zaka 14. Anatsiriza maphunziro ake, ndipo tsopano ali mu utumiki wanthaŵi zonse.

Lars: Mwana wathu woyamba, Martin, ali ndi zaka 27 tsopano. Kusintha kumene anakuona komwe ife tinapanga kunam’ganizitsa zinthu zambiri. Anachoka panyumbapo ndi kukakhala kumbali ina ya dzikoli. Zaka ziŵiri zapitazo, anayamba kuphunzira Baibulo ndi mpingo wina wa Mboni za Yehova wa komwe akukhalako. Pambuyo pa miyezi isanu yokha, iye anali wokonzekera kubatizidwa. Akupitiriza ndi zolinga zake zabwino za moyo wake wa m’tsogolo monga Mkristu.

Pakali pano, mwana wathu wachiŵiri, Thomas, si wa Mboni za Yehova. Timam’kondabe, komanso timamvana naye kwambiri. Ndi wosangalala chifukwa cha kusintha kumene kunachitika m’banja mwathu. Ndipo tonsefe timavomereza kuti banja lathu lagwirizananso chifukwa cha thandizo la mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zomwe makolofe tinaphunzira. Ndi dalitso lalikulu kwambiri kwa ife kuti tsopano banja lathu limakumana kaŵirikaŵiri, anyamata onse atatu ndi makolo onse aŵiri!

Moyo Wathu Lerolino

Lars: Sitikunena kuti tsopano ndife anthu angwiro. Koma taphunzira kanthu kenakake—kuti chikondi ndi kulemekezana ndizo zinthu zofunika kwambiri mu ukwati wabwino. Maziko amene tamangapo ukwati wathu tsopano ndi osiyana kwambiri ndi omwe tinamangapo ukwati woyamba. Tonse aŵirife tikugonjera ulamuliro wotiposa enife, chifukwa tazindikira kuti ndi Yehova amene tikukhalira moyo. Ine ndi Judith ndife ogwirizana kwambiri ndipo mwachikhulupiriro timayembekezera zinthu za m’tsogolo.

Judith: Ndikuganiza kuti ndife umboni weniweni wakuti Yehova ndi phungu wabwino kwambiri wa ukwati ndiponso pankhani zabanja.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 30 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mu 1978; tsopano analeka kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 28]

Lars ndi Judith panthaŵi ya ukwati wawo woyamba, mu 1973

[Chithunzi patsamba 29]

Anyamata atatu anataya banja lawo logwirizana ndipo analipezanso

[Chithunzi patsamba 31]

Lars ndi Judith lerolino, anagwirizananso chifukwa chotsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo