Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mabanja Amapiririra Matenda Aakulu

Mmene Mabanja Amapiririra Matenda Aakulu

Mmene Mabanja Amapiririra Matenda Aakulu

KUPIRIRA kungatanthauzidwe monga “mphamvu yokhoza kugonjetsa ndiponso kuthana ndi kuvutika maganizo komwe munthu ali nako.” (Taber’s Cyclopedic Medical Dictionary) Kumatanthauzanso kuthana ndi mavuto a matenda aakulu m’njira yoti mukhoza kuwalamulira ndiponso kukhala paufulu m’maganizo. Ndiponso poganizira kuti matenda aakulu ndi nkhani yokhudza banja, kuti banjalo lipirire mwachipambano m’pofunika kuti aliyense wa m’banjalo achirikize mwachikondi ndiponso mokhulupirika. Tiyeni tione njira zina zimene mabanja amapiririra matenda aakulu.

Kudziŵa N’kofunika

Mwina sikungatheke kuchiza matendawo, komabe kudziŵa mmene mungapiririre kungachepetse kudandaula. Zimenezi n’zogwirizana ndi mwambi wakale umene umati: “Munthu wodziŵa ankabe nalimba.” (Miyambo 24:5) Kodi banja lingadziŵe bwanji mmene lingapiririre?

Choyamba pezani dokotala wochezeka ndiponso wothandizadi, wofunitsitsa kuti azifotokoza zonse bwinobwino kwa wodwalayo ndiponso kwa banja lake. “Dokotala woyenera amaganizira za banja lonselo ndiponso amadziŵa njira zonse zochizira matendawo,” limatero buku lakuti A Special Child in the Family.

Chachiŵiri ndicho kumafunsa mafunso olunjika mpaka mutamvetsa bwino za matendawo. Komabe, kumbukirani kuti pamene muli ndi dokotala, n’kwapafupi kukhala womangika n’kuiŵala zomwe m’mafuna kufunsa. Njira ina yothandiza ndiyo kulemberatu mafunso. Makamaka, mungafune kudziŵa kuti matendawo angafike potani ndiponso kuti mungawachize bwanji komanso kuti mungachite chiyani pankhaniyi.—Onani bokosi lakuti “Mafunso Amene Banja Lingafunse Dokotala.”

N’kofunika kwambiri kuti muwadziŵitse bwino lomwe abale ake a bele limodzi a mwana wodwala matenda aakuluyo. “Fotokozani vuto lake kuyambira masiku oyambirira omwewo,” anatero mayi wina. “Iwo angaganize mosavuta kuti sakuŵerengeredwa m’banjalo ngati sakudziŵa chimene chikuchitika.”

Mabanja ena apezanso chidziŵitso chothandiza mwa kufufuza m’mabuku opezeka m’nyumba yosungira mabuku yakwawoko, m’nyumba yogulitsira mabuku, kapenanso pa intaneti. Nthaŵi zambiri akhala akupeza chidziŵitso chatsatanetsatane cha matenda amene akuwafufuza.

Kukhalabe ndi Moyo Wabwino Ndithu

Anthu a m’banja amafuna kuti wodwala akhalebe ndi moyo wabwino ndipo ichi n’chibadwa. Mwachitsanzo, taganizirani za Neil du Toit yemwe tam’tchula m’nkhani yoyamba ija. Matenda ake amamufooketsa ndipo amathedwabe nzeru ndi zimenezi. Komabe, iye amachita ntchito imene amasangalala nayo kwambiri kwa maola 70 pamwezi, ntchito yolankhula ndi anthu a m’dera limene akukhala za chiyembekezo chake cha m’Baibulo. Iye anati, “Chinanso chimene chimandikhutiritsa ndicho kupereka malangizo a m’Baibulo mumpingo.”

Munthu akakhala ndi moyo wabwino amakhozanso kusonyeza ndiponso kulandira chikondi, kugwira ntchito yosangalatsa, ndiponso kukhalabe ndi chiyembekezo. Odwala angakondebe kusangalala ndi moyo nthaŵi iliyonse imene akupezako bwino panthaŵi imene akulandira chithandizoyo. Bambo wina amene banja lake lapirira matenda kwazaka zoposa 25 anafotokoza kuti: “Timakonda kuyenda kwabasi, koma chifukwa chakuti mwana wathu sangathe kutero, sitipita kutali. Choncho timachita mwanjira ina. Timapita kumalo osavuta kuyenda.”

Inde, odwala amapezanso mphamvu zomwe zimawatheketsa kukhala okhutira ndi moyo kumlingo winawake. Malinga ndi matenda ake, odwala ambiri angayamikirebe zinthu zokongola ndiponso mawu okoma. Akamaona kuti akudzilamulira okha pa zinthu zosiyanasiyana m’moyo wawo, ndiye kuti n’zotheka kuti adzakhalanso ndi moyo wabwino.

Kuthana ndi Maganizo Osautsa

Mbali ina yofunika popirira ndiyo kudziŵa mmene mungaletsere maganizo osautsa. Mkwiyo uli umodzi mwa maganizo oterewo. Baibulo limavomereza kuti munthu angakhale ndi zifukwa zokwiyira. Komabe, limatilimbikitsa kuti “wosakwiya msanga.” (Miyambo 14:29) Kodi n’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kuchita zimenezi? Malinga ndi zimene buku lamaumboni lina limanena, mkwiyo “ungakuvulazeni pang’onopang’ono ndiponso kukusungitsani chakukhosi kapena kukulankhulitsani zinthu zopweteka zimene potsiriza pake mudzanong’oneza nazo bondo.” Ngakhale kukwiya kamodzi kokha kungawononge zinthu zimene zingatenge nthaŵi yaitali kuzikonzanso.

Baibulo limalamulira kuti “dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) N’zodziŵikiratu, kuti palibe chomwe tingachite kuti tichedwetse kuloŵa kwa dzuŵa. Komabe pali njira zomwe tingatsate kuti tichotse mkwiyo mwamsanga kotero kuti usapitirire kutiwononga ifeyo kapena ena. Ndipotu mungathetse bwinopo nkhani inayake ngati mutakhazika mtima pansi.

Mofanana ndi banja lina lililonse, banja lanulo mosakayika lidzakhala ndi mavuto komanso mtendere. Ena amaona kuti angapirire bwinopo atauzana okhaokha kapena atauza munthu wina wachifundo ndi wokoma mtima. Zimenezi n’zimene anachita Kathleen. Iye poyamba ankasamala amayi ake amene ankadwala kansa, ndipo kenako anasamala mwamuna wake amene ankadwala matenda aakulu ovutitsa maganizo yemwenso m’kupita kwanthaŵi anadzadwala matenda otchedwa Alzheimer. Iye anavomereza kuti: “Zinali kunditsitsimula ndiponso kunditonthoza n’kamalankhula ndi mabwenzi omvetsa.” Rosemary, amene ankasamalira amayi ake kwa zaka ziŵiri, akuvomerezana nazo. Iye anati, “kulankhula ndi bwenzi losabisa mawu, kunandithandiza kukhalabe ndi maganizo abwino.”

Komabe, pamene mukulankhula, musadabwe ngati mukulephera kuletsa misozi kutsika. Kulira kumachotsa kuvutika maganizo ndiponso ululu, komanso kumakuthandizani kuthetsa chisoni chanu,” limatero buku lakuti A Special Child in the Family. *

Khalanibe ndi Chiyembekezo

“Mtima wanu wofuna kukhalabe ndi moyo ungakulimbikitseni mukadwala,” inalemba motero Mfumu yanzeruyo Solomo. (Miyambo 18:14, Today’s English Version) Ofufuza amakono apeza kuti zomwe wodwala amayembekezera, kaya zikhale zosangalatsa kapena zokhumudwitsa, nthaŵi zambiri zimakhudza zotsatira za chithandizo chamankhwala chomwe akulandira. Komabe, kodi banja lingakhalebe lolimbikitsa motani litakumana ndi matenda aakulu okhalitsa.

Ngakhale kuti sakunyalanyaza matendawo, mabanja amapirira bwinopo ngati akulimbikira pazinthu zimene akukwanitsabe kuchita. Bambo wina anavomereza ponena kuti: “Zochitika pa matendawo zingakukhumudwitseni kwambiri, komabe muyenera kudziŵa kuti mudakali ndi zinthu zina zambiri zosangalatsa. Ndinu amoyobe, muli pamodzibe, ndiponso muli ndi mabwezi anube.”

Ngakhale kuti matenda aakulu safunika kuwatenga mwachibwanabwana, nthabwala zosangalatsa zimathandiza kupewa mzimu wotaya chiyembekezo. Kukonda nthabwala kwa anthu a m’banja la Du Toit kukusonyeza mfundoyi. Collette, yemwe ndi mlongo wake wa Neil du Toit wam’ng’ono kwambiri, anafotokoza kuti: “Chifukwa chakuti tinaphunzira kupirira zochitika zina, timatha kuseka zinthu zina zimene zatichitikira zomwe kwa ena zingaoneke ngati zokhumudwitsa kwambiri. Komabe kuchita zimenezi kumathandizadi kuchotsa kuvutika maganizo.” Baibulo limatitsimikizira kuti “mtima wosekerera uchiritsa bwino.”—Miyambo 17:22.

Zinthu Zauzimu Zofunika Koposa

Chinthu chofunika kwambiri pachikhalidwe chauzimu cha Akristu oona chimaphatikizapo ‘kulola kuti zopempha zawo zidziŵike kwa Mulungu mwapemphero pamodzi ndi pembedzero.’ Zotsatira zake ndizo zimene Baibulo limalonjeza, zakuti: “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afilipi 4:6, 7) Atalera ana aŵiri odwala matenda aakulu kwa zaka 30, mayi wina anati: “Tadziŵa kuti Yehova amathandiza munthu kupirira. Iye amakulimbikitsadi.”

Komanso, ambiri amalimbikitsidwa ndi malonjezo a Baibulo a dziko lapansi la paradaiso lopanda choŵaŵitsa ndiponso mavuto. (Chivumbulutso 21:3, 4) “Chifukwa cha matenda aakulu amene banja lathu lakumana nawo, timaona kuti malonjezo a Mulungu akuti ‘wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba amatanthauza zinthu zambiri kwa ife.’” Mofanana ndi anthu ena ambiri, banja la a Du Toit likulakalaka kwambiri nthaŵiyo m’Paradaiso pamene “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; 35:6.

Khazikani mtima pansi. Zoŵaŵa ndiponso mavuto amene akupondereza anthu ali pa iwo okha chizindikiro chakuti mikhalidwe yabwino yayandikira. (Luka 21:7, 10, 11) Komabe, padakali pano, anthu ambiri osamala ena ndiponso odwala angachitire umboni kuti Yehova alidi “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mudziŵe zambiri za mmene mungapiririre ululu wa m’maganizo, onani nkhani yakuti “Kusamala Wina Kukwanitsa Votolo,” mu Galamukani! wa February 8, 1997, masamba 3-13.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]

Mafunso Amene Banja Lingafunse Dokotala

• Kodi matendawo adzakula motani, ndipo kodi chidzachitike n’chiyani?

• Kodi padzakhala zizindikiro zotani ndipo kodi tingadzathane nazo bwanji?

• Kodi pali njira zina zotani zothandizira wodwalayo?

• Kodi njira zimenezi zili ndi mavuto, ngozi, ndiponso ubwino wotani?

• Kodi mungachite chiyani kuti matendawo akhaleko bwino, ndiponso muyenera kusachita chiyani?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]

Mmene Mungathandizire

Anthu ena angalephere kucheza kapena kuthandiza ena chifukwa chakuti sakudziŵa zimene anganene kapena mmene angachitire ndi nkhaniyo. Ena angachite zinthu monyanyira, ndipo mwa kulamula ena kuchita zimene iwo amaona kuti n’zothandiza, angawonjezere vuto la banjalo. Ndiyeno, kodi munthu angathandize bwanji anthu amene ali ndi banja limene anthu ake akudwala matenda aakulu popanda kuloŵerera m’nkhani zawo?

Mvetserani Monga Kuti ndi Vuto Lanu. Yakobo 1:19 amati, ‘khalani wotchera khutu.’ Sonyezani kukhudzidwa mwa kukhala womvetsera wabwino ndiponso kulola anthu a m’banjalo kuti atulutse zakukhosi ngati iwo akufuna kulankhulapo. Iwo angafunitsitse kwambiri kuchita zimenezi ngati ataona kuti inuyo ‘mukuwachitira chifundo.’ (1 Petro 3:8) Komabe, kumbukirani kuti, anthu aŵiri kapena mabanja aŵiri osiyana sangachite zinthu zolingana pa matenda aakulu omwe awagwira. Choncho, “musawalangize pokhapokha ngati mukudziŵadi zonse zokhudza matendawo kapena mmene zinthu zilili,” anatero Kathleen, yemwe ankasamala amayi ake ndipo kenako mwamuna wake yemwe ankadwala matenda aakulu. (Miyambo 10:19) Komanso kumbukirani kuti, ngakhale mutadziŵa zinazake zokhudza matendawo, wodwalayo ndi banja lake mwina sangafune kufunsira kapena kulandira malangizo anu.

Perekani thandizo lenileni. Poganizira za kufunika kwa kusaloŵerera m’nkhani zabanjalo, khalani pamodzi ndi banjalo panthaŵi imene iwo akufunadi kuti mukhalepo. (1 Akorinto 10:24) Braam, yemwe mawu ake takhala tikuwalemba m’nkhani zino ananena kuti: “Anzathu achikristu anatithandiza kwambiri. Mwachitsanzo, titakagona kuchipatala chifukwa cha kukula kwa matenda a Michelle, nthaŵi zonse tinkakhala limodzi ndi anzathu okwana anayi kapena mpaka asanu ndi m’modzi usiku wonse. Nthaŵi iliyonse tikafuna thandizo, tinkalipeza.” Ann yemwe ndi mkazi wa Braam, anawonjezera kuti: “Inali nyengo yozizira kwambiri, ndipo kwa milungu iŵiri tinali kupatsidwa chakudya chosiyanasiyana tsiku ndi tsiku. Tinalimbikitsidwa mwa kudya chakudya chotentha ndiponso kusonyezedwa chikondi chosaneneka.”

Pempherani nawo pamodzi. Nthaŵi zina, sipakhala zinthu zambiri zoti ungachite pothandiza, kapenanso pamakhala palibiretu. Komabe, chimodzi mwa zinthu zolimbikitsa kwambiri ndicho kugaŵana nawo mfundo inayake yolimbikitsa ya m’Malemba, kapena kupemphera moona mtima ndi odwalawo pamodzi ndi mabanja awo. (Yakobo 5:16) “Musanyalanyaze mphamvu ya kuwapempherera ndiponso kupemphera nawo odwala matenda aakulu pamodzi ndi mabanja awo,” anatero Nicolas wazaka 18, amene mayi ake akudwala matenda aakulu ovutika maganizo.

Ndithudi, chichirikizo choyenera chingathandize kwambiri mabanja kupirira mavuto a matenda aakulu. Baibulo limanena zimenezi motere: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]

Matendawo Akafika Pakayakaya

Mabanja ena angamakayikekayike kukambirana za kuyandikira kwa imfa ya wokondedwa wawo amene akudwala mwakayakaya. Komabe, buku lakuti Caring—How to Cope limanena kuti “ngati mukudziŵapo kanthu kokhudza zimene mungayembekezere ndiponso zimene muyenera kuchita, zingakuchotseni mantha.” Ngakhale kuti zoti muchite kwenikweni zingasiyanesiyane malinga ndi malamulo ndiponso miyambo yakumaloko, naŵa malingaliro ena amene banja lingafune pamene likusamalira wokondedwa yemwe akudwala mwakayakaya.

Nthaŵi Idakalipo

1. Funsani dokotala zimene mungayembekezere munthuyo akatsala madzi amodzi ndiponso zomwe muyenera kuchita ngati wodwalayo atatsirizika pakati pa usiku.

2. Lembani mayina a anthu omwe adzafunika kuwadziŵitsa za imfayo.

3. Kambiranani mmene mwambo wa maliro udzayendere:

• Kodi ndi zinthu ziti zimene wodwalayo akufuna?

• Kodi akufuna kuti mtembo wake mudzawuike m’manda kapena mudzautenthe? Yerekezerani mtengo ndiponso ntchito za anthu osiyanasiyana oyendetsa mwambo wamaliro.

• Kodi mwambo wamalirowo udzachitike liti? Perekani mpata kuti anthu akonze mayendedwe.

• Kodi ndani adzayendetsa mwambo wamaliro?

• Kodi udzachitikira kuti?

4. Ngakhale wodwalayo atafooka kwambiri, iye angadziŵebe zimene zikulankhulidwa kapena kuchitidwa pafupi naye. Samalani kuti musalankhule kanthu kalikonse pamaso pake kamene mukufuna kuti iye asamve. Mwina mungafune kumulimbikitsa pomamuuza tinkhani ndiponso pofumbata dzanja lake.

Pamene Wokondedwa Uja Amwalira

Nazi zinthu zina zimene ena angachite kuti athandize banjalo:

1. Lolani banja lofedwalo kuti likhale lokha ndi wakufayo kwakanthaŵi ndithu n’cholinga choti lizoloŵere imfayo.

2. Pempherani pamodzi ndi banjalo.

3. Pamene a m’banjalo angafune, angayamikire kuwathandiza podziŵitsa anthu awa:

• Dokotala kuti achitire umboni za imfayo ndiponso kupereka chikalata chaumboni waimfa.

• Woyendetsa mwambo wamaliro, anthu akunyumba yachisoni kapena akunyumba yotenthera mitembo, kuti asamale mtembowo.

• Achibale ndi mabwenzi. (Mwina mungayankhule mwachikulu ponena kuti: “Ndikukuimbirani foniyi malinga ndi nkhani ya wodwala uja [tchulani dzina la wodwalayo]. Pepani kuti nkhani yake siyabwino ayi. Monga mukudziŵa, iye wakhala akudwala [tchulani matenda omwe ankadwala] kwakanthaŵi ndithu ndipo wamwalira [tchulani tsiku limene anamwalira ndi malo].)

• Mungauzenso amanyuzipepala kuti afalitse za imfayo ngati n’koyenera kutero.

4. Banja lofedwalo lingafune kuuza munthu wina kuti alithandize kulongosola mwambo wonse wamalirowo.

[Chithunzi patsamba 17]

Anthu a m’banjamo ayenera kuyesetsa mmene angathere kukhalabe ndi moyo wabwino

[Chithunzi patsamba 18]

Kupemphera pamodzi ndi a m’banjamo kungawathandize kuti apirire