Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pamene Nthenda Yaikulu Yagwira Banja

Pamene Nthenda Yaikulu Yagwira Banja

Pamene Nthenda Yaikulu Yagwira Banja

CHIMWEMWE cha banja la a Du Toit n’chochititsa ena kukhala achimwemwe. N’zochititsa chidwi kwabasi kuona mmene amakonderana. Mutakumana nawo, simungaganize n’komwe zoti iwo apirira mavuto ambiri.

Choyamba, pamene mwana wawo wachisamba Michelle anali ndi zaka ziŵiri, Braam ndi Ann anauzidwa kuti iye ali ndi nthenda yaikulu yotengera mwachibadwa imene imafooketsa minofu.

Ann, yemwe ndi mayi ake a mtsikanayo anafotokoza kuti, “mwadzidzidzi, umayenera kuphunzira mmene ungachitire kuti upirire ndi nthenda yaikulu yofooketsayi. Umadziŵa kuti moyo wabanja zaterepa udzasintha kwambiri.”

Komabe atabereka mwana wina wamkazi ndi wamwamuna, vuto lowonjezereka linagweranso banjali. Tsiku lina ana atatuwo anali kuseŵera panja, kenako ana aakazi aŵiriwo anathamangira m’nyumba uku akulira. “Mayi! Mayi! Bwerani msanga. Neil sali bwino!”

Atatuluka, Ann anaona mutu wa Neil yemwe anali ndi zaka zitatu uli khoba! Iye anali kulephera kuudzutsa.

Ann akukumbukira kuti, “ndinangoti kakasi kusoŵa chochita, ndipo nthaŵi yomweyo ndinazindikira vutolo. Zinandiŵaŵa mumtima podziŵa kuti mwana wamng’ono wathanzi ngati ameneyu adzakhalanso ndi vuto lomwelo la nthenda yofooketsa minofu yomwe inagwira mlongo wake wamkulu.”

“Chisangalalo choti tayamba moyo wabanja tili athanzi, posakhalitsa chinaloŵedwa m’malo ndi mavuto osaneneka amene sitinakumanepo nawo n’kalelonse,” anatero a Braam womwe ndi bambo a m’banjali.

M’kupita kwanthaŵi Michelle, ngakhale kuti amalandira thandizo lamankhwala labwino koposa, anamwalira chifukwa cha matenda ena obwera chifukwa cha nthenda yakeyo. Panthaŵiyo n’kuti ali ndi zaka 14 zokha basi. Neil akupitirizabe kulimbana ndi mavuto a nthenda yakeyo.

Zimenezi zikubweretsa funso lakuti, Kodi mabanja onga ngati la a Du Toit angapirire motani mavuto okhala ndi banja la anthu odwala matenda aakulu? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione njira zina zimene matenda aakulu amakhudzira mabanja.