Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Simungadzafune Kuuphonya!

Simungadzafune Kuuphonya!

Simungadzafune Kuuphonya!

KUPHONYA chiyani? Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wotchedwa “Akuchita Mawu a Mulungu”! Misonkhano yotsatizana imeneyi, imene inayamba m’mwezi wa May ku United States, idzachitika m’mizinda yambiri padziko lonse kwa miyezi ingapo ikubwerayi. M’malo ambiri pulogalamu idzayamba ndi nyimbo pa Lachisanu m’maŵa nthaŵi ya 9:30.

Pambuyo potsegulira pulogalamu yam’maŵa ndi mawu olimbikitsa kumvera zimene Mawu a Mulungu akunena, pulogalamuyo idzapitirira ndi nkhani yakuti “Sangalalani ndi Ubwino wa Yehova” ndiponso yakuti “Kukhalabe Osasunthika Ngati Oona Iye Wosaonekayo.” Kenako pulogalamu yam’maŵayo idzafika kumapeto ndi nkhani yaikulu ya msonkhano wachigawo yakuti “Tamandani Yehova—Wochita Zinthu Zodabwitsa.”

Nkhani yoyamba m’chigawo chamasana idzakhala yakuti, “Musaleme Pakuchita Zabwino,” ndipo idzatsatiridwa ndi nkhani yosiyirana yambali zitatu yonena za mmene tingasankhire mnzathu wamuukwati, kumanga banja lolimba mwauzimu, ndiponso mmene tingaphunzitsire ana kukonda Yehova. Nkhani yomaliza m’tsikuli yakuti, “Kuyendera Limodzi ndi Gulu la Yehova,” idzapenda kusintha koonjezereka kwa mamvedwe a zifuno za Mulungu kumene kwazindikiridwa m’nthaŵi zino.

Pulogalamu ya Loŵeruka m’maŵa ili ndi nkhani ina yosiyirana yambali zitatu imene ili yachiŵiri yakuti, “Atumiki a Mawu a Mulungu.” Nkhani imeneyi idzapereka mfundo za mmene tingachitire ntchito yathu yopanga ophunzira. Kenaka padzabwera nkhani yogwira mtima yakuti “Kusachititsa Manyanzi Mulungu.” Pambuyo pake padzakhala nkhani ya ubatizo, ndipo mpata woti abatizidwe udzaperekedwa kwa amene ayeneretsedwa.

Masana, nkhani yachitatu yosiyirana yambali zitatu idzagogomezera mutu wankhani wakuti, “Limbikirani Kukulitsa Mkhalidwe Wauzimu.” Nkhaniyi idzapereka mfundo zothandiza mmene tingakulitsire mkhalidwe wauzimu. Chigawochi chidzatha ndi nkhani yopatsa chidziŵitso yamutu wakuti, “Yendani M’kuunika Kowalirawalirabe kwa Mawu a Mulungu.” Nkhaniyi idzalongosola machaputala 25 ndi 26 a Yesaya ndipo idzafotokoza mmene tingamvetsetsere bwino buku la m’Baibulo lochititsa chidwi limeneli.

Lamlungu m’maŵa kudzakhala nkhani yosiyirana yomaliza yambali zitatu yamutu wakuti “Ulosi wa Zefaniya Watanthauzo kwa Ochita Chifuniro cha Mulungu.” Nkhaniyi idzafotokoza mmene ulosiwo unagwirira ntchito m’nthaŵi yakale kumtundu wa Ayuda ndiponso mmene udzagwirire ntchito m’nthaŵi yathu, makamaka ku matchalitchi a zipembedzo zadzikoli. Kenaka padzabwera seŵero lomwe ochita ake adzavala zogwirizana ndi za panthaŵiyo lamutu wakuti “Zitsanzo Zotichenjeza M’nthaŵi Yathu,” limene lidzalongosola makhalidwe onyansa a amuna achiisrayeli atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Mapeto achigawo chomaliza cha msonkhano wachigawo pa Lamlungu masana adzakhala nkhani yapoyera yakuti “Chifukwa Chake Tiyenera Kulingalira Ntchito Zodabwitsa za Mulungu.”

Konzekerani pakali pano kuti mudzapezekepo masiku onse atatu. Kuti mudziŵe malo amsonkhano akufupi ndi kwanu, pitani Kunyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kapena lemberani kalata kwa ofalitsa magazini ino. M’magazini yathu ina ya Nsanja ya Olonda, m’kope la February 15, muli m’ndandanda wa malo amisonkhano ku United States, Canada, Britain, ndi Ireland.