Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zithunzi Zamaliseche Zayamba Kupezeka pa Intaneti

Zithunzi Zamaliseche Zayamba Kupezeka pa Intaneti

Zithunzi Zamaliseche Zayamba Kupezeka pa Intaneti

PADZIKO LONSE ANTHU MIYANDAMIYANDA AKUGWIRITSA NTCHITO Intaneti tsiku ndi tsiku. Anthu ambiri amatsegula intaneti pa makompyuta awo pofuna kuchita malonda, kuŵerenga nkhani za padziko lonse zimene anaziphonya, kufuna kudziŵa za nyengo, kuphunzira za mayiko osiyanasiyana, kudziŵa zinthu zina zofunika paulendo, kapena kuyankhulitsana ndi achibale ndiponso anzawo a kumbali zosiyanasiyana za padziko. Koma anthu ena, okwatira ndi osakwatira omwe ngakhalenso ana ochuluka kwambiri, amatsegula intaneti pa chifukwa chinachina: KUTI AKAONE ZITHUNZI ZAMALISECHE.

ZITHUNZI ZAMALISECHE ZA PA KOMPYUTA n’zotchuka kwambiri mwakuti zasanduka malonda opindulitsa zedi. Nyuzipepala ya Wall Street Journal inati: “Ngati mutapeza Malo Achidziŵitso a pa intaneti amene akuyenda malonda kwambiri ndiye kuti n’zachidziŵikire kuti amaonetsapo zamaliseche zokhazokha.”

Nyuziyo inapitiriza kulongosola chifukwa chimene anthu amatsegulira intaneti kuti aone zamaliseche: “Anthu amene analembetsa angaone zinthu zamanyazi popanda kuchita kuzembera ku sitolo yogulitsako mabuku a zolaula kapena kupita kuseli kwa nyumba yapafupi yobwereketsa mavidiyo. Olembetsa angathe kufatsa nazo zonyansazi ali phee m’nyumba kapena muofesi.”

Nkhani ya Zithunzi Zamaliseche ndi Ana

N’zomvetsa chisoni kuti ambiri amene amaona zithunzi zamaliseche pa intaneti ndi ana. Ana saloledwa mwalamulo kugula mabuku a zamaliseche kapena kubwereka mavidiyo a zamaliseche, komabe angathe kuziona zimenezi podiniza kangapo chabe mabatani a pakompyuta. Akatero angopeza kuti malo oonako zoterozo ali mbwee.

Ana ambiri amatsegula kaŵirikaŵiri malo a pa intaneti makolo awo asakudziŵa. Nyuzipepala ya The Detroit News inatchula mfundo yakuti “ana oposa aŵiri mwa ana asanu aliwonse analembetsa kuti azitsegula Malo ena ake Achidziŵitso kapena kuti azichita zinthu zina pa intaneti ngakhale kuti pafupifupi makolo 85 mwa makolo 100 alionse ali ndi malamulo oletsa zimenezi.”

Ana ambiri, ngakhalenso achikulire, amayesetsa kubisa zakuti amaona zamaliseche, koma si onse amene amaona kuti n’kofunika kubisa. Ena amaona kuti limeneli ndi khalidwe losangalatsa limene silivulaza. Ena amanena kuti si bwino kuti ana aziona zamaliseche koma amati zimene anthu achikulire amachita kwaokha akafatsa n’zawo.

M’mayiko ena kusamvana pankhani ya kuona zithunzi zamaliseche kwasanduka mkangano wandale weniweni. Kumbali imodzi kuli anthu amene amati ufulu wa kulankhula n’ngwofunika zedi ndipo otereŵa amauza ena kuti zamaliseche zipitirire kuonetsedwa. Kumbali inayi kuli anthu amene amati makhalidwe abwino a pabanja ndiwo ofunika zedi ndipo iwoŵa akuyesa kuchititsa akuluakulu a boma kuti aletse zamaliseche.

Galamukani! siiloŵerera mu nkhani zandale. Cholinga cha nkhani zotsatizana zino n’chofuna kudziŵitsa aŵerengi athu za kuopsa kwa kuona zithunzi zamaliseche, kutchulapo njira zimene anthu angadzitetezere pamodzi ndi okondedwa awo, ndiponso kupereka malingaliro ozikidwa m’Baibulo kwa aliyense amene wakopeka ndi kuona zamaliseche ndipo akufuna kusiya.