Kodi Mtumiki Ndani?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Mtumiki Ndani?
MADZULO a tsiku limene Yesu anafa imfa yansembe, anzake a pamtima anakangana kwambiri. Malingana n’kunena kwa Luka 22:24, akuti “kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.” Iyi siinali nthaŵi yoyamba kuti pakhale mkangano wotere pakati pa atumwi a Yesu. Yesu anali atawalangizapo kuti asamatero pafupifupi nthaŵi zina ziŵiri m’mbuyomo.
Zinali zomvetsa chisoni kwambiri kuti pausiku wofunika kwambiri umenewu, Yesu anayenera kuwakumbutsanso mmene mtumiki wachikristu ayenera kukhalira. Iye anati: “Iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.”—Luka 22:26.
Sitiyenera kudabwa kuti atumwi anali ndi malingaliro olakwika a udindo ndiponso kudziŵika. Asanam’dziŵe Yesu, chitsanzo chawo chachikulu cha utsogoleri wa chipembedzo chinali choperekedwa ndi alembi ndi Afarisi. M’malo motsogolera anthu mwauzimu, atumiki onyenga ameneŵa anakhazikitsa miyambo ndiponso malamulo okhwima amene “anatsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pawo.” Anali anthu okonda maudindo, ofuna kudziŵika, osamva za ena ndipo ankachita ntchito zawo “kuti aonekere kwa anthu.”—Mateyu 23:4, 5, 13.
Mtumiki Wamtundu Watsopano
Komabe, Yesu, anayambitsa utumiki wamtundu wina kwa ophunzira ake. Iye anaphunzitsa kuti: “Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. . . . Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.” (Mateyu 23:8-11) Ophunzira a Yesu sanayenere kutsanzira atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lawo. Ngati anali kufuna kukhala atumiki enieni, anayenera kutsanzira Yesu. Kodi iye anasiya chitsanzo chotani?
Nthaŵi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito liwu lachigiriki lakuti di·aʹko·nos kutanthauza “mtumiki.” The Encyclopedia of Religion imalongosola kuti liwu limeneli “silisonyeza kufunika kwa mtumikiyo koma mgwirizano wapakati pa iye ndi amene akumutumikira: kutsatira chitsanzo cha Kristu . . . ndiko chinthu chofunika kwambiri patanthauzo la utumiki wachikristu.”
Mogwirizana ndi tanthauzo lolondola la liwu lakuti “mtumiki,” Yesu anapereka chilichonse chimene akanatha kuti athandize anthu. Modekha iye analongosola kuti, “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Mosadzikonda, Yesu anagwiritsa ntchito nthaŵi yake, mphamvu zake, ndi luso lake pothandiza anthu mwakuthupi ndi mwauzimu. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti anawamvera chisoni anthu ozunzidwa mwauzimu amene anali kukhamukira kwa iye kuti akamuone. Anafunitsitsadi kuthandiza. Kukonda kupatsa ndiko kunasonkhezera kuchita utumiki wake, ndipo anafuna kuti ophunzira ake asonyeze mtima wopatsa womwewo.—Mateyu 9:36.
M’moyo wake wonse, Yesu anasiya chitsanzo kwa atumiki am’tsogolo. Iye anati, “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:37, 38) N’zoonadi, atumiki a Kristu anayenera kukhala antchito ochita ntchito yaikulu yoposa imene siinachitikepo padziko, yomwe ili ntchito yopatsa mtundu wa anthu chitonthozo chauzimu polalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 28:19, 20.
Mzimu wopatsa umenewu ndiponso wotumikira zofuna za ena ndiwo unachititsa magwiridwe a ntchito yautumiki a Yesu kukhala osiyana kwambiri ndi ena. Iye anaphunzitsa atumiki ake kukhala antchito, asodzi ndi abusa auzimu osati anthu ongotsatira zinthu zosadziŵika bwino kapena okhala m’kagulu ka anthu ophunzitsidwa mwapadera ndiponso ovala zovala zapadera.—Mateyu 4:19; 23:5; Yohane 21:15-17.
Mmene Baibulo Limaonera Nkhaniyi
N’zomvetsa chisoni kuti m’zaka mazana angapo zapitazi, zinthu zakhota ndipo atumiki sakuonedwanso m’njira yapamwamba imeneyi ndiponso yosadzikonda. Pachiyambi unali utumiki wachikristu koma kenaka unasintha, n’kusanduka dongosolo lochita zinthu mwamwambo ndiponso lokhala ndi maudindo osiyanasiyana. Magulu apadera komanso maudindo anapangidwa, ndipo okhala m’maudindoŵa ankakhala odziŵika komanso amphamvu ndipo nthaŵi zambiri ankapeza chuma chambiri. Izi zinadzetsa kugaŵikana. Panabuka gulu la atsogoleri amatchalitchi achikristu limene linali lotanganidwa kwambiri ndi kutsatira miyambo yodalitsa anthu ndiponso kulangiza olakwa. Chikristu cha m’zaka za zana loyamba chinasintha m’zaka mazana zotsatira. Poyamba chinali chipembedzo chochita ntchito zooneka ndipo aliyense anali mtumiki koma chitasintha chinazizira ndipo amene ankalalikira ndi kuphunzitsa anali anthu ochepa chabe amene anaphunzitsidwa ndi kuvomerezedwa mwapadera.
Komabe, Baibulo silinena kuti mtumiki wachikristu amadziŵika chifukwa cha zovala zapadera, kutsatira miyambo mwatsatanetsatane, malipiro, kapena kuvomerezedwa ndi boma, koma limati amadziŵika ndi ntchito yake yosadzikonda. Mtumwi Paulo ananenapo za mzimu umene atumiki achikristu ayenera kusonyeza. Anawalimbikitsa kuti ‘asachite kanthu monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima.’—Afilipi 2:3.
Mosakayika, Paulo anali kuchita zimene anali kulalikira. Potsatira mosamalitsa chitsanzo cha Kristu, iye anali ‘wosafuna chipindulo chake, koma cha unyinjiwo, kuti apulumutsidwe.’ Iye anali kudziŵa ndiponso kufunitsitsa kukwaniritsa udindo wake wa ‘kulalikira uthenga wabwino kwaulere,’ monga ananenera kuti, “kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.” Iye ‘sanafune ulemerero wa kwa anthu.’—1 Akorinto 9:16-18; 10:33; 1 Atesalonika 2:6.
Iye anaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri cha mtumiki woona wachikristu! Anthu amene amatsatira chitsanzo chake chabwino ndi kuyenda m’chitsanzo chosadzikonda chimene anapereka Yesu Kristu podzipereka mwakufuna kwawo kuti apatse ena chithandizo ndiponso chitonthozo chauzimu cha uthenga wabwino, amasonyeza kuti ndi atumiki oona a Mulungu.—1 Petro 2:21.