Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndisamukire Kudziko lina?

Kodi Ndisamukire Kudziko lina?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndisamukire Kudziko lina?

“Ndinkafuna kukakhalako kwina.”—Sam.

“Ndinkangofuna kudziŵa zinthu basi. Ndinkafuna kuona chinachake chatsopano.”—Maren.

“Mnzanga wapamtima anandiuza kuti kuchoka panyumba kwa kanthaŵi kungandithandize.”—Andreas.

“Ndinkafunitsitsa kupita kutali.”—Hagen.

KODI mumaganizapo zosamukira kudziko lakunja, mwina kwa kanthaŵi kochepa chabe? Chaka chilichonse, achinyamata zikwizikwi amathadi kutero. Pofotokoza za ulendo wake atapita kunja Andreas anati: “Ndingakonde kudzapitanso.”

Achinyamata ena amasamuka kwa kanthaŵi kochepa kuti akapeze ndalama kapena kukaphunzira chinenero chakunja. Mwachitsanzo, m’mayiko ambiri ntchito yotumiza atsikana kunja kukagwira ntchito yosamala pakhomo kuti azipeza malo ogona ndi kuphunzira chinenero china n’njofala. Zimenezi zimatheketsa achinyamata ochokera kunja kugwirira banja linalake ntchito yapakhomo kuti azipeza malo ogona ndi chakudya, ndipo amatha kugwiritsa ntchito nthaŵi yawo yopuma kuphunzira chinenero cha kumeneko. Ndiye palinso achinyamata amene amasamukira kunja kuti akapitirize maphunziro. Ena amasamuka kuti akapeze ntchito n’cholinga choti azithandiza mabanja awo pankhani ya zachuma. Komanso ena amasamuka chifukwa sakudziŵa chochita akamaliza sukulu choncho amafuna kukapuma kunja.

Chosangalatsa n’chakuti, achinyamata ena achikristu asamukira ku mayiko ena kumene kuli alaliki ochepa, kuti apititse patsogolo utumiki wawo. Kaya zifukwa zosamukira zikhale zotani, kukhala kudziko lachilendo kungakhale kopindulitsa pamoyo wauchikulire wodziimira. Kungakuthandizeni kudziŵa chikhalidwe chosiyanasiyana. Mungathenso kudziŵa bwino chinenero chakunja, zimene zingakuthandizeni pamene mukufuna ntchito.

Ngakhale zili choncho, kusamukira kudziko lina si kuti nthaŵi zonse kumakhala kosangalatsa. Mwachitsanzo, Susanne anatha chaka ali kwina monga mwana wasukulu wophunzira kunja mosinthana ndi wina. Iye anati: “Ndinali wotsimikiza kuti ndikasangalala kwambiri kuyambira poyambira mpaka pamapeto. Koma sizinali choncho.” Achinyamata ena adyeredwa masuku pamutu kapenanso agwera m’mavuto aakulu. Ndiyetu musanalongedze katundu wanu, kungakhale kwanzeru kuti muganize mofatsa ndi kuona kaye ubwino ndi kuopsa kwake.

Tsimikizirani Zolinga Zanu

Kuona ubwino ndi kuopsa kwake kungaphatikizepo kupenda zolinga zanu zofunira kupita kunja. Kusamuka n’cholinga chofuna kuchita zinthu zauzimu kapena kuti mukasamalire udindo wabanja ndi nkhani ina. Koma mofanana ndi achinyamata omwe tatchula koyambirira kwa nkhani ino, ambiri amafuna kusamuka chifukwa chakuti akufuna kukaseŵera, ufulu wokwanira kapena kusangalala. Zimenezi si kuti kwenikweni n’zolakwika. Ndiiko komwe, Mlaliki 11:9 amalimbikitsa achinyamata ‘kukondwera ndi unyamata wawo.’ Komatu vesi 10 limachenjeza kuti: “Chotsani zopweteka m’mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako.”

Ngati cholinga chanu posamukira kunja ndicho kuthaŵa zimene makolo amakuletsani, mungakhale mukudziitanira “zoipa.” Kodi mukukumbukira fanizo la Yesu la mwana woloŵerera? Limakhudza wachinyamata amene anapita kunja chifukwa chodzikonda, kwenikweni kuti akakhale ndi ufulu wokwanira. Komabe pasanapite nthaŵi, anapezana ndi vuto ndipo anangozindikira kuti ali wanjala, wosauka komanso wodwala mwauzimu.—Luka 15:11-16.

Palinso ena amene amafuna kusamuka chifukwa chofuna kuthaŵa mavuto kwawo. Koma malingana ndi zimene Heike Berg analemba m’buku lake lotchedwa What’s Up, “ngati mukufuna kuchoka chifukwa chakuti simukusangalala . . . ndiye mukukhulupirira kuti zinthu zonse zikakhala bwino mukapita kwinakwake—zimenezo muiwaliretu!” Inde, n’kwabwino kuthetsa mavutowo moona mtima. Palibe chimene tingapindule pothaŵa mikhalidwe imene sitiikonda.

Zolinga zina zoopsa ndizo umbombo ndi kukonda zinthu zakuthupi. Chifukwa chakukhala ndi chikhumbo chofuna chuma, achinyamata ambiri amakhulupirira maganizo abodza a mmene moyo ulili m’mayiko otukuka. Ena amaganiza kuti anthu onse akumadzulo ndi olemera. Koma zimenezo sizoona konse. Akasamuka, achinyamata ambiri amazindikira kuti ali m’dziko lachilendo, ndipo akulimbana ndi kuthetsa umphaŵi. * Baibulo limachenjeza kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:10.

Kodi Ndinu Wokonzeka?

Mfundo ina yofunika kuiganizira ndi yakuti: Kodi ndinu wokhwima maganizo mokwanira mwakuti mungathe kukathana ndi mavuto, ndi mikangano imene ingabuke kunjako? Mosakayikira muyenera kukakhala ndi mnzanu m’chipinda chimodzi kapena ndi banja komanso kusintha kuti mukagwirizane ndi kachitidwe kawo kazinthu. Ndiye kodi panopa khalidwe lanu n’lotani kunyumba kwanu? Kodi makolo anu amadandaula kuti simuganizira ena ndikuti ndinu wodzikonda? Kodi muli ndi chizoloŵezi chosankha zimene mumadya? Kodi mumavomera kugwira nawo ntchito zapakhomo? Ngati zimenezi zili zovuta kwa inu tsopano, tangoyerekezerani mmene zingakuvutireni m’dziko lachilendo!

Ngati ndinu Mkristu, kodi mudzatha kukhalabe munthu wolimba mwauzimu panokha? Kapena kodi makolo anu amakukumbutsani nthaŵi zonse kuti musamanyalanyaze phunziro la Baibulo, misonkhano yachikristu, ndi ntchito yolalikira? Kodi mungakhale wolimba mwauzimu mwakuti n’kutha kukaniza zitsenderezo ndi mayesero amene simungakumane nawo m’dziko lanu? Patsiku lake loyamba kusukulu ya m’dziko lachilendo, Mkristu wina wachinyamata wosinthana ndi wina, anauzidwa kumene akhoza kupeza mankhwala osokoneza bongo. Pambuyo pake anafunsiridwa ndi mtsikana wa m’kalasi lake. M’dziko lakwawo, mtsikana sangafunsire mwachindunji choncho. Mnyamata winanso wa ku Afirika amene anasamukira ku Ulaya anafotokoza kuti: “Kwathu sungaone zithunzi za maliseche poyera. Koma kuno umangoziona paliponse.” Kusamukira kudziko lina kungaike pangozi moyo wako wauzimu ngati suli “wokhazikika [“wolimba,” NW] m’chikhulupiriro.”—1 Petro 5:9.

Dziŵani Zenizeni!

Musanasamuke, muyenera kudziŵa zenizeni. Musadalire zakumva. Mwachitsanzo, ngati mukuganizira zosinthana ndi mwana wina wasukulu, kodi mudzawononga ndalama zingati? Mungadabwe kudziŵa kuti pamafunika ndalama zochuluka kwambiri. Muyeneranso kudziŵa ngati maphunziro amene mukapeze kudzikolo adzavomerezedwa kwanuko. Komanso, pezani umboni wokwanira monga momwe mungathere wokhudza dzikolo, malamulo ake, chikhalidwe ndi miyambo yake. Kodi pamafunika chiyani kuti ukhale kumeneko? Kodi ndi msonkho wotani umene mudzafunikira kukhoma? Kodi pali zoopsa zokhudza thanzi zimene muyenera kuziganizira? Kungakhale kothandiza kukambirana ndi anthu ena amene anakhalako kumeneko.

Ndiye pali nkhani ya malo okhala. Makolo osunga mwana wasukulu wosinthana ndi mnzake kaŵirikaŵiri sayembekezera kulipidwa kanthu kalikonse. Ngakhale zili choncho, kukhala ndi anthu amene salemekeza mapulinsipulo a Baibulo kungachititse kusweka mtima kwakukulu ndi mikangano. Kukhala ndi anzanu kapena achibale ingakhale njira ina. Koma samalani kuti musakhale mtolo wolemetsa ngakhale pamene akukuumirizani kuti mukhale nawo. Zimenezi zingasokoneze kapenanso kuwononga unansi wanu.—Miyambo 25:17.

Ngati mukufuna kuti mupeze ndalama pamene muli kudziko lina, musaiwale udindo wanu wachikristu, wakumvera akuluakulu a boma. (Aroma 13:1-7) Kodi lamulo limakulolani kugwira ntchito m’dzikolo? Ngati zili choncho, pa mikhalidwe yotani? Ngati mungagwire ntchito mosavomerezeka, mungathe kuwononga mbiri yanu ya kukhala Mkristu woona ndipo mungakhale opanda chitetezo chilichonse, monga ngati insuwalansi ya ngozi. Ngakhale kugwira ntchito kutakhala kovomerezeka, mudzafunikira kukhala atcheru ndi kusamalira mayendedwe anu. (Miyambo 14:15) Olemba ntchito opanda khalidwe kaŵirikaŵiri amadyera masuku pamutu anthu adziko lina.

Kusankha Chochita

Apa tingati zamveka kuti kusankha kusamukira kudziko lina ndi nkhani yaikulu ndipo musaipeputse. Khalani pansi ndi makolo anu ndi kukambirana mofatsa mapindu amene mungayembekezere ndiponso zoopsa zimene zingakhalepo. Yesetsani kuti chikhumbo chanu chisagonjetse kuzindikira kwanu. Khalani oona mtima pamene mukupenda zolinga zanu. Mverani makolo anu mosamalitsa. Chifukwatu, ngakhale mutakhala kutali bwanji iwo adzakhalabe ndi udindo wokusamalirani. Mosakayikira mudzafuna kuti akupatseni thandizo la ndalama zogulira zofunika pa moyo wanu.

Mukalingalira zinthu zonse, mwina mungaone kuti kusamuka panthaŵi ino sikwanzeru. Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa, koma pali zinthu zina zosangalatsa zomwe mukhoza kuchita. Mwachitsanzo, kodi mwafufuza ngati n’kotheka kukaona madera osangalatsa m’dziko lanulo? Kapena, bwanji osayamba panopa kuphunzira chinenero chakunja? Mkupita kwa nthaŵi mwina mwayi wopita kudziko lina udzapezeka.

Bwanji ngati mwasankha kuti musamuke? Nkhani yotsatira idzafotokoza mmene mungakhalire wopambana pamene mukukhala kudziko lina.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Kuŵerengera Mtengo Wakusamukira ku Dziko Lokhupuka,” imene ili mu magazini ya Nsanja ya Olonda ya April 1, 1991, yosindikizidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 27]

Achinyamata ena amasamuka kuti akakulitse Utumiki wolalikira

[Chithunzi patsamba 28]

Kambiranani ndi makolo anu za mapindu ndi kuopsa kwa kusamuka