Kuthandiza Achinyamata Kuthawa “Chikhalidwe cha Imfa”
Kuthandiza Achinyamata Kuthawa “Chikhalidwe cha Imfa”
Kodi chimachititsa achinyamata masiku ano kusangalala ndi nkhani ya imfa n’chiyani? Woimira boma la Illinois, ku United States Henry Hyde, ananena kuti: “Achinyamata ameneŵa ali ndi njala yauzimu imene imawapangitsa kutsata chikhalidwe cha imfa ndiponso chiwawa.”
WOŴERENGA nyuzipepala ya Time wina analemba kuti: “Makolo aulesi, zosangalatsa zachiwawa, kusoŵa khalidwe labwino ndi maziko auzimu, n’zimene zikuchititsa chikhalidwe chachilendo cha imfa chimene achinyamata ali nacho lerolino.”
Kusoŵa ocheza naye ndi vuto linanso lalikulu lomwe likusautsa achinyamata. Achinyamata ena amakhala m’banja limene makolo onse aŵiri amapita kuntchito ndipo sapezeka panyumba masana. Ena ali ndi kholo limodzi lokha. Malinga ndi zomwe buku lina limanena, achinyamata ku United States amakhala ndi makolo awo maola atatu ndi theka okha tsiku lililonse ndiponso maola osapitirira 11 mlungu uliwonse omwe ndi ochepa kwambiri poyerekeza ndi mmene ankachitira achinyamata anzawo m’zaka za m’ma 60. Ndiponso, achinyamata ena sakhala pamodzi n’komwe kapena kuthandizidwa maganizo ndi makolo awo.
Zimene Makolo Angachite
Poganizira za “njala yauzimu” imene achinyamata akulimbana nayo, kodi ndi motani mmene udindo wamakolo ulili wofunika?
Makolo anzeru amazindikira kuti nthaŵi zina ana awo amafunika zosangalatsa zabwino ndiponso kuti amafuna kuwachirikiza nthaŵi ndi nthaŵi. Mosonkhezeredwa ndi chikondi, makolo angalankhule ndi ana awo ponena za nyimbo zimene anawo amakonda, mapulogalamu a pa wailesi yakanema, mavidiyo, mabuku a nthano, maseŵero a pa vidiyo, ndiponso mafilimu. Ngakhale kuti achinyamata sangachite kutchula, ambiri a iwo amalakalaka chikondi ndi chitsogozo chachikondi cha makolo awo. Amafuna mayankho achindunji chifukwa chakuti akukhala m’dziko lodzala ndi zinthu zokayikitsa. Achikulire ayenera kudziŵa kuti ana akukumana ndi zinthu zovuta koposa poyerekeza ndi zomwe iwo ankakumana nazo adakali achinyamata.Makolo amene amafuna kuteteza ana awo amakambirana nawo nthaŵi zonse, kuwamvetsera, ndiponso kuwachenjeza za koopsa kwa kulowerera m’mikhalidwe ya masiku ano. Ngati makolo aika ziletso zamphamvu ndi zosasinthasintha komanso zoyenera limodzi ndi kukonda ana awo, iwo adzapambana.—Mateyu 5:37.
Makolo amene ndi Mboni za Yehova amayesetsa kukambirana ndi ana awo nthaŵi ndi nthaŵi pogwiritsa ntchito Baibulo ndiponso zofalitsa ndi mavidiyo zozikidwa m’Baibulo. * Iwo sagwiritsa ntchito nthaŵi imeneyi kuti adzudzule ana awo koma kuti akambirane nkhani zolimbikitsa mwauzimu. Pamisonkhano yabanja imeneyi, makolo amamva mavuto kapena zopinga zimene zimakhudza mwana aliyense payekha kotero kuti achinyamatawo akhale ndi mwaŵi wothandizidwa payekhapayekha.
Achinyamata amene sapeza chitsogozo chauzimu kuchokera kwa makolo awo angapeze nyonga kuchokera pa Salmo 27:10 limene limati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” Kodi Yehova, Atate wachifundo, amathandiza motani achinyamata? Mipingo ya Mboni za Yehova yakhala kothaŵirako kumene anthu ambiri apezako chikondi cha anthu ena ndipo asiya kukayikira kwawo. M’nyamata wina dzina lake Josías yemwe anaona kuti zimenezi n’zoona ananena kuti: “Gulu la Yehova likuchita ntchito yofunika zedi. Ndinkaganiza kuti moyo ulibe phindu. Ndinkakhala popanda cholinga ndi chiyembekezo. Moyo wanga unasintha kotheratu n’tadziŵa kuti pali anthu ena ondiganizira. Ndimaona abale mumpingo monga banja langa limene linandisiya. Akulu ndiponso mabanja mumpingo ali ngati nangula mu lingaliro lamaganizo.”
Komanso, achinyamata ambiri ndi achikulire omwe awongolera maganizo ndi thanzi lawo lauzimu mwa kupezeka pamisonkhano yampingo ya Mboni za Yehova. Katswiri wa zachikhalidwe cha anthu Patricia Fortuny m’nkhani yake yakuti Los Testigos de Jehová: una alternativa religiosa para enfrentar el fin del milenio (Mboni za Yehova: Chipembedzo Chokhacho Chabwinopo Kumapeto a Zaka Chikwi) ananenapo za thandizoli kuti: “Mboni za Yehova zimapereka dongosolo looneka ndi lomveka bwino lofunika kutsatira m’moyo wa tsiku ndi tsiku, malamulo enieni amene amatsogolera maganizo ndi zochita.” Dongosolo ndiponso malamulo amene akunenedwa pano ndi ozikidwa m’Baibulo. Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amakumana ndi mavuto ndi nsautso zofanana ndi anansi awo, iwo amalimbikitsidwa ndi nzeru yapadera ya buku lakale limenelo. Inde, Mboni zimapeza chitetezo mu ziphunzitso zomveka bwino ndiponso mfundo zachikhalidwe zopezeka m’Baibulo.
Pamene ‘Sikudzakhalanso Imfa’
Chiphunzitso chimene chimaperekedwa ku Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova chimagogomeza nthaŵi ndi nthaŵi za lonjezo la Mulungu lonena za dziko latsopano limene lidzayamba posachedwapa ‘mmene mudzakhalitsa chilungamo’ ndi m’dzikomo ‘simudzakhala wakuwawopsa.’ (2 Petro 3:13; Mika 4:4) Komanso, mneneri Yesaya analemba kuti panthaŵiyo Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse ndipo Ambuye Mfumu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’ Imfa imakantha mtundu wa anthu chifukwa cha tchimo la munthu woyamba, Adamu, komabe lonjezo la Mulungu n’lakuti posachedwapa “sipadzakhalanso imfa”.—Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:3, 4; Aroma 5:12.
Ngati inu ndinu wachinyamata amene mukufunafuna thandizo, tikukupemphani kuti mupeze chiyembekezo ndi chifukwa chokhalira ndi moyo kuchokera m’Baibulo. Mothandizidwa ndi Mboni za Yehova, mungakhale ndi chiyembekezo chakuti nthaŵi zabwino koposa zidakali m’tsogolo mwathu m’dziko latsopano limene Mulungu akulonjeza.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Vidiyo yakuti, Young People Ask—How Can I Make Real Friends? yopangidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Pali pano idakali m’Chingelezi ndipo ikuthandiza kwambiri achinyamata.
[Chithunzi patsamba 9]
Makolo ayenera kupeza nthaŵi yomvetseradi ana awo ndiponso kudziŵa mavuto awo
[Zithunzi patsamba 10]
“Mboni za Yehova zimapereka dongosolo looneka ndi lomveka bwino lofunika kutsatira m’moyo wa tsiku ndi tsiku”