Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musanyengedwe ndi Nkhani Zokopa!

Musanyengedwe ndi Nkhani Zokopa!

Musanyengedwe ndi Nkhani Zokopa!

“Wopusa amakhulupirira chilichonse.”—MIYAMBO 14:15, TODAY’S ENGLISH VERSION.

KUPHUNZITSA n’kosiyana kwambiri zedi ndi nkhani zokopa. Maphunziro amakusonyezani mmene muyenera kuganizira. Nkhani zokopa zimakuuzani zimene muyenera kuganiza. Ophunzitsa abwino amalongosola nkhani yonse osasiyapo kanthu ndipo amafuna kuti muzikambirana. Anthu okopa ena amakukakamizani kumva maganizo awo ndipo safuna kukambirana. Nthaŵi zambiri zolinga zawo zenizeni sizidziŵika. Amachita kusankha mfundo, kutengapo zowakomera zokha ndi kubisa zinazo. Amakhotetsanso mfundo, ndipo ndi akatswiri a bodza ndiponso amaphatikiza bodza ndi zenizeni. Cholinga chawo n’chakuti mungotengeka mtima m’malo moganizirapo mofatsa pankhani ina yake.

Wokopayo amaonetsetsa kuti uthenga wake uoneka kukhala wolondola ndiponso wovomerezeka ndi kutinso ngati mutaumvera ukupangitsani kudziona monga wofunika ndi wokondedwa. Iwo amafuna kuti mukhulupirire zakuti mukamvera uthenga wawo mukhala wochenjera, simukhala nokha, mukhutira ndiponso simukhala ndi nkhaŵa.

Kodi mungadziteteze bwanji kwa anthu otereŵa amene Baibulo limawatcha kuti “olankhula zopanda pake” ndi “onyenga”? (Tito 1:10) Mukadziŵa ena mwa machenjera awo, m’posavuta kuti mupende bwino uthenga kapena nkhani iliyonse imene mungauzidwe. Nazi njira zina zodziŵira zimenezi.

Sankhani: Maganizo ongovomereza zilizonse angayerekezedwe ndi paipi imene chilichonse chingathe kudutsamo, ngakhale zonyansa. Palibe munthu amene amafuna kukhala ndi maganizo oipitsidwa. Solomo, amene anali mfumu ndiponso wophunzitsa m’nthaŵi zakale, anachenjeza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Choncho tiyenera kusankha. Tiyenera kupenda bwino chilichonse chimene tauzidwa, ndi kusankha choti tivomere ndi choti tikane.

Komabe, sitikufuna kuti tikhale osamva za ena mwakuti mpaka n’kumakana kuganizira mfundo zimene zingatithandize kulingalira bwino. Kodi tingadziŵe bwanji malire? Tiyenera kukhala ndi muyezo wopendera nkhani yatsopano imene tangomva. Apa Mkristu ali ndi gwero la nzeru zazikulu. Ali ndi Baibulo lomwe limatsogolera maganizo ake mosaphonyetsa. Komanso, iye ali ndi maganizo ofuna kumva za ena, kapena kuti, olandira chidziŵitso chatsopano. Iye amapenda bwinobwino zimene wamvazo pogwiritsa ntchito Baibulo monga muyezo ndipo kuyamba kugwiritsa ntchito zimene zili zoona m’nkhanizo akamaganiza. Kwinaku, maganizo ake amaona kuopsa kwa nkhani zimene zili zotsutsana kotheratu ndi mfundo zozikidwa m’Baibulo zimene iye amatsatira.

Gwiritsani ntchito kuzindikira: Kuzindikira ndi “luntha la kuweruza.” Ndi “mphamvu kapena luso limene maganizo amasiyanitsira zinthu.” Munthu wozindikira amatha kuona kusiyana kobisika zedi kwa malingaliro kapena zinthu ndipo amaweruza bwino.

Pogwiritsa ntchito kuzindikira, tidzatha kutulukira anthu amene akungogwiritsa ntchito “mawu osalaza ndi osyasyalika” pofuna kuti ‘asocheretse mitima ya osalakwa.’ (Aroma 16:18) Kuzindikira kumakutheketsani kusiya mfundo zosafunikira kapena mfundo zosocheretsa ndi kuona imene ili mfundo yeniyeni m’nkhaniyo. Koma kodi mungazindikire bwanji nkhani ikakhala yosocheretsa?

Yesani Mawuwo: Yohane, amene anali mphunzitsi wachikristu m’zaka za zana loyamba anati: “Okondedwa, musamakhulupirira mawu ouziridwa alionse, koma yesani mawu ouziridwawo.” (1 Yohane 4:1, NW) Anthu ena lero ali ngati zinkhupule; amangomwa chilichonse chimene akhudzana nacho. N’kwapafupi zedi kuvomereza zilizonse zomwe timazimva kaŵirikaŵiri.

Koma ndi bwino kwambiri kuti aliyense payekha azisankha zimene akufuna kuti ziziloŵa m’maganizo mwake. Pali mawu akuti zakudya zathu zimakhudza moyo wathu, ndipo mawuŵa angatanthauze chakudya cha thupi ndiponso maganizo. Chilichonse chimene mukuŵerenga kaya kuonera kapena kumvetsera, chiyeseni ngati chili chabodza kapena ngati chili choona.

Kuphatikizanso apo, ngati tikufuna kuganiza moyenera, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuwayesabe maganizo athu tikamamva zinthu zatsopano. Tiyenera kuzindikira kuti kwenikweni, iwo ndi malingaliro chabe. Angakhale odalirika kokha ngati tili ndi mfundo zotsimikizirika, timalingalira bwino, ndiponso ngati miyezo imene timasankha kugwiritsa ntchito ili yoyenera.

Funsani mafunso: Monga taonera, pali ambiri lerolino amene angakonde ‘kutisokeretsa ndi mawu okopa.’ (Akolose 2:4) Choncho, tikauzidwa mfundo zokopa, tiyenera kufunsa mafunso.

Choyamba, onani ngati pali kukondera. Kodi cholinga cha uthengawo n’chiyani? Ngati uthengawo uli ndi mayina amwano ndiponso ngati uli ndi mawu onyoza, mudzifunse kuti n’chifukwa chiyani uli wotero? Ngakhale titaiwalako kaye za mawu onyozawo, kodi uthengawo paokha n’ngwokhutiritsa motani? Chinanso, ngati n’kotheka, yesani kuona ngati oyankhulawo ali ndi mbiri yabwino. Kodi n’ngodziŵika kuti amanena zoona? Ngati atchulapo “maumboni,” kodi n’ndani kapena ndi ati? Kodi n’chifukwa chiyani mukukhulupirira kuti munthu ameneyo kapena bungwe kapena chofalitsa chimenecho, zili ndi chidziŵitso cholondola kapena chodalirika pankhaniyo? Ngati mukuona kuti n’zotenga mtima, dzifunseni kuti, ‘Kodi uthengawo tikauganizira mosatengeka maganizo, uli ndi mfundo zanji zokhutiritsa?’

Osangotsatira Gulu: Ngati mwazindikira kuti zimene aliyense akukhulupirira si zoona, muli ndi ufulu woganiza mosiyana. Ngakhale zitaoneka kuti anthu ena onse akuganiza mofanana, kodi ndiye kuti inuyo muyeneranso kutero? Zimene ambiri akuganiza si ndizo muyezo wodziŵira choonadi. M’zaka zambiri m’mbuyomu ambiri avomerezapo malingaliro osiyanasiyana, koma pambuyo pake n’kudzazindikira kuti anali olakwa. Komatu, chikhumbo chochita zinthu m’chigulugulu chimakhalapobe. Lamulo loperekedwa pa Eksodo 23:2 n’lothandiza monga mfundo yabwino yachikhalidwe. Ilo limati: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.”

Kusiyana kwa Chidziŵitso Choona ndi Nkhani Zokopa

M’mbuyomu tatchula kuti Baibulo n’lotsimikizika potsogolera anthu kuganiza molongosoka. Mboni za Yehova zimavomereza ndi mtima wonse mawu a Yesu kwa Mulungu akuti: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Izi zili choncho chifukwa chakuti Mulungu, amene ali Mlembi Wamkulu wa Baibulo, ndi “Mulungu wa choonadi.”—Salmo 31:5.

Inde, m’nyengo ino ya nkhani zokopa zedi, tingadalire Mawu a Yehova kuti ndiwo tingapezemo choonadi. Potsiriza pake kutero kudzatiteteza kwa anthu amene amafuna ‘kutiyesa malonda ndi mawu onyenga.’—2 Petro 2:3.

[Chithunzi patsamba 17]

Kuzindikira kumakutheketsani kusiya mfundo zosafunikira kapena zosocheretsa

[Chithunzi patsamba 18]

Yesani chilichonse chimene mukuŵerenga kaya kuonera kapena kumvetsera, kuti muone ngati chili choona

[Chithunzi patsamba 19]

Zinthu zimene anthu ambiri amakhulupirira si kuti nthaŵi zonse zimakhala zodalirika

[Chithunzi patsamba 19]

Tingadalire Mawu a Mulungu kuti ndiwo tingapezemo choonadi