“Ndimakonda Mmene Imalongosolera Nkhani”
“Ndimakonda Mmene Imalongosolera Nkhani”
Izi n’zomwe ananena mnyamata wina wa m’boma la Yucatán, ku Mexico amene ali wothandiza mkulu wa zamalonda. Iye anali kunena za mmene Galamukani! imalongosolera nkhani. Analemba kalata imene analongosolamo kuti anadziŵa Galamukani! chifukwa cha mnzake wakuntchito amene ali wa Mboni. Iye ndi mnzakeyo akugwira ntchito limodzi pa kampani ya inshuwalansi.
Ponenapo za Galamukani! iye anati: “Imakhala ndi nkhani zenizenidi ndiponso choonadi. Ndimakonda mmene imalongosolera nkhani, chifukwa siichirikiza ndale za mtundu uliwonse ndipo siiona anthu ena kukhala ofunika kuposa ena. Ndapeza njira zothetsera mavuto poŵerenga magazini imeneyi. Iyi ndi magazini yosangalatsa, yolinganizidwa bwino, yosimba zimene zikuchitika panthaŵi yake, ndiponso yophunzitsa zinthu. Ndikukuthokozani kuchokera pansi pa mtima!”
Zaka za m’mboyomu Galamukani! inalongosola za kuthana ndi vuto la kumwalira kwa munthu amene mumakonda. Pambuyo pake nkhani zimenezo zinakonzedwanso n’kulembedwa m’bulosha yotchedwa Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. N’kutheka kuti inuyo kapenanso munthu wina amene mumam’dziŵa angalimbikitsidwe poŵerenga bulosha ya masamba 32 imeneyi. Mungathe kuiitanitsa polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi yosonyezedwapoyo kapena ku adiresi yoyenera pa madiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ino.
□ Munditumizire bulosha yakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.