Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Zokopa Zingaphetse Anthu

Nkhani Zokopa Zingaphetse Anthu

Nkhani Zokopa Zingaphetse Anthu

“Bodza lingathe kuyenda mtunda wautali zedi choonadi chisanayambe kulitsatira.”—Mawuŵa ananena ndi MARK TWAIN.

“MYUDA wopusa iwe!” anakalipa motero mphunzitsi wina wamkazi, uku akumenya pama mwana wake wasukulu wazaka zisanu ndi ziŵiri. Kenaka anauza ana onse m’kalasilo kuti akhale pamzere moyang’anizana naye n’kumamulavulira kumaso.

Mphunzitsiyo, yemwe anali azakhali a mnyamatayu, ankadziŵa bwinobwino kuti mnyamatayu, pamodzi ndi makolo ake sanali Ayuda, ndipo mwanayu naye ankadziŵa zimenezi. Ndiponso iwo sanali m’chipembedzo cha Chiyuda. Koma, iwo anali a Mboni za Yehova. Pakuti Ayuda anali anthu odedwa, mphunzitsiyu anapezerapo mwayi wosonkhezera ena kuda mwana wake wasukuluyu mwa kumutcha Myuda. Mphunzitsiyu ndiponso ana a m’kalasi lake anali kuuzidwa ndi wansembe wawo kwa zaka zambiri kuti a Mboni za Yehova n’zitsiru. Makolo a mnyamatayo anawatcha kuti anthu ochirikiza chipani cha Chikomyunizimu ndiponso kuti ndi akazitape a bungwe la CIA (Central Intelligence Agency). Motero ana a m’kalasi la mnyamatayo anandanda pamzere, pokonzekera kulavulira kumaso “Myuda wopusa” ameneyo.

Mnyamatayo anapulumuka n’kusimba nkhaniyo. Koma Ayuda mamiliyoni asanu ndi limodzi amene ankakhala m’dziko la Germany ndi mayiko ena oyandikana nalo zaka 60 zapitazo sanapulumuke. Nkhani zokopa zokokomeza ndizo zinaphetsa Ayuda amenewo m’zipinda za mpweya wa poizoni za Anazi komanso ku ukaidi. Kulikonse anthu ankadana koopsa ndi Ayuda. Unali udani woopsa ndiponso udani wopha nawo munthu ndipo unachititsa ambiri kuganiza kuti kupha Ayuda n’koyenera komanso n’kololeka. Apatu, nkhani zokopa anthu zinali njira yopululira anthu ambiri.

Inde, nkhani zokopa zingafalitsidwe poyera pogwiritsa ntchito zizindikiro zosonyeza chidani monga mtanda wotchedwa swastika kapenanso ponena nthabwala zonyoza. Nthaŵi zambiri kukopa kwa nkhanizi kumagwiritsidwa ntchito ndi olamulira ankhanza, andale, abusa, onenerera malonda, ogulitsa zinthu, atolankhani, aulutsi a pawailesi ndi a pa TV, ofalitsa nkhani, ndi anthu ena ofuna kusintha maganizo ndiponso zochita za anthu ena.

N’zoona, kuti mauthenga okopa angagwiritsidwe ntchito m’njira zothandiza anthu, monga pochita ndawala yolimbikitsa anthu kuchepetsa khalidwe loyendetsa galimoto atamwa moŵa. Komanso nkhani zokopa zingagwiritsidwe ntchito polimbikitsa anthu kuti adane ndi mafuko ndiponso zipembedzo zing’onozing’ono kapenanso pokopa anthu kuti azigula fodya. “Tsiku lililonse timauzidwa nkhani zambiri zokopa,” anatero ofufuza otchedwa Anthony Pratkanis ndi Elliot Aronson. “Nkhanizi sizitikopa mwa kutipatsa mfundo zokhutiritsa, koma mwa kugwiritsa ntchito zizindikiro komanso mwa kungotitenga mtima ndiponso maganizo. Kaya zibweretse zabwino kapena zoipa, mfundo n’njakuti tikukhala m’nthaŵi imene nkhani zokopa zikufalitsidwa.”

Kodi nkhani zokopa zagwiritsidwa ntchito motani posintha maganizo a anthu m’zaka zonsezi m’mbuyomu? Kodi mungatani kuti mudziteteze ku nkhani zokopa? Kodi pali kwina kumene kungapezeke nkhani zoti n’kuzikhulupirira? Mafunso aŵa ndi enanso ayankhidwa m’nkhani zotsatira.

[Chithunzi patsamba 11]

Chipani cha Nazi chinagwiritsa ntchito nkhani zokopa m’nyengo imene chinali kupulula Ayuda