Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoopsa za Kukwera Matola

Zoopsa za Kukwera Matola

Zoopsa za Kukwera Matola

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU AUSTRALIA

Tsiku lina m’nyengo yachilimwe dzuŵa likuswa mtengo m’chaka cha 1990, mnyamata wa zaka 24 wa ku Britain wotchedwa Paul Onions anali kuimitsa matola ataberekera katundu wake kumbuyo mumsewu waukulu wotchedwa Hume, kumwera kwa mzinda wa Sydney, ku Australia. Paul anakondwera pamene munthu wina wosam’dziŵa anaimitsa galimoto yake kuti amutenge. Iye sanadziŵe kuti kukwera galimotoyo pang’onong’ono kukanam’phetsa. *

POSAGANIZAKO za choopsa chilichonse, Paul anakhala kutsogolo kwa galimotoyo n’kumacheza ndi dalaivala. Pakutha kwa mphindi zingapo dalaivalayo amene anali kuoneka ngati wabwino anayamba zamtopola ndiponso zamkangano. Kenako mwadzidzidzi dalaivalayo anaimitsa galimotoyo ponena kuti akufuna kutenga matepi a nyimbo pansi pa mpando. Iye sanatulutse matepi, koma anatulutsa mfuti ndipo anam’loza nayo Paul pachifuwa.

Ponyalanyaza lamulo la dalaivalayo lakuti akhale pansi, Paul anamasula lamba wapampando pake mwamsanga ndi kudumphamo m’galimotoyo, ndipo analiyala liwiro lamtondo wadowoka kuloŵera kumtunda kwa msewuwo. Dalaivalayo analiyatsa liŵiro kum’thamangitsa uku anthu a m’magalimoto ena akuona. Potsirizira pake anam’peza, nam’gwira shati yake, ndi kum’gwetsa pansi. Paul anaphiriphitha n’kupulumuka, ndipo anayamba kuthamanga moyang’anizana ndi galimoto imene inkabwera kutsogolo kwake. Mayi amene anali kuyendetsa galimotoyo momwe ananyamulamo ana, anakakamizika kuima. Paul atam’chonderera kwambiri, mayiyo anam’lola kukwera m’galimotoyo, ndipo anapotoloka n’kuiyendetsa mothamangitsa zedi. Anadziŵa pambuyo pake kuti munthu amene anagwira Paul uja anali chigaŵenga ndipo anali ataphako kale alendo asanu ndi aŵiri oyenda atanyamula katundu wawo kumbuyo, ena a iwo anali kuimitsa matola ali aŵiriaŵiri.

Kodi n’chiyani chinachititsa kuti chigaŵenga chimenechi chipezerere anthu ameneŵa? Pamene anali kuchiyimba mlandu, woweruza anapeza kuti: “Ophedwawo onse anali ang’onoang’ono. Iwo anali apakati pa zaka za 19 ndi 22. Onse anali kuyenda ulendo wautali, kotero kuti chinachake chitawachitikira palibe amene akanaganizako mwamsanga zoti akusoŵa.”

Ufulu wa Kuyendayenda

Masiku ano anthu ambiri akutha kuyenda kupita kunja kusiyana ndi zaka zingapo zapitazo. Mwachitsanzo, m’zaka zisanu chabe, chiŵerengero cha anthu a ku Australia amene amapita ku Asia chaŵirikiza. Pofuna kukumana ndi zinthu zachilendo kapena pofuna kukaseŵera, achinyamata ambiri ndi ena aakulupo amakwera ndege zopita kumadera akutali kwambiri. Apaulendo ambiri otereŵa amakonzekera zokakwera matola kuti asakawononge ndalama zambiri. Tsoka ilo, m’mbali zambiri za dziko lapansi, ulendo woyenda pa matola si wosangalatsa ndiponso wotetezeka monga mmene unalili kale, kwa apaulendowo ngakhalenso kwa eni magalimotowo.

Kungoganizira chabe kuti zinthu zikayenda bwino sikungathandize koposa kuganiza kwanzeru kothandizadi. Buku lina lolembedwa kaamba ka mabanja amene akufunafuna ana awo amene anasoŵa limati, “Kufunitsitsa kupanga ulendo nthaŵi zambiri kumachititsa achinyamata kuyamba ulendo popanda kuukonzekera bwino ndiponso asanadziŵe bwino kuopsa kwake kapenanso zoyenera kuchita.”

Bukulo likupitiriza kunena kuti “anthu amene amayenda pamodzi ndi gulu loyendera malo lolinganizidwa bwino, ndiponso anthu amene amayendera zantchito, kapena anthu amene amakonzekera kupita kumalo enaake okha basi kaŵirikaŵiri sasoŵa. Kaya ndi ku Australia kapena ku dziko lina lililonse, anthu ambiri amene amadzakhala m’gulu la anthu osoŵa, zikuoneka kuti amakhala anthu amene amabereka katundu wawo n’kumakwera galimoto zotsika mtengo.”

Kaya mukwere matola kapena ayi, kuyenda nokha komanso kuyenda mwachisawawa, ngakhale kuti ena amaona kuti n’kwabwino chifukwa safuna kukhala womangika, kungapangitse kuti munthu achitidwe zachiŵembu mosavuta. Pamene achibale ndiponso mabwenzi sakudziŵa kumene wapaulendo ali, m’povuta kuti athandizepo kwambiri ngati patachitika chinthu mwadzidzidzi. Mwachitsanzo, kodi iwo angatani wapaulendo atapezeka kuti wakomoka kuchipatala ndipo palibe aliyense wa kwawo amene akudziŵa kumene ali?

Kudziŵitsana za Moyo

M’buku lake lochedwa Highway to Nowhere, mtolankhani wa ku Britain wotchedwa Richard Shears analemba za apaulendo asanu ndi aŵiri okwera matola amene “anangosiya mwadzidzidzi kuyankhulana ndi mabanja awo ndiponso anzawo.” N’zoona kuti poyamba mabanja sangakhale otsimikiza kuti kaya achibale awo asoŵa kapena kaya angoleka chabe kuwadziŵitsa za moyo wawo. Motero pamene sakumva chilichonse chokhudza apaulendo aja iwo angachite mphwayi kuti adziŵitse apolisi.

Wapaulendo wina wokwera matola nthaŵi zambiri ankalephera kumaliza kuyankhulana ndi makolo ake patelefoni ndalama zake zamakobiri zikatha. Atazindikira zimenezi, makolo ake analimbikitsa mabanja kuti azipatsa ana awo makadi oimbira telefoni kapena njira zina zoti azitha kuimbira telefoni kwawo. Ngakhale kuti zimenezi sizikanapulumutsa moyo wa mtsikanayu, kuyankhulana ndi makolo pafupipafupi nthaŵi zambiri kungathandize wapaulendoyo kupeŵa, kapena kungothana chabe, ndi mavuto aang’ono.

N’zotheka kuti apaulendo asanu ndi aŵiri oberekera katundu amene anataya miyoyo yawo aja anali ataŵerenga mabuku a apaulendo amene amatcha dziko la Australia kuti ndi limodzi mwa mayiko abata kwambiri padziko lapansi pankhani ya kukwera matola. Ngakhale zili choncho, kukwera matola kukuoneka kuti n’kusalingalira bwino, ngakhale mutakhala aŵiri ndiponso ngakhale mutakhala m’mayiko “abata” kwambiri. Kulingalira bwino n’kopindulitsa, peŵani zoopsa kuti mubwereko bwino ndiponso muli wosangalala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dziŵani kuti kumalo ena kukwera matola n’koletsedwa mwalamulo.

[Chithunzi patsamba 25]

Makolo angapeŵe kuda nkhaŵa mwa kupatsa ana awo makadi oimbira telefoni kapena njira zina zoti azitha kuimba telefoni kwawo