Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingakhale Wopambana Motani Pamene Ndikukhala Kudziko Lina?

Kodi Ndingakhale Wopambana Motani Pamene Ndikukhala Kudziko Lina?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingakhale Wopambana Motani Pamene Ndikukhala Kudziko Lina?

“Nditafika pa bwalo la ndege, chimene ndinkafuna kuchita ndi kubwerera kwathu basi! . . . Ndinalibenso chikhumbo chofuna kupita kutali ndipo ndinalibenso m’pang’ono pomwe chikhumbo chofuna kudziŵa zinthu. Kunena zoona ndinapukwa kwathu kuposa kalelonse.”—Uta.

NDI chinthu chochititsa mantha kukhala wekha kudziko lachilendo. Koma monga mmene inafotokozera nkhani yapita, m’nkhani zotsatizanazi, achinyamata ambiri akusankha kukakhalako kunja. Ena amapita kukachita maphunziro akusukulu kapena kukachita maphunziro antchito. Ena amafuna kukaphunzira chinenero. Ena amangofuna kukapeza ndalama. Komanso ena amasamuka kuti akatumikire ku mayiko akunja kumene kukufunikira alaliki a Ufumu.

Tingoyerekeza kuti mukukakhala kunja pazifukwa zomveka bwino, zifukwa zofunika poganizira zolinga zanu zauzimu, * kodi mungachitenji kuti mukakhaleko bwino?

Khalani Wofunitsitsa Kusintha

Choyamba muyenera kukhala wofunitsitsa kusintha. Si kuti muyenera kusiya kutsatira mfundo za chikhalidwe zachikristu kapena kutsatira chizoloŵezi chanu cha zinthu zauzimu. Koma ndiye kuti muyenera kuzoloŵera kudya zakudya zatsopano, kuphunzira kuchita ulemu m’njira ina, kapenanso kuchita zinthu m’njira yatsopano. Zinthu zatsopano zimenezi zingakhale zosiyana kwambiri ndi zimene mumachita kwanu. Koma lamulo la Yesu lakuti “musaweruze” lingagwire ntchito pamenepa. (Mateyu 7:1) Ndithudi, palibe chikhalidwe kapena mtundu umene uli ndi ufulu wonena kuti n’ngwoposa zina. (Machitidwe 17:26) Monga momwe anthu achikulire sayenera kuyerekezera achinyamata am’mbuyomo ndi amasiku ano m’njira yonyoza, chotero achinyamatanso akakhala kunja ayenera kupeŵa kuyerekezera dziko lachilendolo ndi lakwawo m’njira yonyoza. (Mlaliki 7:10) Ganizirani za zinthu zabwino za m’dziko lachilendolo ndiponso za chikhalidwe chake. Ndiponso, mukaphunzira mofulumira chinenero cha dzikolo, mudzazoloŵera mofulumira.

Mtumwi Paulo anali kuzoloŵera bwinobwino zikhalidwe zachilendo mu ntchito yake ya umishonale chifukwa anali wofunitsitsa kukhala “zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22) Mzimu wofananawo ungakuthandizeni kuzoloŵera. Adrianne ndi mtsikana wosamukira ku dziko lina pofuna kukaphunzirako chiyankhulidwe ndipo akukhala ku Germany, ndipo amagwirira ntchito banja lina kuti azipeza malo ogona ndi chakudya. Iye anafotokoza kuti: “Ndimalolera kusintha chifukwa chakuti sindingayembekezere ena kuti andizoloŵere.”

‘Ndapukwa Kumudzi!’

M’milungu ingapo yoyambirira, si chachilendo kukhala ndi chisoni ndiponso kupukwa kumudzi. Baibulo limasonyeza kuti Yakobo ‘mtima wake unali kukhumba nyumba ya atate wake,’ ngakhale kuti Yakoboyu anali atakhala ku dziko lakunja kwa zaka 20! (Genesis 31:30) Chotero musadabwe ngati nthaŵi zina mumangozindikira kuti mukulira. Ndithudi, kumangoganizira zimene munasiya kwanu, kungangokulitsa chisoni chanu. (Numeri 11:4, 5) Njira yabwino yothetsera chisonicho ndiyo kuyesetsa kuzoloŵerana ndi zinthu zimene tsopano muzichita tsiku ndi tsiku ndiponso kuzoloŵerana ndi malo achilendowo. Ngakhale kuti n’kwabwino kudziŵitsana za moyo ndi banja lanu polemberana makalata kapena poyimba telefoni, kuyimba matelefoni kwambiri kumudzi kwanu kungakulepheretseni kuzoloŵera malo atsopanowo.

Achinyamata ambiri achikristu amadziŵa kuti kuyambiranso chizoloŵezi chawo chachikristu ndiyo njira yabwino yothetsera kupukwa. (Afilipi 3:16) Pokumbukira mmene zinthu zinalili m’milungu yoyamba ali kunja Amber anati: “Ndinkapukwa kwambiri makamaka madzulo, pamene ndimakhala ndilibe chochita, kotero ndinaganiza zomaphunzira mowonjezereka kapena kuŵerenga mabuku.” Rachel, mtsikana wa ku Britain wosamukira ku Germany pofuna kukaphunzirako chiyankhulidwe, anafotokoza zimene anakumana nazo polangiza kuti: “Zoloŵeranani ndi mpingo mukangofika. Yambani kuchita nawo misonkhano mwamsanga.” Poyambirira mungafune chithandizo kuti muzipezeka kumisonkhano. Koma m’kati mwa mpingo wachikristu mungapeze anzanu enieni amene angakhale “abale, ndi alongo, ndi amayi.”—Marko 10:29, 30.

Kuchita nawo ntchito yachikristu yolalikira ndi mbalinso yofunika ya chizoloŵezi chauzimu. Kulalikira sikudzapindulitsa inu nokha mwauzimu komanso kudzakuthandizani kuzoloŵerana ndi chikhalidwe ndiponso chinenero chakumaloko.

Pomaliza, khalani ndi chizoloŵezi chopemphera ndi kuchita phunziro laumwini. Zimathandiza kuti mukhale wathanzi mwauzimu. (Aroma 12:12; 1 Timoteo 4:15) N’chifukwa chake, Adrianne, amene tamutchula poyamba uja, anaonetsetsa kuti watenga mabuku a Baibulo a chinenero chakwawo.

Kukhala ndi Banja Lokusungani

Achinyamata ena achikristu akonza kuti azikhala ndi mabanja okhulupirira pamene akukhala kunja. Ngakhale kuti a m’banja lokusungani safunikira kukhala ndi ntchito yokulerani, angakhale mabwenzi enieni ndiponso gwero la chilimbikitso mwauzimu.—Miyambo 27:17.

Ngakhale zili choncho, kukambirana momasuka ndi banja lokusunganilo n’kofunika kuti mukhale ndi unansi wabwino. (Miyambo 15:22; 20:5; 25:11) Amber anati: “Muyenera kukhala ndi ndandanda ya zimene muyenera kukachita. Muyeneranso kudziŵa zimene okusunganiwo akuyembekezera. Nawonso ayenera kudziŵa zimene inu mukuyembekezera.” Dziŵani malamulo a banjalo ndiponso ntchito zapakhomo zimene akuyembekezera kuti muzigwira. Nkhani zotere muyenera kukambirana mwatsatanetsatane.

Mkhalidwe wanu udzakhala wovuta makamaka ngati, mwachitsanzo, banja limene mukuligwirira ntchito lili ndi chikhulupiriro chosiyana ndi chanu. Chifukwa chakuti banjalo silingamvetse kuti ndinu wotsimikiza kutsatira mfundo zachikhalidwe za Baibulo, mungangozindikira kuti muli m’vuto lokuchititsani kugonjera. (Miyambo 13:20) Chifukwa cha kutanganidwa ndi ntchito zapakhomo mungayambe kulephera kukwaniritsa udindo wanu wauzimu, monga misonkhano yachikristu. Choncho ngati mikhalidwe yosapeŵeka ikukakamizani kuti mukhale ndi banja limene lilibe chikhulupiriro chofanana ndi chanu, ndiyetu muyenera kusamala zinthu zingapo.

Rachel, amene ali mtsikana wa ku Britain wogwira ntchito zapakhomo ku Germany kuti aphunzireko chiyankhulidwe, anati: “Adziŵitseni kuti ndinu Mkristu. N’kwabwino kuwadziŵitsa pachiyambi.” Kufotokoza mfundo zanu za chipembedzo ndi makhalidwe abwino kungakuthandizeni kukhala wotetezeka. Komanso, muwadziŵitse bwinobwino abwana anu mmene misonkhano yachikristu ndi ulaliki zilili zofunika kwa inu. Pomaliza, n’kwanzeru kutsimikiza musanayambe ntchito kuti zinthu zofunika monga maola ogwira ntchito, nthaŵi yopuma ndi malipiro zachita kulembedwa. Zimenezi zingakuthandizeni kupeŵa kukhumudwa patsogolo.

Kuthetsa Mavuto

Ngakhale mutayesetsa motani, mavuto adzakhalapobe. Mwachitsanzo, bwanji ngati okusungani atanena kuti muchoke panyumba pawo? Zoterezi zingakusokonezeni maganizo kwambiri. Ngati patakhala kusagwirizana kulikonse, mungayese kukambirana vutolo ndi okusunganiwo mofatsa ndiponso moyenerera. (Miyambo 15:1) Khalani wofunitsitsa kuvomera kulakwa kulikonse kumene mungakhale mutachita. Mwina angasinthe maganizo awo. Ngati sizili tero, muyenera kupeza malo ena okhala.

Mavuto ena angafune kuti mufunse chithandizo kwa anthu ena. Mwachitsanzo, mungakhale ndi vuto la ndalama kapena kudwala. Poopa kuti makolo anu angabwere kudzakutengani, mungaope kuwadziŵitsa zimene zikuchitika. Kuwonjezera apo, iwo ali kutali kwambiri ndipo sangadziŵe mmene angathetsere vuto lamtundu wotere kudziko lachilendo. Komabe akulu akumpingo wakumaloko angakhale ndi chidziŵitso cha momwe angathetsere mavuto amtundu umenewo komanso angapereke malangizo othandiza. Angathenso kukuthandizani kuona ngati vutolo likufunikira kuti makolo anu alidziŵe.

Kubwerera Kumudzi

Ngakhale patakhala zovuta ndi zothetsa nzeru, kukhala kunja kungakhale kopindulitsa, makamaka ngati mwapitako pazifukwa zauzimu. N’zoona kuti padzakhala nthaŵi imene mudzayenera kubwerera kumudzi. Andreas anati: “Chifukwa chakuti panali zinthu zabwino zambiri zimene ndinali kuzikumbukira, zinthu zoipa zinaiŵalika mwamsanga choncho ndinavutika maganizo pamene ndinali kubwerera kwathu.” Ngakhale zitero, musayembekezere kuti anzanu kapena banja lanu kumudzi likasintha kachitidwe kawo ka zinthu mukakangofika chifukwa chakuti mwabwera ndi nzeru zatsopano zimene mwaphunzira kunjako. Kuwonjezera pa zimenezi, si bwinonso kuti muwakhumudwitse powauza mobwerezabwereza mmene anthu amachitira zinthu kunja. Mwachibadwa, mumafuna kuuza aliyense zimene munakaona, koma musakhumudwe ngati ena sakuchita nazo chidwi nkhani zanuzo.

Ndiyetu m’pomveka kuti, kusankha kukakhala kunja ndi nkhani yofunika kuilingalira mosamalitsa. Ngati mwakambirana ndi makolo anu ndiye mwaona kuti pali zifukwa zomveka zoti musamukire, khalani wokonzeka kukathana ndi mavuto amene mungakakumane nawo. Mofanana ndi kusankha kuchita chinthu chilichonse chachikulu m’moyo, n’kwanzeru kuŵerengera mtengo wake poyamba.—Luka 14:28-30.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . “Kodi Ndisamukire Kudziko Lina?” mu Galamukani! wa July 8, 2000.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Malangizo Odzitetezera

● Sungani pasipoti yanu, ndalama zanu ndi tikiti yanu yobwererera kwanu pamalo otetezeka.

● Pangani fotokope pasipoti yanu komanso chilolezo choloŵera m’dziko ndi/kapena viza, tikiti yobwererera ndi mapepala ena ofunika. Sungani mapepala ena a mafotokope ameneŵa, ndipo tumizani ena kwa makolo anu kapena abwenzi anu kumudzi.

● Nthaŵi zonse khalani ndi manambala atelefoni a makolo anu kapena abwenzi anu kumudzi ndi abanja limene likukusungani.

● Dzisungireni khalidwe ndi osiyana nawo ziŵalo, kaya kukhale ku banja lokusunganilo, kusukulu, kuntchito kapenanso malo ena aliwonse.

● Phunzirani mawu ena ofunika ndi ziganizo zina m’chinenero cha dziko limene mukukhala.

● Kayesedweni ku chipatala musananyamuke. Tsimikizirani kuti mankhwala alionse ofunikira muli nawo okwanira.

[Chithunzi patsamba 10]

Ngati pakhala kusagwirizana ndi banja lokusunganilo, kambiranani mofatsa