Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufulu Wokulirapo wa Chikumbumtima Udzaperekedwa M’Mexico?

Kodi Ufulu Wokulirapo wa Chikumbumtima Udzaperekedwa M’Mexico?

Kodi Ufulu Wokulirapo wa Chikumbumtima Udzaperekedwa M’Mexico?

YOLEMBEDWA NDI M’TOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU MEXICO

UFULU wa kupembedza ku Mexico uli wovomerezedwa ndi lamulo. Ngakhale zili choncho, lamulo lili ndi zoletsa zina pa ufulu wa kulambira. Mwachitsanzo, ufulu wokana kugwira ntchito ya zankhondo chifukwa cha chikumbumtima cha munthu n’ngwachilendo m’dzikoli. N’chifukwa chake Bungwe Lofufuza za Malamulo, la National Autonomous University of Mexico (UNAM), linaganiza zoitanitsa msonkhano wa mayiko onse wa mutu wakuti “Ufulu wa Kukana mwa Chikumbumtima mu Mexico ndi pa Dziko Lonse.” Bungwe Lofufuza za Malamulo la UNAM lili m’manja mwa boma, koma cholinga chake ndi kufufuza malamulo okhazikitsidwa ndi mmene amagwirira ntchito. Mboni za Yehova ku Mexico anazipempha kuti zitumize nthumwi yawo yoti ikalankhule pa mutu wakuti “Mboni za Yehova ndi Ufulu wa Kukana mwa Chikumbumtima.”

Mapulofesa Alankhula Zakukhosi

Nkhani yakuti “Kukana mwa Chikumbumtima mu Lamulo la Padziko Lonse,” yokambidwa ndi Dr Javier Martínez Torrón, pulofesa wa pa Granada University of Law, ku Spain, anatchulapo kuti ufulu wa chikumbumtima wokana kutsata malamulo ena kapena maudindo, uli wovomerezeka kale m’mayiko ambiri. Anatchulapo za mkhalidwe wa Mboni za Yehova mu Spain ndi nkhani ya Kokkinakis mu Greece. *

Dr José Luis Soberanes Fernández, pulofesa wa Bungwe Lofufuza za Malamulo la UNAM, analakhula pa mutu wakuti “Mmene Mexico Wachitira pa Nkhaniyi.” “Tiyenera kutchula kuti Lamulo la Mexico pa Magulu a Chipembedzo ndi Kulambira Poyera limaletsa ufulu wokana chinthu mwa chikumbumtima,” anatero, ponena za Mfundo Yoyamba ya lamulo. “M’chochitika chilichonse, chikhulupiriro cha chipembedzo sichingapatule aliyense kuti asatsate malamulo a dzikoli. Aliyense sadzatha kupereka zifukwa za chipembedzo kuti apeŵe udindo ndi ntchito zoperekedwa ndi lamulo.” Pomalizira, Dr Soberanes anati: “Tikhulupirira kuti n’kofunikira kukhazikitsa msanga lamulo m’Mexico pankhani ya kukana mwa chikumbumtima kuchita zinthu zina.”

Anali kunena za mkhalidwe wa ana a Mboni m’Mexico amene chaka chilichonse mazana a iwo amakumana ndi mavuto okhudzana ndi maphunziro awo pokana kupereka sawatcha ku mbendera pachifukwa cha m’Baibulo. Ana ena a Mboni saloledwa ngakhale kulembetsa sukulu. Komabe, mwa kuchita apilo kudzera ku Bungwe loona za Ufulu Wachibadwidwe, ambiri awalolezanso ufulu wawo wa kuphunzira. Ena mwa akuluakulu azamaphunziro akhala akuyesetsa kuteteza ana kuti asamachotsedwe sukulu, koma aphunzitsi ena salimbikitsa zimenezo. Akuluakulu a boma akhala ololera pa kachitidwe ka Mboni, komatu palibe lamulo lolembedwa loti sukulu za ku Mexico zikhoza kutsata.

Msonkhanowu unakhudzanso zinthu zina zokana mwa chikumbumtima zimene zinaperekedwa ndi zipembedzo zina, monga ngati kuumirizidwa kugwira ntchito masiku opatulika kwa iwo, kuuzidwa kuvala zovala za ntchito zimene zimatsutsana ndi zikhulupiriro za chipembedzo chawo, ndi zina zotero. Anakambirananso za kukana ntchito ya zankhondo ndi mitundu ina ya chithandizo cha mankhwala.

Mboni za Yehova ndi Kaisara

Nthumwi ya ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova mu Mexico inakamba nkhani yake yachidule yofotokoza zikhulupiriro zazikulu za Mboni za Yehova. Inafotokoza za kutsatira kwawo malangizo a Baibulo ngati limene laperekedwa pa Luka 20:25, limene limauza Akristu kuti “perekani kwa Kaisara zake za Kaisara.” Nthumwiyo inanenanso za Aroma 13:1 amene amati Akristu ayenera kulemekeza olamulira a dziko. Inanenetsa kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino, ndi nzika zomvera malamulo zomwe zimayesetsa kulipira msonkho, zimakhala ndi moyo wadongosolo, ndiponso zimatumiza ana awo kusukulu.

Ndiye nthumwiyo inapereka chifukwa cha m’Malemba chimene ana a Mboni amakanira kupereka sawatcha ku mbendera, chimene chimapezeka pa Malamulo Khumi, pa Eksodo 20:3-5 chakuti: “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo.”

Mboni za Yehova zimalambira Mulungu yekha, ndipo sizilambira mafano konse. Ngakhale zili choncho, sizidzasonyeza mkhalidwe uliwonse wonyoza chizindikiro cha dziko kapena kulankhula mawu ochinyoza.

Pofuna kugogomeza kaonedwe ka Mboni za Yehova pa nkhani imeneyi, anaonetsa vidiyo yotchedwa Purple Triangles. Vidiyo imeneyi imaonetsa mmene Mboni za Yehova zinalimbikira osasunthika mu ulamuliro wa Germany wolamulidwa ndi Nazi (1933-45). Imafotokoza nkhani ya banja la a Kusserow, lomwe linaima mosasunthika pachikhulupiriro chawo m’nthaŵi ya ulamuliro wa boma la chipani cha Nazi. *

Chifukwa cha m’Malemba chimene Mboni za Yehova zimakanira kuikidwa magazi chinaperekedwa. (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 15:28, 29) Analongosolanso dongosolo la Makomiti Olankhulana ndi Chipatala a padziko lonse. Kuwonjezera pa zimenezo, anasimbanso kupambana kumene madokotala a kufuna kwabwino akhala nako popanga maopaleshoni osagwiritsa ntchito magazi pa Mboni za Yehova.

Tsiku lililonse anthu pafupifupi 100 anabwera kumsonkhano umenewu, ndipo ambiri anali maloya. Oimira Ofesi ya Zipembedzo mu Mexico analipo pa chochitikachi. Onse opezekapo anali ndi mwayi womvetsera malingaliro a akatswiri, ponena za kulemekeza ufulu wa kukana zinthu mwa chikumbumtima. Lingaliro limeneli ndi latsopano kwa opanga malamulo ku Mexico, ngakhale kuti lili lofala ndi lovomerezeka m’mayiko ambiri a demokalase ngati France, Portugal, Spain, ndi United States ngakhalenso m’mayiko amene kale anali a Komyunizimu ngati Czechia, ndi Slovakia.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Bwalo Lamilandu Lalikulu la Ulaya Lichilikiza Kuyenera kwa Kulalikira M’Greece” ndi yakuti “Kuteteza Uthenga Wabwino Mwalamulo” mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1993, ndi ya December 1, 1998.

^ ndime 13 Onaninso Nsanja ya Olonda ya February 15, 1986 pa mutu wakuti, “Kukonda Mulungu kwa Banja Langa Mosasamala Kanthu za Ndende ndi Imfa.” Onaninso kope la January 15, 1994, tsamba 5.

[Chithunzi patsamba 13]

Mboni za Yehova mu Mexico zikuyamikira ufulu wawo wolalikira