Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudzikongoletsa—Kufunika kwa Kusamala

Kudzikongoletsa—Kufunika kwa Kusamala

Lingaliro la Baibulo

Kudzikongoletsa—Kufunika kwa Kusamala

“KUDZITUKUMULA chifukwa cha kuoneka bwino kungam’lepheretse munthu kulingalira mwanzeru,” analemba motero Mfalansa wina wolemba mabuku. Ndithudi, kulingalira mwanzeru sikunasonkhezere kwenikweni zinthu zambiri zomwe anthu adzichitira kwa zaka zambiri zapitazo chifukwa cha kudzitukumula mopambanitsa polingalira kuti n’ngooneka bwino. Mwachitsanzo, poyesayesa kuti akhale ndi chiuno choning’a kwambiri, akazi a m’zaka za m’ma 1800 anali kuvala zovala zam’kati zokhala ndi lamba wamkulu, wothina kwambiri pamimba pawo kotero kuti anali kupuma movutikira. Ena ankadzinenera kuti ali ndi chiuno choning’a kwambiri pafupifupi mamilimita 325. Akazi ena anali kuthinitsa kwambiri chilamba chawocho kotero kuti nthiti zawo zinali kukankhidwira m’chiŵindi chawo, ndipo anali kumwalira.

N’zosangalatsa kuti sitayelo imeneyo ya kavalidwe inatha, komabe kudzigomera chifukwa cha kuoneka bwino komwe kunayambitsa sitayelo imeneyo n’nkofalanso lerolino monga momwe kunalili nthaŵiyo. Amuna ndi akazi amachita zinthu zovuta ndi zoopsa kuti asinthe kaonekedwe kawo kachibadwa. Mwachitsanzo, malo ojambulira zinthu zodzikongoletsera pakhungu ndi kuboola ziwalo, omwe kale kunkangopita magulu a anthu amikhalidwe yopanda pake okha, akungotsegulidwa m’malo azamalonda ndi m’milaga nthaŵi ina iliyonse. Kwenikweni, m’zaka zaposachedwapa, kutema mphini zokongoletsa thupi inali bizinesi ya chisanu ndi chimodzi mwa mabizinesi opita patsogolo mofulumira zedi ku United States.

Njira zachilendo zokongoletsera thupi nazonso zikuwonjezereka, makamaka pakati pa achinyamata. Kuboola ziwalo zathupi monyanyira—monga nsonga za maŵere, mphuno, malilime, ngakhalenso mpheto—kwafala mowonjezereka kwambiri. Kwa anthu ena ochepa, kuboola ziwalo monyanyira kumeneko sikumawasangalatsa mokwanira. Akuyesa njira zina zomkitsa monga kudzidinda chizindikiro ndi chidindo chamoto, kudzicheka mochititsa mantha, * ndi kudzisema thupi ndi chinthu chomwe chimaloŵa m’khungu ndi kupanga ziboo ndi mizera ikuluikulu.

Chizoloŵezi Chakalekale

Kukongoletsa kapena kusintha maonekedwe a thupi si kwachilendo. M’mbali zina za Africa, kudzikongoletsa ndi zipsera ndi kudzitema mphini kwagwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri monga chizindikiro cha mitundu kapena mafuko. Chochititsa chidwi n’chakuti, m’madera ambiri mwa ameneŵa, miyambo imeneyi anthu anayamba kudana nayo ndipo ikumka ichepa.

Kutema mphini, kuboola ziwalo, ndi kudzicheka kunalinso kuchitika m’nthaŵi za m’Baibulo. Kaŵirikaŵiri mitundu yakunja n’njomwe inkachita zimenezi mogwirizana ndi zipembedzo zawo. M’pomveka kuti Yehova analetsa anthu ake, Ayuda, kutsanzira akunja amenewo. (Levitiko 19:28) Monga “mtundu wa anthu wa pa wokha [“wapadera” NW]” wa Mulungu, Ayuda anali otetezereka ku zochita zoyaluka za zipembedzo zonyenga.—Deuteronomo 14:2.

Ufulu Wachikristu

N’zoona kuti Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose, ngakhale kuti chilamulochi chimapereka mfundo zinazake zachikhalidwe zomwe zimagwiritsidwa ntchito mu mpingo wachikristu. (Akolose 2:14) Chotero angasankhe okha zodzikongoletsera zimene angafune kuvala koma mosatailira. (Agalatiya 5:1; 1 Timoteo 2:9, 10) Komatu, ufulu umenewu uli ndi malire.—1 Petro 2:16.

Paulo, pa 1 Akorinto 6:12 analemba kuti: “Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula.” Paulo anadziŵa kuti ufulu wake monga Mkristu sunam’patse chilolezo chochitira chilichonse chimene anali kufuna popanda kulingalira za ena. Kukonda ena kunasonkhezera khalidwe lake. (Agalatiya 5:13) Iye analimbikitsa kuti: “Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Malingaliro ake osadzikondawo ali chitsanzo chabwino kwambiri kwa Mkristu aliyense amene akulingalira zokongoletsa thupi m’njira ina iliyonse.

Mfundo za M’Baibulo Zoyenera Kuzilingalira

Imodzi mwa ntchito zomwe Akristu anapatsidwa ndiyo kulalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino. (Mateyu 28:19, 20; Afilipi 2:15) Mkristu sangafune kuti china chilichonse, kuphatikizapo kaonekedwe kake, kachotse chidwi mwa ena chakuti amvetsere uthenga umenewo. (2 Akorinto 4:2)

Ngakhale kuti kudzikongoletsa kotereku monga kuboola thupi kapena kutema mphini kungakhale kofala kwambiri pakati pa anthu ena, Mkristu ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi kudzikongoletsa kumeneku angakuone motani anthu a ku dera lomwe ndikukhala? Kodi adzandiika m’gulu linalake mwa timagulu tochita zinthu zosadziŵika bwino? Ngakhale chikumbumtima changa chitalola, kodi ngati n’tadziboola thupi kapena kudzitema mphini zingakhudze motani anthu ena mumpingo? Kodi iwo angaone zimenezi monga chinthu chosonyeza “mzimu wa dziko lapansi”? Kapena kodi zingakayikitse anthu kuti ndine “[w]odziletsa”?’—1 Akorinto 2:12; 10:29-32; Tito 2:12.

Mitundu ina ya kusintha kaonekedwe ka thupi ingadzetse matenda aakulu. Kujambula zithunzi pakhungu ndi nsingano zosasamalidwa bwino akuti kungafalitse matenda a kutupa chiŵindi ndi HIV. Kuwonongeka kwa khungu nthaŵi zina kumachitika chifukwa cha utoto womwe umagwiritsidwa ntchito. Zilonda za ziwalo zobooledwazo zingatenge miyezi yochuluka kuti zipole ndipo nthaŵi yonseyi zingakhale zikupweteka kwambiri. Zingathenso kuwononga magazi, kuyambitsa matenda a kukha magazi, kuundana kwa magazi, kuwonongeka kwa mitsempha, ndi matenda enanso oopsa. Komanso, zinthu zina zikachitika zimavuta kwambiri kuzisintha. Mwachitsanzo, malinga ndi kukula ndi mtundu wake, kuchotsa chojambula pa khungu kungafune maopaleshoni angapo ndiponso opweteka. Kuboola ziwalo kungasiye zipsera zomwe sizingachoke kwa moyo wanu wonse.

Kulolera kapena kukana kukumana ndi mavuto ngati ameneŵa, n’kufuna kwa munthu. Koma munthu amene amafuna kukondweretsa Mulungu amazindikira kuti kukhala Mkristu kumaphatikizapo kudzipereka kwa Mulungu. Matupi athu ndiwo nsembe zamoyo zoperekedwa kwa Mulungu kuti azigwiritse ntchito. (Aroma 12:1) Choncho, Akristu okhwima samaona matupi awo monga awoawo omwe angathe kuwawononga kapena kuwasintha maonekedwe mmene akufunira. Amene ali oyenerera kutsogolera mumpingo kwenikweni ndiwo amene amadziŵika chifukwa cha kudzisunga, kudziletsa, ndi kufatsa kwawo.—1 Timoteo 3:2, 3.

Kukulitsa ndi kugwiritsa ntchito mphamvu ya kulingalira imene anaphunzira m’Baibulo kudzathandiza Akristu kupeŵa kuchita zinthu mopambanitsa, mikhalidwe yosangalatsa koma yopweteka imene ili m’dzikoli, limene mopanda chiyembekezo chilichonse, lili ‘loyesedwa lachilendo pa moyo wa Mulungu.’ (Aefeso 4:18) Potero angachititse kufatsa kwawo kuzindikirika kwa anthu onse.—Afilipi 4:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Pali kusiyana kooneka bwino lomwe pakati pa mphini zotemedwa ndi cholinga chopaka mankhwala kapenanso kudzikongoletsa ndi kudzicheka mochititsa nthumanzi kapena kudula ziwalo komwe achinyamata ambiri, makamaka asungwana osakwana zaka makumi aŵiri akuchita. Kudzitema kotereku nthaŵi zambiri kumakhala chizindikiro cha kupsinjika maganizo kapena kuchitiridwa nkhanza ndipo n’kofunika thandizo la madokotala.