Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwiritsa Ntchito Wailesi ya Kanema Mosamala Kwambiri

Kugwiritsa Ntchito Wailesi ya Kanema Mosamala Kwambiri

Kugwiritsa Ntchito Wailesi ya Kanema Mosamala Kwambiri

WAILESI ya kanema imagwira ntchito ngati “wokamba nkhani wamkulu, wolera mwana ndi wosonkhezera malingaliro a anthu,” linatero lipoti lotchedwa Not in the Public Interest—Local TV News in America (Nkhani Zosapindulitsa Anthu za m’ma TV a mu America) lolembedwa ndi gulu lina lopenda nkhani ku United States. “Ma TV ali ponseponse . . . Monga utsi wa fodya wosuta munthu wina, mawailesi akanema ali mu mpweya.” Ndipo monga momwe kupuma utsi wa fodya wosuta munthu wina kulili koopsa, chimodzimodzinso kuthera maola ambirimbiri mukuonerera mapulogalamu a pa TV osankhidwa mosasamala kuli ndi zotsatira zovulaza makamaka kwa ana.

Ponena za kuphana ndi ziwawa pa TV, lipoti limodzimodzilo linati “maphunziro ambirimbiri ofufuza zimenezi asonyeza kuti kuonerera zochitika kapena zithunzi zachiwawa kumaphunzitsa ana zinthu zoipa, zimawasonkhezera kukhala aukali ndi kuwapanga kukhala opanda chifundo.” M’chaka cha 1992, American Medical Association inanena kuti “ziwawa za pa wailesi yakanema n’zochitika zoopsa zomwe zikuopseza thanzi la achinyamata.”

Kodi mungatetezere motani ana anu kuti asakhudzidwe ndi mapulogalamu oipa a pa TV? Lipotilo linandandalika njira zina zothandiza kwambiri zotengedwa mu mfundo zovomerezedwa ndi mabungwe angapo a zaumoyo, za mmene munthu angagwiritsire ntchito wailesi ya kanema mosamala kwambiri. Zina mwa njirazo ndi izi.

▪ Sankhani nthaŵi ndi kuika malire a nthaŵi yanu yoonerera TV. Ikani lamulo pa nthaŵi yomwe ana anu ayenera kuonerera. Musaike TV m’chipinda cha ana.

▪ Ikani mapu adziko lonse pafupi ndi TV kuti anawo azitha kuona malo komwe pulogalamu akuonerayo ikuchitikira.

▪ Onererani TV limodzi ndi ana anu kuti muziwafotokozera zinthu zina monga kusiyana kwa zongoyerekezera ndi zochitika zenizeni. Ana ambiri osakwana zaka khumi nthaŵi zambiri sangathe kusiyanitsa zongoyerekezera ndi zochitika zenizeni.

▪ Ikani wailesi ya kanema pamalo ovuta kufikira m’nyumba mwanu. Ikani TV mu kabati yomwe mungakhoze kutseka. Kuika TV pa malo ovuta kuwafikira kudzapangitsa kukhala kovuta kutsekula ndi kusinthasintha matchanelo.