Kulera Ana Ophunzitsika Bwino—Motani?
Kulera Ana Ophunzitsika Bwino—Motani?
“Ana amaphunzira kudzilemekeza ndi kudziletsa mwa kulandira zonse ziŵiri, chikondi ndi chilango kuchokera kwa makolo,” linatero lipoti la m’nyuzipepala ya boma yotchedwa The Gazette, ku Montreal, ku Canada. Kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani? Malinga ndi katswiri wa zamaganizo woyang’anira odwala ku Montreal wotchedwa Constance Lalinec, ndi bwino kwambiri kuika malire odziŵika bwino pa khalidwe la mwana.
Lalinec, amene amagwira ntchito ndi ana ndi mabanja, ananenanso kuti “pamene timatchinjiriza ana ku zotsatira za machitidwe awo, timakhala tikuwalepheretsa kuphunzira zambiri.” Kulekerera mwana kungam’lepheretse kukula bwino.
Uphungu wanzeru womwe wakhala wothandiza polera ana kuyambira kalekale wochokera m’Baibulo uli woyenera kwambiri. Umati: “Manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi.” (Mateyu 5:37) Pamene malamulo oyenera akhazikitsidwa ndipo ana anu awamvetsa, agwiritseni ntchito mofulumira ndiponso musasinthesinthe. Mawu anu agwirizane ndi zochita zanu. Zimenezi zidzathandiza ana kuzindikira bwino lomwe malamulo a makolo ndi zimene amayembekezera kwa iwo—kuti anthu ‘adzatuta chimene achifesa.’ (Agalatiya 6:7; Aroma 2:6) Cholinga cholangira ana mwachikondi ndi mogwira mtima n’chakuti aphunzire kumvera malamulo ndi kupirira zopsinja ndi kuyembekezera zosangalatsa kotero kuti akulitse makhalidwe ofunika kuti akule bwino, kukhala achikulire audindo.
Malangizo enanso amene Mulungu amauza makolo onena za kulanga ana awo mwachikondi akupezeka m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Mungalandire buku la masamba 192 limeneli mwa kulemba zofunika pakapepala kali m’munsika ndi kukatumiza ku adiresi yosonyezedwayo, kapena ku adiresi yoyenera patsamba 5 la magazini ino.
□ Tanditumizirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Chonde ndipezeni kuti mundiuze za phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.