Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusagwirizana ndi Mankhwala Osiyanasiyana Matenda Ovuta Kuwamvetsa

Kusagwirizana ndi Mankhwala Osiyanasiyana Matenda Ovuta Kuwamvetsa

Kusagwirizana ndi Mankhwala Osiyanasiyana Matenda Ovuta Kuwamvetsa

Nyumba ya Pam inali m’dera lozunguliridwa ndi minda ya thonje. Kaŵirikaŵiri ndege zinkapopela mankhwala oletsa zomera ndiponso ophera tizilombo m’minda ya thonjeyo; ndipo nthaŵi zambiri mphepo inkauluzira mankhwalawo kunyumba zoyandikana ndi mindayo, kuphatikizanso kunyumba ya Pam.

PAM anayamba kumva kupweteka mutu kwambiri ndiponso kuchita nseru, ndiyeno anadwala kwambiri. M’kupita kwa nthaŵi, iye anayamba kusayanjidwa ndi zinthu zosakhudzana n’komwe ndi mankhwala ophera tizilombo. Zinthu monga mafuta onunkhira, mafuta opha fungo, mankhwala oyeretsera, utoto, kalipeti yatsopano, utsi wa fodya, mankhwala onunkhiritsa m’nyumba, ndiponso zinthu zina. Zizindikiro zomwe ankasonyeza Pam ndi zina mwa zizindikiro zimene zimachititsidwa ndi matenda odabwitsa ndiponso othetsa nzeru kwambiri otchedwa MCS (multiple chemical sinsitivity [kusagwirizana ndi mankhwala osiyanasiyana]). *

“Ndikakhudza mankhwala ogwiritsidwa ntchito tsiku ndi tsiku, ndimayamba kumva kukhala wotopa kwambiri komanso wosokonezeka maganizo, ndimachita chizungulire, komanso nseru,” Pam analongosolera atolankhani a Galamukani! “Ndimatupa, ndipo nthaŵi zina ndimapuma mofulumira kwambiri, ndimakhala ndi mantha aakulu komanso ndimalira mosatonthozeka, mtima umagunda kwambiri ndiponso mofulumira, ndipo m’mapapu mumadzala madzi. Zimenezi nthaŵi zina zandidwalitsapo chibayo.”

Ngakhale kuti zizindikiro za MCS zimasiyanasiyana m’matupi mwa anthu, komabe zingathe kukhala zinthu monga litsipa, kutopa kwambiri, kupweteka kwa minofu, kuphwanya kwa m’mfundo zathupi, dzikulukutu, zipere, zizindikiro zofanana ndi za chimfine, chifuwa cha mphumu, matenda a m’mphuno, nkhaŵa, kupsinjika maganizo, kuiŵalaiŵala, kusatha kuika mtima pa zinthu, kusoŵa tulo, kusagunda bwino kwa mtima, kutupa, kuchita nseru, kusanza, vuto la m’mimba, ndiponso kudwala kwa mwadzidzidzi. N’zoona kuti zambiri mwa zizindikirozi zingayambenso chifukwa cha matenda ena.

Matenda a MCS Ndi Vuto Lomwe Likuwonjezekabe

Ku United States, kufufuza kochitidwa pakati pa anthu a misinkhu yosiyanasiyana kunasonyeza kuti pakati pa anthu 15 mpaka 37 mwa anthu 100 aliwonse a m’dzikomo amaganiza kuti sagwirizana ndi mankhwala omwe amagwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri kapenanso fungo lake. Fungo limeneli ndi monga fungo la utsi wa galimoto, utsi wa fodya, utoto wopakidwa kumene, kalipeti yatsopano, ndi mafuta onunkhiritsa. Komabe, malinga ndi magulu a misinkhu yomwe yafufuzidwa, ndi 5 peresenti yokha kapena kucheperapo, amene anati akudwala MCS. Pafupifupi anthu atatu mwa anthu anayi alionse mwa anthu ameneŵa ndi akazi.

Anthu ambiri odwala MCS amanena kuti mankhwala ophera tizilombo ndiponso mankhwala ena amadzimadzi ndi amene anayambitsa vuto lawo. Zinthu zimenezi zimagwiritsidwa ntchito kwambiri kumene kuli anthu, makamaka mankhwala amadzimadzi. Mankhwala amadzimadzi amauluzika mwamsanga moti angathe kusungunula zinthu zina. Mankhwala ameneŵa ndiwo amene amasakaniza ndi zinthu zina popanga utoto, vanichi, zomatira, mankhwala ophera tizilombo, mankhwala oyeretsera m’nyumba.

M’nkhani zotsatirazi, tiona matenda a MCS mwatsatanetsatane, n’kufotokoza chithandizo chimene chilipo kwa anthu amene ali ndi vutoli. Tionanso mmene anthu amene akudwala ndiponso amene sakudwala matendaŵa angakhalire mogwirizana kuti anthu amene akudwala MCS azikhala mosangalala kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tagwiritsa ntchito dzina lakuti “multiple chemical sensitivity” chifukwa chakuti ndilo dzina lotchuka kwambiri. Koma palinso mayina ena ambiri, monga “environmental illness” ndi “chemical hypersensitivity syndrome.” Mawu onseŵa akutanthauza kuti anthu ena amakhudzidwa ndi mankhwala ngakhale mankhwalawo atakhala pamlingo woyenerera kwa anthu ambiri.