Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Anthu Odwala MCS

Kuthandiza Anthu Odwala MCS

Kuthandiza Anthu Odwala MCS

KUSAGWIRIZANA ndi zinthu zofala kwambiri, kaya ndi mafuta odzola onunkhira kapena mankhwala oyeretsera, sikungopereka vuto la matenda lokha kwa odwala; kumawapatsanso vuto la makhalidwe. Mwachibadwa anthu amakonda kuchezerana, koma vuto la kusagwirizana ndi mankhwala (MCS) limakakamiza anthu ambiri omwe mwinamwake ndi ochezeka, komanso okonda kusangalala kuti azikhala kwaokha. “Ndakhala ndikudwala matenda a mitundu ina m’mbuyomu,” anatero Shelly, wodwala MCS, “koma matenda aŵa n’ngoipa kuposa onsewo. Mbali yake yovuta kwambiri ndiyo kukhala pawekha.”

N’zomvetsa chisoni kuti nthaŵi zina anthu odwala MCS amaonedwa ngati anthu ovuta kuwamvetsa. N’zoona kuti chifukwa chimodzi chochititsa zimenezi n’chakuti MCS ndi nthenda yovuta kuimvetsa bwino ndipo dziko silinaizindikire bwino ndi kudziŵa bwino m’mene lingalimbanirane nayo. Komabe, kusadziŵa bwino matenda a MCS sichingakhale chifukwa chokhalira okayikira ndi anthu odwala nthendayi. Magazini yakuti American Family Physician inati: “Odwala ameneŵa akuvutikadi chifukwa cha zizindikiro za mphamvu ya matendaŵa zomwe amasonyeza.”

M’malo moona anthu odwala MCS ndi diso lonyodola chifukwa chakuti nthenda yawo n’njovuta kuimvetsa bwino, munthu wanzeru ayenera kutsatira mfundo yachikhalidwe yopezeka pa Miyambo 18:13 yakuti: “Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.” N’kofunikatu kwambiri kusonyeza chikondi chonga cha Kristu mopanda tsankho kwa onse amene akudwala! Sitidzakhumudwa ngakhale pang’ono pa chilichonse chimene sayansi ya mankhwala ingadzapeze m’tsogolomo, ngati tisonyeza chikondi cha mtundu umenewu.

Kusonyeza Chikondi Chonga cha Kristu

Chikondi chonga cha Kristu chili ngati mwala wa dayamondi wokhala ndi mbali zokongola kwambiri zoyenerana ndi nthaŵi iliyonse kapena vuto lililonse. Pamene mnzathu wadwala MCS, chikondi chathu chonga cha Kristu chiyenera kuonekera posonyeza chifundo, mwakudziyerekeza tokha tili mumkhalidwe wa munthu wodwalayo. Komanso, chikondi “sichitsata za mwiniyekha” kapena, tinganene kuti, zofuna za icho chokha. Chimatsogoza zofuna za ena. Chimatithandiza kukhala ‘oleza mtima, kukwirira zinthu zonse, kukhulupirira zinthu zonse, ndiponso kupirira zinthu zonse.’ Chikondi chotero “sichitha nthaŵi zonse.”—1 Akorinto 13:4-8.

Mary alibe matenda a MCS, koma ena mwa anzake alinawo. “Ndimakonda kudzola mafuta onunkhiritsa,” analemba motero Mary, “koma sindigwiritsa dala ntchito mafutaŵa ndikamapita kukacheza kwa anthu amene ali ndi MCS.” Apatu tingati mwa njira yakeyake, motsanzira Yesu, Mary akuti, “Ndikufuna kuthandiza.” (Marko 1:41) Trevor anayamba kudwala MCS ali wakhanda. Amayi ake anati: “Anthu amene ndakhala ndikugwira nawo ntchito analikudzipereka pochita zinthu momuganizira mwana wanga.” Joy, yemwe ndi mmodzi wa Mboni za Yehova amene amakhala ku Australia ndipo amavutika kwambiri ndi MCS, ananena kuti iye amalimbikitsidwa ndi anzake komanso abale ake amene amam’chezera kaŵirikaŵiri ndi kusonyeza kuti amamvetsetsa mavuto ake.

Komanso, anthu amene akudwala MCS ayenera kuyesetsa kukhala oleza mtima ndi anthu amene adzola mafuta onunkhiritsa n’kukhala nawo pafupi. Ernest, amene wagwidwa mawu m’nkhani yapitayo, analongosolera atolankhani a magazini ya Galamukani! kuti: “Matenda athu n’chikatundu chathu chimene tiyenera kuchinyamula ndithu. Anthu ena nawonso ali ndi mavuto awo, ndiye timawayamikira akatithandiza pa mavuto athu.” Inde, kupempha mgwirizano, osati kukakamiza, n’kwabwino nthaŵi zonse. “Munthu amene wagwiritsa ntchito mafuta onunkhiritsa akandifunsa chifukwa chake sindikuoneka bwino,” anatero Lorraine, “ndimamuuza kuti, ‘ndimavutika ndi mankhwala onunkhiritsa, ndipo zikuoneka ngati usiku uno zachita kunyanya.’ Nthaŵi zambiri kwa anthu ozindikira, mawu amenewo n’ngokwanira.” Inde, zimenezi sizikutanthauza kuti ngati mukudwala MCS simungakumbutse anzanu mwaulemu kuti mumafuna thandizo lawo.

Nkhani yomwe ili yosangalatsa ndi yomwe Pam, amene wagwidwa mawu poyambirira uja, analemba, yakuti: “Zinthu zonse zimene timavutika nazo lerolino n’zakanthaŵi chabe.” N’chifukwa chiyani Pam ananena kuti “kanthaŵi chabe”? Chifukwa chakuti chikhulupiriro chake chozikidwa pa Baibulo n’chakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzafafaniza kuvutika konse padziko lapansi. Komanso udzachotsa imfa—chinthu chimene ngakhale munthu wathanzi labwino bwanji chiyenera kudzam’fikira basi.—Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4.

Padakali pano, onse amene akulimbana ndi matenda opanda mankhwala angayembekeze ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, pamene ‘sipadzakhala munthu amene adzanene kuti: Ine ndidwala.’ (Yesaya 33:24) Pamene tikulimbana ndi ziyeso zimene zimatigwera m’dogosolo lino la zinthu, tiyeni tonsefe tiyesetse kukhala monga Yesu ndi kuika maganizo athu pa mphoto yoikidwa patsogolo pathu.—Ahebri 12:2; Yakobo 1:2-4.

[Bokosi patsamba 25]

Kusonyezana Chikondi

Mfundo zotsatirazi zochokera m’Baibulo zingakuthandizeni ngati bwenzi lanu kapena mbale wanu ali ndi vuto la kusagwirizana ndi mankhwala (MCS) kapenanso ngati muli nalo inuyo:

“Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”Mateyu 7:12.

“Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”Mateyu 22:39.

“Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Tonsefe timafuna kulimbikitsidwa mwauzimu, makamaka pamene tikudwala. N’zoyamikirika kwambiri kuti Akristu ambiri odwala MCS amayesetsa kufika pamisonkhano; ena amene akudwala modetsa nkhaŵa nthaŵi zina amachita nawo misonkhano mwa kugwiritsa ntchito telefoni. Nthaŵi zina, pa Nyumba ya Ufumu pamasungidwa malo a anthu omwe sagwiritsa ntchito mafuta onunkhiritsa kuti pakhale anthu amene ali ndi MCS. Koma zimenezi sizingachitike kapenanso kukhala zothandiza nthaŵi zonse.

“Musaiwale kuchitira chokoma . . . ; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:16) Onani kuti nthaŵi zonse kuchita zokoma kumafuna kuti munthu adzipereke. Kodi ndinu wokonzeka kudzipereka kuti muthandize winawake amene ali ndi MCS? Komanso anthu amene ali ndi MCS sayenera kuchita kuyembekezera zinthu zambiri kuchokera kwa ena. Mwachitsanzo, akulu achikristu sangaike malamulo a mmene mafuta onunkhiritsa angagwiritsidwire ntchito, komanso sangathe kumalengeza za nkhani imeneyo nthaŵi ndi nthawi. Kuwonjezera pamenepo, atsopano ndiponso alendo amene amadzola mafuta onunkhiritsa amabwera ku misonkhano ya mpingo, ndipo timaŵalandira. Sitingafune kuwakhumudwitsa kapena kuwachititsa kukhala omangika chifukwa adzola mafuta onunkhiritsa.

‘Funafunani mtendere ndi kuulondola.’ (1 Petro 3:11) Mwachionekere, nkhani zokhudza thanzi la munthu siziyenera kusoŵetsa mtendere Akristu. “Nzeru yochokera kumwamba ndi . . . yamtendere, yaulere [yoganizira ena, NW], . . . yodzala chifundo,” amatero Yakobo 3:17. Anthu amtendere, kaya akudwala MCS kapena ayi, sangakhale onyanyira kapena olamulira ponena za kugwiritsa ntchito kapena kusagwiritsa ntchito mankhwala oopsa. Chimodzimodzinso, anthu oganizira ena omwe ali ‘odzala ndi chifundo’ angapeŵenso kukakamira kunena kuti ali ndi ufulu wogwiritsa ntchito mafuta onunkhiritsa akazindikira kuti zimenezi zingadwalitse munthu wina. Mwanjira imeneyi amasonyeza kuti nawonso akufunafuna ‘mtendere’ ndipo “akuchita mtendere.”—Yakobo 3:18.

Komanso, kukhala waliuma, kusalingalira bwino zinthu, kaya n’kwa wodwalayo kapena kwa munthu wina, kuli monga mgula wogaŵanitsa anthu. Maganizo ngati amenewo sapindulitsa aliyense ndipo akhoza kuwononga unansi wa munthu ndi Mulungu.—1 Yohane 4:20.

Inde, Akristu ali ndi chinthu chachikulu kwambiri—mzimu wa Yehova. Pamene akupempha Yehova nthaŵi ndi nthaŵi kuti awapatse mzimu wake, iwo amakulitsa zipatso zabwino kwambiri za mzimu, makamaka chikondi chimene ndi “chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Panthaŵi yomweyonso, amalolera modekha kuti mzimuwo uchirikize mikhalidwe yonga ya Kristu m’mitima ya ena.—Agalatiya 5:22, 23.

[Chithunzi patsamba 26]

Anthu odwala MCS amafuna kukhala ndi anzawo monga momwe aliyense amafunira