Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Kukonda Kukhulupirira Mizimu Kwafala Motere?

N’chifukwa Chiyani Kukonda Kukhulupirira Mizimu Kwafala Motere?

N’chifukwa Chiyani Kukonda Kukhulupirira Mizimu Kwafala Motere?

Kukhulupirira mizimu kwamasuliridwa kuti ndiko “Chikhulupiriro chakuti mzimu m’thupi la munthu sumafa pa imfa ya thupi ndipo ungakhoze kulankhulana ndi amoyo, kaŵirikaŵiri kupyolera mwa munthu wobwebweta.”

MU 1998, buku lofotokoza mmene anthu angalankhulire ndi akufa linafala kwambiri ku United States moti pasanapite nthaŵi linakhala buku logulidwa kwambiri pa m’ndandanda wa mabuku ogulitsidwa m’nyuzipepala ya New York Times.

Zaka zingapo zapitazo ku Moscow, maula ndiponso misonkhano ya openduza yolankhulana ndi mizimu inangokhala mwambo womwe anthu andale ndiponso azamalonda, amene ankalipira ndalama zambiri akafunsira kwa amaulawo, anali kuiyembekezera mwachidwi.

Ku Brazil, mapulogalamu amaseŵero a pawailesi yakanema oonetsa zamizimu amakopa anthu oonerera ambirimbiri.

Kwa anthu ambiri okhala ku Africa kapena ku Asia, kukhulupirira mizimu n’kofala ngati malonda a tomato pamsika.

Chifukwa Chimene Ambiri Amakhulupirira Mizimu

Anthu ambiri amakhulupirira mizimu kuti apeze chitonthozo pambuyo pa imfa ya okondedwa awo. Kudzera mwa obwebweta okhulupirira mizimu, iwo angalandire uthenga wapadera womwe umaoneka ngati ukuchokera kwa wakufa uja. Mapeto ake, anamfedwa oterowo nthaŵi zambiri amakhulupirira kuti okondedwa awo akufawo adakali moyo ndikuti kulankhulana nawo kudzawatonthoza.

Enanso amakopeka kukhulupirira mizimu chifukwa chakuti auzidwa kuti mizimu idzawathandiza kupeza mankhwala a matenda aakulu, kuthaŵa mavuto a umphaŵi, kupeza chibwenzi, kuthetsa mavuto a m’banja, kapena kupeza ntchito. Ndipo ena ambiri amakhulupirira mizimu chifukwa chongofuna kudziŵa zinthu.

Komabe, chifukwa chinanso chimene anthu miyandamiyanda amakhulupirira mizimu n’chakuti, iwo anaphunzitsidwa, monga momwe katswiri wina wa nkhani zimenezi anafotokozera, kuti kukhulupirira mizimu “n’chipembedzo chowonjezera” chimene chimayendera “limodzi ndi Chikristu.” Ndi mmene nkhani zachipembedzo zilili ku Brazil.

Dziko la Brazil lili ndi chiŵerengero chachikulu koposa cha Akatolika padziko lapansi, koma malinga ndi mmene wolemba Sol Biderman ananenera, “Akatolika okhulupirira miyandamiyanda amayatsa makandulo m’tchalitchi chakatolika komanso m’magome amizimu ndipo amaona [kuti palibe] cholakwa chilichonse.” Ndiponso, nyuzipepala ya ku Brazil yotulutsidwa mlungu ndi mlungu yotchedwa Veja inanena kuti, 80 peresenti ya anthu amene kaŵirikaŵiri amapita ku magome amizimu ku Brazil ndi Akatolika obatizidwa amenenso amapezeka pa Misa. Komanso, chifukwa chakuti ngakhale atsogoleri ena a matchalitchi achikristu amachita nawo misonkhano ya zamizimuyi, mungaone chifukwa chimene okhulupirira ambiri amaganizira kuti kulankhulana ndi mizimu kaamba ka chitonthonzo ndiponso chitsogozo n’kovomerezeka ndi Mulungu. Koma kodi zimenezi n’zoona?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 3]

Mitundu Yosiyanasiyana ya Kukhulupirira Mizimu

Kukhulupirira mizimu kungaphatikizepo kufunsira kwa wobwebweta, kufunsira kwa akufa, kapena kukhulupirira malodza. Mtundu umodzi wofala kwambiri wa kukhulupirira mizimu ndiwo kuwombeza, kuyesa kudziŵa zam’tsogolo kapena zosadziŵika mothandizidwa ndi mizimu. Mitundu ina ya kuwombeza ndiyo kupenda nyenyezi, kuyang’ana pa mpira wa galasi, kumasulira maloto, kupenda m’zikhatho, ndiponso kulosera mwayi pogwiritsa ntchito makadi amwayi.