Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khama Langa Lofuna Kusankha Zinthu Mwanzeru

Khama Langa Lofuna Kusankha Zinthu Mwanzeru

Khama Langa Lofuna Kusankha Zinthu Mwanzeru

YOSIMBIDWA NDI GUSTAVO SISSON

Pamene ndinali ndi zaka 12, ngakhale kuti kusambira kunali kutandiloŵerera kwambiri, ndinaganiza zakuti ndidzakhale dokotala. Koma cha panthaŵi yomweyi, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndipo, monga chotsatirapo chake, ndinayamba kufuna kudzakhala mtumiki. Kodi zinthu zinatha bwanji popeza zimene ndinkalakalaka kuchita zinali zosiyana? Kodi zinali zoti n’kuyenderana?

MU 1961 Olive Springate, amene anali mmishonale wa Mboni za Yehova ku Brazil, anayamba kuphunzira Baibulo ndi amayi anga pamodzi ndi ine. Koma chifukwa choletsedwa ndi bambo anga amene anali dokotala wotchuka mumzinda wa Pôrto Alegre tinasiya kuphunzira. Komabe, Olive ankalankhulana nafe, ndipo m’kupita kwa nthaŵi ndinazindikira kuti zimene ndinaphunzira zinali zoona. Panthaŵiyi kutanganidwa ndi maseŵera osambira kunali kutandisokoneza kuchita zinthu zauzimu.

Pamene ndinali ndi zaka 19, ndinakumana ndi kamtsikana kokongola kotchedwa Vera Lúcia ku malo a za maseŵera komwe ndinkasambira, ndipo tinayamba chibwenzi. Amayi anga anamuuza mtsikanayu zimene timakhulupirira, ndipo iye anachita chidwi. Motero ndinapezana ndi Olive uja, ndipo anayamba kuphunzira nafe Baibulo ngakhale kuti bambo ake a Vera Lúcia anali kutiletsa.

Vera Lúcia anapitiriza kuphunzira, ndipo analidziŵa kwambiri Baibulo. Moti anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi antchito a ku malo amene ndinkachitirako maseŵera osambira. Panthaŵi yomweyo, maganizo anga onse anali pa kukonzekera mpikisano wosambira wa m’dziko lathu umene unali utayandikira.

Titaphunzira ndiponso kupita kumisonkhano pafupifupi chaka chathunthu, bambo ake a Vera Lúcia anayamba kutikayikira. Tsiku lina tikuchokera kumsokhano, iwo anatidikirira ndipo anafuna kudziŵa kumene tinali. Ndinayankha kuti tinali kuchokera kumsonkhano wachikristu ndi kuti ngakhale kuti kwa iwowo chipembedzo si chinali nkhani yofunika, kwa ife chinali nkhani ya moyo kapena imfa. Anapumira m’mwamba ndi kunena kuti: “Chabwino ngati ili nkhani ya moyo kapena imfa ndiye kuti ineyo ndingololera basi.” Kuyambira tsiku limenelo, maganizo awo anasintha, ndipo ngakhale kuti sanadzakhale a Mboni za Yehova, anasanduka bwenzi lathu lapamtima ndiponso mnzathu wotithandiza tikakhala pamavuto.

Kusankha Zochita

Ndinaganiza zosiya mpikisano wosambira utatha mpikisano wofuna kupeza katswiri wadziko lathu, koma chifukwa chakuti ndinali nditapambana kaŵiri ndiponso ndinali nditapambana pa mpikisano wa m’dziko lonse la Brazil wosambira mmene ukufunira pa mamita 400 ndi mamita 1,500, zinachititsa kuti ndiitanidwe ku mpikisano wotchuka wotchedwa Pan American Games womwe unachitikira mu mzinda wa Cali ku Colombia, mu 1970. Ngakhale kuti Vera Lúcia sankafuna kuti ndipiteko, ndinayamba kukonzekera mpikisanowo.

Nditasambira bwino kwambiri ku Cali, ophunzitsa maseŵerawa anandifunsa ngati ndinali kufuna kukonzekera mpikisano wotchedwa Olimpiki wamayiko onse. Ndinaganizira za maphunziro anga a zachipatala amene ndinali ndisanamalize ndiponso za choonadi chochititsa chidwi chonena za zolinga za Yehova chimene ndinali nditaphunzira, ndipo nditatero ndinasiyiratu kuganizanso za ntchito yosambira. Kuyambira pamenepo ndinapita patsogolo kwambiri mwauzimu. M’chaka cha 1972, chomwenso chinali cha mpikisano wa Olimpiki womwe unachitikira mu mzinda wa Munich, ku Germany, Vera Lúcia ndi ine tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Zimenezi zinalimbikitsa amayi kuti ayambirenso phunziro lawo la Baibulo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi nawonso anabatizidwa.

Amayi anga atabatizidwa, bambo anga anapitiriza kutiletsa. Potsiriza pake banja linatha, ndipo poti ndinali ndidakali ku yunivesite, tinayamba kudzisamalira pogwiritsa ntchito ndalama zawo zochepa za penshoni ndiponso ndalama zimene tinapeza titagulitsa nyumba yathu. Motero ine ndi Vera tinasintha tsiku la ukwati wathu kuti likhale m’tsogolo. Kwenikweni malangizo amene ndinalandira kuchokera kwa Bambo anga ndiwo anandithandiza kusankha kuchita zinthu zonsezi. Nthaŵi zambiri ankanena kuti: “Osaopa kuchita zinthu zosiyana ndi ena” ndiponso ankati, “Ngati anthu ambiri akuvomerezana pa chinthu chimodzi si ndiye kuti nthaŵi zonse amakhala olondola.” Mawu ena amene ankakonda kunena anali akuti, “Kufunika kwa munthu kumadziŵika poyang’ana zinthu zimene amachitira ena.”

Monga m’modzi wa Mboni za Yehova, ndagwiritsa ntchito malangizo abwino kwambiri ameneŵa amene Bambo anandiuza. Ndinali pamphepete pa bedi lawo pamene anamwalira mu 1986. Tinakhalanso mabwenzi ndipo tinkalemekezana. Ndikukhulupirira kuti ankandinyadira, chifukwa chakuti ndinatsata mapazi awo, n’kukhalanso dokotala wa zachipatala.

Apatu n’kuti nditamaliza sukulu ya zachipatala mu 1974. Ndinaganiza zoyamba udokotala wothandiza kuchiza matenda osiyanasiyana, koma kenaka, nditaganiza mofatsa, ndinaona kuti ndingathe kuthandiza kwambiri abale anga achikristu pokhala dokotala wochita opaleshoni. (Machitidwe 15:28, 29) Choncho ndinalimba mtima ndipo ndinakhala zaka zina zitatu ndikuphunzira za udokotala wa opaleshoni.

Kulimbana ndi Malamulo a Boma

Nkhani yomvetsa chisoni kwambiri imene inandikhudza ndi ya mtsikana wa Mboni wa zaka 15 amene ankadwala matenda otuluka magazi m’mimba. Anali atayera ndiponso magazi ake sanali kuthamanga mokwanira koma anali wotsimikiza kwambiri kuti sakufuna kuikidwa magazi. Nditam’patsa mankhwala ochititsa kuti magazi ake awonjezeke, ndinam’chita opaleshoni yong’amba pamimba ndipo ndinatsuka bala lonselo ndi madzi a mchere ozizira kuti magazi asiye kutuluka. Poyamba anakhalako bwino, koma patatha maola 36, ali kumagetsi, mosayembekezeka magazi aja anayambanso kutuluka. Ngakhale kuti dokotala amene anali kugwira ntchito panthaŵiyo anayesetsa, analephera kuletsa kutuluka kwa magaziko ndi kutinso magazi ake asachepe, ndipo mtsikanayo anamwalira.

Izi zitachitika, komiti yoona za mwambo wamadokotala inandilanda kaye chilolezo chokhala dokotala wophunzirira ndipo inandineneza ku bungwe la zachipatala la m’chigawocho. Ndinaimbidwa mlandu wophwanya malamulo atatu opezeka m’buku la mwambo wa madokotala, zimene zikanachititsa kuti chilolezo changa chokhala dokotala chilandidwe, ndiponso ntchito yanga ikanathera pompo.

Komiti ina inagwirizana zakuti ndiyenera kupereka kalata yodziteteza pasanathe masiku 30. Maloya anga anakonza mfundo zalamulo ndi zovomerezeka, ndipo ineyo ndinakonza mfundo zodzitetezera mogwirizana ndi mfundo zachipatala ndi zasayansi mothandizidwa ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala (HLC) yam’dera lakwathu imene ili gulu la Mboni za Yehova lofuna kulimbikitsa mgwirizano wapakati pa zipatala ndi odwala. Pamulanduwo komiti yolangiza inandifunsa mafunso amene makamaka anali okhudza zimene ndimakhulupirira monga dokotala ndiponso monga wa Mboni za Yehova. Komabe, yankho langa lodziteteza linali lokhudza kwenikweni mfundo zachipatala ndiponso zasayansi komanso lokhudza malipoti operekedwa ndi madokotala odziŵika bwino ochita opaleshoni.

Umboni umene unaperekedwa unatsimikizira kuti wodwalayo anakana kulandira magazi ndi kutinso ine sindinachite chilichonse kuti iye asankhe kutero. Pamlanduwo anatsimikiziranso kuti mwamadokotala anayi amene anafunsidwa, ndi ine ndekha amene ndinayamba kupereka chithandizo chogwirizana ndi zimene wodwalayo ankafuna.

Kenaka mlandu wanga unapititsidwa ku komiti ija kuti ikavote anthu ake onse alipo. Ndinayankhula kwa mphindi khumi, ndipo monga mmene ndinachitira poyamba m’kalata yanga yodziteteza, ndinatchula mfundo zogwirizana ndi zachipatala basi. Atandimvetsera, anthu aŵiri a mukomitiyo ananena kuti ngakhale kuti sindinagwiritse ntchito njira yoika magazi, chithandizo chimene ndinapereka chinali chogwirizana kwambiri ndi sayansi. Dokotala wina ananena motsindika kuti chithandizo chopanda magazi chimagwira ntchito bwino ndi kutinso anthu ambiri samafa akathandizidwa motere. Mlangizi wotsiriza ananena kuti nkhani ili apa si yakuti kuika munthu magazi monga mankhwala n’kwabwino kapena ayi. Nkhani yagona pakuti kodi dokotala angathe kukakamiza odwala kulandira chithandizo chimene sakufuna? Ndipo mlangizi wotsirizayu anati sakuganiza kuti dokotala anali ndi ufulu wotero. Motero, alangizi 12 mwa alangizi 14 anavotera kuti ndilibe mlandu uliwonse, motero milandu yanga inatha.

Kuchirikiza Ufulu wa Wodwala

Madokotala ena akhala akutenga zilolezo za kukhoti kuti akakamize odwala a Mboni kulandira magazi, ndipo nthaŵi zina ndaperekapo umboni pamilandu ya kukhoti umene wathandiza kuletsa zilolezo zimenezi. Mlandu wina unali wokhudza wa Mboni wina amene mitsempha ya kum’mero kwake inali yotupa, vuto limene limachititsa kuti m’mimba muzituluka magazi kwambiri. Panthaŵi imene anapititsidwa kuchipatala, anali atatha magazi kwambiri, ndipo mbali yofunikira ya magazi ake yotchedwa hemoglobin inali itatsika kufika pa magalamu 4.7 pa desilita iliyonse. * Poyamba, sanali kumukakamiza kulandira magazi koma anali kupatsidwa mankhwala ongochepetsa vutolo.

Kenaka atatha sabata lathunthu m’chipatalacho, wodwalayo anadabwa atayenderedwa ndi mkulu wina wakukhoti amene anabweretsa chikalata cholamula kuti am’patse magazi. Panthaŵiyi n’kuti hemoglobin m’thupi lake itachuluka n’kufika pa magalamu 6.4 pa desilita iliyonse, ndipo anali kupezako bwino. Zikuoneka kuti woweruza milanduyo anaganiza zochita zimenezi poganizira za mlingo woyamba uja wa hemoglobin osati mlingo wachiŵiriwu, umene unali wokwera.

Komiti ya zachipatala ya HLC inadzipereka kuti ithandizepo. Wodwalayo anandipempha kuti ndimuyeze. Ndinatero ndipo kenaka ndinakam’pereka kuchipatala chimene akanatha kuthandizidwako popanda magazi. Panthaŵi yomweyi, maloya ake anatsutsa lamulo la khoti lakuti wodwalayo am’patse magazi.

Ndinalamulidwa kuti ndikaonekere kwa woweruza, ndipo anandifunsa za mmene wodwalayo anali kupezera. Pozenga mlandu umenewo, iye anandiloleza kuti ndipitirize kuthandiza wodwalayo kwinaku akukambirana kuti aone ngati lamulo la khotilo linali loyenerera. Panthaŵi imene tinapita kukaonekera pa kuzenga kwina, wodwalayo n’kuti atachira ndipo atatulutsidwa m’chipatala. Pamene ndinaitanidwa kuti ndikaperekenso umboni, loya wachipatalacho, pofuna kundipanikiza, anandiuza kuti ndisonyeze ngati chithandizo chimene ndinam’patsa chinali chogwirizana ndi sayansi. Anachita manyazi pamene ndinasonyeza nkhani yovomereza chithandizo cha mtunduwo yochokera m’magazini ya zachipatala yolembedwa ndi chipatala chimene iye anali kuimiracho!

Chiweruzo chitaperekedwa, tinasangalala kwambiri kumva kuti mfundo yathu yodalira chithandizo cha mankhwala osati kuikidwa magazi inavomerezedwa. Chipatalacho chinalamulidwa kuti chilipire ndalama zonse zimene zinawonongedwa, kuphatikizapo zolipirira kukhoti. Ngakhale kuti chipatalacho chinapititsanso nkhaniyo kukhoti chinalepheranso.

Kusamalira Banja Lathu

Kungoyambira pamene ndinakhala Mboni, Vera Lúcia wakhala akundithandiza monga mnzanga weniweni ndiponso monga mkazi wojijirika komanso wopereka chitsanzo chabwino kwa ana athu. Kodi iye wathana nawo bwanji mavuto onse amene takumana nawo, monga kusamalira nyumba yathu ndiponso kuthandiza kusamalira ana athu, amene tsopano ali anyamata amphamvu? Watha kutero chifukwa chakuti iye amakonda kwambiri Yehova ndiponso utumiki wachikristu.

Monga makolo, taphunzitsa ana athu ziphunzitso ndiponso mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kuyambira ali aang’ono kwambiri. Ngakhale kuti timakhala otanganidwa kwambiri, timayesetsa kuchita utumiki wa nthaŵi zonse kwa miyezi ingapo chaka chilichonse. Ndipo timayesetsa kuti titsatire ndandanda yosonyeza kuŵerenga Baibulo mokhazikika, kukambirana lemba lochokera m’Baibulo tsiku lililonse, ndiponso kugaŵana zikhulupiriro zathu ndi ena mu utumiki wachikristu. Posachedwapa banja lathu lakhala likuchititsa maphunziro a Baibulo okwana 12 mlungu uliwonse ndi anthu amene si a Mboni.

Ine ndi Vera Lúcia timayesetsanso kuti ana athu tizichitira nawo zinthu pamodzi, koma sitiiwalanso kuwapatsa ufulu wosankha kuchita zimene amakonda. Timakhulupirira kuti pali zinthu zitatu zofunika kuti makolo athe kusamalira bwino mabanja awo. Chinthu choyamba ndicho kuphunzitsa koyenera, kozikidwa m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Chachiŵiri, chitsanzo chabwino, chimene chimapatsa ana umboni woonekeratu wakuti makolo awo amaopa Mulungu moyenerera. Ndipo chachitatu, ndicho mabwenzi oyenerera amene ali Akristu a misinkhu yosiyanasiyana ndiponso okhala m’mikhalidwe yosiyanasiyana, amene angathe kupereka mphatso ndiponso maluso osiyanasiyana m’banja. Ine ndi mkazi wanga, tinagwirizana kuti cholinga chathu chikhale kupatsa banja lathu zinthu zimenezi.

Tikamayang’ana m’mbuyo zaka pafupifupi 30 zomwe takhala tikutumikira Yehova, ine ndi mkazi wanga tinganene mosakayikira, kuti m’moyo wathu iye watipatsa zinthu zabwino koposa ndipo watipatsa chimwemwe chochuluka pamodzinso ndi madalitso. Ngakhale kuti sindinathe kupita kumpikisano wa Olimpiki, ndimakondabe kusambira mitunda ingapo sabata lililonse. N’zoona kuti pokhala dokotala komanso pokhala wa Mboni za Yehova ndakhala otanganidwa kwambiri, koma ndaona kuti kuthandiza abale ndi alongo anga achikristu kuchita khama potumikira Mulungu m’kati mwa chiyeso n’kopindulitsa kwambiri.

Nthaŵi zambiri ndimafunsidwa ngati ndimada nkhaŵa podziŵa kuti ndidzasiya ntchito yanga dongosolo latsopano la Mulungu likadzabwera pamene sikudzakhalanso matenda. Ndimayankha kuti ineyo ndiye ndidzakhale woyamba kudumpha mosangalala pa nthaŵi imene “wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba” ndi pamene “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; 35:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Munthu wamwamuna wathanzi labwino amakhala ndi hemoglobin yokwana pafupifupi magalamu 15 pa desilita imodzi.

[Chithunzi patsamba 15]

Kuchita opaleshoni munthu wodwala

[Zithunzi patsamba 15]

Ndili ndi Vera Lúcia, pa phunziro lathu la banja