Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Adzasiya Mkhalidwe Wauchinyama?

Kodi Anthu Adzasiya Mkhalidwe Wauchinyama?

Kodi Anthu Adzasiya Mkhalidwe Wauchinyama?

Nduna yoona za Mgwirizano wa Zachitukuko ku Italy yomwe dzina lake ndi Livia Turco, anaipatsa magazini imodzi ya Galamukani! ya pa March 8, 2000, yonena za vuto loopsa logwira anthu ukapolo, limene, n’zomvetsa chisoni kuti likupitirirabe m’mbali zina za dziko lonse. Iyeyu analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Italy, ndipo anati:

“Ukapolo wa makono, umene makamaka umakhudza akazi ndi ana wafika poipa zedi ndipo ukuchititsa anthu mamiliyoni kukhala mwauchinyama.” Iye anatulutsa mfundo yakuti: “Maganizo alionse amene anganenedwe pa vuto losafunikali n’ngofunika kwambiri, ndipo akafika kwa anthu ochuluka onga amene amaŵerenga [Galamukani!], ndiye kuti ndi opindulitsa kwambiri.”

Chifukwa cha kufalitsidwa kwa magazini okwana 20 miliyoni a kope lililonse la Galamukani! m’ziyankhulo 82, oŵerenga mamiliyoni ambiri adziŵa mmene mavuto a lero alili komanso apeza mayankho ochokera m’Baibulo othetsera mavutowa.

Komabe funso n’lakuti, Ngati kulidi Mulungu, kodi n’chifukwa chiyani amalola anthu ambiri osalakwa kuvutika? Anthu ambiri amadzifunsa kuti, ‘Kodi Ndingakonde Bwanji Mlengi amene nzeru zake zimaoneka poyera poyang’ana zodabwitsa za m’chilengedwe koma yemwe saonetsa kuti amachitira chifundo anthu lerolino?’ Mafunso ngati ameneŵa amayankhidwa mogwira mtima m’bulosha lotchedwa Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Mungathe kuliitanitsa polemba zofunika m’kabosi kali pamusika ndi kukatumiza ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni bulosha lotchedwa Kodi Mulungu Amatisamaliradi?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.