Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Zina Zimene Maso Anu Saona?

Kodi Mumaona Zina Zimene Maso Anu Saona?

Kodi Mumaona Zina Zimene Maso Anu Saona?

OYENDETSA galimoto sangathe kuona kutsogolo kwa msewu pokhota popanda chowathandiza. Koma mothandizidwa ndi galasi loikidwa pokhoterapo, magalimoto obwera angathe kuonedwa ndipo ngozi zingathe kupewedwa. Chonchonso anthu sangathe kumuona ndi maso Mlengi amene ali wosaoneka. Kodi pali njira iliyonse yodziŵira kuti pali Munthu wotereyu?

Wolemba wina wa m’zaka za zana loyamba anatchulapo za mmene tingazindikirire zinthu zimene sitingaone. Iye analemba kuti: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuŵiringula.”—Aroma 1:20.

Tangoganizirani zimenezo. Kodi mumaona kuti panagona nzeru kuti kukhale zinthu zimene timazionazi zomwe anthu sangakwanitse kuzilenga? Kodi zinthu zimenezi zimakuthandizani kuona ndi “maso anu a kuzindikira” kuti pali munthu wina wamkulu kuposa anthu? Tiyeni tionepo zitsanzo zingapo.—Aefeso 1:18, King James Version.

Kuphunzira Poona Chilengedwe

Kodi munayamba mwachitapo chidwi ndi maonekedwe okongola a kuthambo kukakhala nyenyezi zambiri pa usiku wopanda mwezi, ndipo kodi munaona kuti umenewo ndi umboni wakuti kuli Mlengi Wamkulu? “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake,” anatero pogoma munthu wina wakale amene anachita chidwi. Mwamunayu analingaliranso kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukire? Ndi mwana wa munthu kuti mucheze naye?”—Salmo 8:3, 4; 19:1.

N’zosadabwitsa kuti ife timagoma tikamaona zolengedwa zodabwitsa kwambiri zimenezi zomwe anthu sangathe kuziyerekezera n’komwe kuti azipange. Pali mawu otchuka a m’ndakatulo ina amene amati: “Ndi Mulungu yekha amene angapange mtengo.” Komatu, chinthu chodabwitsa koposa ndicho kupangidwa kwa mwana, kumene sikuchita kulamulidwa ndi makolo ake. Pamene umuna wa bambo uphatikizana ndi dzira la mayi, pamabadwa selo lokhala ndi molekyu yotchedwa DNA ndipo mwamsanga molekyu imeneyi imakonzekera mwadongosolo kuti ipange mwana. Akuti “malangizo amene amakhala mu DNA atati alembedwe angathe kudzadza mabuku 1,000 a masamba 600 lililonse.”

Komatu chimenecho ndi chiyambi chabe. Selo lija limagaŵikana n’kusanduka maselo aŵiri, kenaka anayi, kenaka asanu ndi atatu, ndiye n’kumangopitirirabe. Pakatha masiku pafupifupi 270, kakhanda kokhala ndi maselo amoyo mamiliyoni zikwi zambiri a mitundu yoposa 200 kamabadwa. Ndiyetu n’zodabwitsadi kuganiza kuti selo loyamba lija limakhala ndi chidziŵitso chokwanira kupanga maselo amitundu yosiyanasiyana pa nthaŵi yomwe akufunika! Kodi zimenezi zikukuchititsani kufuna kutamanda Mlengi wathu? Taonani chitamando chimene wamasalmo anapereka polemba kuti: “Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.”—Salmo 139:13-16.

Anthu amene afufuza zambiri za “zodabwitsa” zimenezi amachita nthumanzi. Dr. James H. Hutton, pulezidenti wakale wa mabungwe a zamankhwala a m’maboma a Chicago ndi Illinois ku Amereka, anati anadabwa kwambiri ndi “mmene selo limagaŵira uthenga wosankhidwa bwino kumaselo obadwawo. N’zosangalatsadi kuti asayansi athu ofufuza atha kudziŵa zinthu zimenezi. Koma ndithudi payenera kuti pali Nzeru zaumulungu zimene zinakonza zinthu zimenezi.”

Dr. Hutton anapitiriza kunena kuti: “Inenso pa ukatswiri wanga wa zamankhwala opangidwa m’thupi ndaona kuti kuphunzira matenda ogwira mbali zathupi zopanga mankhwalawa, ndiko kumakhutiritsanso munthu kuti Mphamvu yaumulungu ndiyo inapanga zinthu zocholowana ndiponso zogwira ntchito motere.” Iye anamaliza mwakunena kuti: “Ineyo ndikuona kuti kuganizira mofatsa za zodabwitsa zimenezi kumakhutiritsa kuti pali munthu wamphamvuyonse ndiponso mwininzeru amene anakonza chilengedwechi, n’kuchilola kuti chiyambe kugwira ntchito yake ndipo ndiye amachiyang’anira.”

Atanena mfundo zonsezi, Dr. Hutton anafunsa kuti: “Kodi iye ndi Munthu amene tingati ndi Mulungu wosamalira munthu aliyense payekhapayekha ndipo amaona mpheta iliyonse imene imagwa pansi?” Iye anayankha kuti: “Penapake ndimakayikira zimenezi. Ndiponso sindikhulupirira kuti Iyeyo amaganizirako ngakhale pang’ono zimene ndimachita tsiku n’tsiku zomwe n’zopanda ntchito kwa iye.”

N’chifukwa chiyani anthu ambiri amavomereza kuti nzeru zili umboni wa “zodabwitsa” za m’chilengedwe koma n’kumakayikiranso kuti pali Mulungu wosamalira munthu aliyense payekhapayekha ndipo amene amaganizira anthu?

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

Anthu ambiri amanena kuti chikhala kuti kuli Mulungu, sadakalola kuti anthu azivutika chonchi. Funso lotchuka limene anthu ena akhala akufunsa n’lakuti, “Kodi Mulunguyo anali kuti pamene ife timavutika?” Munthu wina amene anapulumuka pamene anthu mamiliyoni anaphedwa ndi chipani chotchedwa Nazi pa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse anadandaula kwambiri chifukwa cha zovuta zimene anaona mwakuti ananena kuti: “Mtima wanga ungakupheni ndi poizoni ngati mutaunyambita.”

Choncho kwa anthu ambiri nkhani imeneyi imangowasiya m’malere. Monga mmene anaonera wofufuza zinthu wakale tam’tchula poyamba uja, umboni wakuti pali Mlengi n’ngosachita kufunsa tikapenda dongosolo lozizwitsa ndiponso kapangidwe ka zinthu. Koma, ngati Iye ali Mulungu wotiganizira, angalole bwanji kuvutika kodetsa nkhawa chonchi? Ngati tikufuna kuti timvetse ndi kulambira Mulungu moyenera, tiyenera kukhala ndi yankho logwira mtima la funso limeneli. Kodi yankho lake tingalipeze kuti?

Tikukupemphani kuti muitanitse bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Kuti mudziŵe mmene mungaliitanitsire, onani patsamba 32 la magazini ino ya Galamukani! Tikukhulupirira kuti mukadzaŵerenga mosamalitsa zigawo zakuti “Chifukwa Chake Mulungu Walola Kuvutika” ndi “Kodi Nchiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?” mudzapeza mayankho ogwira mtima.

[Zithunzi patsamba 11]

Kodi mukamaona zinthu ngati izi mumaona umboni wakuti pali Mlengi?