Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingachitenji Ndikamavutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi?

Kodi Ndingachitenji Ndikamavutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingachitenji Ndikamavutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi?

“Anyamata amandilizira timalikhweru tachikondi komanso amandikuwiza.”—Carla, Ireland.

“Atsikana amangondiimbira telefoni. Amafuna kuti mpaka utheke.”—Jason, United States.

“Mnyamatayo ankangokhudzakhudza mkono wanga ndi kumayesa kundigwira dzanja.”—Yukiko, Japan.

“Atsikana amakonda kundiuza mawu osayenera.”—Alexander, Ireland.

“Mnyamata wina ankakonda kundiseleula ali m’basi ya kusukulu. Si kuti kwenikweni anali kundifuna chibwenzi. Anali kungondivutitsa basi.”—Rosilyn, United States.

KUYANG’ANA mokopa, mawu “oyamikira” achikondi, nthabwala yolaula, kukugwira modzutsa chilakolako cha kugonana—zinthu zoterezi, ngati winayo sakusangalala nazo ndipo ngati zikubwerezedwabwerezedwa, ndizo zimene nthaŵi zambiri zimatchedwa kuti kuvutitsidwa ndi amuna kapena akazi. Ngakhale kuti n’kovuta kupeza ziŵerengero za padziko lonse, kufufuza kukusonyeza kuti achinyamata ambiri ausinkhu wopita kusukulu ku United States anavutitsidwapo.

Kodi kuvutitsidwa ndi amuna kapena akazi n’chiyani kwenikweni? Buku lotchedwa Coping With Sexual Harassment and Gender Bias (Kulimbana ndi Kuvutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi Komanso ndi Kusankhana Kuti Wina Ndi Mwamuna Kapena Ndi Mkazi), lolembedwa ndi Dr. Victoria Shaw, limatanthauzira mawuŵa kuti ndi “kusautsa munthu m’njira yokhudza kugonana . . . Zingachitike pathupi lamunthu (monga ngati kumugwira momudzutsa chilakolako cha kugonana), mwa mawu (monga ngati kulankhula za kaonekedwe ka munthu wina zimene iye sizimusangalatsa), kapena popanda mawu n’komwe.” Nthaŵi zina kuvutitsako kumakhala kufunsira chibwenzi mosayenerera.

Mwinamwake kusukulu mumavutitsidwa kwambiri ndi anzanu. Komabe, nthaŵi zina anthu akuluakulu, monga ngati aphunzitsi, ndiwo achita khalidwe loipali. Nkhani ina mu magazini yotchedwa Redbook inanena kuti aphunzitsi oŵerengekawo amene amapezekadi olakwa pa milandu ya kugonana “mwinamwake amaimira chiŵerengero chochepa chabe cha aphunzitsi amene amachita zimenezi.”

Akazi, ndipo nthaŵi zinanso amuna, anali kuvutitsidwa moteremu ngakhale m’mbuyomo m’nthaŵi za m’Baibulo. (Genesis 39:7; Rute 2:8, 9, 15) Ndipo Baibulo linalosera nkhani yodetsa nkhaŵa yakuti: “Mudzakhala nthaŵi zovuta m’masiku otsiriza. Anthu adzakhala odzikonda, adyera, odzitamandira, ndi onyada; adzakhala achipongwe . . . ; adzakhala ouma mtima, opanda chifundo, oneneza, achiwawa, ndi aukali.” (2 Timoteo 3:1-3, Today’s English Version) Motero n’zotheka, ndiponso zingachitike kumene, kuti inuyo mungadzavutitsidwe ndi mwamuna kapena mkazi.

Lingaliro la Mulungu

Zoona, si achinyamata onse amene amanyansidwa ndi khalidwe lamtopola lodzutsana chilakolako cha kugonana. Ena zimawasangalatsa, kapenanso kuwachititsa kudziona ngati otsogola. Kafukufuku wina wokhumudwitsa wa ku United States anasonyeza kuti pakati pa anthu amene anavutitsidwapo, 75 peresenti ya iwo anavomera kuti iwonso anavutitsapo anthu ena. Anthu ena akuluakulu angawonjezere vutolo mwa kupeputsa kuopsa kwa khalidwe lamtopola limeneli ponena kuti lili chabe maseŵera a ana. Koma kodi Mulungu amaliona motani?

Mawu a Mulungu, Baibulo, amatsutsa momveka bwino mchitidwe uliwonse wa kuvutitsa amuna kapena akazi. Timauzidwa ‘kusawononga ufulu’ wa ena mwa kulumpha malire a zakugonana. (1 Atesalonika 4:3-8, NW) Kwenikweni, anyamata akulamulidwa mosapita m’mbali kuti azichitira “akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Ndiponso, Baibulo limatsutsa ‘kulankhula zopusa.’ (Aefeso 5:3, 4) Motero, mukavutitsidwa sikulakwa kukalipa, kupsa mtima, kusokonezeka maganizo, ndipo ngakhale kumva kuti mwanyazitsidwa!

Kodi Ndinganenenji?

Ndiyeno, kodi muyenera kuchitanji ngati munthu wina akukusautsani moteremu? Nthaŵi zina kuyankha mofooka kapena mosamveka bwino kumamupatsa mphamvu wovutitsayo kuti akuvuteni kwambiri. Baibulo limatiuza kuti pamene Yosefe anali kunyengereredwa ndi mkazi wa bwana wake, iye sanangomunyalanyaza. M’malo mwake, anakanitsitsa kunyengedwa kuchita zonyansazo. (Genesis 39:8, 9, 12) Masiku ano, kukhala wolimba mtima ndiponso kuyankhula mosabisa mawu kudakali njira yabwino yophererera kuvutitsidwa.

N’zoona, munthu amene akukusautsaniyo angakhale kuti sakufuna kukukhumudwitsani. Munthu wooneka ngati akukuvutani kwenikweni angakhale akuyesayesa mosalingalira bwino kukuchititsani kukhala naye n’chidwi. Motero musaganize kuti muyenera kusonyeza khalidwe losasangalatsa kuti amene akukufunaniyo akusiyeni. Kungonena mawu monga akuti, ‘Nkhani zotere sindigwirizana nazo’ kapena, ‘Ayi musandikhudze’ kungakhale kokwanira kufotokoza malingaliro anu. Mulimonse mmene munganenere mawuwo, musasukulutse uthenga wanu. Ayi wanu akhaledi ayi! Mnyamata wotchedwa Andrea ananena kuti: “Ngati sakumvetsetsa mawu anu okoma mtimawo, muyenera kuwauza mosabisa chicheŵa. Kaŵirikaŵiri zimafika potero.” Kunena motsimikiza kuti ‘Zimenezo ayi!’ kungakhale kokwanira.

Ngati mkhalidwewo ukuipiraipira, musayese kulimbana nawo nokhanokha. Yesani kukambirana ndi makolo anu kapena anthu ena achikulire. Angakupatseni malingaliro okuthandizani mmene mungachitire ndi mkhalidwewo. Monga njira yomalizira, iwo angaone kukhala koyenera ngakhale kukadziŵitsa akuluakulu a sukulu. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakuumitseni thupi, kudzakutetezani kuti musavutitsidwenso.

Kupeŵa Kuvutitsidwa

Zoonadi, ndi bwino kupeŵeratu kuvutitsidwa. Kodi n’chiyani chingathandize pambaliyi? Andrea analangiza kuti: “Musapatse munthu chithunzithunzi chakuti mwinamwake mukusangalatsidwa naye. Ena adzamva zimenezo, ndipo mudzapitirira kuvutitsidwa.” Kavalidwe kanu kangakuthandizeni kwambiri. Wachinyamata wotchedwa Mara anati: “Sindivala ngati agogo, koma ndimapeŵa zovala zimene zimachititsa anthu kuyang’anitsitsa thupi langa.” Kukana kuvutitsidwa kotereku koma panthaŵi imodzimodziyo n’kumavala zovala zotenga mtima anthu kungakhale kuuza anthu mauthenga otsutsana. Baibulo limayamikira kuvala ‘mwamanyazi ndi modziletsa.’—1 Timoteo 2:9.

Anzanu amene mumasankha nawonso amakhudza mmene ena amakuonerani. (Miyambo 13:20) Rosilyn anati: “Pamene atsikana ena pagulu linalake amakonda kuti adzionedwa ndi anyamata, anyamatawo amalingalira kuti n’zimene atsikana onse pagulupo amakonda.” Carla anatchula mfundo yofananayi kuti: “Ngati umagwirizana ndi anthu amene amalola mawu oterowo kapena amene amasangalala ndi kuuzidwa zotero, ndiye kuti iwenso azikuvutitsa.”

Baibulo limasimba nkhani ya mtsikana wina wotchedwa Dina amene anali kugwirizana ndi atsikana a ku Kanani, kumene akazi anali otchuka n’kutayirira. Zimenezi zinachititsa kuti agwiriridwe. (Genesis 34:1, 2) Pachifukwa chabwino Baibulo limati: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru.” (Aefeso 5:15) Inde, kuvala “bwino,” kulankhula “bwino,” ndi kugwirizana ndi anthu ‘abwino’ kungakutetezeni kwambiri kuti musavutitsidwe.

Komabe, kwa achinyamata achikristu imodzi mwa njira zabwino koposa zophererera kuvutitsidwa ndiyo kungodziŵitsa anthu ena za chikhulupiriro chanu pa nkhani ya kupembedza. Mnyamata wotchedwa Timon, amene n’ngwa Mboni za Yehova, anakumbukira kuti: “Anyamata ankadziŵa kuti ndinali Mboni, motero nthaŵi zambiri sankandivutitsa ngakhale pang’ono.” Andrea anati: “Kuwauza kuti ndiwe wa Mboni kumathandiza kwambiri. Adzazindikira kuti mumasiyana m’zochita zambiri ndi kuti uli ndi miyezo yachikhalidwe yolimba kwabasi.”—Mateyu 5:15, 16.

Ngati Mwavutitsidwa

Ngakhale kuti mungayesetse kwambiri, simungapeŵeretu anthu amwano ndi ovuta anzawo. Koma ngati munthu wovutitsa akuvutitsani, palibe chifukwa choti muzivutika n’kuganiza kuti munalakwa, malinga ngati inu munali kuchita zinthu monga Mkristu. (1 Petro 3:16, 17) Ngati simukupeza bwino m’malingaliro chifukwa cha mkhalidwewo, pezani chichirikizo mwa kulankhula ndi makolo anu kapena anthu ena achikulire mu mpingo wachikristu. Rosilyn anavomereza kuti n’kovuta kusangalala pamene munthu wina akukuvutitsa. “Kungokhala ndi winawake pafupi, munthu amene ungalankhule naye, n’kothandiza kwambiri,” iye anatero. Kumbukiraninso kuti “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye.”—Salmo 145:18, 19.

Kulimbana ndi kusautsidwa n’kovuta, koma n’kofunika zedi. Mwachitsanzo, talingalirani nkhani ya m’Baibulo ya mtsikana wina wa ku Sunemu. Ngakhale kuti sanali kuvutitsidwa m’lingaliro limene mawuŵa akugwiritsidwira ntchito kaŵirikaŵiri masiku ano, anali kufunsiridwa ndi Solomo, mfumu yolemera ndiponso yamphamvu ya Yuda, zimene iye sanafune. Chifukwa kuti anali pachibwenzi ndi mwamuna wina, anakana kunyengedwa. Motero iye anatha kunena monyadira kuti, “Ndine khoma.”—Nyimbo ya Solomo 8:4, 10.

Inunso onetsani kuti ndinu olimba pa makhalidwe abwino ndi kuti muli otsimikiza mtima. Khalani “khoma” pamene munthu akukufunsirani musakufuna. Onani kuti aliyense amene mukucheza naye akudziŵa bwino zimene munatsimikiza kuchita monga Mkristu. Mwa kutero, mungakhalebe “osalakwa ndi oona” ndi kukhala ndi chidaliro chakuti mwakondweretsa Mulungu.—Afilipi 2:15. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 27 Uphungu wina pa kuvutitsidwa ndi amuna kapena akazi uli mu makope a Galamukani! a June 8, 1996; September 8, 1995; ndi June 8, 1991.

[Chithunzi patsamba 17]

Kuchititsa aliyense kudziŵa za zikhulupiriro zanu zachikristu kungakutetezeni

[Chithunzi patsamba 17]

Mwa kusagwirizana ndi gulu lolakwika, mungapeŵe kuvutitsidwa