Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukwaniritsa Zolingazo

Kukwaniritsa Zolingazo

Kukwaniritsa Zolingazo

KUFUNIRANA zabwino, ubale, ndiponso mtendere wapadziko lonse ndi zolinga zimene aliyense angaziyamikire. Baron Pierre de Coubertin, yemwe anayambitsanso maseŵera a Olimpiki ankakhulupirira kuti maseŵeraŵa angathe kuthetsa mikangano ya mayiko mwa kulimbikitsa opikisanawo kulemekezana kwambiri mosaona mtundu, chipembedzo, kapena kuti uyu ndi mwamuna kapena mkazi. Iye ankaganiza kuti “dziko labwinopo lingathe kupangidwa kokha ndi anthu abwino.” Koma kodi maseŵera angabweretsedi mtendere wa dziko? Tikaona zomwe zachitika m’mbuyomu, tingayankhe kuti ayi.

Ngakhale kuti maseŵera amathandiza kumbali yawo, maphunziro ochokera m’Baibulo ndiwo njira yolimbikitsira mtendere weniweni. Ndithudi, mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zitha kupanga “anthu abwino” monga momwe Coubertin ananenera. Taganizirani malemba ena amene amalimbikitsa anthu amene amawagwiritsa ntchito kukhala ndi mtendere, mosasamala kanthu za mtundu wawo.

“Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.

“Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:18.

“Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma.”—Agalatiya 6:10.

“Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake om’posa iye mwini.”—Afilipi 2:3.

“Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.”—1 Timoteo 4:8.

Kodi malingaliro otchulidwa m’malemba ameneŵa amathandizadi? Taganizirani zomwe zinachitika mumzinda wa Munich ku Germany. Mu 1974, patangotha zaka ziŵiri chichitikireni Maseŵera a Olimpiki mumzindawo amene anasokonezeka chifukwa cha uchigaŵenga ndiponso kuphedwa kwa anthu, Mboni za Yehova zinachita msonkhano wa mayiko pa bwalo la zamaseŵera la Olimpiki lomwelo. Ena mwa anthu amene anapezekapo anali ochokera ku Greece ndi Turkey, mayiko amene ankamenyana. Ndiponsotu m’nyengo yachilimwe yomweyo, magulu ankhondo a ku Greece ndi Turkey n’kuti akulimbirana chilumba cha Cyprus. Kodi zimenezi zinasokoneza Akristu amene ankachita msonkhanowo? Ayi ndithu! Zinalidi zochititsa chidwi kwa anthu oonerera kuona Agiriki ndi anthu a ku Turkey akukumbatirana ndi kuitanana kuti mbale wanga ndiponso mlongo wanga!

Mboni za Yehova zimadziŵika padziko lonse chifukwa chokhala ndi ubale wamtendere umene sumaona dziko la munthu, mtundu wake, kapena fuko lake. Inde, iwo samadzinenera kuti afika pa umodzi ndiponso mgwirizano wapadziko lonse wangwiro. Mofanana ndi wina aliyense, iwo amayenera kulimbika kwambiri kutsatira uphungu wa Mkristu mtumwi Paulo wakuti: ‘Vulani munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo valani watsopano.’ (Akolose 3:9, 10) Komabe, iwo amakhulupirira kwambiri kuti kutsatira mfundo zachikhalidwe za Baibulo kungathandize anthu kuti “afunefune mtendere ndi kuulondola.”—1 Petro 3:11.

Chomvetsa chisoni n’chakuti maseŵera a Olimpiki, ngakhale kuti zolinga zake n’zotamandika, ayambitsa anthu ambiri makhalidwe oipa. Mosiyana ndi zimenezo, Mawu a Mulungu omwe ali amphamvu akonza makhalidwe a anthu n’kukhala abwino koposa, ndipo potero alimbikitsa kukoma mtima ndi mtendere padziko lonse.

[Zithunzi patsamba 24]

Maseŵera a Olimpiki amalimbikitsa mpikisano

[Mawu a Chithunzi]

Aus dem Fundus der MŪNCHNER OLYMPIAPARK GMBH, Mūnchen

[Zithunzi patsamba 25]

Baibulo limalimbikitsa mtendere