Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Ndimaikirapo Mtima Kwambiri Ndicho Kukhalabe Wokhulupirika

Chimene Ndimaikirapo Mtima Kwambiri Ndicho Kukhalabe Wokhulupirika

Chimene Ndimaikirapo Mtima Kwambiri Ndicho Kukhalabe Wokhulupirika

YOSIMBIDWA NDI ALEXEI DAVIDJUK

Munali m’chaka cha 1947, chapafupi ndithu ndi mudzi wathu wa Laskov, ku Ukraine, moyandikana ndi malire a dziko la Poland. Mnzanga wamasiku amenewo wotchedwa Stepan anali wozembetsa mabuku ofotokoza Baibulo kuchokera ku Poland kubweretsa ku Ukraine. Tsiku lina usiku msilikali wina wolondera malire anamuona, ndipo anam’thamangitsa mpaka kumuwombera. Patapita zaka 12, imfa ya Stepan inadzandikhudza kwabasi m’moyo wanga, monga mmene ndilongosolere.

PANTHAŴI yomwe ine ndinkabadwa ku Laskiv mu 1932, mabanja khumi a m’mudzi wathu anali Ophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo panthaŵiyo. Ena mwa anthu ameneŵa anali makolo anga omwe anapereka chitsanzo chabwino cha kukhulupirika kwa Yehova mpaka nthaŵi yomwe anamwalira chapakatikati pa m’ma 1970. Inenso, chomwe ndakhala ndikuikirapo mtima kwambiri m’moyo wanga wonse ndicho kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu.—Salmo 18:25.

Mu 1939, chaka chomwe nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse inayamba, dera lomwe tinkakhala chakum’maŵa kwa dziko la Poland linaloŵetsedwa mu mgwirizano wa mayiko a Soviet Union. Tinkalamulidwa ndi dziko la Soviet mpaka mu June 1941 pamene dziko la Germany linalanda dera lathulo.

M’nthaŵi yankhondo yachiŵiri yapadziko lonse, ndinali kuvutika kwambiri kusukulu. Ana asukulu anali kuphunzitsidwa kuimba nyimbo zafuko ndiponso kuphunzira nawo nkhondo. Ndiponso, ena mwa maphunziro athu anali okhudza kaponyedwe ka mabomba. Koma ine ndinakana kuimba nawo nyimbo zafukozo ndiponso kuphunzira nawo nkhondo. Kuphunzira kuchirikiza chikhulupiriro changa cha m’Baibulo ndidakali wam’ng’ono kunandithandiza kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu m’zaka zotsatira.

M’gawo lomwe munali mpingo wathu munali anthu ambiri ochita chidwi ndi choonadi cha m’Baibulo moti mpaka apainiya (dzina limene atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova amatchedwa nalo) aŵiri anatumizidwa m’dera lathulo kuti athandize kuphunzitsa anthuwo. M’modzi mwa apainiyawo wotchedwa Ilja Fedorovitsch ankandiphunzitsa Baibulo ndiponso kundiphunzitsa utumiki. Pamene dziko la Germany linalanda ulamuliro, Ilja anagwidwa, n’kuikidwa mumsasa wina wachibalo wa Nazi ndipo anafera komweko.

Bambo Anga Analimba Kuti Asaloŵerere Nkhondo

Mu 1941 akuluakulu a boma la Soviet anayesa kukakamiza abambo anga kuti asaine chikalata cholonjeza kuti azipereka ndalama zothandizira pankhondo. Iwo anakana kuti sangachirikize mbali iliyonse m’nkhondoyo ndiponso ananena kuti monga mtumiki wa Mulungu woona, saloŵerera mbali iliyonse. Abambo anga anatchedwa mdani ndipo anawalamula kukakhala kundende zaka zinayi. Koma iwo anakhalako masiku anayi okha basi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti atamangidwa, Lamlungu lotsatira, dziko la Germany linalanda dera limene tinkakhalalo.

Pamene olondera ndende anamva kuti Ajeremani ali pafupi, iwo anatsegula zitseko za ndende n’kuthaŵa. Atatuluka kunja, ambiri amene anali m’ndendeyo anawomberedwa ndi asilikali a dziko la Soviet. Abambo anga sanatuluke nawo nthaŵi yomweyo koma kenako anatuluka n’kukabisala m’nyumba ya anzawo ena. Ali kumeneko anatuma munthu kukauza amayi kuti abweretse chikalata chotsimikizira kuti iwo anamangidwa chifukwa chokana kuchirikiza Asovieti pankhondo. Abambo ataonetsa chikalatacho kwa akuluakulu a boma la Germany, iwo sanawaphe.

Ajeremani ankafuna kudziŵa mayina a anthu onse amene ankagwirizana ndi Asovieti. Moti anakakamiza abambo anga kuti aulule mayinawo koma iwo anakana. Anafotokoza kuti iwo sachirikiza mbali iliyonse. Akanaulula munthu aliyense, ndiye kuti munthuyo akadaphedwa. Choncho, posachirikiza mbali iliyonse, abambo anga anapulumutsa miyoyo ya anthu ena ndipo anthuwo anawathokoza kwambiri abambo anga.

Kuchita Zinthu Mobisa

Asovieti anabwerera ku Ukraine mu 1944, ndipo m’May 1945 ku Ulaya, nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse inatha. Kenako, lamulo lokhwima loletsa anthu kuloŵa kapena kupita ku mayiko a Soviet Union linachititsa kuti ife amene tinali ku Soviet Union tipatulidwe ku mayiko ena onse apadziko lapansi. Ngakhale kuyenderana ndi a Mboni za Yehova anzathu a m’dziko loyandikana nafe la Poland kunali kovuta. Mboni zolimba mtima zinali kudutsa malire mozemba n’kukatenga magazini angapo amtengo wapatalidi a Nsanja ya Olonda. Popeza kuti malire anali pamtunda wa makilomita asanu ndi atatu okha kuchokera kumudzi kwathu ku Laskiv, zoopsa zonse zomwe anthuŵa ankakumana nazo ndinali kuzimva.

Mwachitsanzo, wa Mboni wina wotchedwa Silvester anadutsa malirewo maulendo aŵiri n’kubwerako bwinobwino. Koma paulendo wachitatu, asilikali olondera malire ndiponso agalu awo anamuona. Asilikaliwo anamuuza kuti aime koma Silvester anathamanga kwambiri pofuna kupulumutsa moyo wake. Njira yokha yomwe akanathaŵira agaluwo inali kukabisala m’nyanja yomwe inali pafupi. Anakhala usiku onse m’madzi wolekeza m’khosi atabisala m’maudzu aatali. Potsiriza pake, asilikaliwo atatopa kumufunafuna, Silvester anayenda mongodzikakamiza kupita kunyumba atafooka kwambiri.

Monga ndanenera kale, mphwake wa Silvester wotchedwa Stepan anaphedwa pamene ankafuna kudutsa malire. Komabe, kuyenderanabe ndi anthu a Yehova kunali kofunika kwambiri. Chifukwa cha khama la anthu olimba mtima, tinkatha kulandira chakudya chauzimu ndiponso malangizo othandiza.

Chaka chotsatira, mu 1948, ndinabatizidwa usiku m’nyanja yaying’ono yapafupi ndi kwathu. Anthu okabatizidwa onse anasonkhana kunyumba kwathu, koma chifukwa chakuti unali usiku ndiponso kuti zonse zinkachitika mobisa kwabasi, sindinadziŵe kuti iwo anali ndani. Okabatizidwafe sitinali kulankhulana. Sindinadziŵe amene anakamba nkhani yaubatizo, kundifunsa mafunso aubatizo tili chiimire m’mbali mwanyanja, kapena amene anandibatiza. Patapita zaka zambiri ndithu, ine ndi mnzanga wina tinkakumbana ndipo tinazindikirana kuti tonse tinali m’gulu lomwe linabatizidwa usiku umenewo!

Mu 1949 Mboni za ku Ukraine zinalandira kalata yochokera ku Brooklyn yowalimbikitsa kuti apemphe boma la Moscow kuti liloleze mwalamulo ntchito yolalikira ku Soviet Union. Motsatira malangizowo, pempholo linatumizidwa kudzera mwa nduna ya za m’dziko kupita ku komiti yaikulu ya m’bungwe lotchedwa Supreme Soviet la ku U.S.S.R. Kenako, Mykola Pyatokha ndi Ilya Babijchuk anapemphedwa kupita ku Moscow kukatenga yankho la boma papempho lathulo. Iwo anavomera ndipo anapita ku Moscow m’nthaŵi yachilimweyo.

Mkulu wa boma amene analandira alendo aŵiriwa anamvetsera mwatcheru pomwe ankam’fotokozera zolinga zochokera m’Baibulo za ntchito yathu. Iwo analongosola kuti ntchito yathu inkachitika pofuna kukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Komabe, mkulu wa bomayo ananena kuti boma silingatilole m’pang’ono pomwe.

Mbonizo zinabwerera kwawo ndipo zinapita ku mzinda wa Kiev womwe ndi likulu la dziko la Ukraine kukapempha kuti ntchito yathu iloledwe mwalamulo ku Ukraineko. Nawonso akuluakulu a boma akumeneko anakana pempholo. Iwo ananena kuti Mboni za Yehova zingasiye kuvutitsidwa pokhapokha ngati zitayamba kuchirikiza dziko. Iwo anati Mboni zinkafunikira kumenya nawo nkhondo ndiponso kuchita nawo chisankho. Kachiŵirinso, Mbonizo zinafotokoza kuti siziloŵerera nkhani zotere, kutanthauza kuti potsatira Mbuye wathu Yesu Kristu, sitikhala mbali ya dziko.—Yohane 17:14-16.

Ndiyeno zitatero, mbale Pyatokha ndi mbale Babijchuk anamangidwa, kuimbidwa mlandu, ndipo kuweruzidwa kuti akakhale m’ndende zaka 25. Pasanapite nthaŵi mu 1950, Mboni zambiri, kuphatikizapo abambo anga zinatengedwa ndi akuluakulu a boma. Abambo anga analamulidwa kukhala m’ndende zaka 25 ndipo anatumizidwa ku Khabarovsk chakum’maŵa kwa Soviet Union pafupifupi makilomita 7,000 kuchokera kwathu!

Anatitengera ku Ukapolo ku Siberia

Kenaka mu April 1951, boma la Soviet linakonza zoti Mboni zizunzidwe m’mayiko akumadzulo omwe tsopano ndi Latvia, Estonia, Lithuania, Moldova, Belarus, ndi Ukraine. M’mwezi umenewo anthu okwana 7,000 kuphatikizapo ine ndi amayi, tinatumizidwa ku ukapolo ku Siberia. Asilikali anangobwera kunyumba kwathu usiku kudzatitenga kupita nafe kokwerera sitima. Kumeneko anatitsekera m’mabogi onyamula ng’ombe, momwe ankatiika anthu pafupifupi 50 m’bogi imodzi, ndipo titayenda masabata oposa aŵiri, tinakatsika pamalo otchedwa Zalari amene ali pafupi ndi nyanja ya Baikal m’boma la Irkutsk.

Titaimirira pachipale chofeŵa mphepo yozizira kwabasi ikuwomba komanso asilikali onyamula zida atatizinga, ndinkadzifunsa kuti kaya chitichitikire n’chiyani. Kodi ndikwanitsa bwanji kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova kunoko? Tinayamba kuimba nyimbo za Ufumu kuti tisamve kuzizidwa. Kenako mamanijala amakampani a boma akumeneko anafika. Ena ankafuna amuna kuti azikagwira ntchito yofunika chamuna, pamene ena ankafuna amayi kuti azikasamala ziŵeto. Ine ndi mayi anga tinatengedwa kupita ku malo omwe ankamangako malo amphamvu zamagetsi otchedwa Tagninskaya Hydroelectric Power Station.

Titafika, tinaona mizera ya nyumba zopangidwa ndi matabwa zomwe akapolo ankagonamo. Ine ndinapatsidwa ntchito yoyendetsa thalakita komanso yokonza zinthu zamagetsi, ndipo amayi anapatsidwa ntchito yolima kumunda. Ifeyo anatiika m’gulu la anthu othamangitsidwa m’dziko osati akaidi. Motero tinkaloledwa kukayenda chapafupi pompo koma ankatikaniza kukayenda kumudzi wina womwe unali pa mtunda wa makilomita asanu ndi atatu kuchokera pamalopo. Akuluakulu a boma anatikakamiza kuti tisaine chikalata chosonyeza kuti tidzakhala kumeneko mpaka kalekale. Kwa mnyamata wazaka 19 ngati ine imeneyo inali nthaŵi yaitali kwambiri moti ndinakana kusaina. Komabe, tinakhala m’deralo kwa zaka 15.

Ku Siberia kumeneko, malire ndi dziko la Poland sanalinso pamtunda wokwana makilomita asanu ndi atatu okha kuchokera kumene kunali ife koma anali kutali makilomita oposa 6,000! Mbonife tinayesetsa kupanganso mipingo ndiponso kusankha amuna otsogolera. Poyamba, tinalibe mabuku ofotokoza Baibulo kupatulapo makope ena angapo amene Mboni zina zinatha kubwera nawo kuchokera ku Ukraine. Makope ameneŵa ankalembedwanso pamanja ndipo tinkagaŵana.

Posakhalitsa tinayamba kuchita misonkhano. Popeza kuti ambirife tinkakhala m’misasa nthaŵi zambiri tinkakumana usiku. Mpingo wathu unali ndi anthu 50, ndipo ine ndinaikidwa kuti ndizichititsa Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Mumpingo wathu munali abale ochepa, choncho alongo analinso kukamba nkhani za ophunzira. Mipingo ya Mboni za Yehova kulikonse inauzidwa kuchita zimenezi m’chaka cha 1958. Onse ankachita mopanda chibwana mbali zomwe apatsidwa, pakuti ankaona sukuluyo monga njira yotamandira Yehova ndiponso yolimbikitsira anthu ena mumpingo.

Utumiki Wathu Unadalitsidwa

Popeza kuti tinkakhala limodzi ndi anthu omwe si a Mboni, tsiku silinali kungopita osalankhula ndi ena za chikhulupiriro chathu ngakhale kuti kunali koletsedwa kutero. Joseph Stalin yemwe anali nduna yayikulu ya dziko la Soviet atamwalira mu 1953, zinthu zinasintha ndithu. Tsopano tinkaloledwa kulankhula poyera ndi anthu ena za zikhulupiriro zathu za m’Baibulo. Titalankhulana ndi anzathu ku Ukraine, tinadziŵa kumene Mboni zina zinali m’dera lathulo ndipo tinagwirizananso. Zimenezi zinachititsa kuti tigaŵe mipingo yathu m’madera.

Mu 1954, ndinakwatira Olga yemwenso anali wogwidwa ukapolo wochokera ku Ukraine. Kwazaka zambiri iye anakhala akundichirikiza kwambiri muutumiki wanga kwa Yehova. Stepan amene anaphedwa m’malire a dziko la Ukraine ndi Poland uja mu 1947, anali m’chimwene wake wa Olga. Kenako, tinabala mwana wamkazi dzina lake Valentina.

Olga ndi ine tinapeza madalitso ochuluka muutumiki wathu wachikristu ku Siberia. Mwachitsanzo, tinakumana ndi George yemwe anali mkulu wa gulu linalake la mpingo wa Baptist. Tinkam’chezera pafupipafupi ndiponso tinkaphunzira naye magazini a Nsanja ya Olonda aliwonse omwe analipo. George anayamba kuyamikira kuti zomwe atumiki a Yehova anali kulalikira kuchokera m’Baibulo ndizo zinalidi zoona. Tinayambanso kuphunzira ndi anzake ena ambiri a mpingo wa Baptist. Zinalitu zosangalatsa kwabasi kwa ife kuona George ndi anzake angapo akubatizidwa n’kukhala abale athu auzimu!

Mu 1956, ndinaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda, ntchito yomwe inkafuna kuti ndizichezera mipingo m’dera lathulo sabata iliyonse. Ndinkagwira ntchito tsiku lonse kenako madzulo ndinkanyamuka panjinga yanga yamoto kukachezera mpingo. Ndinali kubwerako m’mamaŵa wake n’kupita kuntchito. Mykhailo Serdinsky yemwe anaikidwa kuti azindithandiza m’ntchito yoyendayendayi anafa pangozi yapamsewu mu 1958. Iye anamwalira Lachitatu, komabe tinachedwetsa kuika malirowo mpaka Lamlungu kuti tipatse a Mboni ambiri mwayi woti adzakhalepo.

Pamene gulu lathu lomwe linali lalikulu linayamba kuyenda kupita kumanda, mamembala a gulu lachitetezo cha boma anatitsatira. Tidakati tikambe nkhani yokhudza chiyembekezo cha m’Baibulo cha chiukiriro ndiye kuti tidakatha kumangidwa. Komabe ine ndinadzikakamiza kukamba za Mykhailo ndiponso chiyembekezo chake chabwino kwambiri cham’tsogolo. Ngakhale kuti ndinagwiritsa ntchito Baibulo, gulu lachitetezo cha bomalo silinandimange. Zikuoneka kuti iwo anaganiza kuti palibe phindu ngati atandimanga popeza kuti ankandidziŵa bwino chifukwa choti ndinali “kabwerebwere” ku malikulu awo kukayankha mafunso.

Kuperekedwa Ndi Kazitape

Mu 1959 gulu lachitetezo laboma linamanga Mboni 12 zimene zinkatsogolera ntchito yolalikira. Anthu ena ambiri anaitanidwa kukayankha mafunso ndipo ine ndinali m’gululo. Itafika nthaŵi yanga yoti ndiyankhe mafunso ndinadabwa kumva akuluakulu a boma akutchula mwatsatanetsatane zinsinsi zina zokhudza ntchito yathu. Kodi iwo anadziŵa bwanji zinthu zimenezo? Zinaonekeratu kuti panali wina amene ankadziŵa bwino za ife amenenso wakhala akugwira ntchito yaboma kwa nthaŵi yaitali.

Anthu 12 amene anamangidwawo anawaika m’maselo ogundizana ndipo iwo anagwirizana kuti asalankhulenso kanthu kalikonse kwa akuluakulu a bomawo. Mwakutero, kazitapeyo anayenera kubwera yekha kukhoti kuti adzapereke umboni pankhaniyo. Ngakhale kuti ine sanandipeze ndi mlandu, ndinapita nawo kukhoti kuti ndikaone zomwe zikachitike. Woweruza anafunsa mafunso, koma anthu khumi ndi aŵiriwo sanayankhe. Kenako, wa Mboni wotchedwa Konstantyn Polishchuk yemwe ndinkamudziŵa kwazaka zambiri anabwera kudzapereka umboni woneneza anthu khumi ndi aŵiriwo. Mlanduwo unathera poti Mboni zina zinaweruzidwa kukakhala m’ndende. Titatuluka panja pa khotilo, ndinakumana ndi Polishchuk uja.

Ndinam’funsa kuti, “n’chifukwa chiyani ukutipereka?”

“Chifukwa chakuti sindinenso wokhulupirira,” iye anayankha motero.

“Kodi sukukhulupiriranso chiyani?” ndinam’funsa motero.

“Sindingadzakhulupirirenso Baibulo,” iye anayankha.

Polishchuk akanatha kundiperekanso ine, koma mu umboni wakewo sanatchulemo dzina langa. Motero ndinam’funsa chifukwa chimene sananditchulire.

“Sindifuna kuti iwe upite kundende,” iye anatero. “Ndimadzimvabe kukhala ndi mlandu pa imfa ya mlamu wako Stepan. Ndine amene ndinam’tuma usiku uja umene anaphedwa. Ndimamvadi chisoni kwambiri chifukwa cha zimenezo.”

Mawu ameneŵa anandizunguza mutu kwambiri. Chikumbumtima chake chinalidi chitasokonezeka bwanji! Ankadandaula chifukwa cha imfa ya Stepan, koma iye yemweyo apa anali kupereka atumiki a Yehova. Kuchokera nthaŵiyo sindinamuonenso Polishchuk. Iye anamwalira miyezi ingapo yotsatira. Koma ine, ndinakhumudwa kwambiri kuona munthu amene ndinkam’khulupirira kwa zaka zambiri akupereka abale athu. Komabe, zimenezi zinandipatsa phunziro lofunika kwambiri: Polishchuk anakhala wosakhulupirika chifukwa chakuti anasiya kuŵerenga ndiponso kukhulupirira Baibulo.

Ndithudi tiyenera kukumbukira phunziro ili nthaŵi zonse kuti: Ngati tikufuna kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova tiyenera kumachita phunziro la Malemba Opatulika mosadumphadumpha. Baibulo limati: ‘Chinjiriza mtima wako pakuti magwero a moyo atulukamo.’ Komanso, mtumwi Paulo anauza Akristu kuti azichenjera. Chifukwa? ‘Kuopera kuti ungayambe mwa wina wa iwo mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.’—Miyambo 4:23; Ahebri 3:12.

Kubwerera ku Ukraine

Pamene ukapolo wathu ku Siberia unatha mu 1966, Olga ndi ine tinabwerera ku Ukraine, ku tauni yotchedwa Sokal, yomwe ili pamtunda wamakilomita 80 kuchokera ku L’viv. Tinali ndi ntchito yaikulu chifukwa chakuti ku Sokal ndiponso m’matauni ena ozungulira Cervonograd kunali Mboni zokwana 34 zokha basi. Tsopano m’derali muli mipingo 11!

Olga anamwalira ali wokhulupirika mu 1993. Patatha zaka zitatu ndinakwatira Lidiya, ndipo kuchokera nthaŵiyo iyeyu wakhala akundilimbikitsa. Komanso, mwana wanga wamkazi Valentina ndi banja lake ndi atumiki achangu a Yehova ndipo nawonso akhala akundilimbikitsa. Komabe, chimene chikundisangalatsa kwambiri mpaka pano n’chakuti ndakhalabe wokhulupirika kwa Yehova, Mulungu amene amachita mokhulupirika.—2 Samueli 22:26.

Alexei Davidjuk anamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova pa February 18, 2000 nkhani ino ili m’kati mokonzedwa kuti ifalitsidwe.

Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 28]

Mpingo wathu womwe unkasonkhana m’misasa chakum’maŵa kwa Siberia mu 1952

[Chithunzi patsamba 31]

Sukulu yathu ya Utumiki Wateokalase mu 1953

[Chithunzi patsamba 31]

Mwambo wamaliro a Mykhailo Serdinsky mu 1958

[Chithunzi patsamba 32]

Ndi mkazi wanga Lidiya