Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhalabe Okhulupirika mu Ulamuliro Wankhanza

Kukhalabe Okhulupirika mu Ulamuliro Wankhanza

Kukhalabe Okhulupirika mu Ulamuliro Wankhanza

YOSIMBIDWA NDI MICHAEL DASEVICH

“Ku Germany tinkapha Mboni za Yehova. Ukuiona mfuti iyo?” anandifunsa motero mkulu wa apolisi a Gestapo uku akuloza mfuti imene inali pakona. “Ndikhoza kukubaya ndi mpeni ndipo sindingapalamule.”

Munali mu 1942 dziko lathu lili mu ulamuliro wa Nazi pamene anandiopseza motero ndili ndi zaka 15 zokha.

NDINABADWA mu November m’chaka cha 1926 m’mudzi waung’ono wapafupi ndi Stanislav (umene tsopano umatchedwa Ivano-Frankivs’k), umene kale unali mbali ya Poland. Mu nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, kuyambira September 1939 mpaka May 1945, dera lathuli linatengedwa koyamba ndi Soviet Union, kenako kwakanthaŵi linatengedwa ndi Germany, pomalizira pake linatengedwanso ndi Asovieti. Nkhondo itatha unakhala mbali ya Soviet Socialist Republic la Ukraine, ndipo Soviet Union itatha mu 1991, unakhala mbali ya Ukraine.

Bambo anga a ku Poland ndi mayi anga a ku Belorussia anali a tchalitchi cha Greek Catholic. Komano, mu 1939, amayi aŵiri amene anali m’gulu la Mboni za Yehova 30 za m’mudzi wapafupi wa Horyhliady anatipatsa kabuku kakuti Universal War Near (Nkhondo Yapadziko Lonse Yayandikira). Kanafotokoza zochitika zimene ndinkaziona zikuchitika. Choncho, pamene kabukuko kanafunsa kuti, “Kodi kwenikweni n’chifukwa chiyani anthu akuchita nkhondo?” ndinagwira mafotokozedwe a m’Baibulo amene kabukuko kananena.

Ku Ukraine vuto lathu silinali nkhondo yokha. Kunalinso chilala choopsa. Mfundo za nduna yaikulu ya ku Soviet, Joseph Stalin zinapangitsa kuti titumizidwe ku Russia. Mavuto amene ndinaona anandichititsa kusanthula Baibulo mosamala. Ndinapempha Mboni ina ku Horyhliady kuphunzira nane Baibulo.

Mudzi wathu wa Odajiv uli kutsidya la mtsinje wa Dniester kuchokera ku Horyhliady, ndipo kangapo pamlungu, ndinkakwera boti laling’ono kuwoloka mtsinjewo kukaphunzira Baibulo. Mu August 1941, ine, mlongo wanga Anna ndi anthu ena aŵiri tinabatizidwa mu mtsinje umenewo.

Apolisi a Gestapo Anandipanikiza ndi Mafunso

Ulamuliro wa Germany unayamba mu 1941, ndipo ngakhale kuti anapitirizabe kutiwopseza, sitinasiye ntchito yathu yachikristu. Chaka chotsatira nditayamba kuchita upainiya, ndinkayenda panjinga. Mosakhalitsa ndinakumana ndi wapolisi wa Gestapo wa ku Germany amene ndam’tchula koyambirira uja. Nazi zimene zinachitika.

Tsiku lina ndikubwerera kunyumba kuchokera ku utumiki, ndinapita kukaona Akristu anzanga aŵiri, mayi winawake ndi mwana wake wamkazi. Mwamuna wa mwana wamkaziyo ankatsutsa kwambiri chikhulupiriro chathu ndipo ankafunitsitsa kudziŵa kumene mkazi wake ankatenga mabuku ake onena za Baibulo. Tsiku limenelo ndinanyamula mabuku komanso malipoti a utumiki a Akristu anzanga. Mwamuna wakeyo anandiona ndikutuluka m’nyumba yawo.

“Ima!” Anakuwa motero. Ndinanyamula chikwama changa n’kuliyatsa liŵiro.

“Ima! Wakubayo!” Anafuula motero. Ogwira ntchito m’munda anaganiza kuti chilipo chimene ndaba, choncho anandikakamiza kuti ndiime. Mwamunayo ananditengera ku polisi, kumene kunali mkulu wa apolisi a Gestapo.

Ataona buku m’chikwama changa, mkuluyo anafuula m’Chijeremani kuti: “Rutherford! Rutherford!” Sindinafunikire munthu kuti andiuze chimene chinam’zunguza mutu munthu ameneyu. Dzina la Joseph F. Rutherford, amene anali pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, linali kulembedwa patsamba la ofalitsa la mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Choncho mwamunayo anandiimba mlandu wakuti ndinali kunyengana ndi mkazi wakeyo. Apolisi ndi mkulu wa Gestapo anaona kuti izi zinali zam’kutu, chifukwa mkazi wakeyo anali wamkulu zedi usinkhu wa mayi anga. Ndiyeno anandigundikiza nawo mafunso.

Anafuna kudziŵa dzina langa, kwathu ndiponso kwenikweni kumene ndinatenga mabukuwo. Koma sindinaulule. Anandimenya kangapo konse ndiponso kundiseŵeretsa, atatha zimenezi ananditsekera m’selo. Ndinafunsidwa masiku atatu otsatira. Kenako ananditengera ku ofesi ya mkulu wa apolisi a Gestapo, kumene anandiopseza kuti andibaya ndi mpeni wake. Kwa mphindi zingapo sindinadziŵe kuti kaya achita zimene amanenazo kapena ayi. Ndinaŵeramitsa mutu pansi, tonse tinangoti duu kwakanthaŵi ndithu. Ndiyeno modzidzimukira anangoti: “Zipita.”

Mutha kuona kuti panthaŵi imeneyo, zinali zovuta kwambiri kuti tilalikire komanso kuti tichite misonkhano. Tinachita mwambo wapachaka wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu pa April 19, 1943, pogwiritsa ntchito zipinda ziŵiri za nyumba ya ku Horyhliady. (Luka 22:19) Tili pafupi kuyamba msonkhano wathu, tinamva phokoso losonyeza kuti apolisi anali kubwera kufupi ndi nyumbayo. Ena tinabisala m’munda, koma m’chemwali wanga Anna ndi alongo ena atatu anabisala m’chipinda cha pansi. Apolisi anawapeza momwemo ndipo anawatulutsa m’modzim’modzi kukawafunsa. Anawazunza kwambiri, ndipo m’modzi mwa iwo anam’vulaza zedi.

Zinthu Zisintha

M’chaka cha 1944 munthaŵi yachilimwe, Ajeremani anabwerera ndipo Asovieti anabwerera m’dera lathu. Monga atumiki a Yehova, tinasungabe mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zimene tinagwiritsa ntchito mu ulamuliro wa Nazi. Tinakana kutenga mbali m’zankhondo kapena m’ndale. Kukhulupirika kwathu pamfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zimenezi mosakhalitsa kunayesedwa.—Yesaya 2:4; Mateyu 26:52; Yohane 17:14.

M’masiku angapo, Asovieti anayamba kukakamiza anyamata kuti awalembe usilikali. Zinthu zinafika povuta kwambiri chifukwa choti, si Asovieti okha amene amafuna kulemba anthu usilikali. Anthu ogalukira a ku Ukraine anafunanso anyamata m’deralo, amene ankapita nawo ku nkhalango kukawaphunzitsa nkhondo. Choncho, a Mbonife tinali pavuto zedi lofuna kusonyeza kuti sitikuchirikiza gulu lililonse pa magulu aŵiri otsutsana ameneŵa—la Asovieti ndi la anthu ogalukira.

Magulu aŵiri ameneŵa anamenyana m’mudzi mwathu, ndipo anthu ogalukira aŵiri anaphedwa n’kusiyidwa mumsewu wapafupi ndi nyumba yathu. Akuluakulu a Asovieti anabwera ku nyumba yathu kudzafunsa ngati tinkawadziŵa anthu amene anaphedwawo. Akuluakulu amene anabwerawo anaganiza zoti anditenge kukandilemba m’gulu lawo la asilikali, limene linali gulu lalikulu la asilikali a ku Poland. Chifukwa chakuti ndinali wa ku Poland, ndinayenera kulembedwa m’gululi.

Ine pamodzi ndi Mboni zina zinayi, tinakana kulembedwa usilikali, choncho anatitenga pa sitima kupita nafe ku Dnipropetrovs’k mzinda womwe uli pamtunda wa makilomita 700 chakum’maŵa. Kumeneko, titafotokoza kuti sitingaloŵe usilikali chifukwa cha zikhulupiriro zathu za m’Baibulo, anatimanga uku tikudikira kuti agamule mlandu wathu. Titakaonekera m’khoti, tinaona kuti wapolisi yemwe ankafufuza mlanduwo anali m’Yuda. Podziteteza tinalongosola zikhulupiriro zathu, ndipo wapolisiyo anamvetsera kwambiri. Tinafotokoza zinthu zimene tinkadziŵa kuti zim’sangalatsa, kuphatikizapo kuzunzidwa kwa Aisrayeli ndi kuwomboledwa kwawo ku Igupto kudzera mwa Mose.

M’miyezi imene akhoti anatenga kuti agamule mlandu wathu, tinali titaikidwa m’selo momwe munali anthu ena pafupifupi 25. Atamva kuti tinakana kuloŵa usilikali, anafuula kuti: “Ndinu abale athu!” Komabe, titakhala pang’ono, tinaona kuti sanali a Mboni koma anali a Baptist. Ankafuna kuloŵa usilikali, koma anamangidwa chifukwa chokana kugwira zida za nkhondo.

Mu May 1945, tidakali m’manja mwa apolisi ku Dnipropetrovs’k, tsiku lina tinadzuka pakati pausiku chifukwa cha kulira kwa mfuti ndi kukuwa kwa anthu kumene kunkachokera ku nyumba za asilikali ndi m’misewu. Sitinadziŵe kuti kaya chinali chipolowe, nkhondo, kapena chikondwerero. M’maŵa mwake pachakudya cham’maŵa, tinamva nkhani kuchokera m’kanyumba kometeramo tsitsi kuti: Nkhondo yatha! Patapita nthaŵi pang’ono, khoti linagamula mlandu wathu. Tinalandira chilango chofanana ndi a Baptist chomwe chinali kukhala zaka 10 mu msasa wandende.

Kumsasa Wandende wa ku Russia

A Mboni asanufe tinaikidwa mu msasa wandende wa ku Russia. Titatha milungu iŵiri tili paulendo wa pa sitima ya pamtunda, tinakatsika pa Sukhobezvodnoje tauni imene ili pamtunda wa makilomita 400 kum’maŵa kwa Moscow. Pa Sukhobezvodnoje panali palikulu loyang’anira misasa yachibalo ina 32 imene inali mphepete mwa njanji. Msasa uliwonse unkasunga anthu ambiri zedi. Patapita miyezi isanu ndi umodzi tili ku Sukhobezvodnoje, ananditumiza kumsasa wa nambala 18. Okhala kumeneko ambiri anali apandu kapena oukira boma.

Akuluakulu a boma anatipatsa ntchito yodula mitengo, imene inali ntchito yowawa kwambiri. Nthaŵi zina tinkadutsa m’zitunda zazitali za chipale chofeŵa, kudula mitengo ndi sowo yaing’ono, kenako n’kumaguza mtengowo kudutsa nawo pachipale chofeŵa. Kamodzi pamlungu, tsiku Lamlungu tikadya chakudya cha m’maŵa, ndinali ndi mpata wokambirana nkhani za m’Baibulo ndi a Mboni ena anayi omwe analinso mumsasawo. Imeneyi ndiyo inali misonkhano yathu. Chaka china mwambo wa Chikumbutso tinachitira m’chipinda chosambiramo. Tinagwiritsa ntchito madzi a zipatso zakuda chifukwa chakuti tinalibe vinyo woti n’kugwiritsa ntchito ngati chizindikiro cha mwazi wa Yesu.

Maganizo odzimva kuti ndili ndekha anali kukula kwambiri. Ndinam’khuthulira Yehova mtima wanga, amene anandilimbitsa monga anam’limbitsira Eliya pamene mneneriyo anali ndi nkhawa yofananayo. (1 Mafumu 19:14, 18) Mulungu anandithandiza kuona kuti sitinali tokha. Iye analidi mzati waukulu, wolimba m’moyo wanga, ngakhale m’nthaŵi zovuta ngati zimenezo.

M’misasa ina yapafupi ndi Sukhobezvodnoje uliwonse unali ndi a Mboni angapo, ndipo kaŵirikaŵiri tinkatha kulankhulana nawo kupyolera mwa wa Mboni wina amene ntchito yake inam’theketsa kumafika m’misasa yonse. Iyeyu anali ngati m’khala pakati, wobweretsa ndiponso kutulutsa mabuku m’misasa. Izi zinachititsa kuti tizibwerekana mabuku ochepa amene tinali nawo. Zimenezi zinalidi zolimbikitsa zedi!

Kubwereranso ku Ukraine

Mwalamulo lolengezedwa ndi Boma, chilango changa chokhala mumsasa wandende chinachepetsedwa kuchoka pa zaka 10 kufika pa zisanu. Choncho, mu April 1950, ndinabwerera ku mpingo wa kwathu ku Horyhliady. Ntchito yathu ku Ukraine inali idakali yoletsedwa, ndipo zinali zovuta kwambiri kuchita utumiki. Komabe mapindu analinso ochuluka kwambiri.

Nditangobwerera kumudzi, ndinalankhula ndi mwamuna wina dzina lake Kozak, amene ankakhala m’mudzi wotchedwa Zhabokruky, womwe unali pamtunda wa makilomita 20 kuchokera kwathu. Ndinam’funsa mmene moyo wake ndi wabanja lake unalili. Ndinkadziŵa kuti anthu olima m’minda ya boma ankavutika kupeza zofunika pamoyo wawo, choncho ndinadziŵa kuti funso ngati limeneli lingakhale labwino kwambiri kuyambira kukambirana. Ndinafotokoza kuti Baibulo linaneneratu za njala ndi nkhondo zochitika m’nthaŵi yathu. (Mateyu 24:3-14) Iye anafuna kudziŵa zochuluka. Chotero ndinam’pitiranso kachiŵiri. Mlungu uliwonse ndinkayenda mtunda wa makilomita 40 kapena kuposa pamenepo kupita ku Zhabokruky kukachititsa phunziro la Baibulo ndi banja la Kozak. Banja la Kozak litabatizidwa mu August 1950, tinaiŵala mavuto onse popanda kutchula kuchuluka kwa nthaŵi imene tinawononga.

Banja la Kozak litangobatizidwa kumene linatengedwa ukapolo pamodzi ndi Mboni zina zochuluka. Asilikali onyamula zida za nkhondo ndiwo anasonkhanitsa anthuwo pamodzi chakumayambiriro kwa April 1951 ndipo asanawaimbe mlandu kapena kuwafunsa, anawatumiza ku Siberia. Kumeneku banja la Kozak ndi anzanga ena ambiri anakakamizika kupeza nyumba zawo zatsopano. *

Mwa mabanja 15 a Mboni amene anali ku Horyhliady, mabanja 4 okha ndi amene anatengedwa ukapolo. Komabe, m’mipingo ina, chiŵerengero cha Mboni zimene zinagwidwa chinali chochuluka kwambiri. Kodi magulu ameneŵa ankagwidwa bwanji? Eya, akuluakulu a boma anali ndi ndandanda ya mayina a Mboni chotero ankatha kusonkhanitsa chiŵerengero cha anthu ochuluka momwe iwo akufunira. Zikuoneka ngati ndandandayo inalembedwa mu 1950, nthaŵi imene ndinali ku msasa wandende ku Russia, choncho dzina langa panalibe. Mwezi umodzi zimenezi zisanachitike, mu March 1951, ndinakwatira Fenia, mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Banja la Fenia lonse linagwidwa ukapolo, koma vuto limeneli silinam’khudze chifukwa tinali titakwatirana chotero anali atasintha dzina kutenga dzina langa, limene panalibe pa ndandandayo.

Ziyeso Zovuta za Chikhulupiriro

Atatha kuwasamutsa, tonse amene tinatsala kumudzi tinalinganizanso ntchito. Ndinapemphedwa kuti ndiziyang’anira mipingo ya m’chigawo chapafupi cha Ivano-Frankivs’k, kumene ngakhale anthu anali atasamutsidwako, mu mpingo uliwonse pa mipingo 15 ya kumeneko munali mutatsala Mboni 30. Monga kalipentala wodziimira, ndinali ndi ndandanda yabwino yotha kusinthika, choncho ndinkatha kukumana mobisa ndi abale mumpingo uliwonse kamodzi pamwezi.

Kaŵirikaŵiri tinkakumana usiku kumanda kumene tinkaona kuti tiliko tokha. Nkhani yaikulu imene timakambirana inali ya mmene tingachitire kuti tionetsetse kuti mipingo yonse ili ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo. Nthaŵi zina timalandira magazini yatsopano ya Nsanja ya Olonda, ya m’chilankhulo cha ku Poland kapena cha ku Romania ndipo timaimasulira m’chilankhulo cha ku Ukraine. Komabe, akuluakulu a boma nthaŵi zonse ankatilondalonda, kuyesa kupeza ndi kuwononga makina athu achikale osindikizira.

Koma vuto lathu lalikulu linali lakuti tinali olekanitsidwa ndi abale athu achikristu a m’mayiko ena, kuphatikizapo amene anali ku Brooklyn, New York, amene anali kutsogolera ntchito yathu yachikristu. Chotsatira chake chinali chakuti nthaŵi zambiri mipingo yathu inkakambirana za mikangano, mphekesera, ndiponso kukonzerana zichiwembu. Mboni zina zinachoka m’gululi n’kukayambitsa timagulu totsutsa. Kunafala nkhani zabodza ndiponso zoipitsa anthu ena ngakhale amene amatsogolera ku Brooklyn.

Choncho, ambirife ziyeso zathu zovuta za chikhulupiriro si zinali chifukwa cha kuzunzidwa ndi otsutsa koma mikangano ya m’mipingo momwemo. Ngakhale kuti ena anasankha kuti sapitiriza kulambira nafe, tinadziŵa kuti n’kofunika kumamatirabe ku gulu ndi kudikira Yehova kuti akonza zinthu. N’zosangalatsa kuti, ambiri a Mboni za m’dera lathu anachita zimenezi. N’zosangalatsanso kuti ambiri mwa anthu amene anachoka m’gulu anazindikira kulakwa kwawo kenako anabwerera kudzatumikira nafe Yehova.

Ngakhale m’nthaŵi zovuta zokhala patokha zimenezo, tinakhalabe otanganidwa muutumiki wapoyera ndipo tinadalitsidwa kwambiri. Ndipo si madalitso ake amene taona! Nthaŵi iliyonse ndikafika pa Phunziro la Buku la Mpingo, ndimakumbuka madalitso a Yehova. Aliyense wa anthu 20 kapena kuposerapo a m’gulu lathu la phunziro anaphunzitsidwa choonadi ndi a m’banja langa.

Makolo anga ndi mlongo wanga Anna, onse anamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova. Ine ndi Fenia tikutumikirabe Yehova mwachangu. Nthaŵi yapitadi mofulumira. M’zaka 30 zapitazo, Mboni za Yehova ku Ukraine zakumana ndi zinthu zosangalatsa zimene sizingatheke kuzifotokoza m’nkhani yochepayi. Koma ndikayang’ana m’mbuyo ndimakhutitsidwa ndi kutumikira kwanga Yehova zaka zambiri, ndili ndi chikhulupiriro kuti adzakhalabe mzati wanga wolimba ndi m’chirikizi wanga, pakuti iye mwini amati: “Ine Yehova sindisinthika.”—Malaki 3:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 32 Onani nkhani yakuti “Zaka Zoposa 40 Tili Oletsedwa Kupembedza mu Ulamuliro wa Chikomyunizimu,” mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1999 patsamba 24-9, ndiponso yakuti “Pamene Anatitengera ku Ukapolo ku Siberia!” mu Galamukani! wa May 8, 1999 patsamba 20-5.

[Chithunzi patsamba 20]

Ine ndi Fenia mu 1952

[Chithunzi patsamba 22]

Ndi Fenia masiku ano