Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Maseŵera Angozi”—Kodi Muyenera Kuika Moyo Wanu Pachiswe Mwakuwachita?

“Maseŵera Angozi”—Kodi Muyenera Kuika Moyo Wanu Pachiswe Mwakuwachita?

Lingaliro la Baibulo

“Maseŵera Angozi”—Kodi Muyenera Kuika Moyo Wanu Pachiswe Mwakuwachita?

“MASIKU ANO AMBIRI A IFE TASIYA KUNGOONERERA CHABE MASEŴERA, TIKUFUNA KUMAULUKA TOKHA M’MALELE NDI PALACHUTI, KUMATSETSEREKA M’MAPIRI, KUMAPALASA BWATO PAMATHITHI AMADZI, NDIPONSO KUMASAMBIRA PAMODZI NDI NSOMBA ZAZIKULU ZOTCHEDWA SHARK PANSI PA NYANJA.”—INATERO NDI NYUZIPEPALA YOTCHEDWA WILLOW GLEN RESIDENT.

MAWU ameneŵa akufotokoza khalidwe lomwe likukulirakulira pazamaseŵera. Kutchuka kwadzaoneni kwa maseŵera monga kudumpha m’ndege, kukwera pachipale chofeŵa, kuuluka m’malele ndi palachuti ndiponso kudumpha kuchoka pamwamba pa zinthu zina kotchedwa BASE *, kukusonyeza kuti dziko lili ndi chilakolako chofuna kuika moyo pachiswe. Zitsulo zomwe amavala kumapazi akamatsetsereka pachipale chofeŵa, njinga zamagiya, nsapato zamatayala ndiponso zinthu zina zamtunduwu zimathandizanso oseŵerawo kuyesetsa mopitirira mphamvu za thupi lawo kulimbana ndi mapiri otsetsereka kwabasi, zitunda zazitali koposa, ndiponso kudumpha pamwamba kwambiri. Monga inanenera magazini ya Time, kutchuka kwadzaoneni kwa “maseŵera angozi” amene oseŵera ake amaika moyo wawo pachiswe, kukusonyeza kuti anthu miyandamiyanda ali ndi chilakolako chofuna “kuseŵera paulimbo.” Anthu ochita maseŵerawa pa Loŵeruka ndi Lamlungu lokha ngakhalenso akatswiri akadziika paulimbo chonchi amakhudzidwa ndi zinthu monga ngozi, luntha, ndiponso mantha pofunitsitsa kuchita zinthu zimene sanachitepo.

Komabe, kutchuka kwadzaoneni kwa maseŵeraŵa kumadzetsanso mavuto ena aakulu. Anthu ochulukirachulukira amavulala pamene akuchita mopambanitsa maseŵera ena osavulaza kwenikweni. M’chaka cha 1997 m’zipatala za ku United States, chiŵerengero cha anthu opita kuchipinda cha anthu ovulala pangozi chinakwera kwambiri moti anthu ovulala pamaseŵera otsetsereka m’mapiri kapena pamaseŵera ena amtunduwu anawonjezeka ndi maperesenti oposa 33, ndipo ovulala pamaseŵera otsetsereka pachipale chofeŵa anawonjezeka ndi 31 peresenti komanso ovulala pamaseŵera okwera mapiri anawonjezeka ndi 20 peresenti. Anthu enanso ambiri akufa pa zifukwa zokhudzana ndi maseŵera amitundu ina kusonyeza kuti maseŵera amenewonso n’ngoopsa zedi. Anthu amene amachirikiza maseŵerawa amadziŵa ndithu za kuopsa kwa maseŵera otere. Mkazi wina amene amachita nawo maseŵera ena angozi otsetsereka pa chipale chofeŵa otchedwa skiing ananena kuti: “Nthaŵi zonse ndimaganiza za imfa basi.” Katswiri wina wamaseŵera otsetsereka pachipale chofeŵa ananena kuti “ukapanda kuvulala ndiye kuti sukuseŵera mwakhama.”

Poganizira mfundo zimenezi, kodi kuchita nawo maseŵera otereŵa Mkristu ayenera kukuona motani? Kodi Baibulo lingatithandize motani kuganizira ngati n’koyenera kuchita nawo maseŵera angozi ameneŵa? Kuona mmene Mulungu amaonera kupatulika kwa moyo kutithandiza kuyankha mafunso ameneŵa.

Mmene Mulungu Amaonera Moyo

Baibulo limatiuza kuti Yehova ndiye “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) Iye sanangolenga munthu komanso anasamala kwambiri potipatsa zomwe timafuna kuti tisangalale ndi moyo. (Salmo 139:14; Machitidwe 14:16, 17; 17:24-28) Choncho, n’koyenera kunena kuti iye amafuna kuti ife tisamale zimene watipatsa mwachifundo. Malamulo ndiponso mfundo zachikhalidwe zimene anapereka ku mtundu wa Israyeli zimatithandiza kuzindikira mfundo imeneyi.

Chilamulo cha Mose chinkalamula kuti munthu azitsatira malangizo ena ake pofuna kuteteza miyoyo ya anthu anzake. Ngati munthu atafa chifukwa chakuti malangizowo sanatsatidwe, munthu amene akanachititsa kuti ngoziyo ipeŵeke ndiye anali ndi mlandu wakupha munthu. Mwachitsanzo, mwini nyumba ankalamulidwa kumanga kampanda patsindwi la nyumba yake ikakhala yatsopano. Apo ayi, munthu akagwa kuchokera patsindwilo n’kuferatu, mwini nyumbayo anali ndi mlandu wakupha. (Deuteronomo 22:8) Ngati ng’ombe yagunda munthu mwadzidzidzi mpaka kufa, mwini ng’ombeyo analibe mlandu. Komabe, ngati ng’ombeyo inali yodziŵika kuti n’njoopsa ndipo mwini ng’ombeyo anachenjezedwa koma anailekerera, ndiyeno ng’ombeyo n’kugunda munthu wina, ndiye kuti mwini ng’ombeyo ankatha kuzengedwa mlandu wakupha munthu ndipo akanatha kuphedwa. (Eksodo 21:28, 29) Popeza kuti moyo uli wamtengo wapatali kwa Yehova, Chilamulo chake chinali kulemekeza kwambiri njira zochirikiza ndiponso zoteteza moyo.

Atumiki okhulupirika a Mulungu anali kuzindikira kuti malangizo ameneŵa anagwiranso ntchito pa nkhani ya kuika moyo pachiswe. M’nkhani ina ya m’Baibulo, Davide analakalaka kumwa “madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu.” Panthaŵiyo n’kuti Betelehemu akulamulidwa ndi Afilisiti. Atamva pempho la Davide, asilikali ake atatu analoŵerera m’misasa ya Afilisiti kukatunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Kodi Davide anatani? Iye sanamwe madziwo, m’malo mwake, anawathira pansi. Amvekere: “Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kuchita ichi. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wawo, inde akadataya moyo wawo, pakukatenga madziŵa.” (1 Mbiri 11:17-19) Kwa Davide chinali chinthu choipitsitsa kuika moyo pachiswe chifukwa chofuna kudzikhutiritsa.

Yesu anachitanso chimodzimodzi. N’zotheka kuti munali m’masomphenya pamene Mdyerekezi anamuyesa kuti adzigwetse pansi kuchoka pamwamba pa chimbudzi cha kachisi kuti aone ngati angelo angamuteteze kuti asavulale. Yesu anayankha kuti: “Usamuyese Ambuye Mulungu wako.” (Mateyu 4:5-7) Inde, Davide ndi Yesu yemwe anazindikira kuti n’kulakwira Mulungu kuchita zinthu zoika moyo pachiswe.

Poganizira zitsanzo zimenezi, tingafunse kuti ‘Kodi tingasiyanitse bwanji maseŵera angozi ndi amene sali angozi? Pakuti ngakhale maseŵera odziŵika bwino, osaopsa, angathe kuchitidwa moika moyo pachiswe, kodi tingadziŵe motani polekezera?’

Kodi N’ngwoyeneradi Kuwaikira Moyo Pachiswe?

Kupenda moona mtima maseŵera aliwonse amene tingawaganizire kudzatithandiza kuzindikira yankho la funsoli. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ziŵerengero za anthu ovulala pamaseŵerawa n’zotani? Kodi maseŵerawa ndikuwadziŵa mokwanira kapena kodi ndatenga zovala zodzitetezera kuti ndisavulale? Kodi ngati nditagwa, kapena kudumpha mosakwanira, kapena ngati zovala zanga zodzitetezera zitagwa zotsatira zake n’zotani? Kodi ndidzangonyuka kapena ndidzavulala kodetsa nkhaŵa mwina kufa kumene?’

Kuika moyo pachiswe chifukwa cha zosangalatsa kungasokoneze unansi wamtengo wapatali wa Mkristu woona ndi Yehova komanso kuyenerera kwake kulandira maudindo mumpingo. (1 Timoteo 3:2, 8-10; 4:12; Tito 2:6-8) N’zoonekeratu kuti ngakhale pamene akungoseŵera, Akristu angachite bwino kuganizira mmene Mlengi amaonera kupatulika kwa moyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mawu akuti BASE akuimira building, antenna, span, and earth (nyumba, zipilala zazitali, milatho, ndiponso zitunda zazitali). Maseŵera ameneŵa odumpha kuchoka pamwamba pa zinthu monga nyumba, milatho ndiponso zitunda zazitali akuti n’ngangozi kwambiri moti bungwe la National Park Service ku United States linawaletsa.